PHUNZIRO 7
Kulankhula Zoona Komanso Zofika Pamtima
Luka 1:3
MFUNDO YAIKULU: Muzigwiritsa ntchito maumboni odalirika kuti anthu amene mukukambirana nawo adziwe zoona.
MMENE MUNGACHITIRE:
Muzigwiritsa ntchito maumboni odalirika. Zolankhula zanu zizikhala zochokera m’Mawu a Mulungu ndipo ngati n’zotheka muzichita kuwerenga m’Baibulo. Ngati mukufuna kupereka umboni wochokera kwa asayansi, nyuzi, kapena zinthu zina muzitsimikizira kuti n’zodalirika komanso zolondola.
Muzigwiritsa ntchito bwino maumboniwo. Zimene mukufotokoza pa lemba zizikhala zogwirizana ndi nkhani yonse ya lembalo, Baibulo lonse komanso zimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wafalitsa. (Mat. 24:45) Ngati mukugwiritsa ntchito umboni wina muzionetsetsa kuti ukugwirizana ndi nkhani yonse komanso cholinga cha wolembayo.
Fotokozani m’njira yogwira mtima. Mukawerenga lemba kapena kutchula umboni winawake, muzifunsa mafunso abwino kapena kupereka chitsanzo chothandiza anthu kuzindikira zimene mukutanthauza.