Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 67 tsamba 160-tsamba 161 ndime 4
  • “Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyo”
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Alephera Kumgwira
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Alephera Kumugwira Iye
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Tenganipo Phunziro pa Zomwe Nikodemo Anachita
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Yesu Anaphunzitsa Nikodemo
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 67 tsamba 160-tsamba 161 ndime 4
Asilikali amene anatumidwa kuti akagwire Yesu abwera chimanjamanja

MUTU 67

“Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyo”

YOHANE 7:32-52

  • AFARISI ANATUMA ALONDA KUTI AKAGWIRE YESU

  • NIKODEMO ANALANKHULA MOIKIRA KUMBUYO YESU

Yesu anali akadali ku Yerusalemu ku Chikondwerero cha Misasa (kapena kuti Chikondwerero cha Zokolola). Iye anasangalala kwambiri kuona anthu ambiri atayamba kumukhulupirira. Koma zimenezi sizinasangalatse atsogoleri achipembedzo moti anatumiza alonda, omwe anali ngati apolisi otumidwa ndi chipembedzo, kuti akamugwire. (Yohane 7:31, 32) Yesu sanayese n’komwe kuthawa kuti akabisale.

Iye anapitirizabe kuphunzitsa poyera ku Yerusalemuko ndipo ankanena kuti: “Ndikhala nanube kanthawi pang’ono ndisanapite kwa iye amene anandituma. Mudzandifunafuna, koma simudzandipeza, ndipo kumene ndidzapiteko inu simudzatha kukafikako.” (Yohane 7:33, 34) Ayudawo sankamvetsa zimene Yesu ankatanthauza ndipo anayamba kufunsana kuti: “Ameneyu akufuna kupita kuti, kumene ife sitingathe kukam’peza? Kapena akufuna kupita kwa Ayuda omwazikana mwa Agiriki ndi kukaphunzitsa Agirikiwo? Kodi akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mudzandifunafuna, koma simudzandipeza, ndipo kumene ine ndidzapite inu simudzatha kukafikako’?” (Yohane 7:35, 36) Yesu ankanena za imfa yake komanso kuti akadzaukitsidwa adzapita kumwamba, komwe adani akewo sakanatha kumutsatira.

Tsiku la 7 la chikondwerero chija linafika. Pa nthawi yonse ya chikondwererochi, m’mawa uliwonse wansembe ankathira madzi paguwa la nsembe ndipo madziwo ankayenderera pansi pamene panali guwa la nsembelo. Madziwa ankawatunga padziwe la Siloamu. Zimene Yesu ananena ziyenera kuti zinakumbutsa anthu amene ankamvetserawo zimene wansembe ankachita m’mawa uliwonse chifukwa ananena kuti: “Ngati wina akumva ludzu, abwere kwa ine adzamwe madzi. Wokhulupirira mwa ine, ‘Mkati mwake mwenimwenimo mudzatuluka mitsinje ya madzi amoyo,’ monga mmene Malemba amanenera.”—Yohane 7:37, 38.

Ponena mawu amenewa Yesu ankatanthauza zimene zidzachitike ophunzira ake akadzadzozedwa ndi mzimu woyera posonyeza kuti akakhala ndi moyo kumwamba. Anthu opita kumwambawa anayamba kudzozedwa Yesu ataphedwa n’kuukitsidwa. Patatha chaka chimodzi Yesu atanena mawu amenewa madzi amoyo anayamba kuyenda. Zimenezi zinayamba kuchitika pa tsiku la Pentekosite pamene ophunzira a Yesu amene anadzozedwa ndi mzimu woyera anayamba kuphunzitsa anthu choonadi.

Anthu ena atamva zimene Yesu ankaphunzitsa ananena kuti: “Ameneyu ndi Mneneri ndithu.” Iwo ankanena za mneneri wamkulu kuposa Mose amene ankamuyembekezera kuti adzabwera. Ena ananena kuti: “Khristu uja ndi ameneyu.” Koma ena anati: “Iyayi, kodi Khristu angachokere mu Galileya? Kodi Malemba sanena kuti Khristu adzatuluka mwa ana a Davide, komanso mu Betelehemu mudzi umene Davide anali kukhala?”—Yohane 7:40-42.

Choncho anthuwo anali ndi maganizo osiyanasiyana. Ngakhale kuti ena ankafuna kumugwira Yesu, palibe amene anakwanitsa kuchita zimenezo. Alonda aja atabwerera kwa atsogoleri achipembedzo ali chimanjamanja, ansembe aakulu komanso Afarisi anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simunabwere naye?” Alondawo anayankha kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” Atsogoleri achipembedzowo anakwiya kwambiri moti anayamba kulankhula monyoza kuti: “Kodi inunso mwasocheretsedwa? Palibe ndi mmodzi yemwe mwa olamulira kapena Afarisi amene wakhulupirira mwa iye, alipo ngati? Koma khamu lonseli la anthu osadziwa Chilamulo ndi lotembereredwa.”—Yohane 7:45-49.

Nikodemo akulankhula m’malo mwa Yesu

Atangonena zimenezi Nikodemo, yemwe anali Mfarisi komanso yemwe anali mmodzi wa oweruza m’khoti la Sanihedirini analimba mtima n’kuyamba kulankhula moikira kumbuyo Yesu. Zaka ziwiri ndi hafu izi zisanachitike, Nikodemo anapita kwa Yesu usiku ndipo kuchokera nthawi imeneyo anayamba kukhulupirira Yesu. Nikodemo anayamba kulankhula kuti: “Chilamulo chathu sichiweruza munthu asanafotokoze maganizo ake choyamba ndi kudziwa zochita zake, chimatero ngati?” Podziikira kumbuyo anthuwo anayankha Nikodemo kuti: “Kodi iwenso ndiwe wochokera ku Galileya eti? Fufuza ndipo sudzapeza pamene pamati m’Galileya mudzatuluka mneneri.”—Yohane 7:51, 52.

Malemba sananene bwinobwino kuti mneneri adzachokera ku Galileya. Komabe Mawu a Mulungu anafotokoza kuti adzachokera kumeneko chifukwa analosera kuti “kuwala kwakukulu” kudzaonekera “ku Galileya kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina.” (Yesaya 9:1, 2; Mateyu 4:13-17) Komanso mogwirizana ndi zimene Malemba ananena, Yesu anabadwira ku Betelehemu m’banja la Davide. Afarisiwo ankadziwa zimenezo. Komabe anali ndi mlandu wofalitsa zinthu zolakwika n’cholinga choti anthu asamudziwe bwino Yesu.

  • Kodi Yesu ananena chiyani chomwe chinkagwirizana ndi zimene wansembe ankachita m’mawa uliwonse pa nthawi ya chikondwerero?

  • N’chifukwa chiyani alonda aja sanamugwire Yesu, nanga atsogoleri achipembedzo anatani ataona zimenezo?

  • N’chiyani chinasonyeza kuti Yesu adzachokera ku Galileya?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena