Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Khulupirirani Yehova—Osati mu “Chiwembu!”
    Nsanja ya Olonda—1987
    • kuchitira umboni mapeto a dziko lakale mu Chigumula chomwe chinamiza mtundu wonse wa anthu kunja kwa chingalawa, iye adzatero, pa maziko okulirapo, kukhalanso ndi mboni pano padziko lapansi ponena za kachitidwe kosadzabwerezedwanso ka kuyeretsa iyemwini monga Wolamulira Wachilengedwe chonse. (2 Petro 3:6, 7, 13, 14) Awa adzakhala awo amene amakhulupirira mwa iye kaamba ka mtendere ndi chisungiko mkati mwa dziko lodetsedwali. Achimwemwe mudzakhala inu pamene mudzaŵerengedwa pakati pa Mboni zoyanjidwa mozizwitsa zimenezo. Mtendere wanu ndi chisungiko zidzakhala zitasonyezedwa kukhala zochokera kwa Yehova Mulungu ndipo osati ku chigwirizano chirichonse, kapena chiwembu, ndi mphamvu za ndale zadziko za dongosolo ili la kachitidwe ka zinthu lolamuliridwa ndi Mdyerekezi.

      20. Ndimotani mmene Yehova adzatulukira, ndipo nchiyani chimene tifunikira kugamulapo kuchita?

      20 Yehova Mulungu adzatuluka wolemekezedwa monga Mmodzi woyenera kulambiridwa ndi kutumikiridwa monga wokhalako Wamkulukulu Waumulungu​—Mulungu wa milungu, wopambana Mmodzi kwa amene mawu ouziridwa a wamasalmo anatsogozedwa: “Kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha inu ndinu Mulungu.” (Masalmo 90:2) Ndi chiyamikiro chomakulakulabe, lolani kuti tisunge kukhulupirira kwathu mwa Yehova Mulungu ndi maunansi athu ndi iye kupyolera mwa Koresi Wamkulu, Yesu Kristu.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1987
    • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

      ◼ Kodi nchiyani chimene chiri “bukhu la moyo” la Mulungu, ndipo kodi ndimotani mmene dzina langa lingalembedwere mu ilo ndi kusungidwa mmenemo?

      Malemba ambiri a Baibulo amasonyeza kuti Yehova Mulungu ali ndi “bukhu,” kapena “mpukutu,” wondandalitsa anthu okhulupirika omwe ali mu mzera wa kulandira moyo wosatha kaya kumwamba kapena padziko lapansi.

      Kuchokera kumwamba Mulungu wowona amadziŵa anthu omwe amasonyeza chikhulupiriro, oyenerera chivomerezo chake ndi chikumbukiro. Timaŵerenga ponena za Ayuda ena mu tsiku la Malaki: “Pamenepo iwo akuwopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake . . . ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi bukhu la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.”​—Malaki 3:16.

      Mwachiwonekere, kuyambira panthaŵi ya Abele kunka mtsogolo, Mulungu wakhala akudziŵa, monga ngati kulemba m’bukhu, awo a mu dziko la mtundu wa anthu okhoza kupulumutsidwa omwe ayenera kukumbukiridwa kaamba ka moyo wosatha. (Mateyu 23:35; Luka 11:50, 51) Akristu odzozedwa, nawonso, anali ndi ‘maina awo m’bukhu limeneli la moyo,’ kapena bukhu la chikumbukiro kaamba ka kulandira moyo wosatha ndipo kwa iwo umenewo ukakhala moyo wa kumwamba.​—Afilipi 3:14, 20; 4:3. Mosiyanako, Chivumbulutso 17:8 chimanena za awo amene “amazizwa mokhumbira” pa “chirombocho”: “Maina awo sanalembedwa m’bukhu la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi.”

      Koma kukhala kwa munthu wodziŵidwa mwa kukumbukiridwa ndi kuvomerezedwa (kukhala ndi dzina lake “m’bukhu la moyo”) sikumatanthauza kuti iye wayeneretsedwa kaamba ka moyo wamuyaya, ngati kuti ichi chinali chonenedweratu kapena chosasunthika. Ponena za Aisrayeli, Mose anafunsa Yehova: “Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kuchimwa kwawo,​—koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundichotsa m’bukhu lanu limene munalemba.” Mulungu anayankha: “Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m’bukhu langa.” (Eksodo 32:32, 33) Inde, ngakhale pambuyo pa kundandalitsa kwa Mulungu winawake ndi chivomerezo mu “bukhu” lake, munthuyo angakhale wosamvera kapena kusiya kukhulupirika kwake. Ngati chimenecho chichitika, Mulungu “adzafafaniza dzina lake kuchokera m’bukhu la moyo.”​—Chivumbulutso 3:5.

      Kumbali ina, ngati maina athu tsopano ali mu “bukhu la moyo” la Mulungu, kapena “bukhu la chikumbukiro,” tifunikira kupitiriza kusonyeza chikhulupiriro. Mu njira imeneyo tidzasunga maina athu mmenemo. Mofananamo, pamene anthu adzaukitsidwa mu ‘chiukiriro cha osalungama’ chikudzacho, iwo adzakhala ndi mwaŵi wa kusonyeza chikhulupiriro ndipo chotero kuyenerera kukhala ndi maina awo olembedwa m’bukhu limenelo. (Machitidwe 24:15) Pomalizira, aliyense payekha wolembedwa adzakhala wokhoza kusunga dzina lake mmenemo kosatha. Ichi chiri chowona ndi odzozedwa pamene akudzitsimikizira iwo eni kukhala “okhulupirika kufikira imfa.” (Chivumbulutso 2:10; 3:5) Ponena za awo okhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi, mwakutsimikizira kukhala okhulupirika tsopano, mpaka mu ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu, ndipo kenaka kupyola chiyeso chodzisankhira chodzatsatira, maina awo adzakhala “olembedwa m’bukhu la moyo kosatha.”​—Chivumbulutso 20:5-15.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena