Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
JANUARY 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 15-16
“Kupereka Mnzako kwa Mdani N’koipa Kwambiri”
Kusakhulupirika Ndi Chizindikiro cha Masiku Otsiriza
4 Chitsanzo choyamba ndi cha Delila, mzimayi wachinyengo amene Woweruza Samisoni ankamukonda. Samisoni ankafunitsitsa kutsogolera anthu a Mulungu pa nkhondo yomenyana ndi Afilisiti. Olamulira asanu a Afilisiti ayenera kuti ankadziwa zoti Delila sankakonda kwenikweni Samisoni choncho anamulonjeza kuti amupatsa ndalama zambiri akawauza chinsinsi cha mphamvu zake zapadera. Iwo anachita zimenezi kuti aphe Samisoni. Chifukwa cha dyera, Delila anavomera koma analephera maulendo atatu kudziwa chinsinsi cha mphamvu zake. Choncho anapitiriza kumupanikiza “ndi mawu ake mosalekeza, ndi kum’chonderera” mpaka Samisoni anafika “potopa nazo kwambiri.” Ndiyeno anamuuza kuti sanametepo tsitsi lake moti atangometa, mphamvu zake zikhoza kuthera pomwepo. Delila atadziwa zimenezi, anaitana munthu wina kuti amumete tsitsilo pamene ankagona pamiyendo pake. Kenako anam’pereka kwa adani ake kuti athane naye. (Ower. 16:4, 5, 15-21) Zimene iye anachitazi zinali zoipa kwambiri. Chifukwa cha dyera, Delila anapereka Samisoni yemwe ankamukonda.
Mfundo Zazikulu za M’buku la Oweruza
14:16, 17; 16:16. Kukonda kulira ndiponso kudandaula pofuna kuti munthu akuchitireni zinazake kungathe kuwononga ubwenzi wanu ndi munthuyo.—Miyambo 19:13; 21:19.
Kusakhulupirika Ndi Chizindikiro cha Masiku Otsiriza
15 Kodi anthu amene ali m’banja angatani kuti akhalebe okhulupirika? Mawu a Mulungu amati: “Usangalale ndi mkazi [kapena mwamuna] wapaunyamata wako.” Amanenanso kuti: “Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi [kapena mwamuna] wako amene umamukonda.” (Miy. 5:18; Mlal. 9:9) Pamene akukula, anthu okwatirana ayenera kuchita zonse zimene angathe kuti azikondana ndiponso kusamalirana kwambiri. Izi zikutanthauza kuti aziderana nkhawa, kukomerana mtima ndiponso azipeza nthawi yocheza limodzi. Ayenera kuganizira mmene angatetezere ukwati wawo ndiponso ubwenzi wawo ndi Yehova. Kuti izi zitheke, iwo ayenera kuphunzira Baibulo limodzi, kuyendera limodzi mu utumiki ndiponso kupemphera limodzi kuti Yehova awadalitse.
KHALANIBE OKHULUPIRIKA KWA YEHOVA
16 Pali Akhristu ena amene anachita machimo akuluakulu ndipo anadzudzulidwa “mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba.” (Tito 1:13) Koma anthu ena amachita zinthu zoyenera kuchotsedwa nazo mu mpingo. “Anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilango” choterechi amadzakhalanso olimba mwauzimu. (Aheb. 12:11) Bwanji ngati wachibale wathu kapena mnzathu wapamtima wachotsedwa? Apa tiyenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu osati munthuyo. Yehova amachita nafe chidwi kuti aone ngati tikumvera lamulo lake lakuti tisamayanjane ndi munthu aliyense amene wachotsedwa.—Werengani 1 Akorinto 5:11-13.
Mfundo Zothandiza
Samsoni Anapambana Chifukwa cha Mphamvu za Yehova
Samsoni anali wotsimikiza kukwaniritsa cholinga chake, chomenyana ndi Afilisti. Samsoni anakakhala kunyumba ya mkazi wadama ku Gaza ndi cholinga chomenyana ndi adani a Mulungu. Samsoni anafunikira malo ogona usiku m’mzinda wa adaniwo, ndipo malowo anapezeka m’nyumba ya mkazi wadama. Samsoni analibe cholinga chochita dama. Iye anachoka kunyumba kwa mkaziyo pakati pa usiku, nazula mageti apachipata cha mzindawo limodzi ndi zimitengo zake zam’mbali ziwiri. Ndipo anazinyamula kupita nazo pamwamba pa phiri pafupi ndi Hebroni, mtunda wa pafupifupi makilomita 60. Mulungu anavomereza zomwe anachitazi ndipo anam’patsa mphamvu yochitira zimenezi.—Oweruza 16:1-3.
JANUARY 10-16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 17-19
“Kusamvera Malamulo a Mulungu Kumabweretsa Mavuto”
it-2 390-391
Mika
1. Munthu wafuko la Efuraimu. Mika anachita zosemphana ndi lamulo la nambala 8 pa Malamulo 10 (Eks 20:15) chifukwa anatenga ndalama zasiliva zokwana 1,100 za mayi ake. Iye ataulula n’kubweza ndalamazo, mayi ake anati: “Ndithudi ndipereka ndalama zasilivazi kwa Yehova kuti zikhale zopatulika. Ndichita zimenezi kuti ndithandize mwana wanga, ndi kuti papangidwe chifaniziro chosema ndiponso chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula. Tsopano ndikubweza ndalamazi kwa iwe.” Kenako iwo anatenga ndalama zasiliva zokwana 200 n’kuzipereka kwa wosula siliva amene anapanga “chifaniziro chosema ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula” zomwe pambuyo pake anaziika m’nyumba ya Mika. Mika, yemwe anali ndi “nyumba ya milungu,” anapanga efodi ndi aterafi, ndipo anapatsa mphamvu mmodzi mwa ana ake kuti azitumikira monga wansembe wake. Ngakhale kuti anapanga zimenezi n’cholinga cholemekeza Yehova, zinali zolakwika kwambiri chifukwa zinali zosemphana ndi lamulo loti asamalambire mafano (Eks 20:4-6) komanso zinali zosemphana ndi zimene Yehova ankafuna zoti anthu azilambira kuchihema ndiponso azikhala ndi ansembe. (Owe 17:1-6; De 12:1-14) Kenako patapita nthawi, Mika anatenga Yonatani, mwana wa Gerisomu mwana wa Mose, kuti azikhala naye kunyumba kwake ndipo anamulemba ntchito kuti azitumikira monga wansembe wake. (Owe 18:4, 30) Mika ankaona zinthu molakwika moti ankaona kuti zikumuyendera bwino, choncho anati: “Tsopano ndadziwa kuti Yehova andichitira zabwino.” (Owe 17:7-13) Komatu Yonatani sanali wa m’banja la Aroni choncho sanali woyenera kutumikira monga wansembe. Zimenezi zinangowonjezera zolakwika zimene Mika anachita.—Nu 3:10.
it-2 391 ¶2
Mika
Pasanapite nthawi, Mika ndi gulu lake anayamba kuthamangitsa anthu a fuko la Dani. Atawapeza, anthuwo n’kumufunsa chimene chinali vuto lake, Mika anayankha kuti: “Mwatenga milungu yanga imene ndinapanga, ndipo mwatenganso wansembe n’kumapita naye. Nanga ine nditsala ndi chiyani?” Atanena zimenezi, ana a Dani anamuopseza kuti akapitiriza kuwalondola n’kumalankhula zakezo, amupweteka. Ataona kuti anthu a fuko la Dani anali amphamvu kuposa gulu lake, Mika anabwerera. (Owe 18:22-26) Anthu a fuko la Dani anaukira ndi kutentha mzinda wa Laisi kenako pamalowo anamangapo mzinda wina n’kuutcha kuti Dani. Yonatani ndi ana ake anakhala ansembe a anthu a fuko la Dani, omwe anaimiritsa “chifaniziro chosema chimene Mika anapanga” ndipo “chinakhalabe choimiritsa masiku onse amene nyumba ya Mulungu woona [chihema] inakhalabe ku Silo.”—Owe 18:27-31.
Mfundo Zothandiza
Baibulo Lomveka Bwino Kwambiri
6 Masiku ano kwapezeka umboni winanso wosonyeza kuti dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Baibulo. Mu Baibulo la Dziko Latsopano lomwe linatuluka mu 1984, dzina la Mulungu linkapezekamo ka 7,210. Koma mu Baibulo lachingelezi lokonzedwanso lomwe linatuluka mu 2013, anawonjezera dzinali m’mavesi enanso 6, choncho limapezekamo ka 7,216. Mavesi ake ndi 1 Samueli 2:25; 6:3; 10:26; 23:14, 16 ndiponso Oweruza 19:18. Anawonjezera dzina la Mulungu pa Oweruza 19:18 chifukwa cha zimene akatswiri anapeza atafufuza m’zolemba zina zakale za Baibulo. Pamavesi enawo, anawonjezera dzinali chifukwa cha zimene anapeza m’mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ija.
JANUARY 17-23
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 20-21
“Muzifunsira Nzeru kwa Yehova”
Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi
Amuna a ku Gibeya, a fuko la Benjamini atagwirira ndi kupha mdzakazi wa Mlevi wina, mafuko ena ananyamuka kukamenyana ndi Abenjamini. (Ower. 20:1-11) Iwo anapemphera kwa Yehova asanakamenye nkhondo imeneyi koma anagonjetsedwa maulendo awiri. (Ower. 20:14-25) Kodi umenewu unali umboni woti Mulungu sanamve mapemphero awo? Kodi Yehova anasangalala kuona anthu amenewa akupita kukabwezera chiwembucho?
Mfundo Zazikulu za M’buku la Oweruza
20:17-48—N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti fuko la Benjamini ligonjetse mitundu inayo kawiri, ngakhale kuti fuko limeneli linafunika kulangidwa? Polola kuti mafuko okhulupirikawo agonje kwambiri poyambirira, Yehova ankafuna kuwayesa mafukowo kuti aone ngati analidi otsimikiza mtima kuchotseratu kuipa konse mu Israyeli.
Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi
Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Mavuto ena mu mpingo amapitirirabe ngakhale kuti akulu mu mpingo akuchitapo kanthu komanso kupemphera kwa Mulungu kuti awathandize. Zimenezi zikachitika, akulu angachite bwino kukumbukira mawu a Yesu akuti: “Pitirizani kufunafuna [kapena kupemphera], ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.” (Luka 11:9) Ngakhale kuti nthawi zina yankho la pemphero lingachedwe, oyang’anira ayenera kudziwa kuti Yehova adzawayankha pa nthawi yake.
Mfundo Zothandiza
Kodi Mukudziwa?
Kodi kale gulaye ankagwiritsidwa ntchito bwanji pa nkhondo?
Davide anagwiritsa ntchito gulaye kupha Goliyati, yemwe anali chiphona. Zikuoneka kuti Davide anaphunzira luso loponya gulaye ali mnyamata pa nthawi imene ankaweta nkhosa.—1 Samueli 17:40-50.
Gulaye amaonekanso pa zithunzi zakale za ku Iguputo ndi za ku Siriya. Chidachi chinkapangidwa ndi chikopa kapena kansalu komwe kankaoneka ngati kathumba, ndipo kankakhala ndi zingwe ziwiri. Munthu woponya gulaye ankatenga mwala wosalala wobulungira n’kuuika pa chikopacho. Kenako ankavukuza m’mwamba gulayeyo mwamphamvu atagwira zingwe zija. Ndiyeno ankasiya chingwe chimodzi ndipo mwalawo unkafwamphuka mwamphamvu n’kukagenda chinthu chimene akufunacho.
Ofukula zinthu zakale ku Middle East anapeza miyala yambirimbiri yomwe inkaponyedwa pogwiritsa ntchito gulaye pa nkhondo. Asilikali odziwa kugwiritsa ntchito bwino gulaye ankatha kuvukuza gulaye n’kuponya mwala womwe unkathamanga paliwiro la makilomita pafupifupi 240 pa ola. Akatswiri ena amanena kuti gulaye anali wamphamvu moti ankagwiritsidwa ntchito pophera munthu kapena nyama ngati mmene uta umachitira. Koma akatswiri ena amatsutsa mfundo imeneyi. Komatu zikuoneka kuti gulaye anali woopsa kwambiri, mwinanso kuposa uta.—Oweruza 20:16.
JANUARY 24-30
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | RUTE 1-2
“Muzisonyeza Chikondi Chokhulupirika”
Tsanzirani Anthu Amene Anali pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova
5 Makolo komanso achibale ake a Rute ankakhala ku Mowabu. Choncho iye akanaona kuti ndi bwino kubwerera kwawoko kuti achibale ake azikamusamalira. Komanso ankadziwa bwino anthu a ku Mowabu ndiponso chikhalidwe ndi chilankhulo chawo. Koma akanapita ku Betelehemu zonse zikanakhala zachilendo. Naomi ankaonanso kuti Rute akapita ku Betelehemu sakapeza mwamuna wokhala naye pa banja. Choncho anauza Rute kuti abwerere ku Mowabu. Ndiye kodi Rute anatani? Iye anasankha mosiyana ndi Olipa. Paja Olipa anabwerera “kwa anthu a kwawo ndi kwa milungu yake.” (Rute 1:9-15) Koma Rute sanafune kubwerera kwawo kuti akayambirenso kulambira milungu yonyenga.
Tsanzirani Anthu Amene Anali pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova
6 N’kutheka kuti Rute anaphunzira za Yehova kuchokera kwa apongozi ake a Naomi kapena kwa malemu mwamuna wake. Anaphunzira kuti Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi milungu ya ku Mowabu. Ndiyeno anayamba kukonda Yehova ndipo anazindikira kuti ndiye Mulungu woyenera kumulambira. Choncho Rute anauza apongozi ake kuti: “Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Izi zikusonyeza kuti Rute ankakonda Naomi komanso ankakonda kwambiri Yehova. N’chifukwa chake pa nthawi ina Boazi anamuyamikira kuti zimene anachita zinali ngati anathawira m’mapiko a Yehova kuti amuteteze. (Werengani Rute 2:12.) Mawu a Boaziwa akutikumbutsa za kamwana ka mbalame kamene kamabisala m’mapiko a mayi ake kuti katetezeke. (Sal. 36:7; 91:1-4) Choncho mawuwa akusonyeza kuti Yehova anateteza Rute ndiponso kumudalitsa. Ndipotu Rute sananong’oneze bondo chifukwa cha zimene anasankhazi.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Rute
1:13, 21—Kodi Yehova ndiye anachititsa kuti Naomi aumve kuwawa moyo pomupatsa mavuto? Ayi, ndipotu Naomi sanaimbe mlandu Mulungu kuti wamulakwira m’njira inayake. Komabe, poona zonse zimene zinam’chitikira, iye anaganiza kuti Yehova sakumuyanja. Motero anawawidwa mtima ndiponso anakhumudwa. Komanso masiku amenewo anthu ankaona kuti kubereka ndi madalitso ochokera kwa Mulungu ndipo kusabereka ankakuona ngati temberero. Popeza kuti analibe zidzukulu ndiponso ana ake aamuna awiri anali atafa, Naomi ayenera kuti ankaona kuti akulondola poganiza kuti Yehova wamunyozetsa.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Kodi Tikati Banja Nchiyani?
5 Rute atamaliza kupuntha balere wake uja nkumuunjika pamodzi, anaona kuti akukwana efa yathunthu. Nkutheka kuti balere ameneyu anali wokwana makilogalamu 14. Atatero mwina anamanga balereyo pansalu nkusenza ndipo anayamba ulendo wopita ku Betelehemu. Pa nthawiyi, kunja kunali kutada.—Rute 2:17.
6 Naomi anasangalala ataona mpongozi wakeyu, yemwe ankamukonda kwambiri, ndipo mwina anadabwa ataona kuchuluka kwa balere amene Rute anakunkha. Rute anali atabweretsanso chakudya chimene chinatsala, chomwe Boazi anampatsa pamene ankadya ndi anyamata ake. Rute ndi Naomi anayamba kudya chakudyachi. Ndiyeno Naomi anamufunsa kuti: Kodi unakakunkha kuti lero? Adalitsike amene wakuganizirayo. (Rute 2:19) Naomi ataona balere amene Rute anabweretsa, anadziwa kuti pali munthu wina amene anamukomera mtima Ruteyo kuti apeze balere wochuluka choncho.
JANUARY 31–FEBRUARY 6
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | RUTE 3-4
“Muzikhala ndi Makhalidwe Abwino”
Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”
N’zosakayikitsa kuti zimene Boazi analankhula zinamukhazika mtima pansi Rute. Iye anauza Rute kuti: “Yehova akudalitse, mwana wanga. Kukoma mtima kosatha kumene wasonyeza panopa kukuposa koyamba kuja, popeza sunafune anyamata, kaya osauka kapena olemera.” (Rute 3:10) Rute anasonyeza kukoma mtima “koyamba” pamene anachoka ku Mowabu ndi apongozi ake kupita ku Isiraeli n’kumakawasamalira. Kukoma mtima kwachiwiri kunaonekera pa zimene Rute anachita, kuti sanafune anyamata, kaya osauka kapena olemera. Boazi ankadziwa kuti popeza Rute anali akadali mtsikana, akanatha kukwatiwa ndi mnyamata wa msinkhu wake. Koma iye anasankha kuchitira zabwino Naomi komanso mwamuna wa Naomi amene anamwalira n’cholinga choti dzina la mwamuna wa Naomiyo, lisafe. N’chifukwa chake Boazi anachita chidwi kwambiri ndi Rute.
Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”
Rute ayenera kuti ankasangalala kwambiri akaganizira zimene Boazi ananena zoti anthu onse ankamudziwa kuti iyeyo ndi “mkazi wabwino kwambiri.” Zinali zoyeneradi kuti iye azidziwika ndi mbiri imeneyi chifukwa anali ndi cholinga chodziwa Yehova komanso kumutumikira. Iye anasonyezanso kuti ankadera nkhawa ndiponso kukomera mtima Naomi ndi anthu a mtundu wake ndipo anali wofunitsitsa kutsatira miyambo yawo, yomwe mosakayikira inali yosiyana kwambiri ndi yakwawo. Kutsanzira chikhulupiriro cha Rute kungatithandize kuti nafenso tizilemekeza kwambiri anthu ena komanso miyambo ya chikhalidwe chawo. Tikamachita zimenezi, ifenso tidzakhala ndi mbiri yoti ndife anthu abwino kwambiri.
Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”
Zitatere, Boazi anakwatira Rute. Baibulo limati: “Yehova anam’dalitsa [Rute] ndipo anatenga pakati n’kubereka mwana wamwamuna.” Akazi a ku Betelehemu anayamba kudalitsa Naomi komanso kutamanda Rute kuti anachita zazikulu kwa Naomi zoposa zimene ana aamuna oposa 7 akanachita. Baibulo limasonyeza kuti mwana wa Rute anadzakhala kholo la Mfumu Davide. (Rute 4:11-22) Ndiyeno Davideyo anadzakhala kholo la Yesu Khristu.—Mateyu 1:1.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Rute
4:6—Kodi munthu wowombola ‘akanawononga’ bwanji cholowa chake powombola mkazi? Chifukwa choyamba n’chakuti, ngati munthu amene analowa muumphawi uja anagulitsa cholowa chake cha malo, wowombolayo anayenera kuwombolanso malowo pamtengo wogwirizana ndi zaka zimene zatsala kuti Chaka Choliza Lipenga chifike. (Levitiko 25:25-27) Potero ndiye kuti wowombolayo anali kuika pachiswe katundu wake yemwe. Chifukwa chinanso n’chakuti mwana wamwamuna amene Rute akanabereka ndiye anali woyenerera kulowa malo owomboledwawo, osati achibale apafupi a wowombolayo ayi.
FEBRUARY 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 1-2
“Muzimuuza Yehova Zamumtima Mwanu Mukamapemphera”
Anapemphera Kuchokera Pansi pa Mtima
12 Pamenepa Hana anapereka chitsanzo chabwino kwa atumiki onse a Mulungu pa nkhani ya pemphero. Yehova amafuna kuti atumiki ake azipemphera kwa iye momasuka, osakayikira chilichonse. Iye amafuna kuti anthu azimuuza mavuto awo onse monga mmene mwana amachitira popempha chinthu kwa kholo lake limene limamukonda. (Werengani Salimo 62:8; 1 Atesalonika 5:17.) Mtumwi Petulo analemba kuti popemphera kwa Yehova ‘tizimutulira nkhawa zathu zonse, pakuti amatidera nkhawa.’—1 Pet. 5:7.
Mmene Hana Anapezera Mtendere
Kodi tingaphunzire chiyani pankhani imeneyi? Tikamapemphera kwa Yehova chifukwa choti tili ndi nkhawa, tizimuuza mmene tikumvera ndipo tizim’pempha mokhudzidwa mtima. Tikayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe poyesa kuthetsa vutolo, tizisiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Palibe njira ina yabwino kuposa imeneyi.—Miyambo 3:5, 6.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Woyamba
2:10—N’chifukwa chiyani Hana anapemphera kuti Yehova “adzapatsa mphamvu mfumu yake” pamene mu Israyeli munalibe mfumu? Chilamulo cha Mose chinali chitaneneratu kuti Aisrayeli adzakhala ndi mfumu. (Deuteronomo 17:14-18) Muulosi umene anaunena ali pafupi kumwalira, Yakobo anati: “Ndodo yachifumu [chizindikiro cha ulamuliro wa mfumu] siidzachoka mwa Yuda.” (Genesis 49:10) Komanso, ponena za Sara, mayi wa fuko la Israyeli, Yehova anati: “Mafumu a anthu adzatuluka mwa iye.” (Genesis 17:16) Choncho, m’pemphero lakeli, Hana ankanena za mfumu ya m’tsogolo.
FEBRUARY 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 3-5
“Yehova Amatiganizira”
Yehova Ndi Wamphamvuyonse Koma Amaganizira Ena
3 Samueli anayamba “kutumikira Yehova” kuchihema ali wamng’ono kwambiri. (1 Sam. 3:1) Tsiku lina akugona panachitika zinthu zodabwitsa. (Werengani 1 Samueli 3:2-10.) Iye anamva munthu akumuitana. Poyamba ankaganiza kuti akuitanidwa ndi Eli ndipo anathamanga kupita kwa iye n’kunena kuti: “Ndabwera mbuyanga, ndamva kuitana.” Koma Eli anamuuza kuti sanamuitane. Zimenezi zinachitikanso maulendo ena awiri ndipo Eli anazindikira kuti Mulungu ndi amene ankaitana Samueli. Choncho anamuuza mmene angayankhire ndipo Samueli anachita zomwezo. N’chifukwa chiyani Yehova sanathandize Samueli kuzindikira ulendo woyamba womwewo kuti iye ndi amene ankamuitana? Baibulo silinena, koma zimene zinachitika zikusonyeza kuti Yehova anachita zimenezi chifukwa choti ankamuganizira Samueliyo. N’chifukwa chiyani tikutero?
Yehova Ndi Wamphamvuyonse Koma Amaganizira Ena
4 Werengani 1 Samueli 3:11-18. Yehova analamula ana kuti azilemekeza achikulire, makamaka amene akutsogolera. (Eks. 22:28; Lev. 19:32) Ndiye kodi mukuganiza kuti Samueli akanakwanitsa kungodzuka m’mawa n’kupita kwa Eli kukamuuza uthenga woopsa wochokera kwa Mulungu? Ayi. Baibulo limanena kuti Samueli “anaopa kuuza Eli za masomphenya amene anaona.” Koma Mulungu anathandiza Eli kudziwa kuti ndi iyeyo amene ankamuitana Samueli. Choncho Eli ndi amene anauza Samueliyo kuti afotokoze zimene anauzidwa. Anamulamula kuti: ‘Usandibisire ngakhale mawu amodzi pa mawu onse amene iye wakuuza.’ Samueli anamvera ndipo “anamuuza mawu onse.”
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Woyamba
3:3—Kodi Samueli anagonadi m’Malo Opatulikitsa? Ayi, sanagonemo. Samueli anali Mlevi wa fuko la Kohati lomwe silinali fuko la ansembe. (1 Mbiri 6:33-38) Pa chifukwa chimenechi, iye sanali wololedwa ‘kulowa kukaona zopatulikazo.’ (Numeri 4:17-20) Mbali yokha ya malo opatulikawo kumene Samueli anali waufulu kufikako inali bwalo la chihemacho. Ayenera kuti iye anagona kumeneko. Zikuoneka kuti Eli nayenso anali atagona penapake m’bwalo lomweli. Mawu akuti “mmene munali likasa la Mulungu,” ayenera kuti akunena malo amene panali chihemacho.
FEBRUARY 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |1 SAMUELI 6-8
“Kodi Mfumu Yanu ndi Ndani?”
it-2 163 ¶1
Ufumu wa Mulungu
Anapempha Kuti Akhale ndi Mfumu. Patatha zaka pafupifupi 400 kuchokera pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo, komanso zaka zoposa 800 kuchokera pamene Mulungu anachita pangano ndi Abulahamu, Aisiraeli anapempha kuti akhale ndi mfumu yoti iziwatsogolera, chifukwa ngakhale mitundu inanso inali ndi owalamulira. Zimene anapemphazi zimasonyeza kuti anakana kuti Yehova aziwalamulira. (1Sa 8:4-8) N’zoona kuti anthuwo ankayembekezera kukhala ndi mfumu mogwirizana ndi zimene Mulungu analonjeza Abulahamu komanso Yakobo. Chiyembekezo chawo chokhala ndi mfumu chinakula chifukwa cha ulosi umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira wokhudza Yuda (Ge 49:8-10), chifukwa cha mawu a Yehova opita kwa Aisiraeli atatuluka kumene ku Iguputo (Eks 19:3-6), chifukwa cha pangano la Chilamulo (De 17:14, 15), komanso chifukwa cha mbali ya uthenga umene Mulungu anauzira Balamu kuti alankhule (Nu 24:2-7, 17). Mayi ake a Samueli, Hana, omwe anali okhulupirika anatchulanso za chiyembekezochi m’pemphero. (1Sa 2:7-10) Komabe, Yehova anali asanaulule bwinobwino “chinsinsi chopatulika” chokhudza ufumuwo komanso anali asananene kuti udzakhazikitsidwa liti, udzakhala wotani ndiponso kuti udzakhala wa padziko lapansi, kapena wakumwamba. Choncho pa nthawiyi, anthuwo anasonyeza mwano popempha mfumu yoti iziwalamulira.
Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Anakumana ndi Mavuto
Koma tamvani zimene Yehova anayankha Samueli atamuuza nkhaniyi m’pemphero. Yehova anati: “Mvera zonse zimene anthuwo akunena kwa iwe, pakuti sanakane iweyo koma akana ine kuti ndisakhale mfumu yawo.” Mawu a Yehova amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri Samueli. Komabe mawuwa anasonyeza kuti anthuwo anachitira Mulungu Wamphamvuyonse chipongwe chachikulu. Yehova anauza mneneri Samueli kuti achenjeze Aisiraeli za kuipa kokhala ndi munthu woti aziwalamulira ngati mfumu yawo. Koma Samueli atawachenjeza, iwo anaumirirabe kuti: “Ife tikufuna kuti mfumu izitilamulira.” Popeza nthawi zonse Samueli ankamvera Mulungu, iye anapita kukadzoza mfumu imene Yehova anasankha.—1 Samueli 8:7-19.
Yehova Ndiye Woyeneradi Kulamulira
9 Zimene zakhala zikuchitika zasonyeza kuti zimene Yehova anachenjezazi zinali zoona. Aisiraeli ankavutika kwambiri chifukwa cholamulidwa ndi anthu makamaka olamulirawo akakhala osakhulupirika. Tikaganizira chitsanzo cha Aisiraeli chimenechi, timamvetsa chifukwa chake maboma a anthu alephera kuthetsa mavuto. N’zoona kuti atsogoleri ena amapempha Mulungu kuti awadalitse n’cholinga chakuti abweretse bata ndi mtendere. Komabe kodi Mulungu angadalitse bwanji anthu amene sagonjera ulamuliro wake?—Sal. 2:10-12.
Mfundo Zothandiza
N’chifukwa Chiyani Tifunika Kubatizidwa?
13 Tiyenera kutembenuka tisanabatizidwe kukhala Mboni za Yehova. Munthu amafuna yekha kutembenuka akasankha ndi mtima wonse kuti atsatire Kristu Yesu. Munthu wotero amasiya zochita zake zoipa zakale ndipo amatsimikiza mtima kuchita zinthu zimene Mulungu amaziona kuti n’zabwino. M’Malemba, aneni a Chihebri ndi Chigiriki otanthauza kutembenuka ali ndi ganizo la kubwerera, kusiya. Kumasonyeza kusiya zoipa ndi kutembenukira kwa Mulungu. (1 Mafumu 8:33, 34) Kutembenuka kumafuna kuchita “ntchito zoyenera kutembenuka mtima.” (Machitidwe 26:20) Kumafuna kuti tisiye kulambira konyenga m’malo mwake kutsatira malamulo a Mulungu, ndi kulambira Yehova yekha basi. (Deuteronomo 30:2, 8-10; 1 Samueli 7:3) Kutembenuka kumatichititsa kusintha mmene tinkaganizira, zolinga zathu, ndiponso mtima wathu. (Ezekieli 18:31) ‘Timabwerera’ pamene umunthu watsopano uloŵa m’malo mwa makhalidwe oipa.—Machitidwe 3:19; Aefeso 4:20-24; Akolose 3:5-14.
FEBRUARY 28–MARCH 6
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 9-11
“Sauli Anali Wodzichepetsa Poyamba”
Tiziyenda Modzichepetsa ndi Mulungu
11 Taganizirani zimene zinachitikira Mfumu Sauli. Ali mnyamata, anali wodzichepetsa. Iye ankadziwa malire ake moti nthawi ina anakayikira kuti sakanakwanitsa kukhala ndi udindo waukulu. (1 Sam. 9:21; 10:20-22) Koma patapita nthawi, Sauli anayamba kudzikweza ndipo anachita zinthu zimene sankayenera kuchita. Anayamba kusonyeza khalidweli atangokhala mfumu. Pa nthawi ina, analephera kudikira moleza mtima kuti mneneri Samueli afike. M’malo modalira Yehova kuti athandize anthu ake, Sauli anapereka nsembe ngakhale kuti umenewu sunali udindo wake. Zimenezi zinachititsa kuti Yehova asiye kumukonda ndipo pamapeto pake ufumu wake unatha. (1 Sam. 13:8-14) Chitsanzochi chikutiphunzitsa kuti tiyenera kupewa kuchita zinthu modzikweza.
Kodi Tingatani Kuti Tikhalebe ndi Mtima Wodzipereka?
8 Sauli, yemwe anali mfumu ya Isiraeli, anali wodzipereka koma anayamba kukhala wodzikonda. Ife tiyenera kusamala kuti tisatengere zimene anachita. Sauli atangoikidwa kukhala mfumu anali wodzichepetsa. (1 Sam. 9:21) Iye anasankhidwa ndi Mulungu kukhala mfumu ndipo zikanakhala zomveka kuti alange Aisiraeli amene ankakana zimenezi. Koma sanawalange. (1 Sam. 10:27) Sauli analola kuti mzimu wa Mulungu uzimutsogolera pa nkhondo yomenyana ndi Aamoni ndipo anapambana. Kenako ananena modzichepetsa kuti Mulungu ndi amene anamuthandiza.—1 Sam. 11:6, 11-13.
Aamoni—Anthu Amene Anabwezera Udani pa Kukoma Mtima
Aamoni kachiŵirinso anabwezera udani pa kukoma mtima kwa Yehova. Yehova sananyalanyaze chiwopsezo chankhanza chimenechi. “Sauli atamva mawu amenewa [a Nahasi], mzimu wa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo anapsa mtima kwambiri.” Motsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, Sauli anasonkhanitsa amuna ankhondo 330,000 amene anakanthiratu Aamoni kwakuti “sipanatsale anthu awiri ali limodzi.”—1 Samueli 11:6, 11.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Woyamba
9:9—Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi mawu akuti “iye wotchedwa mneneri makono ano, anatchedwa mlauli kale”? Mawu amenewa akusonyeza kuti pamene aneneri anali kuchuluka m’masiku a Samueli komanso m’nthawi imene Israyeli anayamba kulamuliridwa ndi mafumu, anthu anasiya kugwiritsa ntchito liwu lakuti “mlauli” m’malo mwake anayamba kugwiritsa ntchito liwu lakuti “mneneri.” Samueli anali mneneri woyamba mwa aneneri amenewo.—Machitidwe 3:24.