MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Munthu Akhoza Kusintha Akaona Ulemu Komanso Khalidwe Lanu Labwino
Nthawi zambiri, akazi okwatiwa akamasonyeza makhalidwe abwino amathandiza amuna awo kuti ayambe kutumikira Yehova. Koma kuti alongowa achite zimenezi amafunika kupirira kwa zaka zambiri. (1 Pet. 2:21-23; 3:1, 2) Ngati mwamuna wanu amakuponderezani, muyenera kupitirizabe kugonjetsa choipa pochita chabwino. (Aroma 12:21) N’kutheka kuti mwamuna wanu sangamvetsere mukamamuuza za Yehova. Komabe akaona khalidwe lanu labwino, akhoza kukopeka n’kuyamba kuphunzira.
Muziyesetsa kumvetsa zimene zikuchititsa mnzanuyo kuchita zinthu mwa njira inayake. (Afil. 2:3, 4) Muzichita zinthu mokoma mtima komanso muziyesetsa kukwaniritsa udindo wanu. Muzimumvetsera akamafotokoza maganizo ake. (Yak. 1:19) Muzikhala oleza mtima ndipo muzimutsimikizira kuti mumamukonda kwambiri. Ngakhale zitaoneka kuti mnzanuyo sayamikira zimene mumamuchitira, muzikumbukira kuti Yehova amasangalala akamaona kukhulupirika kwanu.—1 Pet. 2:19, 20.
ONERANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA AMATILIMBIKITSA KUTI TITHE KULIMBANA NDI MAVUTO ATHU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi zinthu zinali bwanji a Grace Li atangolowa m’banja?
N’chiyani chinachititsa kuti ayambe kuphunzira Baibulo?
Kodi Mlongo Li anakumana ndi mavuto otani atangobatizidwa?
Kodi Mlongo Li ankapempha chiyani kwa Yehova zokhudza mwamuna wake?
Kodi Mlongo Li anadalitsidwa bwanji chifukwa cholemekeza kwambiri mwamuna wake komanso kusonyeza khalidwe labwino?
Ulemu komanso khalidwe lanu labwino zikhoza kusintha mtima wa mwamuna wanu!