Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 18 tsamba 21
  • Nkhani Yophunzitsadi Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhani Yophunzitsadi Anthu
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kulankhula ndi Mtima Wonse
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuwafika Pamtima Anthu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 18 tsamba 21

PHUNZIRO 18

Nkhani Yophunzitsadi Anthu

Lemba

1 Akorinto 9:19-23

MFUNDO YAIKULU: Muzithandiza anthu kuganiza mpaka kufika pozindikira kuti aphunziradi mfundo zothandiza.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Ganizirani zimene anthu akudziwa kale. M’malo mongofotokoza zimene anthu akuzidziwa kale, athandizeni kuiganizira nkhaniyo m’njira yatsopano.

    Mfundo yothandiza

    Mfundo zomwe anthu akuzidziwa kale muzizitchula mofulumira koma mukafika pa mfundo zatsopano muzilankhula pang’onopang’ono.

  • Muzifufuza komanso kuganizira kwambiri nkhaniyo. Ngati n’zotheka, muzigwiritsa ntchito mfundo zimene anthu sakuzidziwa kwambiri kapena nkhani zimene zangochitika kumene pofotokozera mfundo zikuluzikulu. Muziganizira kwambiri nkhani yanu n’kumaona ngati mfundo zimene mukufuna kugwiritsa ntchito zikugwirizanadi ndi nkhaniyo.

    Mfundo yothandiza

    Mukamaganizira nkhaniyo, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi akuti chiyani pamenepa, chifukwa chiyani, zinachitika liti, zinachitika kuti, akunena za ndani, nanga zinachitika bwanji?’ Ndiyeno mukamakamba nkhani yanu muzifunsa mafunso ngati amenewa n’kumawayankha.

  • Muzithandiza anthu kuona kuti nkhaniyo ndi yofunika kwambiri. Muzifotokoza mmene Malemba angathandizire anthu pa moyo wawo. Muzifotokoza mfundo zogwirizana ndi zimene zimachitikira anthu, zimene anthu amachita komanso zimene anthu amaganiza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena