Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 6/1 tsamba 3-5
  • Kodi Sayansi Imatithandiza Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Sayansi Imatithandiza Bwanji?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI SAYANSI YAFIKA PATI MASIKU ANO?
  • Kodi Chilengedwe Chonsechi Ndiponso Zamoyozi Zinakhalako Bwanji?
    Galamukani!—2002
  • Kugwirizanitsa Sayansi ndi Chipembedzo
    Galamukani!—2002
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaona Bwanji Sayansi?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Sayansi Kufunafuna Chowonadi kwa Mtundu wa Anthu Komapitirizabe
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 6/1 tsamba 3-5
Zimene sayansi yakwanitsa kuchita monga kupanga galimoto, GPS, masetilaiti, ndege ndi kupanga sikani ubongo

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SAYANSI INGALOWE M’MALO MWA BAIBULO?

Kodi Sayansi Imatithandiza Bwanji?

Buku lina lotanthauzira mawu limanena kuti sayansi ndi “kufufuza zachilengedwe komanso zinthu zina pofuna kudziwa mmene zimachitikira. Pofufuzapo amayeza zinthu, kuyeserera komanso kuona zotsatira zake.” Komatu kuchita zimenezi ndi ntchito yaikulu ndi yotopetsa zedi, chifukwa nthawi zambiri pamatenga nthawi yaitali akugwira ntchitoyi. Ndipotu nthawi zina sapeza n’komwe yankho la zimene akufufuzazo. Komabe nthawi zambiri amapeza zimene akufuna kudziwazo ndipo zimakhala zothandiza kwa anthufe. Taonani zitsanzo izi.

Kampani ina ya ku Europe inaphatikiza mapulasitiki ndi zinthu zina n’kupanga zosefera madzi. Zosefera madzizi zimathandiza kuti anthu azimwa madzi aukhondo, makamaka pakachitika mavuto ogwa mwadzidzidzi. Mwachitsanzo, zinathandiza kwambiri pa nthawi ya chivomerezi chomwe chinachitika ku Haiti mu 2010.

Asayansi apanga chipangizo china chothandiza kudziwa mapu a dziko lonse chotchedwa GPS. Chipangizochi chimagwiritsa ntchito setilaiti ndipo chimathandiza munthu kudziwa kumene akupita. Poyamba asilikali ndi amene ankagwiritsa ntchito GPS. Koma masiku ano imagwiritsidwanso ntchito ndi oyendetsa galimoto, oyendetsa ndege, oyenda panyanja, alenje komanso okwera mapiri. Izi zikusonyeza kuti asayansi anagwira ntchito yotamandika popanga chipangizochi chifukwa n’chothandiza kwambiri.

Ambirife timagwiritsa ntchito foni, kompyuta kapena Intaneti. Ena akafuna kupita kwinakwake amakwera ndege. Palinso anthu ambiri omwe anachira kapena kukhala ndi moyo wathanzi chifukwa cha mankhwala enaake. Zonsezi zikusonyeza kuti zimene asayansi apanga, zimatithandiza m’njira zosiyanasiyana.

KODI SAYANSI YAFIKA PATI MASIKU ANO?

Asayansi akufufuza chilengedwechi kuti adziwe zambiri. Ena akuyesetsa kufufuza zambiri zokhudza maatomu. Pomwe ena akufufuza zomwe zinachitika zaka mabiliyoni apitawo n’cholinga choti adziwe kuti zinthu zamoyo zinachokera kuti. Asayansi enanso afika kutali kwambiri m’mlengalenga ndipo amaona kuti Mulungu yemwe amatchulidwa m’Baibulo akanakhala kuti alipodi, bwenzi atamupeza.

Wolemba mabuku wina dzina lake Amir D. Aczel ananena kuti “asayansi komanso afilosofi ena atafufuza kwambiri, anayamba kukayikira zoti Mulungu alipo.” Mwachitsanzo, wasayansi wina wotchuka padziko lonse ananena kuti: “Popeza sitinapeze umboni uliwonse wosonyeza kuti kuli Mulungu yemwe analenga zinthu, m’pomveka kuganiza kuti Mulunguyo kulibe.” Ena amaganiza kuti si zoona kuti kuli Mulungu wotchulidwa m’Baibulo ndipo nkhani zonena za zimene Mulungu ankachita, n’zongofuna kupusitsa anthu. Amaonanso kuti amene amakhulupirira zimenezi amangokhulupirira zamatsenga.a

Komabe, kodi panopa asayansi akudziwa zonse zokhudza chilengedwechi moti zonse zomwe anganene zingakhale zolondola? Ayi. N’zoona kuti sayansi yapita patsogolo kwambiri, komabe asayansi ambiri amadziwa kuti padakali zinthu zambiri zomwe sakuzidziwa komanso zoti sangathe kuzidziwa. Wasayansi wina, dzina lake Steven Weinberg, anati: “Ngakhale titayesetsa bwanji, sitidzadziwa zonse.” Pulofesa wina, dzina lake Martin Rees, ananenanso kuti: “Pali zinthu zambiri zimene anthufe sitingathe kuzimvetsa.” Apa mfundo ndi yakuti, ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo, asayansi sangatithandize kudziwa zonse. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

  • DNA

    Asayansi samvetsa zimene zimachitika mkati mwa selo. Sakudziwa bwinobwino kuti maselo amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zimene amapeza kuchokera ku dzuwa, zakudya ndi zinthu zina. Sakudziwanso kuti maselowa amapanga bwanji mapuloteni komanso kuti amachulukana bwanji.

  • Mnyamata akunjanjitsa mpira

    Mphamvu yokoka ya dziko lapansi imathandiza kwambiri. Komatu asayansi sadziwa bwinobwino mmene mphamvuyi imagwirira ntchito. Mwachitsanzo, sadziwa kuti mphamvuyi imatikokera bwanji pansi tikadumpha m’mwamba. Sadziwanso mmene mphamvuyi imathandizira kuti mwezi uzizungulira dziko lapansili.

  • Chithunzi cha chilengedwe chonse

    Asayansi ena amaganiza kuti 95 peresenti ya zinthu zakuthambo ndi zinthu zosaoneka ndipo ngakhale atagwiritsa ntchito zipangizo zawo sangathe kuzitulukira. Asayansiwa sadziwanso mmene zinthu zimenezi zimagwirira ntchito.

Wasayansi winanso wotchuka anati: “Zinthu zimene timadziwa ndi zochepa kwambiri poyerekeza ndi zimene sitidziwa. Choncho wasayansi sayenera kumangokhutira ndi zomwe amadziwa. Ineyo ndimaona kuti ukamafufuza zambiri za sayansi, m’pamene umaonanso kuti pali zambiri zomwe sudziwa.”

Ndiyeno ngati mumaona kuti sayansi yangotsala pang’ono kulowa m’malo mwa Baibulo kapena kupangitsa anthu kuti asamakhulupirire Mulungu, mungachite bwino kuganizira mfundo iyi: Ngati akatswiri asayansi omwe ali ndi zipangizo zamphamvu kwambiri sakudziwabe zonse zokhudza chilengedwechi, kodi ndi bwino kufulumira kuganiza kuti Mulungu kulibe chifukwa choti asayansi sanapeze umboni woti alipo? Mpake kuti buku lina limanena kuti, “ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo kwambiri, zimene tikudziwa panopa sizikusiyana kwenikweni ndi zimene akatswiri ofufuza zakuthambo akale, monga a ku Babulo, ankadziwa zaka 4,000 zapitazo. Zikuoneka kuti padakali zambiri zimene sitikuzidziwa.”—Encyclopedia Britannica.

A Mboni za Yehova amadziwa kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha zimene akufuna kukhulupirira pa nkhaniyi. Amachita zimenezi chifukwa amatsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” (Afilipi 4:5) Komabe, tikukupemphani kuti muone kugwirizana kwa zimene asayansi apeza ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani zasayansi.

a Anthu ena sakhulupirira Baibulo chifukwa cha zimene matchalitchi ena amaphunzitsa. Matchalitchiwa amaphunzitsa kuti dziko lapansili ndiye pakati pa chilengedwe chonse komanso kuti Mulungu analenga dzikoli m’masiku 6 enieni a maola 24.—Onani bokosi lakuti, “Baibulo Silitsutsana Ndi Mfundo Zolondola Zasayansi.”

Baibulo Silitsutsana Ndi Mfundo Zolondola Zasayansi

N’zoona kuti Baibulo si buku lophunzitsa sayansi. Komabe, zimene anthu olemba Baibulo analemba zokhudza sayansi sizitsutsana ndi mfundo zolondola zasayansi. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

  • Chithunzi cha chilengedwe chonse

    Kutalika kwa nthawi yomwe dziko lapansili komanso chilengedwe chonse chakhalako

    Asayansi amati dziko lapansili lakhalako zaka pafupifupi 4 biliyoni ndiponso chilengedwe chonse chakhalapo zaka 13 kapena 14 biliyoni. Baibulo silinena kutalika kwa nthawi yomwe chilengedwe chonse chakhalako. Komanso silinena kuti dziko lapansili langokhalapo zaka masauzande ochepa. Vesi loyambirira la m’Baibulo linangonena kuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Popeza Baibulo langoti “pa chiyambi,” zimene asayansi amapeza zokhudza kutalika kwa nthawi imene dzikoli komanso chilengedwe chonse chakhalapo, sitingati n’zotsutsana ndi zimene Baibulo limanena pavesili.

  • Mapiri, zomera ndi madzi

    Mulungu sanalenge dziko lapansili m’masiku 6 enieni

    Chaputala 1 cha Genesis chimagwiritsa ntchito mawu akuti “tsiku” pofotokoza nthawi imene Mulungu anayamba kukonza dziko lapansi kuti pakhale zamoyo. Limanenanso kuti pomaliza, Mulungu analenga anthu. Baibulo silinena kuti masiku 6 amene Mulungu analenga zinthu, anali aatali bwanji. Choncho asayansi akhoza kufufuza n’kudziwa kuti nthawi imene Mulungu analenga dzikoli inali yaitali bwanji. Timadziwa kuti masiku 6 amene Mulungu analenga zinthuwa, si a maola 24 enieni.

  • Dziko lapansi

    Dziko lapansili lili m’malere

    Baibulo limanena kuti dziko lapansili lili “m’malere.” (Yobu 26:7) Baibulo silinena kuti dzikoli lili pamsana pa njovu zomwe zaima pamsana pa kamba wamkulu wa m’madzi, ngati mmene anthu ena akale ankaganizira. Komabe silinenanso chimene chimapangitsa kuti dzikoli likhale m’malere. Wasayansi wina dzina lake Nicolaus Copernicus, ndi wina dzina lake Johannes Kepler anapeza kuti pali mphamvu inayake imene imathandiza kuti mapulaneti azikhala m’malere n’kumayenda mozungulira dzuwa. Kenako wasayansi winanso, dzina lake Isaac Newton, anatulukira kuti mphamvu yokoka imathandiza kuti zinthu zonse m’mlengalenga ziziyenda mwadongosolo.

  • Mabakiteriya

    Malangizo okhudza ukhondo komanso kupewa matenda

    M’buku la Levitiko muli malangizo omwe ankathandiza Aisiraeli kupewa matenda opatsirana. Mulinso malamulo ena onena kuti munthu wodwala matenda opatsirana azikhala kwayekha. Komanso lamulo lomwe lili pa Deuteronomo 23:12, 13 linkathandiza Aisiraeli kuti azikhala aukhondo. Linkanena kuti munthu akafuna kudzithandiza, azipita kunja kwa msasa ndipo akamaliza ‘azikwirira zoipazo.’ Komatu si kale kwambiri pamene asayansi komanso madokotala anatulukira kuti malamulo amenewa ndi othandiza ndipo nawonso amalimbikitsa anthu kuti azitsatira malangizowa.

Mfundo za m’Baibulo zimene zili m’nkhaniyizi, zinalembedwa kale kwambiri. Ndiye kodi anthu amene analemba Baibulo, anakwanitsa bwanji kulemba zolondola zokhudza sayansi, pomwe anthu ophunzira a m’nthawi yawo sankadziwa mfundo zimenezi? N’chifukwa choti anathandizidwa ndi Mulungu yemwe ndi wanzeru kuposa anthu. Mulungu amatiuza m’Baibulo kuti: “Monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi, momwemonso njira zanga n’zapamwamba kuposa njira zanu, ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.”—Yesaya 55:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena