Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr22 September tsamba 1-16
  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Timitu
  • SEPTEMBER 5-11
  • SEPTEMBER 12-18
  • SEPTEMBER 19-25
  • SEPTEMBER 26–​OCTOBER 2
  • OCTOBER 3-9
  • OCTOBER 10-16
  • OCTOBER 17-23
  • OCTOBER 24-30
  • OCTOBER 31–NOVEMBER 6
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwbr22 September tsamba 1-16

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

SEPTEMBER 5-11

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 9-10

“Tizitamanda Yehova Chifukwa ndi Wanzeru”

w99 7/1 30 ¶6

Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambiri

Mfumukaziyo itakumana ndi Solomo, inayamba kumuyesa ndi “mafunso ovuta.” (1 Mafumu 10:1) Mawu a Chiheberi amene anagwiritsidwa ntchito pamenepa, angamasuliridwenso kuti “ndagi.” Koma izi sizikutanthauza kuti mfumukaziyo inkacheza ndi Solomo nkhani zopanda pake. Chosangalatsa n’chakuti, pa Salimo 49:4, liwu la Chiheberi lomweli likugwiritsidwanso ntchito pofotokoza za mafunso ofunika kwambiri okhudza uchimo, imfa, ndi kupulumutsidwa. Choncho, n’kutheka kuti mfumukazi ya ku Sheba inkakambirana ndi Solomo nkhani zofunika kwambiri zomwe zinachititsa kuti aone kuchuluka kwa nzeru zake. Baibulo limati iye anayamba “kunena zonse zimene zinali kumtima kwake.” Ndipo Solomo “anaiyankha mfumukaziyo mafunso ake onse. Panalibe chimene mfumuyo inalephera kuyankha.”​—1 Mafumu 10:2b, 3.

w99 11/1 20 ¶6

Anthu Ambiri Owolowa Manja

Podabwa ndi zimene inamva ndi kuona, mfumukaziyo inanena kuti: “Odala atumiki anuwa amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzeru zanu.” (1 Mafumu 10:4-8) Ngakhale kuti zinalidi choncho, mfumukaziyi sinanene kuti anyamata a Solomo anali odala chifukwa chakuti komwe ankakhala kunali chuma chambiri. M’malomwake, anyamata a Solomo anali odala chifukwa chakuti nthawi zonse anali ndi mwayi womvetsera nzeru zimene Solomo anapatsidwa ndi Mulungu. Mfumukazi ya ku Sheba ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu a Yehova masiku ano, amene amasangalala kuphunzira nzeru za Mlengi wawo komanso Mwana wake, Yesu Khristu.

w99 7/1 30-31

Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambiri

Mfumukazi ya ku Sheba inagoma kwambiri ndi nzeru za Solomo komanso ulemerero wa ufumu wake kotero kuti “inazizira nkhongono.” (1 Mafumu 10:4, 5) Ena amati mfumukaziyo “inabanika.” Katswiri wina wamaphunziro mpaka ananena kuti mwina inakomoka. Kaya panachitika zotani, mfumukaziyi inadabwa ndi zimene inaona ndi kumva. Inati anyamata a Solomo anali odala chifukwa ankamva nzeru za mfumuyi, ndipo inadalitsa Yehova chifukwa chopatsa Solomo ufumu. Kenako mfumukaziyi inapereka kwa mfumuyo mphatso zamtengo wapatali, moti golide yekha anali wokwana ndalama pafupifupi $40,000,000 mogwirizana ndi mitengo ya masiku ano. Nayenso Solomo anapereka kwa mfumukazi ya ku Sheba “zofuna zake zonse zimene inapempha.”​—1 Mafumu 10:6-13.

Mfundo Zothandiza

w08 11/1 22 ¶4-6

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mfumu Solomo inali ndi golide wochuluka bwanji?

Malemba amanena kuti Hiramu mfumu ya ku Turo, inatumiza matani anayi a golide kwa Solomo ndipo mfumukazi ya ku Seba inaperekanso matani anayi a golide. Komanso zombo za Solomo zinkabweretsa matani oposa 14 a golide kuchokera ku Ofiri. Baibulo limati: “Kulemera kwake kwa golidi anafika kwa Solomo chaka chimodzi kunali matalenti mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golidi.” Amenewa ndi matani oposa 22. (1 Mafumu 9:14, 28; 10:10, 14) Kodi zimenezi ndi zoona? Kodi panthawi imeneyo nkhokwe za golide za mafumu zinali zazikulu bwanji?

Zolemba zakale, zimene akatswiri amati ndi zodalirika, zimanena kuti Farao Thutmose III wa ku Iguputo (yemwe anakhalako zaka pafupifupi 3,500 zapitazo) anapereka matani pafupifupi 12 a golide ku kachisi wa Amun-Ra ku Karnak. Cha m’ma 700 B.C.E., mfumu ya Asuri Tigilati Pilesere III, inalandira matani anayi a golide kuchokera ku Turo ngati msonkho, ndipo Sarigoni II anaperekanso matani anayi ngati mphatso kwa milungu ya ku Babulo. Mfumu Filipo II ya ku Makedoniya (359-336 B.C.E.) akuti inkakumba matani oposa 25 a golide chaka chilichonse m’migodi ya Pangaeum ku Thrace.

Mwana wa Filipo, Alesandro Wamkulu (336-323 B.C.E.) atalanda mzinda wa ku Perisiya wotchedwa Susa, akuti anatenga matani pafupifupi 1,070 a golide. Iye anatenganso matani oposa 6,000 kuchokera ku Perisiya konse. Choncho, tikayerekezera ndi zitsanzo zimenezi, zimene Baibulo limanena zokhudza golide wa Mfumu Solomo si kukokomeza.

SEPTEMBER 12-18

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 11-12

“Sankhani Mwanzeru Munthu Wokwatirana Naye”

w18.07 18 ¶7

“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

7 Pali zinthu zambiri zimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Mfumu Solomo. Iye ali wachinyamata ankadalira Yehova kuti amupatse malangizo. Ndipo Yehova anamupatsa nzeru zambiri komanso udindo womanga kachisi waulemerero ku Yerusalemu. Koma Solomo anasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova. (1 Maf. 3:12; 11:1, 2) Mulungu anapereka lamulo loletsa mafumu a Chiheberi kukwatira ‘akazi ambiri kuti mtima wawo ungapatuke.’ (Deut. 17:17) Koma Solomo sanamvere lamuloli moti anakwatira akazi 700 komanso anali ndi akazi ena apambali okwana 300. (1 Maf. 11:3) Ambiri mwa akaziwa sanali Aisiraeli ndipo ankalambira milungu yonyenga. Choncho Solomo sanamverenso lamulo la Mulungu loletsa kukwatira akazi amitundu ina.​—Deut. 7:3, 4.

w19.01 15 ¶6

Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?

6 Satana ndi chigawenga chodzikonda komanso chosamvera Yehova ndipo amafuna kuti nafenso tizichita zomwezo. Koma sangatikakamize kutengera maganizo kapena zochita zake. Choncho amagwiritsa ntchito njira zina pofuna kutisokoneza. Mwachitsanzo, angagwiritse ntchito anthu a m’dzikoli omwe wawasocheretsa kale. (1 Yoh. 5:19) Iye amafuna kuti tizicheza nawo kwambiri ngakhale kuti timadziwa mfundo yoti kugwirizana ndi anthu oipa “kumawononga” maganizo ndi makhalidwe athu. (1 Akor. 15:33) Satana anagwiritsa ntchito njira imeneyi posokoneza Mfumu Solomo. Paja Solomo anakwatira akazi ambiri osalambira Yehova omwe pamapeto pake “anapotoza mtima” wake.​—1 Maf. 11:3.

w18.07 19 ¶9

“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

9 Koma Yehova salekerera machimo. Baibulo limanena kuti: “Yehova anamukwiyira kwambiri Solomo chifukwa mtima wake unapatuka kwa Yehova . . . , amene anamuonekera kawiri konse. Pa nkhani imeneyi, Mulungu anali atamulamula kuti asatsatire milungu ina, koma iye sanasunge zimene Yehova analamula.” Zochita za Solomo zinachititsa kuti Yehova asiye kumukonda komanso kumuthandiza. Ana ake anataya mwayi wolamulira mtundu wonse wa Isiraeli chifukwa ufumuwo unagawikana ndipo anakumana ndi mavuto ambiri.​—1 Maf. 11:9-13.

Mfundo Zothandiza

w18.06 14 ¶1-4

Akanatha Kusangalatsa Mulungu

Anthu atachoka mu ufumu wake, Rehobowamu anasonkhanitsa asilikali ake. Koma Yehova anatumiza mneneri Semaya kuti akamuuze kuti: “Musapite kukamenyana ndi abale anu, ana a Isiraeli. Aliyense abwerere kunyumba kwake, chifukwa zimene zachitikazi, zachitika mwa kufuna kwanga.”​—1 Maf. 12:21-24.

Rehobowamu ayenera kuti anavutika kwambiri kutsatira zimene Mulungu ananenazi chifukwa chodera nkhawa zimene Aisiraeliwo angaganize. Iye anali atanena kuti awalanga ndi “zikoti zaminga.” Ndiye kodi Aisiraeliwo akanaganiza bwanji ataona kuti sakuchita chilichonse pamene iwo ankachoka mu Ufumu wake? (Yerekezerani ndi 2 Mbiri 13:7.) Ngakhale zinali choncho, mfumuyo ndiponso asilikali ake “anamvera mawu a Yehova n’kubwerera kwawo.”

Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kumvera Mulungu ngakhale pamene tikuona kuti anthu atinyoza chifukwa chochita zimenezi. Tikamamvera Mulungu, iye adzasangalala nafe komanso kutidalitsa.​—Deut. 28:2.

Rehobowamu anamveradi Mulungu ndipo anasiya mapulani ake okamenyana ndi ufumu watsopanowo. Kenako anayamba kumanga mizinda m’mafuko a Yuda ndi Benjamini omwe ankawalamulirabe. Iye ‘analimbitsanso kwambiri’ mizinda yochuluka. (2 Mbiri 11:5-12) Koma chofunika kwambiri n’chakuti kwa nthawi ndithu anamvera malamulo a Yehova. Anthu a mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 umene unkalamuliridwa ndi Yerobowamu anayamba kulambira mafano. Choncho ambiri anapita ku Yerusalemu ‘kukalimbikitsa Rehobowamu’ komanso kukasonyeza kuti anali kumbali ya kulambira koona. (2 Mbiri 11:16, 17) Apatu Rehobowamu analimbitsa ufumu wake chifukwa chomvera Yehova.

SEPTEMBER 19-25

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 13-14

“N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Okhutira Komanso Odzichepetsa?”

w08 8/15 8 ¶4

Khalani Okhulupirika ndi Mtima Wonse

4 Ndiyeno Yerobiamu anauza munthu wa Mulunguyo kuti: “Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso.” (1 Maf. 13:7) Kodi pamenepa mneneriyo akanatani tsopano? Kodi akanavomera kupita ku nyumba kwa mfumuyo atapereka uthengawo? (Sal. 119:113) Kapena kodi akanakana kupita ku nyumba kwa mfumu ngakhale kuti mfumuyo inali itazindikira kulakwa kwake? Yerobiamu anali wolemera moti akanatha kupatsa anthu mphatso zamtengo wapatali. Ngati mneneri wa Mulungu anali ndi kamtima kokonda chuma, mphatso zimene mfumuyo imafuna kum’patsa zikanakhala chiyeso chachikulu. Koma Yehova anali atauza mneneriyo kuti: “Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.” Choncho, mneneriyo anayankha mfumuyo mwamphamvu kuti: “Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowa kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.” Ndipo mneneriyo atachoka ku Beteli anadzera njira ina. (1 Maf. 13:8-10) Kodi zimene mneneriyu anachita zikutiphunzitsa chiyani pankhani yokhulupirika ndi mtima wonse.​—Aroma 15:4.

w08 8/15 11 ¶15

Khalani Okhulupirika ndi Mtima Wonse

15 Kodi zimene mneneri wa ku Yuda analakwitsa zikutiphunzitsanso chiyani? Lemba la Miyambo 3:5 limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” M’malo moti mneneriyu akhulupirirebe Yehova monga amachitira kale, iye anayendera maganizo ake. Zimenezi zinam’phetsa komanso zinachititsa kuti asakhale ndi dzina labwino ndi Mulungu. Izi zikusonyezeratu kuti tifunika kukhala odzichepetsa ndiponso okhulupirika potumikira Yehova.

w08 8/15 9 ¶10

Khalani Okhulupirika ndi Mtima Wonse

10 Mneneri wa ku Yuda akanatha kudziwa kuti mneneri wokalambayu amamunamiza. Iye akanadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova watumiza mngelo kuuza munthu wina malangizo osiyana ndi amene anandiuza?’ Mneneriyu akanatha kupempha Yehova kuti am’fotokozere bwinobwino nkhaniyo, koma Malemba sasonyeza kuti iye anachita zimenezi. Komano, “anabwerera naye [munthu wokalambayo], nakadya kwawo, namwa madzi.” Koma Yehova sanasangalale ndi zimenezi. Mneneri amene ananamizidwayo akubwerera kwawo ku Yuda, anapezana ndi mkango panjira ndipo unamupha. Ntchito yake ya uneneriyo inathera pomwepo.​—1 Maf. 13:19-25.

Mfundo Zothandiza

w10 7/1 29 ¶5

Amaona Zabwino mwa Anthu

Chofunika kwambiri ndi chakuti mawu a pa 1 Mafumu 14:13 amatiphunzitsa mfundo ina yabwino kwambiri yokhudza Yehova ndiponso zimene amaona mwa ife. Kumbukirani kuti chinthu china chabwino ‘chinapezedwa mwa’ Abiya. Zikuoneka kuti Yehova anafufuza mumtima wa Abiya mpaka atapeza chinthu chabwino. Pomuyerekezera ndi anthu a m’banja lake, katswiri wina wamaphunziro ananena kuti Abiya anali “ngati mwala wamtengo wapatali womwe uli pamulu wamiyala wamba.” Yehova anasangalala chifukwa cha zabwino zimene Abiya anachita. Chifukwa cha zimenezi Mulungu anachitira chifundo munthu ameneyu, amene anali wabwino m’banja lawo lonse.

SEPTEMBER 26–​OCTOBER 2

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 15-16

“Kodi Mumachita Zinthu Molimba Mtima Ngati Asa?”

w12 8/15 8 ¶4

“Mudzapeza Mphoto Chifukwa cha Ntchito Yanu”

Asa anayamba kulamulira mu 977 B.C.E. Nthawi imeneyi n’kuti Isiraeli ndi Yuda atagawikana kukhala maufumu awiri kwa zaka 20. Pa nthawiyi, kulambira konyenga kunali ponseponse mu Yuda. Nawonso anthu a maudindo mu ufumuwu ankalambira milungu ya ku Kanani imene ankati ndi yobereketsa. Ponena za Mfumu Asa, Baibulo limati: “Anachita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake.” Iye “anachotsa maguwa ansembe achilendo, anagwetsa malo okwezeka, anaphwanya zipilala zopatulika ndi kudula mizati yopatulika.” (2 Mbiri 14:2, 3) Asa anachotsanso m’Yuda monse “mahule aamuna a pakachisi” amene ankagonana ndi amuna anzawo polambira milungu yawo. Koma pali zinanso zimene Asa anachita. Iye analimbikitsanso anthu kuti “afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatira chilamulo” chake.​—1 Maf. 15:12, 13; 2 Mbiri 14:4

w17.03 19 ¶7

Tizitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

7 Tonsefe tiyenera kufufuza mtima wathu kuti tione ngati timatumikira Mulungu modzipereka kwambiri. Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndimafunitsitsa kusangalatsa Yehova, kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera komanso kuteteza anthu a Mulungu ku zinthu zoipa?’ Asa anafunikatu kukhala wolimba mtima kuti achotse a Maaka pa udindo wokhala “mayi wa mfumu.” Nthawi zina inunso mungafunike kukhala olimba mtima ngati Asa. Mwachitsanzo, kodi mumatani ngati wachibale kapena mnzanu wapamtima wachita tchimo koma sanalape ndipo wachotsedwa mumpingo? Kodi mungalimbe mtima n’kusiya kuchita naye zinthu? Kodi mtima wanu umakulimbikitsani kutsatira malangizo a Mulungu?

it-1 184-185

Asa

Ngakhale kuti nthawi zina Asa ankachita zinthu mopanda nzeru komanso ankalephera kusonyeza kuzindikira pa zinthu zokhudza kulambira, n’zoonekeratu kuti zinthu zabwino zomwe ankachita monga makhalidwe ake abwino komanso kupewa zinthu zampatuko zinkaposa zolakwa zimene ankachita, ndipo ankaonedwa kuti ndi mmodzi wa mafumu a Yuda. (2 Mbiri 15:17) Asa analamulira kwa zaka 41, ndipo analamulira pa nthawi yofanana ndi mafumu 8 a Isiraeli omwe ndi Yerobowamu, Nadabu, Basa, Ela, Zimiri, Omuri, Tibini (yemwe analamulira gulu lina la Aisiraeli omwe ankatsutsana ndi Omuri) ndi Ahabu. (1Mf 15:9, 25, 33; 16:8, 15, 16, 21, 23, 29) Asa atamwalira, mwana wake Yehosafati anakhala mfumu.​—1Mf 15:24.

Mfundo Zothandiza

w98 9/15 21-22

Kodi Mumaona Kuti Mulungu Ndi Weniweni kwa Inu?

Mwachitsanzo, werengani za ulosi wonena za chilango chimene munthu amene adzamangenso Yeriko adzalandire ndipo onani mmene unakwaniritsidwira. Lemba la Yoswa 6:26 limati: “Yoswa analumbira kuti: ‘Adzakhale wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzamangenso mzinda wa Yerikowu. Akadzangoyala maziko ake, mwana wake woyamba adzafe, ndipo akadzaika zitseko zake za pachipata, mwana wake wotsiriza adzafe.’” Ulosiwu unakwaniritsidwa patapita zaka pafupifupi 500, ndipo ndi zimene timawerenga pa 1 Mafumu 16:34 kuti: “M’masiku ake, [a Mfumu Ahabu] Hiyeli wa ku Beteli anamanga Yeriko. Atangoyala maziko ake, Abiramu mwana wake woyamba anafa, ndipo atangoika zitseko zake za pachipata, Segubu mwana wake wotsiriza anafa. Izi zinachitika mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni.” Mulungu woona yekha ndi amene anganene maulosi oterewa n’kukwaniritsidwa.

OCTOBER 3-9

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 17-18

“Kodi Mukayikakayika Mpaka Liti?”

w17.03 14 ¶6

Muzikhulupirira Yehova Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru

6 Aisiraeli ali m’Dziko Lolonjezedwa ankafunika kusankha kulambira Yehova kapena milungu ina. (Werengani Yoswa 24:15.) Zimene akanasankha pa nkhaniyi zikanachititsa kuti akhale ndi moyo kapena afe. Mwina mungaganize kuti nkhani imeneyi inali yosavuta kusankha. Komabe n’zodabwitsa kuti m’nthawi ya oweruza, Aisiraeli mobwerezabwereza sankasankha zochita mwanzeru. Iwo ankasiya kutumikira Yehova n’kumatumikira milungu ina. (Ower. 2:3, 11-23) Kenako m’nthawi ya Eliya, Aisiraeli ankafunika kusankha kutumikira Mulungu kapena Baala. (1 Maf. 18:21) Ena angaganize kuti zinalinso zosavuta kusankha pa nkhaniyi chifukwa woyenera kumulambira ndi Yehova. Munthu woganiza bwino sangasankhe kulambira mulungu wopanda moyo. Koma Aisiraeliwo analephera kusankha ndipo ‘ankangokayikakayika.’ Choncho Eliya anawalimbikitsa kuti ayenera kusankha kulambira Yehova chifukwa ndi Mulungu woona.

ia 88 ¶15

Sanasunthike pa Kulambira Koona

15 Zitatero ansembe a Baala analusa kwambiri ndipo “anayamba kuitana mokuwa kwambiri n’kumadzicheka ndi mipeni ndi mikondo ing’onoing’ono malinga ndi mwambo wawo, mpaka magazi anayamba kutuluka ndi kuyenderera pamatupi awo.” Koma zonsezi sizinaphule kanthu chifukwa “sipanamveke mawu alionse. Palibe anawayankha kapena kuwamvera.” (1 Maf. 18:28, 29) Izi zinasonyeza kuti Baala anali mulungu wongopeka chabe, woti kunalibe. Satana ndi amene anapangitsa anthuwo kuti aziganiza kuti kuli Baala n’cholinga choti asiye kulambira Yehova. Koma zomwe tiyenera kudziwa ndi zakuti, ngati titasankha mbuye wina osati Yehova, tidzagwiritsidwa mwala ndiponso tidzachita manyazi.​—Werengani Salimo 25:3; 115:4-8.

ia 90 ¶18

Sanasunthike pa Kulambira Koona

18 Eliya asanapemphere, anthuwo ayenera kuti ankaganiza kuti Yehova nayenso saatha kuyatsa moto. Koma zimene anthuwa anaona Eliya atangomaliza kupemphera, zinawapangitsa kuti asakayikenso. Nkhaniyi imati: “Atatero, moto wa Yehova unatsika n’kunyeketsa nsembe yopsereza ija, nkhuni, miyala ndi fumbi lomwe. Unaumitsanso madzi amene anali m’ngalande muja.” (1 Maf. 18:38) Ili linalidi yankho lothetsa makani. Koma kodi anthu anatani ataona zimenezi?

Mfundo Zothandiza

w08 4/1 19, bokosi

Anali Watcheru Ndiponso Anadikira

Kodi Panadutsa Nthawi Yotalika Motani Kuti Chilala cha M’masiku a Eliya Chithe?

Eliya, mneneri wa Yehova anauza Mfumu Ahabu kuti chilala chomwe chinatenga nthawi yaitali chinali chitatsala pang’ono kutha. Eliya ananena zimenezi mu “chaka chachitatu” kuchokera panthawi imene iye analengeza kuti kudzakhala chilala. (1 Mafumu 18:1) Ndipo Yehova anavumbitsadi mvula, Eliya atangolengeza kumene kuti chilalacho chitha. Choncho anthu ena angaganize kuti chilalacho chinatha m’kati mwa chaka cha chitatu ndipo zimenezi zingasonyeze kuti sichinathe zaka zitatu. Komabe, Yesu ndi Yakobe amati chilalacho chinatenga “zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi.” (Luka 4:25; Yakobe 5:17) Kodi pamenepa Baibulo likudzitsutsa lokha?

Ayi, sichoncho. Monga mmene mwaonera, ku Isiraeli nyengo ya chilimwe inali yaitali ndithu mpaka miyezi 6. Mosakayikira Eliya anafika kwa Ahabu m’nyengo ya chilimwe kudzamuuza kuti kudzakhala chilala. Ndipo panthawiyi n’kuti chilala chitayamba kale chifukwa nthawi imene nyengo ya chilimwe imayenera kutha inali itapitirira. Ndipo zimenezi zikutanthauza kuti panali patapita pafupifupi miyezi 6 kuchokera pamene chilalacho chinayamba. Choncho, kuchokera pamene Eliya analengeza kuti kudzakhala chilala kufikira nthawi imene analengeza kuti chitha, panadutsa ‘zaka zitatu.’ Izi zikusonyeza kuti chilalacho chinatha zaka zitatu ndi theka. Motero, panthawi imene anthu anasonkhana ku phiri la Karimeli kudzaonerera zochitika za pakati pa aneneri a Baala ndi Eliya, panali patadutsa “zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi.”

Taganiziraninso nthawi yoyamba imene Eliya anapita kukaonana ndi Ahabu. Anthu anali kukhulupirira kuti Baala ndiye “woyendetsa mitambo,” mulungu amene anali kubweretsa mvula kuti nyengo ya chilimwe ithe. Nyengo ya chilimwe ikatalika kwambiri, mwina anthu ankafunsa kuti: ‘Kodi Baala ali kuti? Kodi adzabweretsa liti mvula?’ Koma zimene Eliya analengeza zoti sikudzagwa mvula ngakhale mame mpaka nthawi imene adzalengezanso kuti mvula igwe, ziyenera kuti zinakhumudwitsa kwambiri anthu olambira Baala.​—1 Mafumu 17:1.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w14 2/15 14-15

Mkazi Wamasiye wa ku Zarefati Anadalitsidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro

Ndiyeno poyankha, mayiyo anati: “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ndilibe mkate, koma ufa pang’ono mumtsuko waukulu ndi mafutanso pang’ono mumtsuko waung’ono. Panopa ndikutola tinkhuni kuti ndipite kukaphika chakudya choti ineyo ndi mwana wanga tidye. Tikadya, tiziyembekezera kufa.” (1 Maf. 17:12) Tsopano tiyeni tione zimene tikuphunzira pa nkhaniyi.

Mkazi wamasiyeyu ankadziwa kuti Eliya anali Mwisiraeli woopa Mulungu. Tikudziwa zimenezi chifukwa cha mawu ake akuti “pali Yehova Mulungu wanu wamoyo.” Zikuoneka kuti ankadziwa ndithu za Mulungu wa Aisiraeli koma anali asanafike pomuona kuti ndi Mulungu wake. Mayiyu ankakhala kutauni ya Zarefati yomwe inali pafupi ndi mzinda wa Sidoni m’chigawo cha Foinike ndipo zikuoneka kuti zinthu zambiri kutauniyi zinkachokera ku Sidoniko. N’zosakayikitsa kuti ku Zarefati kunkakhala anthu olambira Baala. Koma Yehova ayenera kuti anaona mayiyu kukhala wosiyana kwambiri ndi athu a m’deralo.

Ngakhale kuti mayi wamasiyeyu ankakhala ndi anthu olambira mafano, iye anasonyeza chikhulupiriro. Yehova anauza Eliya kuti apite kwa mayiyu n’cholinga choti onse awiriwo athandizike. Apansotu tikhoza kuphunzirapo mfundo ina yofunika.

Sikuti anthu onse a m’tauni ya Zarefati anali oipa. Potumiza Eliya kwa mkazi wamasiyeyu, Yehova anasonyeza kuti amathandiza anthu oona mtima amene sanayambe kumutumikira. Choncho m’pomveka kunena kuti “[Mulungu] amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Mac. 10:35.

Kodi ndi anthu angati m’dera lanu amene ali ngati mkazi wamasiye wa ku Zarefati? Ngakhale kuti amakhala ndi anthu otsatira zipembedzo zonyenga, mwina iwo amafunitsitsa kudziwa choonadi. N’kutheka kuti amangodziwa pang’ono za Yehova kapena samudziwa n’komwe, choncho afunika kuthandizidwa kuti ayambe kumulambira. Kodi inuyo mumafufuza ndiponso kuthandiza anthu oterewa?

“UKAYAMBE WANDIKONZERA MTANDA WAUNG’ONO WA MKATE”

Taganizirani zimene Eliya anapempha mayi wamasiyeyu. Mayiyu anali atangomuuza kumene kuti ufa wake unali wongophika kamodzi kokha chakudya cha iyeyo ndi mwana wake, kenako aziyembekezera kufa. Koma kodi Eliya anati chiyani? Iye anati: “Usachite mantha. Pita ukachite mogwirizana ndi mawu ako. Koma pa zimene uli nazozo, ukayambe wandikonzera mtanda waung’ono wa mkate, n’kubwera nawo kwa ine. Kenako, ukakonze chakudya chako ndi cha mwana wako. Pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ufa umene uli mumtsuko waukulu siutha, ndipo mafuta amene ali mumtsuko waung’ono saatha, kufikira tsiku limene Yehova adzagwetse mvula padziko lapansi.’”​—1 Maf. 17:11-14.

Mwina ena atauzidwa zimenezi, anganene kuti, ‘Sitingachite zimenezo chifukwa chakudya chimene tatsala nacho n’chokhachi.’ Koma mayi wamasiyeyu sananene zimenezo. Ngakhale kuti Yehova sankamudziwa bwinobwino, anakhulupirira Eliya ndipo anachita zimene anamupemphazo. Apatu chikhulupiriro chake chinayesedwa kwambiri, ndipo iye anachita zinthu mwanzeru.

Mulungu anathandizadi mayi wamasiyeyu. Zimene Eliya analonjeza zinachitikadi chifukwa Yehova anachulukitsa ufa ndi mafutawo moti Eliya, mayi wamasiyeyo ndi mwana wake anali ndi chakudya chokwanira mpaka chilalacho chitatha. Paja Baibulo limati: “Ufa umene unali mumtsuko waukulu sunathe, ndipo mafuta amene anali mumtsuko waung’ono sanathe, mogwirizana ndi mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Eliya.” (1 Maf. 17:16; 18:1) Ngati mayiyu akanakana zimene Eliya anamupemphazo, ufa ndi mafutawo akanangophikiradi kamodzi kokha. Koma mayiyu anali ndi chikhulupiriro komanso anadalira Yehova, choncho anakonzera Eliya chakudya.

Apa tikuphunzira kuti Mulungu amadalitsa munthu amene ali ndi chikhulupiriro. Mukasonyeza chikhulupiriro pamene muli pa mayesero, Yehova adzakuthandizani. Adzakupatsani zofuna zanu, adzakutetezani ndiponso adzakhala Mnzanu.​—Eks. 3:13-15.

Mu 1898, magazini ya Nsanja ya Olonda inanena za mayi wamasiyeyu kuti: “Popeza kuti mayiyu anasonyeza chikhulupiriro ndipo anamvera, Ambuye anamuthandiza kudzera mwa Mneneri. Koma akanapanda kusonyeza chikhulupiriro, pakanapezeka mayi wina wamasiye amene akanachita zimenezo. Ifenso nthawi zina Ambuye amalola kuti chikhulupiriro chathu chiyesedwe. Tikasonyeza chikhulupiriro amatidalitsa, koma tikapanda kutero timataya mwayiwu.”

Tikakumana ndi mayesero, tizifufuza malangizo a Mulungu kuchokera m’Malemba komanso mabuku athu. Tikapeza malangizowo, tizichita zimene Yehova akufuna ngakhale zitakhala zovuta kwambiri. Mulungu adzatidalitsa tikatsatira malangizo anzeru akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”​—Miy. 3:5, 6.

KODI ‘MWABWERA KUDZAPHA MWANA WANGA’?

Koma mayi wamasiyeyu anakumananso ndi mayesero ena. Baibulo limati: “Pambuyo pa zimenezi, mwana wamwamuna wa mayi wa m’nyumbamo, anadwala. Matenda ake anakula kwambiri mpaka anamwalira.” Mayiyo anadabwa nazo zimenezi ndipo polira anafunsa Eliya kuti: “Ndili nanu chiyani inu munthu wa Mulungu woona? Mwabwera kwa ine kudzandikumbutsa cholakwa changa ndi kudzapha mwana wanga.” (1 Maf. 17:17, 18) Kodi mayiyu ankatanthauza chiyani ponena zimenezi?

Kodi mwina anakumbukira zinthu zina zimene analakwitsa m’mbuyomo zomwe zinkavutitsa chikumbumtima chake? Kodi ankaganiza kuti imfa ya mwana wakeyo ndi chilango chochokera kwa Mulungu ndipo Eliyayo anatumidwa kudzapereka chilangocho? Baibulo silinena chilichonse pa nkhaniyi koma mfundo ndi yakuti: Mayi wamasiyeyu sanaimbe mlandu Mulungu pa vuto lakeli.

Eliya ayenera kuti anamva chisoni kwambiri kuona mwanayo atamwalira komanso kumva mayiyo akunena kuti iye anabwera kudzapha mwana wake. Ndiyeno Eliya anatenga mwana wakufayo n’kupita naye m’chipinda chapamwamba komwe anakafuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, kodi mukuchitiranso zoipa mkazi wamasiye amene ndikukhala naye monga mlendo wake, mwa kupha mwana wake?” Eliya ankadera nkhawa kuti dzina la Mulungu likhoza kunyozeka ngati Mulunguyo atalola kuti vuto la mayi wokoma mtimayu lipitirire. Choncho anachonderera Mulungu kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, chonde chititsani kuti moyo wa mwanayu ubwerere mwa iye.”​—1 Maf. 17:20, 21.

“TAONA, MWANA WAKO ALI MOYO”

Yehova anayankha pempheroli. Anatero chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu anapereka chakudya kwa mneneri wa Mulungu ndipo anasonyeza chikhulupiriro. Zikuoneka kuti Mulungu analola kuti mwanayu amwalire podziwa kuti adzamuukitsa ndipo ngati atatero zidzapereka chiyembekezo kwa anthu ena m’tsogolo. Ndipotu m’Baibulo, imeneyi ndi nkhani yoyamba yofotokoza za kuuka kwa akufa. Choncho Eliya atachonderera kwambiri, Yehova anaukitsa mwanayo. Kodi mukuganiza kuti mayiyo anamva bwanji pamene Eliya anamuuza kuti “Taona, mwana wako ali moyo”? Zitatero, mayiyu anauza Eliya kuti: “Tsopano ndadziwadi kuti ndinu munthu wa Mulungu ndipo mawu a Yehova amene ali m’kamwa mwanu ndi oona.”​—1 Maf. 17:22-24.

Nkhani ya mkazi wamasiyeyu imathera pomwepa. Koma popeza Yesu anamutchulanso, ayenera kuti ankatumikira Yehova mokhulupirika pa zaka zomaliza za moyo wake. (Luka 4:25, 26) Nkhani imeneyi ikusonyeza kuti Yehova amadalitsa anthu amene amachitira atumiki ake zabwino. (Mat. 25:34-40) Ikusonyezanso kuti Yehova amapereka zinthu zofunika kwa atumiki ake ngakhale pamene zinthu zafika poipa kwambiri. (Mat. 6:25-34) Imatithandizanso kudziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu zoukitsa akufa ndipo amafunitsitsa kuchita zimenezi. (Mac. 24:15) Izitu ndi zifukwa zomveka zotichititsa kukumbukira mkazi wamasiye wa ku Zarefati.

OCTOBER 10-16

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 19-20

“Tizidalira Yehova Kuti Atilimbikitse”

w19.06 15 ¶5

Tizidalira Yehova Tikakhala ndi Nkhawa

5 Werengani 1 Mafumu 19:1-4. Yezebeli ananena kuti adzapha Eliya ndipo Eliyayo anachita mantha kwambiri moti anathawira ku Beere-seba. Iye anakhumudwa kwambiri mpaka kufika ‘popempha kuti afe.’ N’chifukwa chiyani anamva chonchi? Eliya sanali wangwiro ndipo ‘anali munthu ngati ife tomwe.’ (Yak. 5:17) N’kutheka kuti anafooka chifukwa cha nkhawa komanso kutopa kwambiri. Iye ankaganiza kuti zimene ankachita polimbikitsa kulambira koona sizinaphule kanthu. Ankaonanso kuti palibe chilichonse chimene chasintha mu Isiraeli ndipo mtumiki wa Yehova amene watsala ndi iye yekha. (1 Maf. 18:3, 4, 13; 19:10, 14) Mwina tikhoza kudabwa tikaganizira mmene mneneriyu anamvera. Koma Yehova anamumvetsa.

ia 103 ¶13

Analimbikitsidwa Ndi Mulungu Wake

13 Kodi mukuganiza kuti Yehova anamva bwanji pamene anayang’ana ali kumwambako n’kuona mneneri wake wokondedwa atagona m’chipululu pansi pa kamtengo akupempha kuti angofa? Kuti tidziwe mmene Yehova anamvera, tiyeni tione zimene zinachitika. Eliya ali mtulo, Yehova anatumiza mngelo. Mngeloyo anamugwedeza Eliya pang’onopang’ono ndipo anamuuza kuti: “Dzuka udye.” Eliya anadzukadi ndipo anadya mkate wotentha ndiponso anamwa madzi amene mngeloyo anamubweretsera. Sitikudziwa ngati Eliya anathokoza mngeloyo chifukwa nkhaniyi imangofotokoza kuti mneneriyu anadya ndi kumwa kenako n’kugonanso. N’kutheka kuti Eliya sanathokoze chifukwa chakuti anali atakhumudwa kwambiri moti sankafuna kulankhula. Komabe patapita nthawi mngeloyo anadzutsanso Eliya ndipo mwina tsopano unali m’bandakucha. Apanso mngeloyo anauza Eliya kuti: “Dzuka udye,” ndipo anawonjezeranso kuti: “Popeza ulendowu wakukulira.”​—1 Maf. 19:5-7.

ia 106 ¶21

Analimbikitsidwa Ndi Mulungu Wake

21 Nkhaniyi imafotokoza kuti Yehova sanali mu zinthu zachilengedwe monga mphepo, chivomezi ndiponso moto zimene Eliya anaonazi. Eliya ankadziwa kuti Yehova si mulungu wongoganiziridwa kuti alipo ngati mmene zinalili ndi Baala amene anthu omwe ankamulambira ankamutamanda kuti ndi woyendetsa mitambo, kapena kuti wobweretsa mvula. Mphamvu zochititsa mantha zimene zili m’zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe, zinachokera kwa Yehova. Koma iye ndi wamkulu kwambiri kuposa chilichonse chimene analenga. Ndipo ngakhale kumwamba kumene timaonaku, Yehova sangakwaneko. (1 Maf. 8:27) Ndiyeno kodi zimene Eliya anaonazi zinamuthandiza bwanji? Kumbukirani kuti Eliya anapezeka pamalo amenewa chifukwa chochita mantha. Popeza kuti Yehova Mulungu, yemwe ali ndi mphamvu zimenezi, anali kumbali ya Eliya, panalibe chifukwa chakuti iye aziopa Ahabu ndi Yezebeli.​—Werengani Salimo 118:6.

ia 106 ¶22

Analimbikitsidwa Ndi Mulungu Wake

22 Moto uja utapita, pamalopo panakhala bata ndipo Eliya anamva “mawu achifatse apansipansi.” Mawuwo anali omupempha kuti anenenso zakukhosi kwake ndipo zimenezi zinachititsa kuti kachiwirinso Eliya afotokoze zinthu zomwe zinkamudetsa nkhawa. Zimenezi ziyenera kuti zinamulimbikitsanso kwambiri. Komanso mosakayikira, Eliya analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene “mawu achifatse apansipansi” aja anamuuza. Yehova anatsimikizira Eliya kuti ndi munthu wofunika. Kodi anachita bwanji zimenezi? Mulungu anamuuza kuti nkhondo yothetsa kulambira Baala mu Isiraeli ipitirizabe. Ndiyetu apa n’zoonekeratu kuti ntchito imene Eliya anagwira sinapite m’madzi chifukwa Mulungu anali akuyendetsabe zinthu kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. Komanso, Yehova anali akugwiritsabe ntchito Eliya popeza anamupatsa malangizo omveka bwino n’kumuuza kuti abwerere akagwire ntchito yomweyi.​—1 Maf. 19:12-17.

Mfundo Zothandiza

w97 11/1 31 ¶1

Chitsanzo cha Kudzimana ndi Kukhulupirika

Atumiki ambiri a Mulungu masiku ano amasonyezanso mzimu wodzimana. Ena asiya “minda” yawo kapena ntchito zawo, kuti akalalikire uthenga wabwino kumadera akutali kapena kukatumikira pa Beteli. Ena apita ku mayiko akutali kukathandiza pa ntchito zomangamanga. Ambiri akugwira ntchito zimene zingaoneke ngati zotsika. Komabe, palibe mtumiki wa Yehova amene akuchita utumiki wosafunika. Yehova amayamikira onse amene amam’tumikira ndi mtima wonse, ndipo adzawadalitsa chifukwa cha mzimu wawo wodzipereka.​—Maliko 10:29, 30.

OCTOBER 17-23

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 21-22

“Muzitsanzira Mmene Yehova Amagwiritsira Ntchito Udindo Wake”

it-2 21

Yehova wa Makamu

Yoswa ataona mngelo pafupi ndi Yeriko anam’funsa ngati anali mlendo wa Aisiraeli kapena wa adani awo ndipo anayankha kuti, “Iyayi, koma ine pokhala kalonga wa gulu lankhondo la Yehova, tsopano ndabwera.” (Yos 5:13-15) Mneneri Mikaya anauza Mfumu Ahabu ndi Mfumu Yehosafati kuti, “ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu, makamu onse akumwamba ataimirira kudzanja lake lamanja ndi kumanzere kwake,” apa n’zoonekeratu kuti ankatanthauza ana auzimu a Yehova. (1Mf 22:19-21) M’poyenera kunena kuti “Yehova wa makamu” chifukwa pa magulu ankhondo a angelo pamafotokozedwa kuti pali akerubi, aserafi ndi angelo enanso. (Yes 6:2, 3; Ge 3:24; Chv 5:11) Kuwonjezera pamenepa, angelo ali m’magulumagulu enanso moti Yesu ananena kuti akanatha kuitana “magulu ankhondo oposa 12 a angelo” kuti amutumikire. (Mt 26:53) Pamene Hezekiya ankapempha Yehova kuti amuthandize, anamutchula kuti, “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wokhala pa akerubi,” ndipo n’kutheka ankatanthauza likasa la pangano lomwe linali ndi zifaniziro za akerubi pamwamba pake, kuimira mpando wachifumu wa Yehova. (Yes 37:16; yerekezerani ndi 1Sa 4:4; 2Sa 6:2.) Mtumiki wa Elisa amene ankachita mantha, anaona masomphenya amene anamulimbitsa mtima, ndipo m’masomphenyawo anaona dera lonse lamapiri kuzungulira mzinda umene Elisa ankakhala utadzaza “ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo oyaka moto,” omwe ndi mbali ya gulu la angelo a Yehova.​—2Mf 6:15-17.

w21.02 4 ¶9

“Mutu wa Mwamuna Aliyense Ndi Khristu”

9 Kudzichepetsa. Yehova ndi wanzeru kuposa wina aliyense. Komabe, iye amamvetsera maganizo a atumiki ake. (Gen. 18:23, 24, 32) Iye amalola amene akuwatsogolera kufotokoza maganizo awo. (1 Maf. 22:19-22) Yehova ndi wangwiro, koma samayembekezera kuti anthufe tizichita zinthu popanda kulakwitsa kalikonse. M’malomwake, iye amathandiza atumiki ake omwe si angwiro kuti zinthu ziziwayendera bwino. (Sal. 113:6, 7) Ndipotu Baibulo limafotokoza kuti Yehova ndi “m’nthandizi” wathu. (Sal. 27:9; Aheb. 13:6) Mfumu Davide ananena kuti anakwanitsa kugwira ntchito yaikulu imene anapatsidwa chifukwa chakuti Yehova ndi wodzichepetsa ndipo anamuthandiza.​—2 Sam. 22:36.

it-2 245

Bodza

Yehova Mulungu amalola kuti anthu amene amakonda bodza “anyengedwe ndipo azikhulupirira bodza” m’malo mokhulupirira uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu. (2At 2:9-12) Mfundo imeneyi inaonekera bwino pa zimene zinachitikira Mfumu Ahabu ya Isiraeli. Aneneri abodza anatsimikizira Ahabu kuti akapambana nkhondo ku Ramoti-giliyadi, pomwe mneneri Mikaya analosera za tsoka. M’masomphenya amene Mikaya anaona, Yehova analola cholengedwa chauzimu kuti chikhale “mzimu wabodza” m’kamwa mwa aneneri a Ahabu. Zimenezi zikutanthauza kuti cholengedwa chauzimucho chinagwiritsa ntchito mphamvu zake pa aneneriwo moti analankhula zabodza zomwe ankafuna komanso zomwe Ahabu ankafuna kumva. Ngakhale kuti anali atachenjezedwa kale, Ahabu anasankha kuti apusitsidwe ndi mabodza a aneneriwo ndipo anafa.​—1Mf 22:1-38; 2Mb 18.

Mfundo Zothandiza

w21.10 3 ¶4-6

Kodi Kulapa Kwenikweni N’kutani?

4 Pamapeto pake, nthawi yoti Yehova apitirize kumulezera mtima inatha. Iye anatumiza Eliya kuti akauze Ahabu ndi Yezebeli chilango chimene adzawapatse. Anthu onse a m’banja lawo anali oti adzaphedwa. Mawu amene Eliya analankhulawa anachititsa Ahabu kudzimvera chisoni kwambiri. N’zodabwitsa kuti munthu wodzikuzayu panthawiyi ‘anadzichepetsa.’​—1 Maf. 21:19-29.

5 Ngakhale kuti Ahabu anadzichepetsa panthawiyi, zimene ankachita pambuyo pake zinasonyeza kuti sanalape kuchokera pansi pamtima. Iye sanathetse kulambira Baala mu ufumu wake komanso sanalimbikitse anthu kuti azilambira Yehova. Ahabu anachitanso zinthu zina zosonyeza kuti sanali ndi mtima wolapa.

6 Pa nthawi ina, Ahabu anaitana Mfumu Yehosafati ya ku Yuda kuti akamuthandize pankhondo yolimbana ndi Asiriya. Yehosafati ananena kuti choyamba afunsire kwa mneneri wa Yehova. Poyamba Ahabu anakana ndipo anati: “Pali munthu mmodzi amene tingathe kufunsira kwa Yehova kudzera mwa iye, koma ineyo ndimadana naye kwambiri, chifukwa salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa.” Ngakhale zinali choncho, iwo anafunsirabe kwa mneneri Mikaya. Mogwirizana ndi mmene Ahabu ananenera, munthu wa Mulunguyo analoseradi zoipa zokhudza iye. M’malo molapa n’kupempha Yehova kuti amukhululukire, mfumu yoipa Ahabu anachititsa kuti mneneriyu atsekeredwe m’ndende. (1 Maf. 22:7-9, 23, 27) Ngakhale kuti mfumuyo inakwanitsa kutsekera m’ndende mneneri wa Yehova, siinalepheretse kuti ulosi umene ananenawo ukwaniritsidwe. Ahabu anaphedwa pankhondo imene anakamenyayo.​—1 Maf. 22:34-38.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w15 3/15 9-11 10-12

“Munavomereza Kuti Zimenezi Zichitike”

10 Koma Yehova wakhala akuthandiza “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azichita zinthu mwanzeru kwambiri. Choncho gulu layamba kusamala kwambiri kuti lisamafulumire kunena kuti zinthu zinazake zikuphiphiritsira zinthu zina. Limachita zimenezi pokhapokha ngati pali umboni wa m’Malemba. Zikuonekanso kuti anthu ambiri zimawavuta kumvetsa nkhani za m’Baibulo zimene zinafotokozedwa m’njira yosonyeza kuti zikuphiphiritsira zinazake. Kafotokozedwe kameneka kamakhala kovuta kumvetsa, kukumbukira komanso kutsatira mfundo zake pa moyo wathu. Koma vuto lalikulu ndi lakuti phunziro lenileni la nkhaniyo limasokonekera chifukwa choti tikuyesa kufufuza kuti zinthuzo zikuimira chiyani. Choncho masiku ano, gulu lasintha ndipo limafotokoza zinthu m’njira yosavuta. Limatsindika zimene tikuphunzira pa nkhani ya chikhulupiriro, kupirira, kudzipereka kwa Mulungu komanso makhalidwe ena abwino.

11 Ndiyeno kodi tingafotokoze bwanji nkhani ya Naboti? Masiku ano mabuku athu amafotokoza nkhaniyi m’njira yosavuta. Amati Naboti anafa chifukwa choti anali wokhulupirika kwa Mulungu ndipo nkhani yake siimira zimene zinachitikira Yesu kapena odzozedwa. Naboti sanasiye kumvera lamulo la Yehova ngakhale pamene ankazunzidwa ndi olamulira. (Num. 36:7; 1 Maf. 21:3) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yake? Ifenso tiyenera kumvera Yehova ngakhale pamene tikuzunzidwa. (Werengani 2 Timoteyo 3:12.) Aliyense angamvetse mosavuta, kukumbukira komanso kutsatira zimene tikuphunzira pa nkhaniyi.

12 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti nkhani zonse za m’Baibulo zimangopereka phunziro popanda kuimira zinazake? Ayi. N’zoona kuti masiku ano mabuku athu sakonda kunena kuti nkhani inayake ikuphiphiritsira zakutizakuti. Koma m’malomwake, amanena kuti nkhaniyo ikutikumbutsa zakutizakuti kapena ikufanana ndi zakutizakuti. Mwachitsanzo, tikhoza kunena kuti kukhulupirika kwa Naboti pozunzidwa kumatikumbutsa za kukhulupirika kwa Yesu ndi odzozedwa. Koma ikhoza kutikumbutsanso za kukhulupirika kwa anthu ambiri a “nkhosa zina.” Yehova amakonda kwambiri kuphunzitsa m’njira yosavuta chonchi.

OCTOBER 24-30

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 1-2

“Chitsanzo Chabwino cha Kuphunzitsa Ena”

w15 4/15 13 ¶15

Zimene Mungachite Pophunzitsa Ena Kuti Akhale Akulu

15 Nkhani ya Elisa ikusonyezanso zimene abale angachite posonyeza kuti amalemekeza akulu amene atumikira nthawi yaitali. Tsiku lina, Eliya ndi Elisa anakumana ndi ana a aneneri ku Yeriko ndipo kenako anapita kumtsinje wa Yorodano. Atafika, “Eliya anatenga chovala chake chauneneri n’kuchipinda. Atatero anamenya nacho madzi a mtsinjewo, ndipo pang’onopang’ono madzi onsewo anagawanika.” Iwo anawoloka pouma ndipo ankayenda, uku akulankhulana. Pa nthawiyi Elisa sankadzitenga kuti akudziwa zonse. Elisa ankasunga mumtima mawu onse amene Eliya ankamuuza. Ankachita zimenezi mpaka nthawi imene Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho. Ndiyeno pobwerera Elisa anafikanso pamtsinje paja. Iye anatenga chovala cha Eliya chija n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” Atatero madziwo anagawanikanso.​—2 Maf. 2:1-14.

w15 4/15 13 ¶16

Zimene Mungachite Pophunzitsa Ena Kuti Akhale Akulu

16 Taonani kuti chozizwitsa choyamba chimene Elisa anachita chinali chofanana ndendende ndi chimene Eliya anachita. Kodi tikuphunzirapo chiyani? N’kutheka kuti Elisa sankaganiza kuti ali ndi mphamvu zonse moti akhoza kuchita zosiyana ndi zimene Eliya ankachita. Iye ankatsatira zimene Eliya ankachita potumikira Yehova ndipo izi zinachititsa aneneri a ku Yeriko kutsimikizira kuti mzimu wa Eliya uli pa Elisa. (2 Maf. 2:15) Elisa anagwira ntchito yauneneri kwa zaka 60 ndipo Yehova anamuthandiza kuchita zozizwitsa zambiri kuposa zimene Eliya anachita. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa?

Mfundo Zothandiza

w05 8/1 9 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Wachiwiri

2:11​—Kodi “kumwamba” kumene ‘Eliya anakwera ndi kavulumvulu’ ndi kumwamba kuti? Kumeneku si kumalo kwinakwake m’miyambamu kotalikirana kwambiri ndi dziko lapansi, ndiponso si kumalo auzimu amene Mulungu ndi ana ake aungelo amakhala. (Deuteronomo 4:19; Salmo 11:4; Mateyu 6:9; 18:10) “Kumwamba” kumene Eliya anapita ndi mumlengalenga, osati kumwamba kwenikweni. (Salmo 78:26; Mateyu 6:26) Galeta la moto limene linatenga Eliya linayenda mumlengalenga n’kumupititsa ku mbali ina ya dziko lapansi, kumene anakakhala kwa kanthawi. Ndipotu patatha zaka zingapo, Eliya analemba kalata yopita kwa Yehoramu, mfumu ya Yuda.​—2 Mbiri 21:1, 12-15.

OCTOBER 31–NOVEMBER 6

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 3-4

“Nyamulani Mwana Wanu”

w17.12 4 ¶7

“Ndikudziwa Kuti Adzauka”

7 Nkhani yachiwiri inachitika nthawi ya Elisa, yemwe analowa m’malo mwa Eliya. Mkazi wina wachiisiraeli, yemwe anali wodziwika ku Sunemu, analandira bwino Elisa m’nyumba yake. Yehova anadalitsa mkaziyo ndi mwamuna wake wachikulire moti anakhala ndi mwana wamwamuna. Koma patapita zaka zingapo, mwanayo anamwalira. Kodi inuyo mukuganiza kuti mayi ake anamva bwanji? Iye atakambirana ndi mwamuna wake, ananyamuka ulendo wa makilomita 30 kupita kukaonana ndi Elisa kuphiri la Karimeli. Mneneriyo anatuma Gehazi kuti atsogole popita ku Sunemu n’cholinga choti akaukitse mwanayo koma sanathe kumuukitsa. Kenako mayi a mwanayo anafika limodzi ndi Elisa kunyumbako.​—2 Maf. 4:8-31.

w17.12 4 ¶8

“Ndikudziwa Kuti Adzauka”

8 Elisa anafika pafupi ndi thupi la mwanayo n’kupemphera. Mnyamatayo anauka ndipo anamupereka kwa mayi ake omwe anasangalala kwambiri. (Werengani 2 Mafumu 4:32-37.) Mayiyu ayenera kuti anakumbukira mawu amene Hana ananena m’pemphero lake popereka Samueli kuti azitumikira kuchihema. Paja ananena kuti: “Yehova ndi . . . Wotsitsira Kumanda, ndiponso Woukitsa.” (1 Sam. 2:6) Ku Sunemu, Mulungu anasonyezadi kuti ali ndi mphamvu youkitsa munthu wakufa.

Mfundo Zothandiza

it-2 697 ¶2

Mneneri

“Ana a Aneneri.” Buku lina lotchedwa Gesenius’ Hebrew Grammar (Oxford, 1952, tsa. 418), limafotokoza kuti mawu a Chiheberi akuti ben (mwana wa) kapena akuti benehʹ (ana a) angatanthauze “membala wa gulu linalake (kapena mtundu winawake).” (Yerekezerani ndi Ne 3:8, pomwe “mmodzi wa opanga mafuta onunkhira” angatanthauze “mwana wa opanga mafuta onunkhira.”) Choncho mawu akuti “ana a aneneri” akhoza kutanthauza sukulu yophunzitsa anthu amene anasankhidwa kukhala aneneri kapena gulu la aneneri. Magulu a aneneri amenewa amatchulidwa kuti anali ku Beteli, ku Yeriko ndi ku Giligala. (2Mf 2:3, 5; 4:38; yerekezerani ndi 1Sa 10:5, 10.) Samueli ankatsogolera gulu la aneneri ku Rama (1Sa 19:19, 20), pomwe Elisa analinso ndi udindo ngati womwewu m’nthawi yake. (2Mf 4:38; 6:1-3; yerekezerani ndi 1Mf 18:13) Baibulo limafotokoza kuti ankakhala m’nyumba yawoyawo, komanso ankabwereka zipangizo zogwiritsa ntchito, zimene zimasonyeza kuti ankakhala moyo wosalira zambiri. Ngakhale kuti nthawi zambiri ankakhala m’nyumba imodzi komanso ankagawana chakudya, n’kutheka kuti aliyense ankapatsidwa utumiki wakewake.​—1Mf 20:35-42; 2Mf 4:1, 2, 39; 6:1-7; 9:1, 2.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w13 8/15 28-29

Elisa Anaona Magaleta Oyaka Moto​—Kodi Inunso Mukuwaona?

Pa nthawi ina, mfumu ya Siriya inkasakasaka mneneri Elisa ndipo inamva zoti ali kumzinda wa Dotana. Mzindawu unali paphiri ndipo unali ndi mpanda. Ndiyeno usiku, mfumuyi inatumiza mahatchi, magaleta ankhondo ndiponso asilikali kumzindawu. Pofika m’mawa, asilikaliwo anali atazungulira mzinda wonsewo.​—2 Maf. 6:13, 14.

Mtumiki wa Elisa atadzuka, anaona gulu la asilikaliwo. Iye anadandaulira Elisa kuti: “Kalanga ine mbuyanga! Titani?” Koma Elisa anati: “Usaope, popeza ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.” Kenako mneneriyu anayamba kupemphera kuti: “Inu Yehova, m’tseguleni maso chonde kuti aone.” Ndiyeno nkhaniyi imapitiriza kuti: “Nthawi yomweyo Yehova anatsegula maso a mtumiki uja, moti anaona kuti dera lonse lamapiri kuzungulira Elisa linadzaza ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo oyaka moto.” (2 Maf. 6:15-17) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi komanso pa zinthu zina zimene zinachitika pa moyo wa Elisa?

Elisa atazunguliridwa ndi asilikali a ku Siriya, sanachite mantha chifukwa ankakhulupirira Yehova ndipo ankadziwa kuti amuteteza. Ifeyo sitiyembekezera kuti Yehova atiteteza mozizwitsa koma timadziwa kuti iye amateteza gulu la atumiki ake. Zili ngati tazunguliridwa ndi mahatchi komanso magaleta oyaka moto. Kukhulupirira zimenezi kungatithandize kuti tizidalira Mulungu ndipo ‘tidzakhala otetezeka’ komanso Yehova adzatidalitsa. (Sal. 4:8) Tiyeni tsopano tikambirane zimene tikuphunzira pa zinthu zina zomwe zinachitika pa moyo wa Elisa.

ELISA ANAYAMBA KUTUMIKIRA ELIYA

Nthawi ina Elisa akulima, kunafika mneneri Eliya ndipo anam’ponyera chovala chake chauneneri. Elisa anadziwa tanthauzo la zimenezi. Choncho anakonza phwando potsanzikana ndi makolo ake ndipo kenako anapita kukatumikira Eliya. (1 Maf. 19:16, 19-21) Elisa anadzipereka kuchita zonse zimene akanatha potumikira Mulungu. Choncho Yehova anamugwiritsa ntchito kwambiri ndipo anadzakhala mneneri m’malo mwa Eliya.

Elisa anatumikira Eliya kwa zaka pafupifupi 6. Iye ndi “amene anali kuthirira Eliya madzi osamba m’manja.” (2 Maf. 3:11) Pa nthawiyo, anthu akamaliza kudya, wantchito ndi amene ankathirira madzi mbuye wake posamba m’manja. Choncho nthawi zina Elisa ankagwira ntchito zooneka zonyozeka. Komabe ankaona kuti kutumikira Eliya unali mwayi waukulu.

Mofanana ndi Elisa, Akhristu ambiri masiku ano akuchita utumiki wa nthawi zonse. Iwo akuchita zimenezi chifukwa chokhulupirira Yehova ndiponso pofuna kuchita zonse zimene angathe pomutumikira. Ena amachoka kwawo n’kumakatumikira ku Beteli, kukagwira ntchito zomangamanga kapena kuchita utumiki wina. Anthu ena amaona kuti ntchito zina zimene atumiki amenewa amagwira ndi zonyozeka. Koma Akhristu sayenera kuziona choncho. Tikutero chifukwa Yehova amaona kuti ntchitozi ndi zofunika kwambiri.​—Aheb. 6:10.

ELISA SANASIYE UTUMIKI WAKE

Mulungu ‘asanatenge Eliya mumphepo yamkuntho kupita naye kumwamba,’ anamuuza kuti achoke ku Giligala kupita ku Beteli. Asananyamuke, Eliya anauza Elisa kuti asapite naye, koma Elisa anati: “Sindikusiyani.” Ali pa ulendowu, Eliya anamuuzanso Elisa kawiri kuti asapite naye koma Elisa sanalole. (2 Maf. 2:1-6) Mofanana ndi Rute amene anakana kusiya Naomi, Elisa anakakamira Eliya. (Rute 1:8, 16, 17) Iye sanamusiye chifukwa ankayamikira kwambiri ntchito imene Mulungu anamupatsa yotumikira Eliya.

Elisa ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Tikapatsidwa utumiki wina m’gulu la Mulungu, tizikumbukira kuti tikutumikira Yehova. Kuchita zimenezi kungatithandize kuona kuti utumikiwo ndi wofunika kwambiri ndiponso ndi mwayi waukulu.​—Sal. 65:4; 84:10.

“PEMPHA CHIMENE UKUFUNA KUTI NDIKUCHITIRE”

Ndiyeno akuyenda, Eliya anauza Elisa kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikuchitire ndisanakuchokere.” Mofanana ndi Solomo, Elisa anapempha zinthu zomuthandiza kutumikira Mulungu. Iye anapempha kuti alandire “magawo awiri a mzimu” wa Eliya. (1 Maf. 3:5, 9; 2 Maf. 2:9) Ku Isiraeli, mwana woyamba kubadwa ndi amene ankalandira magawo awiri a zinthu za bambo ake monga cholowa. (Deut. 21:15-17) Choncho tingati Elisa anapempha kuti adzalowe m’malo mwa Eliya pa ntchito yauneneri. Koma ankafunanso kuti adzakhale wolimba mtima ngati Eliya amene ankafunitsitsa kuti anthu azilambira Yehova yekha.​—1 Maf. 19:13, 14.

Kodi Eliya anayankha bwanji pempho la mtumiki wakeyu? Iye anati: “Wapempha chinthu chovuta. Ukandiona ndikutengedwa, zimene wapemphazi zikuchitikiradi, koma ukapanda kundiona, sizichitika.” (2 Maf. 2:10) Zikuoneka kuti yankho la Eliya linali ndi mfundo ziwiri. Choyamba, likusonyeza kuti Mulungu yekha ndi amene akanasankha zoti Elisa alandire zimene wapemphazo kapena ayi. Chachiwiri, likusonyeza kuti Elisa akanalandira zinthuzo ngati akanakhalabe ndi Eliya zivute zitani.

ZIMENE ELISA ANAONA

Kodi Mulungu anayankha bwanji pempho la Elisa loti apatsidwe magawo awiri a mzimu wa Eliya? Nkhaniyi imati: “Pamene anali kuyenda n’kumalankhulana, anangoona galeta lankhondo lowala ngati moto ndi mahatchi owala ngati moto. Galeta ndi mahatchiwo zinadutsa pakati pawo n’kuwalekanitsa, ndipo Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho n’kukwera kumwamba. Nthawi yonseyi Elisa anali kuona zimene zinali kuchitikazo.” Iye anaona Eliya akutengedwa, analandira magawo awiri a mzimu wake komanso analowa m’malo mwake monga mneneri. Umu ndi mmene Yehova anayankhira pempho la Elisa.​—2 Maf. 2:11-14.

Elisa anatenga chovala chauneneri chimene Eliya anagwetsa n’kuchivala. Chovala chimenecho chinkasonyeza kuti tsopano Elisa ndi mneneri wa Mulungu. Umboni wina wosonyeza kuti Elisa anaikidwa kukhala mneneri unaoneka pamene anagawa madzi a mtsinje wa Yorodano mozizwitsa.

Mosakayikira Elisa analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene anaona pamene Eliya ankakwera kumwamba. Ndipo zimenezi n’zomveka chifukwa palibe amene anaonapo galeta lankhondo loyaka moto ndi mahatchi owala ngati moto. Zinthu zimenezi zinangopereka umboni woti Yehova wayankha pempho lake. Mulungu akamayankha mapemphero athu, sikuti timaona masomphenya a galeta lankhondo loyaka moto kapena mahatchi owala ngati moto. Koma timadziwa kuti Mulungu akugwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu poonetsetsa kuti chifuniro chake chichitike. Ndipotu tikamaona kuti Yehova akudalitsa mbali ya padziko lapansi ya gulu lake, zimakhala ngati tikuona galeta lake lakumwamba likuyenda.​—Ezek. 10:9-13.

Elisa anaona zinthu zambiri zimene zinam’thandiza kukhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zambiri. Ndipo mzimu wa Mulungu unathandiza mneneriyu kuchita zozizwitsa zokwana 16, pomwe Eliya anangochita 8 zokha. Nthawi yachiwiri imene Elisa anaona mahatchi ndiponso magaleta ankhondo oyaka moto ndi pamene asilikali a ku Siriya anazungulira mzinda wa Dotana.

ELISA ANKAKHULUPIRIRA YEHOVA

Elisa sanachite mantha pamene anazunguliridwa ndi adani ku Dotana. Iye sanaope chifukwa chakuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Ifenso tiyenera kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse. Choncho tizipempha mzimu woyera wa Mulungu kuti tikhale ndi chikhulupiriro ndiponso makhalidwe ena amene mzimuwu umatulutsa.​—Luka 11:13; Agal. 5:22, 23.

Zimene zinachitika ku Dotana zinathandiza Elisa kuti azidalira Yehova ndiponso magulu ake ankhondo akumwamba. Mneneriyu anazindikira kuti Yehova anatumiza angelo ambirimbiri kuti akazungulire mzindawu ndiponso adani ake. Mulungu anachititsa khungu adaniwo ndipo anapulumutsa Elisa ndi mtumiki wake. (2 Maf. 6:17-23) Mofanana ndi mmene ankachitira nthawi zonse, apanso Elisa anakhulupirira Yehova ndiponso kumudalira ndi mtima wonse.

Nafenso tizikhulupirira kwambiri Yehova Mulungu. (Miy. 3:5, 6) Tikatero, “Mulungu adzatiyanja ndi kutidalitsa.” (Sal. 67:1) N’zoona kuti sitinazunguliridwe ndi magaleta oyaka moto ndi mahatchi. Koma pa “chisautso chachikulu” Yehova adzateteza gulu lake la padziko lonse. (Mat. 24:21; Chiv. 7:9, 14) Mpaka nthawi imeneyo, tiyeni tizikumbukira kuti “Mulungu ndiye pothawirapo pathu.”​—Sal. 62:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena