Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
JANUARY 11-17
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 20-21
“Yehova Amafuna Kuti Anthu Ake Azikhala Osiyana ndi Ena”
it-1 1199
Cholowa
Cholowa ndi katundu kapena zinthu zina zimene mwiniwake akamwalira zimaperekedwa kwa woyenera kupatsidwa zinthuzo, kaya mwana wake kapena kwa munthu wina. Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “cholowa” ndi na·chalahʹ. Mawuwa amanena za kulandira kapena kupereka zinthu zakumtundu kwa munthu wina, ndipo nthawi zambiri wolandirayo amalowa m’malo mwa womwalirayo. (Nu 26:55; Eze 46:18) Mawu ena ofanana nawo akuti ya·rashʹ nthawi zina ankagwiritsidwa ntchito ponena za “wolowa m’malo” koma nthawi zambiri ankagwiritsidwa ntchito ponena za “kutenga katundu.” (Ge 15:3; Le 20:24) Mawuwa amatanthauzanso ‘kuthamangitsa anthu pamalo n’kulanda malowo,’ mwankhondo. (De 2:12; 31:3) Mawu a Chigiriki amene anawagwiritsa ntchito ponena za cholowa ndi wofanana ndi mawu akuti kleʹros. Poyamba mawuwa ankatanthauza “maere” koma kenako anayamba kutanthauza “kukhala ndi gawo” ndipo kenako anayamba kutanthauza “cholowa.”—Mt 27:35; Mac 1:17; 26:18.
it-1 317 ¶2
Mbalame
Chigumula chitatha, Nowa anapereka nsembe ya ‘zouluka zoyera’ komanso nyama zina. (Ge 8:18-20) Pambuyo pake Mulungu analola kuti anthu azidya mbalame koma asamadye ndi magazi omwe. (Ge 9:1-4; yerekezerani ndi Le 7:26; 17:13.) Pa nthawi imeneyo, mbalame inkatengedwa kuti ndi ‘yoyera’ ngati Mulungu anavomereza kuti iziperekedwa nsembe. Baibulo limasonyeza kuti pa nkhani yogwiritsa ntchito mbalame monga chakudya, palibe mbalame imene inkaonedwa kuti ndi “yodetsedwa” mpaka pamene Chilamulo cha Mose chinayamba kugwira ntchito. (Le 11:13-19, 46, 47; 20:25; De 14:11-20) Baibulo silifotokoza bwinobwino zifukwa zimene zinkachititsa kuti mtundu winawake wa mbalame uzionedwa kukhala ‘wodetsedwa.’ Ngakhale kuti mbalame zambiri zomwe zinkaonedwa kuti ndi zodetsedwa ndi zimene zinkapha nyama zina n’kudya, kapena zomwe zinkadya nyama zakufa kale, si mbalame zonse zimene zinkachita zimenezi zomwe zinkaonedwa kuti ndi zodetsedwa. Kuletsa anthu kudya mitundu ina ya nyama kapena mbalame, kunatha pamene pangano latsopano linakhazikitsidwa monga mmene Mulungu anauzira Petulo m’masomphenya.—Mac 10:9-15.
Mfundo Zothandiza
it-1 563
Kudzicheka
Chilamulo chinkaletsa kudzicheka chifukwa cha munthu yemwe wafa. (Le 19:28; 21:5; De 14:1) Chilamulo chinkaletsa Aisiraeli kuchita zimenezi chifukwa iwo anali mtundu woyera kwa Yehova komanso chuma chake chapadera. (De 14:2) Aisiraeli ankafunika kuti asamachite china chilichonse chokhudzana ndi kulambira mafano. Choncho sankayenera kuchita nawo miyambo imene anthu a mitundu ina ankachita akaferedwa monga kudzichekacheka. Izi zinali choncho chifukwa Aisiraeliwo ankadziwa bwino zimene zimachitika munthu akamwalira komanso anali ndi chikhulupiriro choti akufa adzauka. (Da 12:13; Ahe 11:19) Kuwonjezera pamenepo, kuletsa Aisiraeli kuti asamadzivulaze kunawathandiza kuti azilemekeza thupi lawo, lomwe ndi chilengedwe cha Mulungu.
JANUARY 18-24
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 22-23
“Zikondwerero Zomwe Zimatikhudza”
it-1 826-827
Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa
Tsiku loyamba la Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa linkakhala la msonkhano wapadera komanso tsiku la sabata. Pa tsiku lachiwiri, pa Nisani 16, Aisiraeli ankafunika kupititsa kwa wansembe mtolo umodzi wa balere woyamba kucha ku Palesitina. Chikondwererochi chisanachitike, sankayenera kudya mbewu zimene akolola kumene, kuzigwiritsa ntchito popangira mkate kapena kudya zokazinga. Wansembe ankapereka kwa Yehova mophiphiritsa zokolola zoyamba kuchazi mochita kuweyula mtolo wake uku ndi uku. Mwana wa nkhosa wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi ankaperekedwanso monga nsembe yopsereza limodzi ndi nsembe ya ufa wothira mafuta komanso vinyo wa nsembe yachakumwa. (Le 23:6-14) Panalibe lamulo loti aziwotcha mbewu kapena ufa wake paguwa, ngati zimene pambuyo pake ansembe anayamba kuchita. Sikuti pachikondwererochi Aisiraeli ankangopereka nsembe ya zokolola zoyamba kucha monga gulu basi, koma banja kapena munthu aliyense yemwe akufuna kuthokoza Mulungu chifukwa cha zinthu zomwe anali nazo, ankathanso kupereka nsembe yoyamikira.—Eks 23:19; De 26:1, 2.
Kufunika kwa Mwambowu. Kudya mikate yopanda chofufumitsa kunali kogwirizana ndi malangizo amene Yehova anapatsa Mose omwe amapezeka pa Ekisodo 12:14-20. Ena mwa malangizowo chinali chiletso champhamvu chomwe chili muvesi 19 chakuti: “Musamadzapezeke mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa m’nyumba zanu kwa masiku 7.” Pa Deuteronomo 16:3, mikate yopanda chofufumitsa imatchedwa “mkate wa nsautso,” ndipo chaka chilichonse mikateyi inkakumbutsa Ayuda kuti anachoka ku Iguputo mofulumira kwambiri (analibe nthawi yoika zofufumitsa m’mikate yawo [Eks 12:34]). Zimenezi zinkakumbutsanso Aisiraeli kuti Yehova anawapulumutsa ku ukapolo komanso masautso awo, monga mmene Yehova ananenera kuti, “uzichita zimenezi kuti uzikumbukira tsiku limene unatuluka m’dziko la Iguputo, masiku onse a moyo wako.” Ufulu umene anali nawo pa nthawiyo monga mtundu komanso kuzindikira kuti Yehova ndi amene anawapulumutsa, zinali zifukwa zomveka zomwe zinawachititsa kuti apange chikondwerero chawo choyamba pa zikondwerero zikuluzikulu zitatu zimene ankachita chaka chilichonse.—De 16:16.
it-2 598 ¶2
Pentekosite
Zimene ankachita ndi tirigu woyamba kucha, zinali zosiyana ndi zimene ankachita ndi balere woyamba kucha. Ankatenga ufa wa tirigu wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa (omwe ndi malita 4.4), kuikamo zofufumitsa n’kupanga mikate iwiri. Mikateyi inkafunika kuchokera ‘m’nyumba mwawo’ kutanthauza kuti inkafunika kukhala yofanana ndi imene ankapanga tsiku ndi tsiku monga chakudya chapakhomo, osati yongopangira zochitika zapadera. (Le 23:17) Mikate imeneyi ankaipereka nsembe pamodzi ndi nsembe yopsereza komanso nsembe yamachimo. Ankaperekanso ana a nkhosa amphongo awiri monga nsembe yachiyanjano. Wansembe ankaweyula mikateyo ndi ana a nkhosawo pamaso pa Yehova. Poweyulapo ankanyamula mikateyo komanso nthuli za nyamayo ndipo ankayendetse manja ake uku ndi uku posonyeza kuti akupereka zinthuzo kwa Yehova. Akamaliza, zinthuzo zinkakhala zake ndipo ankazidya monga nsembe yachiyanjano.—Le 23:18-20.
JANUARY 25-31
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 24-25
“Chaka cha Ufulu Komanso Ufulu Womwe Tidzakhale Nawo M’tsogolo”
it-1 871
Ufulu
Mulungu Amapereka Ufulu. Yehova ndi Mulungu amene amapereka ufulu. Anapulumutsa Aisiraeli ku ukapolo ku Iguputo. Anawauza kuti akamamvera malamulo ake, sadzakhala osauka. (De 15:4, 5) Davide ananena za kukhala “opanda nkhawa iliyonse” munsanja za ku Yerusalemu. (Sl 122:6, 7) Komabe m’Chilamulo munali lamulo lakuti ngati munthu wasauka, akhoza kudzigulitsa n’kukhala kapolo kuti azitha kudzisamalira komanso kusamalira banja lake. Koma Chilamulo chinkanenanso kuti m’chaka cha 7 cha ukapolo wake, munthu ameneyu azipatsidwa ufulu. (Eks 21:2) M’Chaka cha Ufulu (chomwe chinkachitika pakatha zaka 50), ankalenga za ufulu kwa anthu onse okhala m’dzikomo. Zikatero Mheberi aliyense ankamasuka ku ukapolo ndipo ankabwerera kumalo ake omwe anali cholowa chake.—Le 25:10-19.
it-1 1200 ¶2
Cholowa
Popeza malo ankakhala chuma chakubanja ndipo ankachoka kwa m’badwo wina kupita m’badwo wina, sizikanatheka kuti akagulitsidwa azikhala a munthu wogulayo mpaka kalekale. Malo ankagulitsidwa potengera kuchuluka kwa zokolola zomwe wogulayo adzapeze pamalowo ndipo mtengo wake unkadalira zaka zimene zatsala kuti Chaka cha Ufulu chifike. Chakachi chikafika malo onse amene anagulitsidwa ankabwezedwa kwa eniake ngati eniakewo sanathe kuwagulanso kapena kuwawombola. (Le 25:13, 15, 23, 24) Lamuloli linkagwiranso ntchito pa nyumba zomwe zinali m’mizinda yopanda mipanda, chifukwa nazonso zinkatengedwa ngati malo. Koma nyumba ikakhala kuti inali mumzinda wa mpanda, mwayi wogulanso nyumbayo unkakhalapo kwa chaka chimodzi ndipo ngati mwiniwake sanathe kuigulanso pa nthawi imeneyi, inkakhala ya wogulayo. Pomwe nyumba zomwe zinali m’mizinda ya Alevi, mwayi wozigulanso unkakhalapo mpaka kalekale chifukwa Alevi analibe cholowa cha malo.—Le 25:29-34.
it-2 122-123
Chaka cha Ufulu
Lamulo lokhudza Chaka cha Ufulu likamatsatiridwa, linkathandiza kuti ku Isiraeli kusamachitike zomwe zikuchitika m’mayiko ambiri masiku ano, zoti anthu ena ndi olemera kwambiri pamene ena ndi osaukitsitsa. Lamuloli linkathandiza mtundu wonse chifukwa panalibe munthu wongokhala chifukwa cha umphawi, koma aliyense anali ndi mwayi wogwiritsa ntchito luso lake kuchita zinthu zomwe zinkathandiza mtundu wonsewo. Pa nthawi imene Aisiraeli ankamvera Yehova, iye n’kumadalitsa zokolola zawo komanso kuwaphunzitsa, ankasangalala ndi ulamuliro wake ndiponso zinthu zinkawayendera bwino.—Yes 33:22.
FEBRUARY 1-7
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 26-27
“Kodi Mungatani Kuti Yehova Azikudalitsani?”
it-1 223 ¶3
Kuopa
Chifukwa cha mmene Yehova ankagwiritsira ntchito Mose komanso kuchitira naye zinthu, Moseyo ankachita zinthu zamphamvu pamaso pa Aisiraeli. (De 34:10, 12; Eks 19:9) Anthu amene anali ndi chikhulupiriro ankamuopa chifukwa cha udindo waukulu umene anali nawo. Iwo ankadziwa kuti Mulungu ankalankhula nawo kudzera mwa iye. Aisiraeli ankafunikanso kuopa malo opatulika a Yehova. (Le 19:30; 26:2) Zimenezi zikutanthauza kuti ankafunika kumalemekeza kwambiri malo opatulika, kulambira Yehova m’njira imene amavomereza komanso kutsatira malamulo ake onse.
“Mtendere wa Mulungu” Uziteteza Mtima Wanu
10 Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Mukapitiriza kutsatira malangizo anga ndi kusunga malamulo anga, ndidzakugwetserani mvula pa nthawi yake. Nthaka idzakupatsani chakudya, ndipo mitengo ya m’munda idzakupatsani zipatso zake. Ndidzakupatsani mtendere m’dzikolo, moti mudzagona pansi popanda wokuopsani. M’dziko lanu simudzapezeka zilombo zoopsa zakutchire, ndipo simudzadutsa lupanga. Motero ndidzayendadi pakati panu ndi kukusonyezani kuti ine ndine Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga.” (Levitiko 26:3, 4, 6, 12) Aisiraeli ankakhala pamtendere chifukwa anali otetezeka kwa adani awo, anali ndi chuma komanso anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Koma kuti zimenezi zitheke ankafunika kumatsatira Chilamulo cha Yehova.—Salimo 119:165.
Mfundo Zothandiza
it-2 617
Miliri
Yobwera Chifukwa Chosiya Kutsatira Chilamulo cha Mulungu. Aisiraeli anachenjezedwa kuti akadzasiya kutsatira pangano lawo ndi Mulungu, Mulunguyo ‘adzawatumizira mliri.’ (Le 26:14-16, 23-25; De 28:15, 21, 22) Malemba amasonyeza kuti kukhala ndi thanzi labwino, kaya mwakuthupi kapena mwauzimu, ndi kogwirizana ndi madalitso a Yehova (De 7:12, 15; Sl 103:1-3; Miy 3:1, 2, 7, 8; 4:21, 22; Chv 21:1-4), pamene matenda ndi ogwirizana ndi uchimo komanso kupanda ungwiro. (Eks 15:26; De 28:58-61; Yes 53:4, 5; Mt 9:2-6, 12; Yoh 5:14) Ngakhale kuti nthawi zina Yehova ankachititsa kuti munthu adwale matenda enaake nthawi yomweyo, ngati mmene zinaliri ndi khate la Miriamu, Uziya komanso Gehazi (Nu 12:10; 2Mb 26:16-21; 2Mf 5:25-27), zikuoneka kuti nthawi zambiri matenda kapena miliri zinkakhala zotsatira za zolakwa zimene anthu kapena mtundu wachita. Ankakhala kuti akukolola zimene anafesa. Ankakumana ndi mavuto chifukwa cha zochita zawo zoipa. (Aga 6:7, 8) Ponena za anthu achiwerewere, mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu “anawasiya kuti achite zonyansa, kuti matupi awo achitidwe chipongwe . . . ndi kulandiriratu mphoto yoyenerera kulakwa kwawo.”—Aro 1:24-27.
FEBRUARY 8-14
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 1-2
“Yehova Amachita Zinthu Mwadongosolo ndi Anthu Ake”
Kuika Kulambira Yehova Pamalo Oyamba pa Moyo Wathu
4 Tiyerekeze kuti muli m’mwamba ndipo mukuyang’ana malo amene Aisiraeli ankakhala m’chipululu, kodi mukanaona zotani? Mukanaona malo aakulu okhala ndi matenti oyalidwa mwadongosolo okhalamo anthu 3 miliyoni kapena kuposa. Anthuwo agawidwa m’magulu a mafuko atatuatatu ndipo gulu lina lili kumpoto, lina kummwera, lina kum’mawa ndipo lina kumadzulo. Mutayang’anitsitsa mukuonanso timagulu tina 4 tamatenti tomwe tili pafupi ndi pakati pamalowo. M’timatenti timeneti munkakhala mabanja a fuko la Levi. Pakati penipeni, panali “chihema chokumanako” chotchingidwa ndi nsalu chimene Aisiraeli “aluso” anamanga mogwirizana ndi pulani ya Yehova.—Numeri 1:52, 53; 2:3, 10, 17, 18, 25; Ekisodo 35:10.
it-1 397 ¶4
Msasa
Msasa wa Aisiraeliwu unkakhala waukulu kwambiri. Munkakhala asilikali okwana 603,550, akazi ndi ana, anthu achikulire, olumala, Alevi 22,000 komanso ‘khamu la anthu a mitundu ina yosiyanasiyana,’ ndipo n’kutheka kuti onse pamodzi ankakwana 3 miliyoni kapena kuposa. (Eks 12:38, 44; Nu 3:21-34, 39) Sizikudziwika kuti msasa umenewu unkakwana malo aakulu bwanji chifukwa anthu amanena zosiyanasiyana. Baibulo limati Aisiraeli atamanga msasa moyang’anizana ndi Yeriko m’Zigwa za Mowabu, msasawo ‘unayambira ku Beti-yesimoti mpaka ku Abele-sitimu.’—Nu 33:49.
Mfundo Zothandiza
it-2 764
Kulembetsa M’kaundula
Nthawi zambiri ankalemba dzina la munthu ndiponso mzere wobadwira potengera fuko lake komanso banja lomwe anabadwira. Cholinga sichinali kungopeza chiwerengero cha anthu. Kulembetsa m’kaundula komwe kumatchulidwa m’Baibulo kunkachitika pa zifukwa zosiyanasiyana monga zokhudza kukhoma msonkho, kupeza oyenera kupita kunkhondo kapenanso kusankha okagwira ntchito pamalo opatulika (ngati anthuwo ndi Alevi).
FEBRUARY 15-21
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 3–4
“Utumiki wa Alevi”
it-2 683 ¶3
Wansembe
M’Pangano la Chilamulo. Pamene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo, Yehova anadzipatulira mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pawo, pa nthawi imene anapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo ndi mliri wa 10. (Eks 12:29; Nu 3:13) Ana oyamba kubadwa amenewa anakhala a Yehova kuti azimuchitira utumiki wapadera. Yehova akanatha kusankha ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli kuti azikhala ansembe komanso kuti azisamalira malo opatulika. Koma m’malomwake, anaona kuti n’koyenera kungotenga amuna achilevi kuti azichita utumiki umenewu. Pachifukwa chimenechi, Yehova analola kuti amuna achilevi alowe m’malo mwa amuna oyamba kubadwa a mafuko ena 12 (Efuraimu ndi Manase omwe anali ana a Yosefe ankatengedwa monga mafuko awiri). Atawerenga ana onse aamuna oyamba kubadwa a mwezi umodzi kupita m’tsogolo, panapezeka kuti ana omwe si achilevi anachuluka ndi 273 kuposa ana oyamba kubadwa achilevi. Chifukwa cha zimenezi, Yehova analamula Mose kuti atenge masekeli asanu (omwe ndi madola 11) pa munthu aliyense monga dipo la ana aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli okwana 273 omwe anapitirira chiwerengero cha Alevi, ndipo ndalamazo akazipereke kwa Aroni ndi ana ake. (Nu 3:11-16, 40-51) Zimenezi zisanachitike, Yehova anali atapatula kale amuna a m’banja la Aroni omwe anali a fuko la Levi kuti azitumikira monga ansembe mu Isiraeli.—Nu 1:1; 3:6-10.
it-2 241
Alevi
Ntchito Zawo. Fuko la Alevi linkapangidwa ndi mabanja atatu a ana a Levi, omwe anali Gerisoni (Gerisomu), Kohati ndi Merari. (Ge 46:11; 1Mb 6:1, 16) Banja lililonse linkapatsidwa malo pafupi ndi chihema m’chipululu. Banja la Kohati, lomwe munali Aroni, linkakhala kutsogolo kwa chihema kum’mawa, pomwe Akohati ena onse ankakhala kum’mwera kwa chihema. Agerisoni ankakhala kumadzulo ndipo Amerari ankakhala kumpoto. (Nu 3:23, 29, 35, 38) Ntchito yomanga, kuphwasula komanso kunyamula chihema inali ya Alevi. Nthawi yosamuka ikakwana, Aroni ndi ana ake ankatsitsa nsalu imene inkalekanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa ndipo ankaphimbira likasa la chipangano, maguwa a nsembe ndi zinthu zina zopatulika. Akohati ndi amene ankanyamula zinthuzi. Agerisoni ankanyamula nsalu za chihema, nsalu zophimbira, nsalu zotchinga pakhomo, nsalu za mpanda wa bwalo ndiponso zingwe za chinsalu (zimenezi ziyenera kuti zinali zingwe za chihema chenichenicho). Pomwe Amerari anali ndi ntchito yosamalira mafelemu, mizati, zitsulo zokhazikapo nsanamira, zikhomo ndi zingwe zolimbitsira nsanamira (izi zinali zingwe za nsanamira za bwalo la chihema).—Nu 1:50, 51; 3:25, 26, 30, 31, 36, 37; 4:4-33; 7:5-9.
it-2 241
Alevi
M’nthawi ya Mose, Mlevi ankayamba kugwira ntchito zake zonse akakwanitsa zaka 30 ndipo ntchito zake zinali monga kunyamula chihema komanso zinthu zogwiritsa ntchito pachihemachi akamasamuka. (Nu 4:46-49) Alevi ankayamba kugwira ntchito zina akakwanitsa zaka 25 koma sizinkakhala zolemetsa ngati kunyamula chihema. (Nu 8:24) Munthawi ya Mfumu Davide, zakazi zinachepetsedwa kufika pa 20. Davide ananena kuti anachita zimenezi chifukwa choti pa nthawiyi chihema sichinkafunikanso kunyamulidwa chifukwa chinali choti chilowedwa m’malo ndi kachisi. Alevi ankasiya kugwira ntchito zawo akakwanitsa zaka 50. (Nu 8:25, 26; 1Mb 23:24-26) Alevi ankafunika azidziwa kwambiri Chilamulo chifukwa ankayenera kuwerengera anthu pagulu komanso kuphunzitsa Chilamulocho.—1Mb 15:27; 2Mb 5:12; 17:7-9; Ne 8:7-9.
FEBRUARY 22-28
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 5-6
“Kodi Mungatsanzire Bwanji Anaziri?”
it-2 477
Mnaziri
Panali malamulo atatu akuluakulu amene munthu amene walumbira kukhala Mnaziri ankayenera kuwatsatira: (1) Sankafunika kumwa chakumwa chilichonse choledzeretsa. Sankafunikanso kudya kapena kumwa chilichonse chochokera ku mtengo wa mpesa. Mwachitsanzo, sankafunika kudya mphesa zosapsa, zakupsa kapena zouma. Sankafunikanso kumwa madzi a mphesa zongothyola kumene, zosasa kapena viniga wochokera ku mphesazo. (2) Sankafunika kumeta tsitsi la m’mutu mwawo. (3) Sankafunikanso kugwira mtembo wa munthu, kaya munthuyo akhale bambo awo, mayi awo, mchimwene wawo kapena mchemwali wawo.—Nu 6:1-7.
Malumbiro Apadera. Munthu amene wachita lonjezo lapadera limeneli ankayenera kukhala “Mnaziri [kutanthauza wodzipereka] kwa Yehova.” Sankafunika kumakokomeza moyo wodzimana umene ankakhala n’cholinga chofuna kudzionetsera kwa anthu. M’malomwake ‘iye ankakhala woyera kwa Yehova masiku onse a unaziri wake.’—Nu 6:2, 8.
Choncho zinthu zimene Anaziri ankafunira kumachita, zinali ndi tanthauzo lapadera pa nkhani ya kulambira Yehova. Mofanana ndi mkulu wansembe, amene sankafunika kugwira mtembo wa munthu chifukwa cha udindo wake, ngakhale munthuyo atakhala wachibale wake wapafupi, nayenso Mnaziri sankafunika kuchita zimenezi. Komanso mkulu wansembe ndiponso ansembe ena, chifukwa cha udindo wawo wapadera, sankafunika kumwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa akamachita utumiki wawo wopatulika pamaso pa Yehova.—Le 10:8-11; 21:10, 11.
Komanso Mnaziri (m’Chiheberi na·zirʹ) ankayenera kukhala “woyera mwa kusiya tsitsi lake la kumutu kuti likule,” ndipo zimenezi zinkachititsa kuti anthu azimuzindikira mosavuta kuti ndi Mnaziri. (Nu 6:5) Mawu a Chiheberi omwewa akuti na·zirʹ ankagwiritsidwanso ntchito ponena za mitengo ya mphesa ‘yosadulira’ pa nthawi ya Sabata lopatulika komanso Chaka cha Ufulu. (Le 25:5, 11) Chochititsanso chidwi n’chakuti kachitsulo kamene kankakhala patsogolo panduwira ya mkulu wansembe, pomwe pankagobedwa mawu akuti “Chiyero n’cha Yehova,” ankakatchula kuti “chizindikiro chopatulika cha kudzipereka” [m’Chiheberi neʹzer, kuchokera ku mawu omwe aja akuti, na·zirʹ]. (Eks 39:30, 31) Komanso chisoti chachifumu chimene mafumu odzozedwa a Chiisiraeli ankavala chinkadziwikanso kuti neʹzer. (2Sa 1:10; 2Mf 11:12) Ponena za zomwe zimachitika mumpingo wa Chikhristu, mtumwi Paulo ananena kuti mkazi anapatsidwa tsitsi lalitali m’malo mwa chovala kumutu. Tsitsili limamukumbutsa kuti malo ake ndi osiyana ndi a mwamuna ndipo amafunika kugonjera dongosolo la Mulungu. Choncho zimene Anaziri ankafunira kumachitazi, zomwe ndi kusameta tsitsi, kupeweratu kumwa vinyo komanso kukhala wosadetsedwa, zinkawakumbutsa kufunika kokhala odzimana ndiponso ogonjera zofuna za Yehova.—1Ak 11:2-16.