Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr22 May tsamba 1-12
  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Timitu
  • MAY 2-8
  • MAY 9-15
  • MAY 16-22
  • MAY 23-29
  • MAY 30–JUNE 5
  • JUNE 6-12
  • JUNE 13-19
  • JUNE 20-26
  • JUNE 27–JULY 3
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwbr22 May tsamba 1-12

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

MAY 2-8

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 27-29

“Mmene Davide Ankamenyera Nkhondo”

it-1 41

Akisi

Maulendo awiri amene Davide ankathawa Sauli, anakabisala kwa Mfumu Akisi. Pa ulendo woyamba, atamuganizira kuti anali mdani, Davide ananamizira kuti ndi wamisala ndipo Akisi anangomusiya kuti apite. (1Sa 21:10-15; Sl 34:Kam; 56: Kam) Pa ulendo wachiwiri Davide anapita ndi amuna ankhondo 600 ndi mabanja awo, ndipo Akisi anawauza kuti azikakhala ku Zikilaga. Patatha chaka chimodzi ndi miyezi 4 ali kumeneko, Akisi anakhulupirira kuti Davide ndi amuna amene anali nawo anakamenya nkhondo ku mizinda ya ku Yudeya pomwe kwenikweni anakamenya nkhondo kwa Agesuri, Agirezi ndi Aamaleki. (1Sa 27:1-12) Komanso Davide anam’pusitsa kwambiri Akisi pamene anamuchititsa kuti amuike kukhala msilikali wake womulondera pomwe Afilisiti ankakonzekera kukamenyana ndi Mfumu Sauli, ndipo anali atangotsala pang’ono kupita pamene “olamulira ogwirizana” a Afilisiti ananena kuti Davide ndi amuna amene anali nawo abwerere ku Zikilaga. (1Sa 28:2; 29:1-11) Davide atangokhala mfumu, anaukira mzinda wa Gati, koma zikuoneka kuti Akisi sanaphedwe, ndipo anakhala ndi moyo mpaka mu ulamuliro wa Solomo.​—1Mf 2:39-41.

w21.03 4 ¶8

Kodi Achinyamata Mungatani Kuti Anthu Ena Azikudalirani?

8 Taganizirani vuto linanso limene Davide anakumana nalo. Atadzozedwa kuti akhale mfumu, iye anafunika kuyembekezera kwa zaka zambiri asanayambe kulamulira. (1 Sam. 16:13; 2 Sam. 2:3, 4) Ndiye pa nthawiyi kodi chinamuthandiza n’chiyani kudikira moleza mtima? M’malo moti zimenezi zimufooketse, Davide ankagwiritsa ntchito nthawi yake pochita zimene akanakwanitsa. Mwachitsanzo, pamene iye anathawira m’dziko la Afilisiti, anagwiritsa ntchito nthawi imeneyi pomenyana ndi adani a Aisiraeli. Pochita zimenezi iye anathandiza kuteteza malire a ufumu wa Yuda.​—1 Sam. 27:1-12.

it-2 245 ¶6

Bodza

Ngakhale kuti Baibulo silivomereza kunama kulikonse, sizikutanthauza kuti munthu ayenera kuuza anthu ena zinthu za chinsinsi zimene sakuyenera kuzidziwa. Yesu Khristu anapereka malangizo akuti: “Musamapatse agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zanu, kuopera kuti zingapondeponde ngalezo kenako n’kutembenuka ndi kukukhadzulani.” (Mt 7:6) N’chifukwa chake pa zochitika zina, Yesu sankafotokoza zinthu zonse kapena sankayankha mwachindunji mafunso ena pa nthawi imene kuchita zimenezi kukanakhala ndi zotsatirapo zosakhala bwino. (Mt 15:1-6; 21:23-27; Yoh 7:3-10) Choncho n’zoonekeratu kuti zomwe anachita Abulahamu, Isaki, Rahabi, komanso Elisa popusitsa kapena posafotokoza zinthu zonse kwa anthu amene sankalambira Yehova, sikunali kunama.​—Ge 12:10-19; chap 20; 26:1-10; Yos 2:1-6; Yak 2:25; 2Mf 6:11-23.

Mfundo Zothandiza

w10 1/1 20 ¶4-5

Kodi Akufa Angathandize Amoyo?

Taganizirani izi: Baibulo limanena kuti munthu akamwalira ‘amabwerera kumka ku nthaka yake,’ ndiponso “zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:4) Sauli ndiponso Samueli ankadziwa kuti Mulungu amadana ndi okhulupirira mizimu. N’chifukwa chake Sauli asanayambe kukhulupirira mizimu, anagwira ntchito yaikulu yothana ndi kulambira mizimu.​—Levitiko 19:31.

Taganizirani bwinobwino nkhaniyi. Zikanakhala kuti Samueli anali moyo kwinakwake ngati mzimu, kodi akanalolera kuswa lamulo la Mulungu pogwirizana ndi sing’anga n’cholinga choti alankhule ndi Sauli? Yehova anali atakana kulankhula ndi Sauli. Ndiyeno kodi sing’anga angakakamize Mulungu, amene ndi Wamphamvuyonse kuti alankhule ndi Sauli kudzera mwa Samueli? Ayi. Apatu n’zachidziwikire kuti mzukwawo sunali Samueli, yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu. Koma chinali chiwanda chimene chinanamizira kuti chinali Samueli amene anamwalira kale.

MAY 9-15

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 30-31

“Dzilimbitseni mwa Yehova Mulungu Wanu”

w06 8/1 28 ¶12

Opani Yehova Kuti Mukhale Achimwemwe

12 Kuopa Yehova kunathandiza Davide kupewa kuchita zoipa ndipo kunam’thandiza m’njira zinanso. Kunam’limbikitsa kuchita zinthu motsimikiza ndiponso mwanzeru pamene anakumana ndi zovuta. Kwa chaka chimodzi ndi miyezi inayi, Davide ndi asilikali ake anathawa Sauli n’kukabisala ku Zikilaga m’dziko la Afilisti. (1 Samueli 27:5-7) Nthawi ina iwowa atachokapo, gulu la Aamaleki linalowerera mumzinda wawo, kuuyatsa moto n’kutenga akazi awo onse, ana awo onse, ndi nkhosa zawo zonse. Atabwerera n’kuona zimene zachitika, Davide ndi asilikali ake analira. Posakhalitsa chisoni chija chinasanduka ukali, ndipo asilikaliwo anayamba kunena zoti am’ponya miyala Davideyo kuti afe. Ngakhale kuti Davide anali atavutika maganizo, sanataye mtima. (Miyambo 24:10) Chifukwa choopa Mulungu, iye anadalira Yehova ndipo “anadzilimbikitsa mwa Yehova.” Mothandizidwa ndi Mulungu, Davide ndi asilikali ake anagonjetsa Aamaleki ndi kuwalandanso zinthu zawo zonse zija.​—1 Samueli 30:1-20.

w12 4/15 30 ¶14

Yehova Amatiteteza Kuti Tidzapulumuke

14 Davide anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wake. (1 Sam. 30:3-6) Mawu ake ouziridwa amasonyeza kuti Yehova ankadziwa mmene Davide ankamvera. (Werengani Salimo 34:18; 56:8.) Mulungu amadziwanso mmene ife timamvera. Iye amatiyandikira tikakhala ndi “mtima wosweka” kapena ‘tikamadzimvera chisoni mumtima.’ Zimenezi zingatilimbikitse ngati mmene zinalimbikitsira Davide. Iye anaimba kuti: “Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha, pakuti mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwera.” (Sal. 31:7) Koma sikuti Yehova amangoona pamene tikuvutika n’kusiyira pomwepo. Iye amatitonthoza ndiponso kutilimbikitsa kuti tipirire. Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi kudzera m’misonkhano ya Chikhristu.

Mfundo Zothandiza

w05 3/15 24 ¶8

Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Woyamba

30:23, 24. Chosankha ichi, chogwirizana ndi lemba la Numeri 31:27, chikusonyeza kuti Yehova amaona anthu amene akugwira ntchito zing’onozing’ono mumpingo kukhala ofunika kwambiri. Chotero pa chilichonse chimene tikuchita tiyenera ‘kugwira ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi.’​—Akolose 3:23.

MAY 16-22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 1-3

“Kodi Tikuphunzira Chiyani Kuchokera pa ‘Uta’?”

w00 6/15 13 ¶9

Muzilemekeza Anthu Amene Akulamulira

9 Kodi Davide anavutika maganizo pamene ankazunzidwa? Davide analirira Yehova kuti: “Pali olamulira ankhanza amene akufuna moyo wanga.” (Salimo 54:3) Iye anauza Yehova m’pemphero kuti: “Inu Mulungu wanga, ndilanditseni kwa adani anga. . . . Inu Yehova, anthu amphamvu akundiukira, ngakhale kuti ine sindinapanduke kapena kuchita tchimo lililonse. Iwo akuthamanga ndi kukonzekera kundiukira, ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse. Nyamukani pamene ine ndikuitana kuti muone zimene zikundichitikira.” (Salimo 59:1-4) Kodi inunso munamvapo chimodzimodzi, kuti palibe chimene mwalakwira munthu waulamuliro, koma akungokusautsani? Davide sanalephere kulemekeza Sauli. Sauli atamwalira, m’malo mosangalala, Davide analemba nyimbo yoimba polira yakuti: “Sauli ndi Yonatani, anthu okondeka ndi osangalatsa pamene anali ndi moyo, . . . Iwo anali aliwiro kuposa chiwombankhanga, Amphamvu kuposa mikango. Ana aakazi a Isiraeli inu, mulirireni Sauli.” (2 Samueli 1:23, 24) Davide anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yolemekeza anthu amene adzozedwa ndi Yehova, ngakhale kuti Sauli anamulakwira.

w12 4/15 10 ¶8

Kusakhulupirika Ndi Chizindikiro cha Masiku Otsiriza

8 Koma Baibulo limafotokozanso za anthu ambiri amene anakhala okhulupirika. Tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri n’kuona zimene tikuphunzirapo. Tiyamba ndi munthu amene anakhala wokhulupirika kwa Davide. Yonatani anali mwana wamwamuna woyamba kubadwa wa Mfumu Sauli. Choncho iye ndi amene ankayembekezera kulowa ufumu wa Isiraeli. Koma Yehova anasankha Davide kuti adzakhale mfumu yotsatira. Yonatani analemekeza zimene Mulungu anasankha ndipo sankachitira nsanje Davide. M’malomwake Yonatani anayamba ‘kugwirizana kwambiri ndi Davide’ ndipo anamulonjeza kuti adzakhalabe wokhulupirika kwa iye. Iye ankalemekeza Davide monga wodzozedwa wa Mulungu mpaka anamupatsa zovala zake, lupanga lake, uta ndiponso lamba wake. (1 Sam. 18:1-4) Yonatani anachita zonse zimene akanatha kuti alimbikitse Davide. Iye anaika moyo wake pa ngozi pofuna kuteteza Davide kuti Sauli asamuphe. Mokhulupirika, Yonatani anauza Davide kuti: “Iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe.” (1 Sam. 20:30-34; 23:16, 17) M’pake kuti Yonatani atamwalira, Davide anaimba nyimbo yosonyeza kuti ankakonda Yonatani ndipo akumva chisoni chachikulu.​—2 Sam. 1:17, 26.

Mfundo Zothandiza

it-1 369 ¶2

M’bale

Mawu akuti “m’bale” angagwiritsidwenso ntchito kwa anthu omwe ndi ogwirizana kapena amene ali ndi zolinga zofanana. Mwachitsanzo, Mfumu Hiramu ya ku Turo inatchula Mfumu Solomo kuti m’bale wake, osati chabe chifukwa chakuti anali ndi mphamvu komanso maudindo ofanana, koma mwina chifukwanso chakuti ankachitira limodzi zinthu zina monga, kupeza matabwa komanso zinthu zina zomangira kachisi. (1Mf 9:13; 5:1-12) Davide analemba kuti: “Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!” Zimenezi zikutanthauza kuti si ubale weniweni wokha umene ungachititse kuti anthu azikhala mwamtendere komanso mogwirizana. (Sl 133:1) Ndipotu Davide anamutchula Yonatani kuti m’bale wake, osati chifukwa chakuti anali a m’banja limodzi, koma chifukwa chakuti ankakondana komanso ankakonda zinthu zofanana. (2Sa 1:26) Anthu amene amagwirizana chifukwa chokonda zinthu zofanana komanso kukhala ndi makhalidwe ofanana, ngakhale makhalidwewo atakhala oipa, amatchulidwabe kuti abale.​—Miy 18:9.

MAY 23-29

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 4-6

“Muzikhala Ndi Mantha Oyenera Poopa Kukhumudwitsa Yehova”

w05 5/15 17 ¶7

Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Wachiwiri

6:1-7. Ngakhale kuti Davide anali ndi zolinga zabwino, zimene anachita ponyamula Likasa pa galeta zinali zotsutsana ndi malamulo a Mulungu ndipo zotsatira zake zinali zoopsa. (Eksodo 25:13, 14; Numeri 4:15, 19; 7:7-9) Zimene zinachitika Uza atagwira Likasa zikusonyezanso kuti zolinga zabwino sizisintha zofuna za Mulungu.

w05 2/1 27 ¶20

Yehova Amachita Chilungamo Nthawi Zonse

20 Kumbukirani kuti Uza anayenera kuchidziwa bwino Chilamulo. Likasa linali kuimira kukhalapo kwa Yehova. Chilamulo chinaneneratu kuti munthu wamba asakhudze Likasa, ndipo chinachenjezeratu kuti ophwanya lamulo limeneli adzalangidwa mwa kuphedwa. (Numeri 4:18-20; 7:89) Motero, ntchito yosamutsa Likasa siinali ntchito wamba. Zikuonetsa kuti Uza anali Mlevi (koma osati wansembe), moti anayenera kudziwa zimene Chilamulo chimanena. Ndiponso, zaka zambiri m’mbuyomo, Likasa linasamutsidwira ku nyumba ya bambo ake kuti likasungidwe bwino. (1 Samueli 6:20–7:1) Linakhala kumeneko zaka 70, mpaka Davide ataganiza zolisamutsa. Choncho kuyambira ali mwana wamng’ono, Uza ayenera kuti anali kudziwa malamulo okhudza Likasa.

w05 2/1 27 ¶21

Yehova Amachita Chilungamo Nthawi Zonse

21 Monga tatchula kale, Yehova amatha kudziwa za mu mtima wa munthu. Popeza Mawu ake amati zimene Uza anachitazo zinali “kusalingirira,” kapena kupanda ulemu, Yehova ayenera kuti anaona kudzikonda kwa mtundu winawake mwa iye kumene nkhaniyo sinatchule mwachindunji. Kodi kapena Uza anali wodzikuza, wokonda kupitirira malire pa zinthu zina? (Miyambo 11:2) Kapena kutsogolera poyera Likasa limene banja lake linali litasunga m’nyumba mwawo kunam’chititsa kunyada? (Miyambo 8:13) Kodi Uza mwina anali ndi chikhulupiriro chochepa zedi, moti anaganiza kuti dzanja la Yehova n’lalifupi, ndipo sangathe kuchirikiza Likasa loimira kukhalapo Kwake kuti lisagwe? Kaya chikhale chifukwa chotani, ndife otsimikiza kuti Yehova anachita chilungamo. Ayenera kuti anaona chinachake mu mtima wa Uza chimene chinam’pangitsa kupereka chiweruzo nthawi yomweyo.​—Miyambo 21:2.

Mfundo Zothandiza

w96 4/1 29 ¶1

Tizimutulira Yehova Nkhawa Zathu Nthawi Zonse

Davide monga mfumu, analinso ndi mlandu wochititsa zimenezi. Zomwe anachita zimasonyeza kuti ngakhale anthu amene ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova akhoza kuvutika kuchita bwino zinthu pamene akumana ndi mavuto. Choyamba Davide anakwiya. Kenako anachita mantha. (2 Samueli 6:8, 9) Iye anayesedwa kwambiri pa nkhani yodalira Yehova. Pamenepa n’zochita kuonekeratu kuti analephera kutulira Yehova nkhawa zake, chifukwa sanatsatire malamulo ake. Kodi zimenezi zingatichitikirenso ifeyo nthawi zina? Kodi timaimba mlandu Yehova kuti wachititsa mavuto amene abwera chifukwa chakuti sitinamvere malangizo ake?​—Miyambo 19:3.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w05 10/1 23-24 ¶14-15

“Dikirani” Chifukwa Nthawi ya Chiweruzo Yafika

14 Pamene tikudikira, kodi tingayembekezere chiyani kuchitika? Buku la Chivumbulutso limasonyeza mmene chifuno cha Mulungu chidzakwaniritsidwira mwatsatanetsatane. Tifunika kumvera zimene bukuli limanena kuti tisonyeze kuti ndife okonzeka. Ulosiwo umafotokoza bwino kwambiri zinthu zimene zidzachitika “tsiku la Ambuye,” limene linayamba nthawi imene Khristu anaikidwa pampando wachifumu kumwamba mu 1914. (Chivumbulutso 1:10) Buku la Chivumbulutso likutisonyeza mngelo amene wapatsidwa “Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire.” Iye akulengeza ndi mawu aakulu kuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake.” (Chivumbulutso 14:6, 7) “Nthawi” ya chiweruzo imeneyi ndi yaifupi, ndipo imaphatikizapo kulengeza ziweruzo ndiponso kupereka ziweruzo zimene zasonyezedwa mu ulosi umenewu. Tsopano tili m’nthawi imeneyo.

15 Panopa, nthawi ya chiweruzo isanathe, tikulangizidwa kuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero.” Kodi zimenezi zimafuna kuti tichite chiyani? Chifukwa choopa Mulungu, tiyenera kupewa zoipa. (Miyambo 8:13) Ngati tilemekeza Mulungu, tidzam’mvera ndi kum’patsa ulemu waukulu. Sitidzakhala otanganidwa kwambiri moti n’kulephera kuwerenga Mawu ake, Baibulo, nthawi zonse. Sitidzaona malangizo ake onena kuti tizifika pamisonkhano yachikristu monga osafunika. (Ahebri 10:24, 25) Tidzayamikira kwambiri mwayi wa kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Mesiya ndipo tidzachita zimenezi mwachangu. Tidzakhulupirira Yehova nthawi zonse ndi mtima wathu wonse. (Salmo 62:8) Chifukwa timazindikira kuti Yehova ndiye Mfumu ya Chilengedwe Chonse, timam’lemekeza mwa kum’gonjera ndi mtima wonse monga Wolamulira moyo wathu. Kodi mumaopadi Mulungu ndi kum’patsa ulemerero m’njira zonsezo?

MAY 30–JUNE 5

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 7-8

“Yehova Anachita Pangano ndi Davide”

w10 4/1 20 ¶3

“Mpando Wachifumu Wako Udzakhazikika”

Komabe, Yehova anasangalala kwambiri ndi mtima umene Davide anasonyeza ndipo anamulonjeza kuti adzasankha wina m’banja lake kuti adzalamulire mpaka kalekale. Mulungu anapangana ndi Davide zimenezi chifukwa choti Davide anali wodzipereka pom’tumikira ndiponso Mulungu ankafuna kukwaniritsa ulosi winawake wa m’Baibulo. Mneneri Natani ndi amene anapereka uthenga umenewu kwa Davide. Iye anati: “Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.” (Vesi 16) Kodi Mfumu yamuyaya imene ikutchulidwa m’pangano limeneli ndi ndani?​—Salmo 89:20, 29, 34-36.

w10 4/1 20 ¶4

“Mpando Wachifumu Wako Udzakhazikika”

Yesu wa ku Nazarete anali mwana wa Davide. Polengeza za kubadwa kwa Yesu, mngelo wina anati: “Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwa muyaya, mwakuti ufumu wake sudzatha konse.” (Luka 1:32,33) Choncho zimene Yehova anapangana ndi Davide zinakwaniritsidwa mwa Yesu Khristu. Panopo iye akulamulira, osati chifukwa chosankhidwa ndi anthu, koma chifukwa cha zimene Mulungu analonjeza kuti iye adzalamulira mpaka kalekale. Zimenezi zikutikumbutsa mfundo yakuti zimene Mulungu amalonjeza, nthawi zonse zimachitikadi.​—Yesaya 55:10, 11.

w14 10/15 10 ¶14

Tizikhulupirira Kwambiri Ufumu wa Mulungu

14 Pangano lake ndi pangano la Davide. (Werengani 2 Samueli 7:12, 16.) Yehova anachita pangano ndi Davide pamene iye ankalamulira ku Yerusalemu ndipo anamulonjeza kuti Mesiya adzachokera m’banja lake. (Luka 1:30-33) Choncho Yehova anasonyeza kuti munthu wochokera m’banja la Davide adzakhala “woyenerera mwalamulo” kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. (Ezek. 21:25-27) Ufumu wa Davide “udzakhazikika mpaka kalekale” kudzera mwa Yesu. Pajanso Baibulo limanena kuti: “Mbewu yake [ya Davide] idzakhala mpaka kalekale, ndipo mpando wake wachifumu udzakhala ngati dzuwa.” (Sal. 89:34-37) Choncho pangano la Davide limatitsimikizira kuti Ufumu wa Mesiya sudzayamba kuchita zinthu mwachinyengo komanso zimene udzachite zidzathandiza anthu mpaka kalekale.

Mfundo Zothandiza

it-2 206 ¶2

Masiku Otsiriza

Ulosi wa Balamu. Aisiraeli anali atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa pamene Balamu anauza Mfumu Balaki ya ku Mowabu kuti: “Koma tamverani, ndikuuzeni zimene anthuwa [Aisiraeli] adzachite kwa anthu anu kumapeto kwa masiku otsiriza. . . . Ndithu nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo, ndodo yachifumu idzatulukadi mu Isiraeli. Ndipo iye adzaphwanya chipumi cha Mowabu ndi chigaza cha ana onse ankhondo.” (Nu 24:14-17) Pa kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosiwu, “nyenyezi” inali Mfumu Davide imene inagonjetsa Amowabu. (2Sa 8:2) Choncho n’zoonekeratu kuti pa kukwaniritsidwa koyambaku, “masiku otsiriza” anayamba pamene Davide anakhala mfumu. Ndiye popeza Davide anali mthunzi wa Yesu yemwe ndi Mfumu komanso Mesiya, ulosiwu udzakwaniritsidwanso pa nthawi imene Yesu adzagonjetse adani ake.​—Yes 9:7; Sl 2:8, 9.

JUNE 6-12

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 9-10

“Davide Anasonyeza Chikondi Chokhulupirika”

w06 6/15 14 ¶6

Mungapezedi Chimwemwe

“Davide analemba kuti: “Wodala [“wachimwemwe,” NW] iye amene asamalira wosauka.” Anapitiriza kuti: “Tsiku la tsoka Yehova adzam’pulumutsa: Yehova adzam’sunga, nadzam’sunga ndi moyo, ndipo [“adzakhala wachimwemwe” NW].” (Salmo 41:1, 2) Chisamaliro chimene Davide anapatsa Mefiboseti, mwana wolumala wa Jonatani, mnzake wapamtima wa Davide, ndi chitsanzo cha mtima woyenera kuuonetsa kwa anthu otsika.​—2 Samueli 9:1-13.

w05 5/15 17 ¶12

Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Wachiwiri

9:1, 6, 7. Davide anakwaniritsa lonjezo lake. Ifenso tiziyesetsa kukwaniritsa zimene talonjeza.

w02 2/15 14 ¶10

Anthu Okhulupirika Analimbana ndi Minga M’matupi Awo

Patapita zaka, Mfumu Davide anam’komera mtima Mefiboseti chifukwa cha chikondi chachikulu chimene anali nacho kwa Yonatani. Davide anam’patsa Mefiboseti minda yonse ya Sauli ndipo anauza mnyamata wa Sauli, Ziba, kuti azisamalira mindayo. Davide anauzanso Mefiboseti kuti: “Udzadya pa gome langa chikhalire.” (2 Samueli 9:6-10) N’zosakayikitsa kuti kukoma mtima kwa Davide kunatonthoza Mefiboseti ndipo kunathandiza kuchepetsa kuwawa kumene anali kumva chifukwa cha kupunduka kwake. Chitsanzo chabwinotu chimenechi! Ifenso tiziwakomera mtima anthu amene akulimbana ndi munga m’thupi mwawo.

Mfundo Zothandiza

it-1 266

Ndevu

Pakati pa anthu ambiri akale a Kum’mawa, kuphatikizapo Aisiraeli, munthu wamwamuna yemwe anali ndi ndevu ankalemekezedwa kwambiri. Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli, chinkawaletsa kuti asamamete ‘ndevu zotsikira m’masaya,’ zomwe ndi tsitsi limene limakhala pakati pa khutu ndi diso, ndiponso asamadule nsonga za ndevu zawo.’ (Le 19:27; 21:5) Zimenezi zinali choncho chifukwa umenewu unali mwambo wachipembedzo cha anthu ena omwe sankalambira Mulungu.

JUNE 13-19

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 11-12

“Musalole Kuti Zilakolako Zoipa Zizikulamulirani”

w21.06 17 ¶10

Mungathe Kupulumuka ku Misampha ya Satana

Dyera linachititsa Mfumu Davide kuiwala zonse zimene Yehova anamupatsa kuphatikizapo chuma, udindo komanso mmene anamuthandizira pankhondo zolimbana ndi adani ake. Poyamikira, Davide anafotokoza kuti mphatso zimene Mulungu anamupatsa zinali ‘zochuluka kwambiri moti sakanatha kuzifotokoza.’ (Sal. 40:5) Koma nthawi ina iye anaiwala zonse zimene Yehova anamupatsa. Sankakhutira ndi zomwe anali nazo moti ankafunanso zina. Ngakhale kuti anali ndi akazi ambiri, Davide anayamba kusirira mkazi wa mwiniwake. Mkaziyo anali Batiseba ndipo mwamuna wake anali Uriya Mhiti. Davide anagona ndi Batiseba ndipo anakhala ndi pakati. Kuwonjezera pamenepo, Davide anachitanso chinthu china choipa kwambiri pokonza zoti Uriya aphedwe. (2 Sam. 11:2-15) Kodi Davide ankaganiza chiyani? Kodi kapena iye ankaganiza kuti Yehova sakuona? Ngakhale kuti anali atatumikira Yehova mokhulupirika kwa nthawi yaitali, iye anachita zinthu modzikonda chifukwa cha dyera ndipo anakumana ndi mavuto aakulu. Komabe chosangalatsa n’chakuti patapita nthawi Davide anavomereza tchimo lake ndipo analapa. Iye anayamikira kwambiri Yehova chifukwa chakuti anamukhululukira.​—2 Sam. 12:7-13.

w19.09 17 ¶15

Tizigonjera Yehova ndi Mtima Wonse

15 Kuwonjezera pa kuyang’anira banja lake, Yehova anasankha Davide kuti aziyang’anira mtundu wonse wa Isiraeli. Popeza anali mfumu, Davide anali ndi mphamvu zambiri. Koma nthawi zina sankagwiritsa ntchito bwino mphamvu zake ndipo anachita machimo aakulu. (2 Sam. 11:14, 15) Koma anasonyeza kuti amagonjera Yehova polandira chilango chimene anapatsidwa. Iye anapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova ndipo ankayesetsa kutsatira malangizo ake. (Sal. 51:1-4) Davide anasonyezanso kudzichepetsa pomvera malangizo othandiza ochokera kwa amuna komanso akazi. (1 Sam. 19:11, 12; 25:32, 33) Iye anaphunzirapo kanthu pa zimene analakwitsa ndipo ankaika kutumikira Yehova pamalo oyamba.

w18.06 17 ¶7

Muziphunzitsa Chikumbumtima Chanu ndi Malamulo Komanso Mfundo za Mulungu

7 Sikuti tiyenera kuphunzira nkhwangwa ili m’mutu kenako n’kuyamba kuona ubwino wotsatira malamulo a Mulungu. Koma tikhoza kuphunzirapo kanthu pa zimene anthu ena otchulidwa m’Baibulo analakwitsa. Lemba la Miyambo 1:5 limati: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka.” Tikamawerenga komanso kuganizira mozama nkhani za m’Baibulo zimene zinachitikadi timapeza malangizo abwino kwambiri ochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Davide zinamupwetekera ataphwanya lamulo la Mulungu n’kuchita chigololo ndi Bati-seba. (2 Sam. 12:7-14) Mukamawerenga nkhaniyi mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Davide akanapewa bwanji mavuto amene anakumana nawo chifukwa chochita chigololo ndi Bati-seba? Kodi ineyo nditakumana ndi mayesero ngati amenewo ndingalimbe? Kodi ndidzathawa ngati Yosefe kapena ndidzakopeka ngati Davide?’ (Gen. 39:11-15) Tikamaganizira mavuto amene tingakumane nawo chifukwa chochita tchimo, tikhoza kutsimikiza mumtima mwathu kuti ‘tizidana ndi zoipa.’

Mfundo Zothandiza

it-1 590 ¶1

Davide

Komabe Yehova ankaona, ndipo iye anaulula nkhani yonse. Ngati Yehova akanalola kuti mlandu wa Davide ndi Batiseba uweruzidwe ndi oweruza omwe anali pansi pa Chilamulo cha Mose, ndiye kuti onse akanaphedwa ndipo mwana wosabadwayo akanafa limodzi ndi mayi ake. (De 5:18; 22:22) Komabe, Yehova anasamalira yekha nkhaniyi ndipo anamusonyeza Davide chifundo chifukwa cha pangano la Ufumu (2Sa 7:11-16), chifukwanso choti mosakayikira Davide anasonyeza ena chifundo (1Sa 24:4-7; yerekezerani ndi Yak 2:13) komanso chifukwa choti Mulungu anaona yekha kuti ochimwawo alapa. (Sl 51:1-4) Komabe anapatsidwa zilango zina. Kudzera mwa mneneri Natani, Yehova ananena kuti: “Ndikukugwetsera tsoka m’nyumba yako yomwe.”​—2Sa 12:1-12.

JUNE 20-26

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 13-14

“Kudzikonda kwa Aminoni Kunabweretsa Mavuto”

it-1 32

Abisalomu

Kuphedwa kwa Aminoni. Aminoni anakopeka ndi kukongola kwa Tamara, yemwe anali mlongo wa m’bale wake, Abisalomu. Aminoni ananamizira kudwala ndipo anakakamira kuti Tamara apite kunyumba kwake kukamuphikira, kenako anamugwiririra. Aminoni anada kwambiri Tamara pambuyo poti wagona naye ndipo anamuthamangitsa. Tamara anang’amba malaya ake amizeremizere omwe ana a mfumu amene anali anamwali ankavala, ndipo anadzithira phulusa kumutu, kenako anakumana ndi Abisalomu. Mwamsanga Abisalomu anazindikira kuti ndi mchimwene wake Aminoni amene wamuchita chipongwecho, ndipo anasonyeza kuti ankadziwa bwino zolakalaka za dyera za mchimwene wakeyo. Komabe Abisalomu anamuuza mchemwali wakeyo kuti asadandaule ndipo anamutenga kuti azikakhala naye kunyumba kwake.​—2Sa 13:1-20.

w17.09 5 ¶11

Tiziyesetsa Kukhala Odziletsa

11 M’Baibulo muli zitsanzo zina za anthu amene analephera kudziletsa pa nkhani ya chiwerewere. Baibulo limasonyezanso mavuto amene munthu angakumane nawo chifukwa cholephera kudziletsa pa nkhaniyi. Tikamayesedwa kuti tichite chiwerewere tingachite bwino kuganizira za mnyamata wopanda nzeru amene watchulidwa m’chaputala 7 cha buku la Miyambo. Tingaganizirenso zimene Aminoni anachita komanso mavuto amene anakumana nawo. (2 Sam. 13:1, 2, 10-15, 28-32) Makolo angathandize ana awo kuti akhale odziletsa komanso azichita zinthu mwanzeru pa nkhani imeneyi. Angachite zimenezi akamakambirana nawo nkhani za m’Baibulo zimene tatchulazi pa kulambira kwa pabanja.

it-1 33 ¶1

Abisalomu

Panatha zaka ziwiri. Nthawi ya chikondwerero chometa ubweya wankhosa itakwana, Abisalomu anakonza phwando ku Baala-hazori, komwe kunali kutali makilomita 22 kumpoto kwenikweni chakum’mawa kwa Yerusalemu, ndipo anaitana Davide limodzi ndi ana ake aamuna. Bambo ake atanena kuti sakapezekako, Abisalomu anapempha kuti alole Aminoni mwana wawo woyamba kuti akapezekeko m’malo mwawo. (Miy 10:18) Ali ku phwandoko, Aminoni ‘atasangalala kwambiri ndi vinyo mumtima mwake,’ Abisalomu anauza atumiki ake kuti amuphe. Ana enawo anabwerera ku Yerusalemu, ndipo Abisalomu anathawira ku Gesuri kum’mawa kwa Nyanja ya Galileya, komwe kunali kwa agogo ake aamuna omwe anali Msiriya. (2Sa 13:23-38) “Lupanga” lomwe mneneri Natani analosera linafika “panyumba” ya Davide, ndipo linakhalabe pomwepo kwa moyo wake wonse.​—2Sa 12:10.

Mfundo Zothandiza

g05 1/8 24-25

Kukongola Kofunika Kwambiri

Mosiyana ndi zimenezi, taganizirani za Abisalomu, mmodzi mwa ana a Davide. Anadzakhala munthu woipa kwambiri ngakhale kuti anali wooneka bwino. Ponena za iye, Baibulo limati: “Ndipo m’Israyeli monse munalibe wina anthu anam’tama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wake mwa iye munalibe chilema.” (2 Samueli 14:25) Komabe, mtima wa Abisalomu wofuna kukhala ndi udindo unamuchititsa kuukira bambo ake ndi kulanda ufumu wawo. Anafika mpaka pogona ndi akazi aang’ono a bambo ake. Chifukwa cha zimenezi, Abisalomu anakwiyitsa Mulungu ndipo anafa imfa yopweteka.​—2 Samueli 15:10-14; 16:13-22; 17:14; 18:9, 15.

Kodi mumakopeka ndi Abisalomu? Ayi ndithu. Iye anali munthu wakhalidwe lonyansa. Kukongola kwake kogometsa sikunalungamitse kukula mtima ndi kusakhulupirika kwake, ndiponso sikunamuteteze kuti asawonongedwe. Koma m’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu anzeru ndiponso okopa amene sanatchulidwe maonekedwe awo. Mwachidziwikire, chimene chinali chofunika kwambiri chinali kukongola kwawo kwa mumtima.

JUNE 27–JULY 3

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 SAMUELI 15-17

“Abisalomu Anaukira Chifukwa cha Kunyada”

it-1 860

Kalambulabwalo

Unali mwambo wa anthu a Kum’mawa kuti ena ankathamanga patsogolo pa galeta la chifumu kuti akakonze malo komanso akalengeze za kubwera kwa mfumu ndiponso kuti azithandiza mfumu pa zinthu zina ndi zina. (1Sa 8:11) Pofuna kutengera zimene mafumuwo ankachita, kudzipezera ulemerero komanso kudzitamandira ndi kugalukira komwe anachita, Abisalomu ndi Adoniya anaika amuna 50 patsogolo pa magaleta awo.​—2Sa 15:1; 1Mf 1:5.

w12 7/15 13 ¶5

Tumikirani Mulungu Amene Amapereka Ufulu

5 M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anapotoza maganizo a anzawo. Chitsanzo china ndi mwana wa Mfumu Davide, dzina lake Abisalomu. Iye anali mwamuna wooneka bwino kwambiri. Koma mofanana ndi Satana, anayamba kulakalaka udindo ndiponso mphamvu. Anayamba kusirira mpando wachifumu wa abambo ake ngakhale kuti sanali woyenera kukhala pa mpandowu. Pofuna kulanda ufumu mochenjera, Abisalomu ankanamizira kuti amakonda kwambiri Aisiraeli anzake. Ankawachititsa kuganiza kuti mfumu ndi anthu ake sawaganizira. Mofanana ndi Mdyerekezi m’munda wa Edeni, Abisalomu ankadzionetsa ngati akufuna kuthandiza anthu koma pa nthawi imodzimodziyo akuipitsa mbiri ya atate wake.​—2 Sam. 15:1-5.

it-1 1083-1084

Heburoni

Patapita zaka, Abisalomu yemwe anali mwana wa Davide anabwerera ku Heburoni ndipo anakonza zoti alande ufumu wa bambo ake. (2Sa 15:7-10) N’kutheka kuti Abisalomu anasankha kuti ayambire kulanda mzinda wa Heburoni chifukwa chakuti poyamba unali likulu la Yuda kapenanso chifukwa chakuti kunali kwawo kobadwira. Kenako mdzukulu wa Davide Rehobowamu anamanganso mzinda wa Heburoni. (2Mb 11:5-10) Ababulo atawononga mzinda wa Yuda, Ayudawo anapita ku ukapolo. Ena mwa amene anabwerera anakakhala ku Heburoni (Kiriyati-ariba).​—Ne 11:25.

Mfundo Zothandiza

w18.08 6 ¶11

Kodi Mukudziwa Nkhani Yonse?

11 Ifenso tikhoza kuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo chifukwa choti anthu ena afalitsa nkhani yokhudza ifeyo koma sanafotokoze mfundo zonse kapena anafotokoza mfundo zina zabodza. Chitsanzo ndi zimene zinachitikira Davide ndi Mefiboseti. Davide anakomera mtima Mefiboseti pomupatsa malo onse a Sauli, yemwe anali agogo ake. (2 Sam. 9:6, 7) Koma patapita nthawi, Davide anamva zinthu zoipa zokhudza Mefiboseti. Iye asanafufuze n’komwe nkhaniyi, analanda Mefiboseti zinthu zake zonse. (2 Sam. 16:1-4) Koma kenako Davide analankhula ndi Mefiboseti n’kuzindikira kuti analakwitsa ndipo anamubwezera zinthu zake zina. (2 Sam. 19:24-29) Davide akanayamba wafufuza kaye kuti adziwe zonse, zinthu zopanda chilungamozi sizikanachitika.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w09 5/15 27-28

Tsanzirani Kukhulupirika kwa Itai

Zikuoneka kuti Itai anali wochokera mumzinda wotchuka wa Afilisti wotchedwa Gati. Kumeneku kunalinso kwawo kwa chimphona chotchedwa Goliati ndiponso adani ena oopsa a Aisiraeli. Popanda kunena za mbiri yake, Baibulo limangoyamba kunena zimene Itai anachita pofotokoza za nthawi imene Abisalomu anaukira Mfumu Davide. Itai ndi anthu 600 amene ankamutsatira anathawa kwawo n’kukakhala kudera la pafupi ndi Yerusalemu.

Zimene zinamuchitikira Itai, ziyenera kuti zinakumbutsa Davide nthawi imene anathawira kudera la Afilisiti limodzi ndi Aisiraeli 600 ankhondo. Iye anakakhala kudera limene Akisi mfumu ya Gati inkalamulira. (1 Sam. 27:2, 3) Kodi Itai ndi anthu ake anatani Davide ataukiridwa ndi mwana wake Abisalomu? Kodi iwo anakhala kumbali ya Abisalomu, ya Davide kapena sanalowerere mbali ina iliyonse?

Tangoganizirani mmene zinalili panthawiyo. Davide atathawa ku Yerusalemu, anaima pamalo otchedwa “Nyumba ya Payokha.” N’kutheka kuti nyumbayi inali yomalizira pochoka ku Yerusalemu kupita ku Phiri la Maolivi, tisanadutse chigwa cha Kidroni. (2 Sam. 15:17) Akudutsa pamenepa, Davide anawerenganso asilikali ake. Iye anadabwa atapeza kuti m’gululi munali Aisiraeli okhulupirika komanso Akereti ndi Apeleti. Panalinso Itai ndi asilikali ake okwana 600 omwe anali Agiti.​—2 Sam. 15:18.

Pamenepa, Davide anafunsa Itai kuti: “Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu [ayenera kuti amatanthauza Abisalomu]; pakuti uli mlendo ndi wopitikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha. Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe.”​—2 Sam. 15:19, 20.

Kukhulupirika kwenikweni kwa Itai kunaonekera ndi mawu amene anayankha. Iye anati: “Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena m’paimfa kapena m’pamoyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.” (2 Sam. 15:21) Pamenepa mwina Davide anakumbukira mawu a Rute, yemwe anali agogo a bambo ake. (Rute 1:16, 17) Mawu a Itai anam’khudza mtima kwambiri Davide moti anamuuza kuti: “Tiye nuoloke” chigwa cha Kidroni. Pamenepo “Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ake onse, ndi ana aang’ono onse amene anali naye.”​—2 Sam. 15:22.

“Zitilangize Ife”

Lemba la Aroma 15:4 limati: “Pakuti zonse zimene zinalembedweratu zinalembedwa kuti zitilangize ife.” Motero ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Itai?’ Taganizirani zimene mwina zinam’chititsa kukhala wokhulupirika kwa Davide. Ngakhale kuti Itai anali mlendo yemwe anapitikitsidwa kwawo kudziko la Afilisiti, iye ankadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu wamoyo ndiponso kuti Davide anali wodzozedwa Wake. Itai sanasunge mumtima chidani chimene chinalipo pakati pa Aisiraeli ndi Afilisiti. Ngakhale kuti Davide anapha Goliati, chimphona cha fuko lake la Afilisiti ndiponso Afilisiti ena ambirimbiri, Itai sankaganizira zimenezi. (1 Sam. 18:6, 7) Itai anaona kuti Davide anali munthu wokonda Yehova ndipo n’zosakayikitsa kuti anaonanso makhalidwe abwino kwambiri amene Davide anali nawo. Izi zinachititsanso kuti Davide ayambe kukonda kwambiri Itai. Ndipo Davide anapereka gawo limodzi mwa magawo atatu a asilikali ake kuti “aliyang’anire Itai” pa nkhondo yaikulu yomenyana ndi Abisalomu.​—2 Sam. 18:2.

Ifenso tiziyesetsa kusaganizira kwambiri za chikhalidwe, fuko, mtundu kapena zinthu zina zilizonse zimene zingachititse kuti tizisala kapena kudana ndi anthu ena. M’malomwake, tiziganizira kwambiri za makhalidwe abwino amene anthuwo ali nawo. Mgwirizano umene unali pakati pa Davide ndi Itai umasonyeza kuti kudziwa Yehova ndi kuyamba kum’konda kungatithandizenso kuona ena m’njira yoyenerera.

Poganizira chitsanzo cha Itai, tingadzifunse kuti: ‘Kodi inenso ndimasonyeza kukhulupirika ngati kumeneku kwa Khristu Yesu, yemwe ndi Davide Wamkulu? Kodi ndimasonyeza kukhulupirika kwanga pochita nawo mwakhama ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira?’ (Mat. 24:14; 28:19, 20) Tingadzifunsenso kuti ‘Kodi ndingalolere kupirira zinthu zotani kuti ndisonyeze kukhulupirika kwanga?’

Mitu ya mabanja ingapindulenso kwambiri posinkhasinkha za chitsanzo cha Itai cha kukhulupirika. Zimene anachita posafuna kulekana ndi Davide ndiponso posankha kukhala m’gulu la mfumu yodzozedwa ndi Mulungu imeneyi zinakhudzanso anthu amene anali naye. Ndi mmenenso zilili ndi zinthu zimene mitu ya banja imasankha kuchita pofuna kuchirikiza kulambira koona. Nazonso zimakhudza anthu a m’banja mwawo ndipo nthawi zina zingathe kuwabweretsera mavuto ena. Komabe, Baibulo limatitsimikizira kuti: ‘Pa munthu wangwiro [kapena kuti wokhulupirika] Yehova amakhalanso wangwiro.’​—Sal. 18:25.

Pambuyo pofotokoza za nkhondo imene Davide anamenyana ndi Abisalomu, Malemba satchulapo chilichonse chokhudza Itai. Komabe, nkhani yachidule yonena za Itai, yomwe ili m’Mawu a Mulungu imatithandiza kwambiri kumudziwa bwino. Timatero poona zimene anachita pa nthawi yovuta kwambiri pa moyo wa Davide. Popeza kuti nkhani ya Itai imapezeka m’Baibulo, zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amaona ndipo amadalitsa anthu okhulupirika.​—Aheb. 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena