Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya February 2020
JANUARY 6-12
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 1-2
“Yehova Analenga Zamoyo Padziko Lapansi”
it-1 527-528
Chilengedwe
Zikuoneka kuti pa tsiku loyamba, pamene Mulungu ananena kuti “Pakhale kuwala,” kuwalako kunayamba kudutsa m’mitambo kufika padziko lapansi. Komabe zinthu zomwe zinkapereka kuwalako sizinkaoneka padzikoli. Zikuoneka kuti sikunawale kamodzin’kamodzi. Izi ndi zomwe womasulira mabuku wina dzina lake J. W. Watts ananena. Iye anati: “Kuwala kunayamba kuonekera pang’onopang’ono.” (Gen. 1:3, A Distinctive Translation of Genesis) Kenako Mulungu analekanitsa kuwala ndi mdima, ndipo kuwalako anakutchula kuti Usana pomwe mdima anautchula kuti Usiku. Zimenezi zikusonyeza kuti dziko linali litayamba kuzungulira dzuwa moti mbali imene yayang’ana dzuwalo inkakhala masana pomwe mbali inayo inkakhala usiku.—Gen. 1:3, 4.
Pa tsiku lachiwiri Mulungu anati pakhale mlengalenga ndipo zimenezi zinachititsa kuti pakhale “cholekanitsa pakati pa madzi ndi madzi.” Madzi ena anakhalabe padziko lapansi pamene ena ochuluka kwambiri anakwera m’mwamba ndipo pakati pa madzi a m’mwambawo ndi a pansiwo, panali mlengalenga. Mulungu anatchula mlengalengawo kuti Kumwamba, potengera kuti dziko lapansi linali m’munsi mwake. Tikutero chifukwa madzi amene anali pamwamba pamlengalengawo sanafike kumene kuli nyenyezi ndi mapulaneti ena.—Gen. 1:6-8.
Pa tsiku lachitatu Mulungu anagwiritsa ntchito mphamvu zake pochititsa kuti madzi a padziko lapansi asonkhane pamodzi ndipo mtunda unaonekera. Mulungu anatchula mtundawo kuti Dziko. Pa tsiku limeneli anachititsa kuti padzikoli pakhale udzu, zomera zina komanso mitengo yazipatso. Sikuti zinthuzi zinangokhalako zokha koma Mulungu anachita kuzilenga. Zinthuzi zinali zoti zizichulukana monga mwa “mtundu wake.”—Gen. 1:9-13.
it-1 528 ¶5-8
Chilengedwe
N’zochititsa chidwi kuti pa Genesis 1:16 sanagwiritse ntchito mawu a Chiheberi akuti ba·raʼʹ, omwe amatanthauza “kulenga.” M’malomwake anagwiritsa ntchito mawu a Chiheberi akuti ʽa·sahʹ, omwe amatanthauza “kupanga.” Popeza dzuwa, mwezi komanso nyenyezi zikuphatikizidwapo pa “kumwamba” komwe kwatchulidwa pa Genesis 1:1, zikuoneka kuti zinthuzi zinali zitalengedwa kale lisanafike tsiku la 4. Pa tsiku la 4 Mulungu anachititsa kuti zinthu zimenezi ziyambe kuonekera. Baibulo likamanena kuti Mulungu “anaziika kuthambo kuti ziunikire dziko lapansi,” limakhala likutanthauza kuti zinthuzi zinayamba kuonekera padziko lapansi n’kumakhala ngati zili mlengalenga. Zounikirazi zinaikidwa kutinso “zikhale zizindikiro, komanso kuti zisonyeze nyengo ndi masiku ndi zaka” zomwe zinadzakhala zothandiza kwambiri kwa anthu m’njira zosiyanasiyana.—Gen. 1:14.
Pa tsiku la 5 m’pamene Mulungu analenga zamoyo zoyambirira padziko lapansi. Sikuti anangolenga chinthu chimodzi n’kuchisiya kuti chizisintha n’kukhala zinthu zina. Koma anagwiritsa ntchito mphamvu zake polenga zamoyo zosiyanasiyana. Baibulo limati: “Mulungu analenga zilombo zikuluzikulu za m’nyanja ndi chamoyo chilichonse chokhala mmenemo. Nyanja inatulutsa zimenezi zambirimbiri monga mwa mitundu yake. Analenganso chamoyo chilichonse chouluka monga mwa mtundu wake.” Mulungu anasangalala kwambiri ndi zimene analenga ndipo anazidalitsa ponena kuti ‘zichuluke.’ N’zotheka kuti zamoyozi zizichulukana chifukwa Mulungu anazilenga kuti ziziberekana “monga mwa mitundu yake.”—Gen. 1:20-23.
Pa tsiku la 6 Mulungu anati, “Dziko lapansi likhale ndi zamoyo monga mwa mitundu yake, nyama zoweta, nyama zokwawa, komanso nyama zakutchire monga mwa mitundu yake.” Ataona zimene analengazi anasangalala nazo monga anachitira ndi zoyamba zija.—Gen. 1:24, 25.
Chakumapeto kwa tsiku lolenga la 6, Mulungu analenga cholengedwa chosiyana kwambiri ndi zinthu zonse zimene anali atazilenga kale. Cholengedwa chimenechi chinali chapamwamba kuposa zinyama, koma chotsikirapo poyerekeza ndi angelo. Cholengedwachi ndi munthu ndipo analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. Lemba la Genesis 1:27 limanena kuti Mulungu analenga “mwamuna ndi mkazi.” Komabe lemba la Genesis 2:7-9 lomwe limanena nkhani yomweyi limafotokoza mwatsatanetsatane kuti Mulungu anaumba munthu kuchokera kufumbi lapansi ndipo anauzira mpweya wa moyo mphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo. Mulungu anamuika m’paradaiso kuti azikhalamo komanso anamupatsa zakudya. Pamenepa Mulungu anagwiritsa ntchito zinthu zomwe anali atalenga kale kuti apange munthuyu ndipo kenako anapanga mkazi pogwiritsa ntchito nthiti yake. (Gen. 2:18-25) Mkaziyu atalengedwa, tinganene kuti nawonso anthu anali oti akhoza kumaberekana “monga mwa mtundu wawo.”—Gen. 5:1, 2.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 52
Yesu Khristu
Kodi nayenso Yesu ndi Mlengi? N’zoona kuti Yesu anagwira nawo ntchito yolenga zinthu. Komabe zimenezi sizikumuchititsa kuti akhale Mlengi mofanana ndi Atate wake chifukwa Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu ya mzimu woyera yochokera kwa Mulungu. (Gen. 1:2; Sal. 33:6) Komanso popeza Yehova ndiye kasupe wa moyo, zamoyo zonse, kaya zooneka kapena zosaoneka, zinakhalapo chifukwa cha iye. (Sal. 36:9) Choncho Mwanayu si Mlengi mofanana ndi Atate wake, koma Mulungu anangomugwiritsa ntchito polenga zinthu. Nayenso Yesu ananena kuti Mulungu ndi amene analenga zonse ndipo izi ndi zimenenso malemba amanena.—Mat. 19:4-6.
JANUARY 13-19
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 3-5
“Mavuto Omwe Anabwera Chifukwa cha Bodza Loyamba”
it-2 186
Zowawa Zapobereka
Umenewu ndi ululu womwe mayi amamva akamabereka. Hava atangochimwa, Mulungu anauza mkazi woyambayu kuti azidzamva kuwawa kwambiri pa nthawi yobereka. Akanapanda kuchimwa, Mulungu akanapitirizabe kumudalitsa ndipo kubereka sikukanakhala kowawa popeza “madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.” (Miy. 10:22) Koma chifukwa choti anali atachimwa, thupi lake lopanda ungwiro linachititsa kuti azimva kuwawa. N’chifukwa chake Mulungu ananena kuti: “Ndidzawonjezera kuvutika kwako pamene uli ndi pakati. Pobereka ana udzamva zowawa.” (Gen. 3:16) (Nthawi zambiri Baibulo likamanena kuti Mulungu walola kuti zinazake zichitike limazinena ngati wazichititsa ndi iyeyo.)
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 192 ¶5
Lameki
Ndakatulo yomwe Lameki anapekera akazi ake (Gen. 4:23, 24), imasonyeza kuti anthu pa nthawiyo ankakonda zachiwawa kwambiri. Ndakatuloyi imati: “Tamverani mawu anga inu akazi a Lameki. Tcherani khutu ku zonena zanga: Ndapha munthu chifukwa chondipweteka, ndaphadi, mnyamata chifukwa chondimenya. Ngati wopha Kaini ati adzalangidwe maulendo 7, ndiyetu wopha ine Lameki, adzalangidwa maulendo 77.” Apa Lameki ankadziikira kumbuyo kuti anapha munthu podziteteza osati ngati zimene Kaini anachita popha m’bale wake mwadala. Lameki ankauza akazi akewo kuti podziteteza, wapha munthu yemwe anamumenya n’kumuvulaza. Choncho iye anapeka ndakatuloyi podziteteza kwa anthu amene ankafuna kumubwezera chifukwa chopha munthuyo.
it-1 338 ¶2
Kunyoza Mulungu
“Kuitanira pa dzina la Yehova” komwe kunkachitika chigumula chisanachitike mu nthawi ya Enosi kunali kosayenera. Zimenezi zinali zosiyana ndi zimene Abele ankachita. (Gen. 4:26; Aheb. 11:4) Akatswiri ena ananena kuti anthu amenewa ankatchula dzina la Mulungu mosayenera polipereka kwa anthu kapena mafano. Ngati ankachitadi zimenezi, ndiye kuti ankanyoza Mulungu.
JANUARY 27–FEBRUARY 2
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 9-11
“Dziko Lonse Lapansi Linali ndi Chilankhulo Chimodzi”
it-1 239
Babulo Wamkulu
Mmene Mzinda Wakale wa Babulo Unalili. Mzindawu womwe unali m’chigwa cha Sinara unamangidwa pamene anthu ankafuna kumanga Nsanja ya Babele. (Gen. 11:2-9) Cholinga chenicheni chimene anthuwa ankamangira nsanja komanso mzindawu sichinali kulemekeza dzina la Mulungu. Koma anthuwo ankafuna kudzipangira ‘dzina loti atchuke nalo.’ Mabwinja a nsanja zina zakale omwe anapezeka ku Babulo komanso ku Mesopotamiya amasonyeza kuti anthu ankagwiritsa ntchito nsanjazi polambira. Zimene Yehova anachita posokoneza ntchito yomanga nsanja ya Babele zimasonyeza kuti iye ankaona kuti anthuwa ankafuna kuyambitsa kulambira konyenga. Dzina lakuti Babele, m’Chiheberi limatanthauza “Chisokonezo,” pomwe m’Chisumeri dzinali ndi Ka-dingir-ra, m’Chiakadi ndi Bab-ilu. Mayina onsewa amatanthauza “Chipata cha Mulungu.” Choncho anthu omwe anatsala mumzindawu anasintha pang’ono dzinali kuti lisinthe tanthauzo. Komabe dzina latsopanoli limagwirizanitsabe mzindawo ndi chipembedzo.
it-2 202 ¶2
Chilankhulo
Nkhani ya m’buku la Genesis imanena kuti anthu amene anakhalapo pambuyo pa chigumula ankagwirizana chifukwa cha chilankhulo moti anayamba kumanga nsanja kuti asabalalikane. Izi zinali zosemphana ndi cholinga cha Mulungu chomwe anauza Nowa ndi ana ake. (Gen. 9:1) M’malo moti abalalikire mbali zosiyanasiyana ‘n’kudzaza dziko lapansi,’ anthuwo anaganiza zokhazikika malo amodzi m’dera lina lomwe linayamba kudziwika kuti Chigwa cha Sinara ku Mesopotamiya. Zikuoneka kuti iwo ankafuna kuti malowa akhale likulu lachipembedzo komanso kuti kukhale nsanja yaitali.—Gen. 11:2-4.
it-2 202 ¶3
Chilankhulo
Mulungu Wamphamvuyonse anasokoneza ntchito yomanga nsanja pochititsa kuti anthu asiye kugwirizana, ndipo anachita zimenezi posokoneza chilankhulo chawo. Zimenezi zinachititsa kuti ntchito yomanga nsanja isiye kuyenda bwino ndipo anthu anabalalikira padziko lonse. Izi zinachititsanso kuti kuipa kusachuluke mofulumira kwambiri chifukwa anthuwo sakanathanso kuchitira zinthu limodzi kuti akwaniritse zolinga zawo zadyera. Komanso chinenero chinachititsa kuti azivutika kugawana nzeru, osati zochokera kwa Mulungu, koma zomwe anapeza poona zimene zinawachitikira pa moyo wawo komanso pochita kafukufuku. (Yerekezerani ndi Mlal. 7:29; Deut. 32:5.) Ngakhale kuti kusokonezeka kwa chilankhulo kunachititsa kuti anthu asamagwirizane, zimenezi zinalinso ndi ubwino wake. Tikutero chifukwa zinachititsa kuti zolinga zoipa komanso zoopsa za anthu, zisachitike mwachangu. (Gen. 11:5-9; yerekezerani ndi Yes. 8:9, 10.) Kungoganizira zimene anthu akukwanitsa kuchita masiku ano chifukwa cha nzeru zimene apeza komanso mavuto amene abwera chifukwa chogwiritsa ntchito nzeruzo molakwika, kungatithandize kudziwa kuti Mulungu anaoneratu mavuto omwe akanabwera ngati zolinga zomanga nsanja ya Babele zikanapitirira.
it-2 472
Mitundu ya Anthu
Mulungu atasokoneza chilankhulo cha anthu, kagulu kalikonse kanayamba kukhala ndi chikhalidwe, luso, miyambo, zochita komanso chipembedzo chawochawo moti aliwonse anayamba kuchita zinthu zosiyana kotheratu ndi anzawo. (Lev. 18:3) Chifukwa choti anasiya kulambira Mulungu, anthuwa anayamba kudzipangira mafano.—Deut. 12:30; 2 Maf. 17:29, 33.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 1023 ¶4
Hamu
N’kutheka kuti Kanani anapalamula nawo ndipo Hamu yemwe anali bambo ake sanamudzudzule. Mwinanso Nowa anayankhula mawu amenewa monga ulosi ataona mtima woipa wa Hamu, womwe n’kuthekanso kuti unkaonekera mwa mwana wake Kanani. Ngati zili choncho ndiye kuti Kanani akanapatsiranso mtima umenewu ana ake. Tembereroli linakwaniritsidwa pamene Aisiraeli omwe anali ana a Semu, anagonjetsa Akanani. Akanani amene sanawonongedwe (mwachitsanzo Agibeoni [Yos. 9]) anakhala akapolo awo. Patadutsa zaka zambiri, tembereroli linakwaniritsidwanso pamene ana a Kanani yemwe anali mwana wa Hamu ankaponderezedwa ndi maulamuliro amphamvu padziko lonse monga a Mediya ndi Perisiya, Girisi komanso Roma, omwe anali ana a Yafeti.
it-2 503
Nimurodi
Ufumu wa Nimurodi unkaphatikizapo mizinda ya Babele, Ereke, Akadi ndi Kaline yomwe inali m’dziko la Sinara. (Gen. 10:10) Choncho n’kutheka kuti Nimurodi ndi amene analamula kuti anthu amange mzinda wa Babele ndi nsanja yake. Zimenezi zikufanananso ndi zomwe Ayuda ankakhulupirira. Mwachitsanzo, katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Josephus analemba kuti: “Pang’ono ndi pang’ono [Nimurodi] anayamba kulamulira mwankhanza. Cholinga chake chinali kupangitsa anthu kuti asiye kuopa Mulungu n’kumadalira mphamvu za iyeyo. Iye ankafuna kubwezera Mulungu ngati ataganizanso zowononga dziko lapansi ndi madzi. Choncho analimbikitsa anthu kuti ayambe kumanga nsanja yaitali kwambiri yoti ikafike kumwamba yomwe sikanamizidwa ndi madzi ndipo ankafuna kuti adzagwiritsire ntchito nsanjayo pobwezera imfa ya makolo awo omwe anaphedwa pa chigumula. Anthu anasangalala kwambiri kumva zimene [Nimurodi] anawauza, chifukwa ankaona kuti kumvera Mulungu ndi ukapolo moti anayamba kumanga nsanja. Nsanjayo inayamba kukwera mofulumira kwambiri.”—Jewish Antiquities, I, 114, 115 (iv, 2, 3).