Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 13 tsamba 28-29
  • Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tikondweretse Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tikondweretse Mulungu?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Mabwenzi a Mulungu Amapeŵa Zoipa
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Kodi Mulungu Adzawononganso Anthu Oipa?
    Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
  • Kodi N’chiyani Chimene Muyenera Kuchita?
    Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
  • Machitachita Amene Mulungu Amadana Nawo
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 13 tsamba 28-29

CHIGAWO 13

Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tikondweretse Mulungu?

Muzipewa kuchita zinthu zoipa. 1 Akorinto 6:9, 10

Zinthu zimene Mulungu amadana nazo—kuba, kuledzera, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza ubongo, ndewu, kulambira mafano

Ngati timakonda Yehova, tiyenera kupewa kuchita zinthu zimene iye amadana nazo.

Yehova safuna kuti tiziba, tiziledzera kapena tizigwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Mulungu amadana ndi aliyense wopha munthu kapena wochotsa mimba, ndiponso amadana n’zoti anthu azigonana amuna kapena akazi okhaokha. Iye safuna kuti tikhale adyera kapena andewu.

Sitiyenera kulambira mafano kapena kuchita zinthu zogwirizana ndi kukhulupirira mizimu.

M’dziko lapansi la Paradaiso limene likubweralo, simudzakhala anthu ochita zoipa.

  • Kodi Mulungu amaziona bwanji zamatsenga?​—Deuteronomo 18:10-12.

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kulambira mafano?​—Yesaya 44:15-20.

Muzichita zinthu zabwino. Mateyu 7:12

Zinthu zimene Mulungu amasangalala nazo—kukonda anthu ena, kukhala olimba mtima komanso wokhululuka

Kuti tikondweretse Mulungu, tiyenera kuyesetsa kumutsanzira.

Muzikonda anthu ena powakomera mtima ndi kuwathandiza.

Mukhale oona mtima.

Mukhale achifundo ndipo muzikhululukira ena.

A Mboni za Yehova akulalikira bambo wina

Muziuza ena za Yehova ndiponso zochita zake.​—Yesaya 43:10.

  • Tsanzirani Yehova.​—1 Petulo 1:14-16.

  • Muzisonyeza kuti mumakonda anthu ena.​—1 Yohane 4:7, 8, 11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena