PHUNZIRO 1
Mawu Oyamba Abwino
Machitidwe 17:22
MFUNDO YAIKULU: M’mawu anu oyamba, muyenera kunena zinthu zochititsa chidwi, kutchula zokhudza nkhani yanu komanso kusonyeza chifukwa chake nkhaniyo ili yothandiza kwambiri kwa omvera.
MMENE MUNGACHITIRE:
Kukopa chidwi. Sankhani funso, mawu enaake, zochitika zenizeni kapena nkhani imene omvera anu angachite nayo chidwi.
Fotokozani nkhani yanu. M’mawu anu oyamba muyenera kuthandiza anthu kudziwa nkhani imene mukambirane komanso cholinga chake.
Sonyezani chifukwa chake nkhaniyo ndi yofunika. Konzekerani nkhani yanu m’njira yoti igwirizane ndi zimene zingathandize anthu amene mukukambirana nawo. Anthuwo ayenera kuona mosavuta kuti nkhaniyo iwathandizadi.