Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
AUGUST 12-18
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | TITO 1–FILIMONI
“Uike Akulu”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Paulo sankalimbikitsa maganizo atsankho omwe ambiri pa nthawiyo anali nawo ponena za Akerete. Iye ankadziwa kuti ku Kerete kunali Akhristu omwe Mulungu anawasankha n’kuwadzoza ndi mzimu wake woyera. (Mac. 2:5, 11, 33) Tikutero chifukwa “mumzinda uliwonse” munali Akhristu ambiri omwe ankasonkhana m’mipingo yosiyanasiyana. Ngakhale kuti Akhristu amenewa anali ochimwa, sitikukayikira kuti ankayesetsa kupewa bodza komanso sanali alesi osusuka. Zikanakhala choncho, Yehova akanasiya kuwakonda. (Afil. 3:18, 19; Chiv. 21:8) Mofanana ndi mmene anthu amitundu yonse amachitira, zikuoneka kuti panali Akerete ena amene anali ndi mtima wabwino. Anthu amenewa sankasangalala ndi makhalidwe oipa omwe ankachitika m’dera lawo ndipo anali oti angasinthe atamva mawu a Mulungu.—Ezek. 9:4; yerekezerani ndi Mac. 13:48.
AUGUST 19-25
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 1-3
“Muzikonda Chilungamo Ndipo Muzidana ndi Kusamvera Malamulo”
it-1 1185 ¶1
Chifaniziro
Kodi Yesu wakhala akusonyeza ulemerero wofanana ndi wa Atate ake kuyambira kalekale?
Mwana woyamba wa Mulungu, yemwe ankadziwika ndi dzina lakuti Yesu atabwera padzikoli, anali chifaniziro cha Atate ake. (2 Akor. 4:4) Popeza ndi zoonekeratu kuti Mulungu ankalankhula ndi Mwana wakeyu pamene ankanena kuti, “tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu,” ndiye kuti Mwanayu wakhala ali ndi ulemerero wofanana ndi Atate ake, yemwe ndi Mlengi, kungoyambira pamene analengedwa. (Gen. 1:26; Yoh. 1:1-3; Akol. 1:15, 16) Atabwera padzikoli n’kukhala munthu wangwiro, Mwana ameneyu ankasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Atate ake moti mpake ananena kuti, “amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9; 5:17, 19, 30, 36; 8:28, 38, 42) Ulemerero umenewu unawonjezereka pamene Atate ake, Yehova Mulungu, anamuukitsa ndi thupi lauzimu n’kumupatsa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” (1 Pet. 3:18; Mat. 28:18) Popeza Mulungu “anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba,” Mwana wa Mulunguyu amasonyeza ulemerero wa Atate ake m’njira yapamwamba kwambiri kuposa umene anali nawo asanabwere padziko lapansi. (Afil. 2:9; Aheb. 2:9) Choncho tinganene kuti panopa Mwanayu ndi “chithunzi chenicheni cha Mulungu weniweniyo.”—Aheb. 1:2-4.
it-1 1063 ¶7
Kumwamba
Mawu a pa Salimo 102:25, 26 amagwiritsidwa ntchito ponena za Yehova. Ndiye n’chifukwa chiyani Paulo anawagwiritsa ntchito ponena za Yesu Khristu? N’chifukwa choti Mulungu anagwiritsa ntchito Mwana wake wobadwa yekhayu polenga chilengedwechi. Paulo ankayerekezera kutalika kwa moyo wa Mwanayu ndi chilengedwechi, chomwe Mulungu atafuna, ‘angachipindepinde ngati mkanjo,” n’kuchichotsa.—Aheb. 1:1, 2, 8, 10-12; yerekezerani 1 Pet. 2:3.
AUGUST 26–SEPTEMBER 1
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 4-6
“Yesetsani Kuti Mulowe Mumpumulo wa Mulungu”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 1139 ¶2
Chiyembekezo
Chiyembekezo chomwe Yehova anapereka kwa anthu ‘amene ali m’gulu la oitanidwa kumwamba,’ (Aheb. 3:1) choti adzakhala ndi moyo womwe sungafe komanso thupi lomwe silingawonongeke, n’chotsimikizirika ndipo sichingalephereke. Tikutero chifukwa chiyembekezochi chimagwirizana kwambiri ndi zinthu ziwiri zomwe n’zosatheka kuti Mulungu aname. Zinthu zake ndi zimene analonjeza komanso kulumbira kuti adzachita, ndiponso chiyembekezo chomwe tili nacho chomwe ndi chotheka kudzera mwa Khristu yemwe ali ndi moyo womwe sungathe kufa kumwamba. Choncho chiyembekezo chimenechi chili ngati “nangula wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika. Chiyembekezochi chimatilowetsa mkati, kuseri kwa nsalu yotchinga, kumene Yesu, yemwe ndi kalambulabwalo anakalowa chifukwa cha ife. Iyeyu wakhala mkulu wa ansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”—Aheb. 6:17-20.