Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 3 tsamba 6
  • Kugwiritsa Ntchito Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwiritsa Ntchito Mafunso
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kuwafika Pamtima Anthu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 3 tsamba 6

PHUNZIRO 3

Kugwiritsa Ntchito Mafunso

Lemba

Mateyu 16:13-16

MFUNDO YAIKULU: Muzigwiritsa ntchito mafunso oyenera kuti anthu akhale ndi chidwi, kuti mukambirane ndi anthu, komanso kuti mutsindike mfundo zofunika.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzithandiza anthu kuti akhale ndi chidwi. Muzifunsa mafunso othandiza anthu kuti azifuna kumva zambiri.

  • Muzikambirana ndi anthu. Kuti anthu akhulupirire mfundo zimene mukunena, muyenera kufunsa mafunso angapo owathandiza kuti atsatire mpaka kufika potsimikizira mfundozo.

  • Muzitsindika mfundo zofunika. Funsani funso limene lingachititse anthu kuyembekezera kuti amve mfundo yofunika. Muzifunsa mafunso obwereza pambuyo pa mfundo yofunika iliyonse kapena pomaliza nkhani yanu.

    Mfundo yothandiza

    Mukawerenga lemba, muzifunsa mafunso amene angathandize anthu kumvetsa mfundo yaikulu yamulembalo.

MU UTUMIKI

Muzifunsa anthu mafunso kuti afotokoze maganizo awo pa nkhani imene mukukambirana. Ndiye muzimvetsera pamene akufotokoza. Muyenera kuchita zinthu mozindikira kuti mudziwe nthawi yoyenera kufunsa funso komanso njira yabwino yofunsira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena