Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 4 tsamba 7
  • Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kufotokoza Bwino Malemba
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kutchula Malemba Moyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuwafika Pamtima Anthu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Mawu Oyamba Abwino
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 4 tsamba 7

PHUNZIRO 4

Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba

Lemba

Mateyu 22:41-45

MFUNDO YAIKULU: Muzithandiza anthu kuti akonzekere kumva mfundo inayake pa lemba limene mukufuna kuwerenga.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Ganizirani chifukwa chimene mukuwerengera lemba. Pouza anthu lemba limene mukufuna kuliwerenga, muzinena mawu amene angawathandize kuzindikira mfundo yofunika imene angaiphunzire palembalo.

    Mfundo yothandiza

    Muziganizira nkhani yonse yokhudza lembalo. Mwachitsanzo, musanatchule munthu amene ananena kapena kulemba mawu a m’Baibulo amene mukufuna kuwerenga, muzitsimikizira kuti munthuyo ndi wolondola.

  • Sonyezani kuti Baibulo ndi lothandiza. Ngati mukukambirana ndi anthu amene amakhulupirira zoti kuli Mulungu, muziwathandiza kuona kuti Baibulo ndi “Mawu a Mulungu” ndipo lingatipatse nzeru yapamwamba kwambiri.

  • Muzithandiza anthu kuti akhale ndi chidwi chofuna kumva mfundo yapalembalo. Funsani funso limene yankho lake lili palembalo, tchulani vuto limene njira yolithetsera ikupezeka palembalo kapena tchulani mfundo imene chitsanzo chake chili palembalo.

    Mfundo yothandiza

    Muziganizira zimene anthu akudziwa kale zokhudza lembalo komanso nkhaniyo. Ngakhale lemba litakhala lodziwika, muzilitchula m’njira imene ingachititse anthu kuyembekezera kuti aphunzirapo mfundo yatsopano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena