Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
MARCH 1-7
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 7-8
“Zimene Tingaphunzire pa Zomwe Zinkachitika pa Msasa wa Aisiraeli”
it-1 497 ¶3
Mpingo
Ku Isiraeli, nthawi zambiri anthu audindo ankachita zinthu poimira anthu ena onse. (Eza 10:14) Choncho Mose atamaliza kumanga chihema chopatulika, “atsogoleri a mafuko” anapereka zopereka. (Nu 7:1-11) Komanso m’nthawi ya Nehemiya, anthu amene anatsimikizira ndi chidindo “pangano lodalirika” anali ansembe, Alevi ndi ‘atsogoleri a anthu.’ (Ne 9:38–10:27) Aisiraeli ali m’chipululu, amuna okwana 250 omwe anali “atsogoleri a anthuwo, owaimira kumisonkhano, amuna otchuka,” anagwirizana ndi Kora, Datani, Abiramu ndi Oni n’kuukira Mose ndi Aroni. (Nu 16:1-3) Komanso potsatira zimene Yehova anamuuza, Mose anasankha akulu 70 mwa akulu a Aisiraeli amene anali oyang’anira kuti amuthandize “kusenza udindo woyang’anira anthuwo” womwe unkamukulira. (Nu 11:16, 17, 24, 25) Lemba la Levitiko 4:15 limatchula za “akulu a khamu la Isiraeli,” ndipo zikuoneka kuti amuna audindo amenewa omwe ankaimira anthu, anali akulu a Isiraeli, atsogoleri, oweruza ndi akapitawo.—Nu 1:4, 16; Yos 23:2; 24:1.
it-2 796 ¶1
Rubeni
Pamsasa wa Aisiraeli, fuko la Rubeni, fuko la Simiyoni komanso la Gadi linkakhala kum’mwera kwa chihema chopatulika. Akamasamuka pamsasapo, mafuko atatu amenewa, omwe fuko la Rubeni ndi lomwe linkatsogola, ankabwera pambuyo pa fuko la Yuda, la Isakara ndi la Zebuloni. (Nu 2:10-16; 10:14-20) Dongosolo limeneli ndi limenenso anatsatira pamene mafuko ankapereka zopereka zawo pa tsiku limene chihema chopatulika anachitsegulira.—Nu 7:1, 2, 10-47.
Mfundo Zothandiza
it-1 835
Mwana Woyamba Kubadwa
Chifukwa choti ana aamuna oyamba kubadwa a Chiisiraeli ankadzakhala atsogoleri a mabanja awo, iwo ankaimira mtundu wonse wa Isiraeli. Ndipotu Yehova anatchula mtundu wonse wa Isiraeli kuti ndi mwana wake “woyamba kubadwa” chifukwa cha pangano lake ndi Abulahamu. (Eks 4:22) Chifukwa choti anapulumutsa ana oyamba kubadwa, Yehova analamula kuti azimupatulira “mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa, wa munthu ndi wa chiweto, pakati pa ana a Isiraeli.” (Eks 13:2) Choncho ana aamuna oyamba kubadwa ankakhala a Yehova.
MARCH 8-14
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 9-10
“Yehova Amatsogolera Anthu Ake”
it-1 398 ¶3
Msasa
Zimene zinkachitika akamasamutsa msasa, womwe unali waukulu kwambiri, kuchoka pamalo ena kupita pamalo ena, zimasonyeza kuti zinthu zinkachitika mwadongosolo kwambiri. (Mu Numeri chaputala 33 Mose anatchula za maulendo pafupifupi 40 a kusamuka kotereku.) Pa nthawi yonse imene mtambo waima pamwamba pa chihema chopatulika, Aisiraeli sankasamuka pamsasapo. Koma mtambowo ukanyamuka, iwonso ankanyamuka. “Yehova akalamula, iwo ankamanga msasa, ndipo Yehova akalamula, iwo ankanyamuka.” (Nu 9:15-23) Kulira kwa malipenga awiri asiliva ndi kumene kunkawathandiza kudziwa zoti Yehova walamula kuti amange msasa kapena anyamuke. (Nu 10:2, 5, 6) Lipenga lolira mosinthasintha linkasonyeza kuti akuyenera kunyamuka. Lipenga lotere linalira koyamba “m’chaka chachiwiri [1512 B.C.E.], mwezi wachiwiri, pa tsiku la 20.” Likasa la pangano ndi limene linali patsogolo. Pambuyo pake panabwera gulu loyamba la mafuko atatu, omwe ndi fuko la Yuda, limene linali patsogolo, kenako la Isakala ndipo kenako la Zebuloni. Pambuyo pawo panabwera Agerisoni ndi Amerari atanyamula mbali zina za chihema chopatulika. Kenako panabwera gulu lachiwiri la mafuko atatu, omwe ndi fuko la Rubeni, limene linali patsogolo, kenako la Simiyoni ndipo kenako la Gadi. Pambuyo pa amenewa panabwera Akohati atanyamula zinthu za m’malo opatulika. Kenako panabwera gulu lachitatu la mafuko atatu omwe ndi fuko la Efuraimu, la Manase ndi la Benjamini. Pomaliza panabwera gulu lina lomwe linkateteza kumbuyo limene patsogolo panali fuko la Dani, kenako la Aseri ndipo kenako la Nafitali. Choncho magulu awiri omwe anali ndi anthu ambiri komanso amphamvu kwambiri anaikidwa kuti aziteteza, lina kutsogolo lina kumbuyo.—Nu 10:11-28.
Mfundo Zothandiza
it-1 199 ¶3
Kusonkhana
Kufunika Kosonkhana. Malangizo okhudza Pasika amene Aisiraeli anapatsidwa amasonyeza kufunika kosonkhana kuti tipindule ndi chakudya chauzimu chimene Yehova amatipatsa. Mwamuna aliyense amene si wodetsedwa kapena sanapite pa ulendo wautali, koma wanyalanyaza kuchita mwambo wa Pasika, ankayenera kuphedwa. (Nu 9:9-14) Pamene Mfumu Hezekiya ankaitana anthu a ku Yuda ndi ku Isiraeli kuti apite ku Yerusalemu kuchikondwerero cha Pasika anawauza kuti: “Inu ana a Isiraeli, bwererani kwa Yehova . . . musaumitse khosi lanu ngati mmene anachitira makolo anu. Gonjerani Yehova, pitani kunyumba yake yopatulika imene waiyeretsa mpaka kalekale. Tumikirani Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake umene wakuyakirani ukuchokereni. . . . Yehova Mulungu wanu ndi wachisomo ndiponso wachifundo, ndipo sadzayang’ana kumbali mukabwerera kwa iye.” (2Mb 30:6-9) Kulephera mwadala kupita ku Pasika kunkasonyeza kuti munthuyo akukana Mulungu. Ngakhale kuti Akhristufe sitichita zikondwerero monga Pasika, Paulo anatilimbikitsa kuti sitiyenera kunyalanyaza misonkhano imene anthu a Mulungu amakhala nayo. Iye anati: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.”—Ahe 10:24, 25.
MARCH 15-21
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 11-12
“N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupewa Mtima Wodandaula?”
it-2 719 ¶4
Kukangana
Kung’ung’udza. Kung’ung’udza kumafooketsa anthu ndipo kumawonongetsa zambiri. Pasanapite nthawi kuchokera pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo, iwo anayamba kung’ung’udzira Yehova, kuti sakuwatsogolera bwino kudzera mwa Mose ndi Aroni. (Eks 16:2, 7) Kudandaula kwawo kunafooketsa kwambiri Mose moti anafuna kuti angofa. (Nu 11:13-15) Kung’ung’udza n’koopsa kwambiri kwa amene akung’ung’udzayo. Yehova ankaona kuti anthu amene akung’ung’udzira Mose akugalukira ulamuliro wa Yehovayo. (Nu 14:26-30) Anthu ambiri anaphedwa chifukwa chokonda kung’ung’udza.
Mfundo Zothandiza
it-2 309
Mana
Mmene Analili. Mana anali ‘oyera ngati njere ya mapira’ ndipo ankaoneka ngati utomoni woonekera mkati ngati galasi. Ankakoma ngati “makeke opyapyala othira uchi” kapena “ngati keke yotsekemera yothira mafuta.” Ankawapera pamphero kapena kuwasinja mumtondo, akatero ankawawiritsa mumphika kapena kuwapanga makeke ozungulira.—Eks 16:23, 31; Nu 11:7, 8.
MARCH 22-28
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 13-14
Mfundo Zothandiza
it-1 740
Dziko Limene Mulungu Anapatsa Aisiraeli
DZIKO limene Mulungu anapatsa Aisiraeli linalidi dziko labwino. Mose atatuma anthu kuti akafufuze zokhudza Dziko Lolonjezedwa n’kutengako zina mwa zipatsa za m’dzikolo, anthuwo anabweretsa nkhuyu, makangaza ndi nthambi yokhala ndi tsango lalikulu la mphesa moti anthu awiri anachita kulinyamula paphewa ndi mitengo yonyamulira. Ngakhale kuti anabwerako ali ndi mantha chifukwa chosowa chikhulupiriro, anabweretsa lipoti lakuti: “Ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi.”—Nu 13:23, 27.
MARCH 29–APRIL 4
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 15-16
Mfundo Zothandiza
Muzionetsetsa Kuti Mukuika Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba
Yehova sanaone kuti nkhaniyi ndi yaing’ono. Baibulo limati: “Yehova anauza Mose kuti: ‘Munthuyo aphedwe basi!’” (Numeri 15:35) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anakwiya kwambiri ndi zimene munthuyo anachita?
Anthuwo anali ndi masiku 6 oti akanatha kutola nkhuni, kupeza chakudya komanso kugwira ntchito kuti apeze zovala ndi malo ogona. Tsiku la 7 ankafunika kuliona kuti ndi loyenera kuchita zinthu zokhudza kulambira. Kutola nkhuni sikunali kolakwika, koma kuchita zimenezo pa nthawi imene ankafunika kulambira Yehova n’kumene kunali kulakwa. Ngakhale kuti Akhristu satsatira Chilamulo cha Mose, nkhani imeneyi ikutiphunzitsa kuti tiyenera kumaika zinthu zofunika pamalo oyamba.—Afilipi 1:10.
APRIL 5-11
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 17-19
Mfundo Zothandiza
Mchere Ndi Wofunika Kwambiri
Mchere unakhalanso chizindikiro cha zinthu zokhazikika ndi zokhalapo mpaka kalekale. Choncho m’Baibulo, pangano limene lakhazikitsidwa linkatchedwa “pangano la mchere” ndipo anthu amene achita panganolo ankadyera limodzi chakudya chothira mchere posonyeza kukhazikitsa panganolo. (Numeri 18:19) M’Chilamulo cha Mose nsembe zimene zinkaperedwa pa guwa ankazithira mchere, posonyeza kuti ndi zosawonongeka.
APRIL 19-25
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 22-24
“Yehova Amasintha Temberero N’kukhala Dalitso”
it-2 291
Misala
Misala Yotsutsana ndi Yehova. Mneneri Balamu anachita zinthu mopusa ndipo ankafuna kulosera zinthu zoipa zokhudza Aisiraeli kuti alandire ndalama kuchokera kwa Baraki, yemwe anali mfumu ya a Amowabu. Koma Yehova analepheretsa zofuna zakezo. Mtumwi Petulo analemba zokhudza Balamu kuti, “nyama yosalankhula yonyamula katundu inalankhula ngati munthu ndi kulepheretsa zochita zamisala za mneneriyo.” Ponena za misala ya Balamu, mtumwiyu anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti pa·ra·phro·niʹa, amene amatanthauza “kusaganiza bwino.”—2Pe 2:15, 16; Nu 22:26-31.
APRIL 26–MAY 2
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NUMERI 25-26
Mfundo Zothandiza
it-1 359 ¶1-2
Malire
Choncho zikuoneka kuti panali zinthu ziwiri zimene anayendera pogawira malo mafuko. Zinthu zake zinali kuchita maere komanso kukula kwa fuko. Maere ankangowathandiza kudziwa mbali imene fuko liyenera kupatsidwa monga cholowa chake. Anawathandiza kudziwa ngati fukolo likuyenera kupatsidwa kumpoto, kum’mwera, kum’mawa, kumadzulo, kuchigwa kapena kudera lamapiri. Zotsatira za maerewo zinkachokera kwa Yehova. Zimenezi zinkathandiza kuti mafukowo asamachitirane nsanje kapena kukangana. (Miy 16:33) Komanso pogwiritsa ntchito njira imeneyi, Mulungu anayendetsa zinthu m’njira yakuti zigwirizane ndi ulosi wa pa Genesis 49:1-33 wokhudza mafuko a Aisiraeli umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira.
Pambuyo poti maere asonyeza mbali imene fuko liyenera kupatsidwa, ankafunika kudziwa kukula kwa malo amene fukolo liyenera kukhala nawo ndipo njira yachiwiri ija ndi imene inkawathandiza. “Mukagawire dzikolo kwa mabanja anu monga cholowa chanu mwa kuchita maere. Banja la anthu ambiri mukaliwonjezere cholowa chawo, ndipo banja la anthu ochepa mukalichepetsere cholowa chawo. Malo alionse amene maere akagwere banja, akapatsidwe kwa banjalo.” (Nu 33:54) Malo amene maere anasonyeza kuti fuko likuyenera kupatsidwa sankasintha, koma kukula kwa malo amene fuko lingakhale nawo kunkatha kusinthidwa. Choncho zitaoneka kuti malo amene fuko la Yuda linapatsidwa ndi aakulu, anachotsako magawo ena n’kuwapereka kwa fuko la Simiyoni.—Yos 19:9.