Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesu Anayeretsanso Kachisi
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Yesu akugubuduza matebulo a osintha ndalama

      MUTU 103

      Yesu Anayeretsanso Kachisi

      MATEYU 21:12, 13, 18, 19 MALIKO 11:12-18 LUKA 19:45-48 YOHANE 12:20-27

      • YESU ANATEMBERERA MTENGO WA MKUYU KOMANSO ANAYERETSA KACHISI

      • YESU ANAYENERA KUFA KUTI ANTHU AMBIRI ADZAPEZE MOYO WOSATHA

      Yesu ndi ophunzira ake anakhala ku Betaniya kwa masiku atatu atachoka ku Yeriko. Kenako Lolemba m’mamawa pa Nisani 10, anayamba ulendo wopita ku Yerusalemu. Ali m’njira, Yesu anamva njala ndipo ataona mtengo wamkuyu anapita kuti akathyole nkhuyu. Kodi anazipezadi nkhuyuzo?

      Zimenezi zinachitika chakumapeto kwa mwezi wa March koma nkhuyu zinkayamba kupsa mwezi wa June. Koma poti mtengowo unali utatulutsa kale masamba, Yesu ankaganiza kuti akhoza kupezamo nkhuyu zoyambirira. Atafika pafupi anapeza kuti munalibe chilichonse. Chifukwa cha masambawo, anthu ankaona ngati mumtengowo muli zipatso. Kenako Yesu ananena kuti: “Munthu sadzadyanso zipatso zako kwamuyaya.” (Maliko 11:14) Nthawi yomweyo mtengowo unayamba kufota ndipo ophunzirawo anamvetsa tanthauzo la zimenezi tsiku lotsatira.

      Pasanapite nthawi yaitali, Yesu ndi ophunzira ake anafika ku Yerusalemu. Atafika anapita kukachisi kumene anali atayendera zinthu za m’kachisi chadzulo lake masana. Koma pa nthawiyi Yesu sanangoyendera kachisi. Iye anachitanso zimene anachita zaka zitatu m’mbuyomo pa nthawi ya Pasika wa mu 30 C.E. (Yohane 2:14-16) Yesu anathamangitsa “ogula ndi ogulitsa m’kachisimo.” Anagubuduzanso “matebulo a osintha ndalama ndiponso mabenchi a ogulitsa nkhunda.” (Maliko 11:15) Iye sanalolenso kuti munthu aliyense amene wanyamula katundu azidutsa m’bwalo la kachisiyo ngati njira yachidule popita mbali ina ya mzindawo.

      N’chifukwa chiyani Yesu anathamangitsa osintha ndalama komanso ogulitsa ziweto m’kachisi? Iye ananena kuti: “Kodi Malemba sanena kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo mitundu yonse’? Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.” (Maliko 11:17) Yesu ananena kuti anthu amenewa anali achifwamba chifukwa chakuti ankagulitsa ziweto, zomwe anthu ankagula kuti apereke nsembe, pamtengo wokwera kwambiri. Choncho Yesu ankaona kuti zimene anthuwa ankachita kunali kuba.

      Ansembe aakulu, alembi komanso anthu ena audindo atamva zimene Yesu anachita anayambanso kukonza zoti amuphe. Koma panali vuto limodzi. Sankapeza njira yabwino yoti amuphere chifukwa anthu ambiri ankapita kwa Yesu kuti akamve zimene ankaphunzitsa.

      Ayuda komanso anthu otembenukira kuchiyuda anabwera ku mwambo wa Pasika. Ena amene anabwera ku mwambowu anali Agiriki. Agirikiwa ankafuna kukumana ndi Yesu ndipo anapempha Filipo ngati zimenezi zingatheke. Iwo anachita zimenezi mwina chifukwa chakuti dzina lakuti Filipo ndi dzina lachigiriki. N’kutheka kuti Filipo ankakayikira ngati zinali zoyenera kuti anthuwo akumane ndi Yesu choncho anakambirana ndi Andireya. Filipo ndi Andireya anapita kukafunsa Yesu za nkhaniyi ndipo pa nthawiyi Yesu anali adakali m’kachisi.

      Yesu ankadziwa kuti kwatsala masiku ochepa kuti aphedwe, choncho sakanagwiritsa ntchito nthawi yotsalayi pongofuna kusangalatsa anthu kapena kuchita zinthu kuti atchuke. Iye anayankha atumwi awiriwo powauza fanizo kuti: “Nthawi yafika yakuti Mwana wa munthu alemekezedwe. Ndithudi ndikukuuzani, Kambewu ka tirigu kakapanda kugwa m’nthaka ndi kufa, kamakhalabe kamodzi komweko. Koma kakafa, kamadzabala zipatso zambiri.”—Yohane 12:23, 24.

      N’zoona kuti kambewu kamodzi ka tirigu kangaoneke ngati kopanda ntchito. Koma kakabzalidwa, kambewuko ‘kamafa’ kenako kamamera ndipo kakakula kamadzabala zipatso zambiri. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene zinachitikira Yesu yemwe anali wangwiro. Yesu anakhala wokhulupirika mpaka nthawi ya imfa yake. Chifukwa cha zimenezi anthu ambiri omwe ali ndi mtima wodzipereka ali ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Aliyense wokonda moyo wake akuuwononga, koma wodana ndi moyo wake m’dziko lino akuusungira moyo wosatha.”—Yohane 12:25.

      Yesu sankangoganizira za madalitso amene iyeyo adzapeze. Tikutero chifukwa iye ananena kuti: “Ngati munthu wafuna kunditumikira ine, anditsatire, ndipo kumene ine ndidzakhala, mtumiki wanga adzakhalanso komweko. Aliyense wonditumikira ine, Atate adzamulemekeza.” (Yohane 12:26) Umenewutu unali mwayi waukulu kwambiri chifukwa anthu amene amalemekezedwa ndi Atate adzalamulira pamodzi ndi Khristu mu Ufumu.

      Chifukwa chakuti Yesu ankadziwa kuti avutika kwambiri komanso afa imfa yopweteka, ananena kuti: “Moyo wanga ukusautsika tsopano, ndinene chiyani kodi? Atate ndipulumutseni ku nthawi yosautsayi.” Sikuti Yesu ankafuna kuti alephere kukwaniritsa zimene Atate wake ankafuna. Tikutero chifukwa anapitiriza kunena kuti: “Komabe nthawi imeneyi iyenera kundifikira pakuti ndiye chifukwa chake ndinabwera.” (Yohane 12:27) Yesu ankafunitsitsa kuchita zonse zimene Mulungu ankafuna kuphatikizapo zoti iyeyo apereke moyo wake monga nsembe.

      • N’chifukwa chiyani Yesu ankaganiza kuti apeza nkhuyu pomwe sinali nthawi ya nkhuyu?

      • N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu sanalakwitse ponena anthu amene ankagulitsa zinthu m’kachisi kuti anali “achifwamba”?

      • N’chifukwa chiyani tingayerekezere Yesu ndi kambewu ka tirigu? Kodi Yesu anali ndi maganizo otani atadziwa kuti avutika komanso kufa imfa yopweteka?

  • Kodi Ayuda Anakhulupirira Yesu Atamva Mulungu Akulankhula?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Yesu akupemphera kuti “Atate lemekezani dzina lanu,” ndipo Ayuda omwe aima pafupi akumva mawu ochokera kwa Mulungu

      MUTU 104

      Kodi Ayuda Anakhulupirira Yesu Atamva Mulungu Akulankhula?

      YOHANE 12:28-50

      • ANTHU AMBIRI ANAMVA MAWU A MULUNGU

      • ZIMENE ZIDZACHITITSE KUTI ANTHU AWERUZIDWE

      Pamene Yesu anali kukachisi, Lolemba pa Nisani 10, ananena za imfa yake. Chifukwa chodera nkhawa mmene imfa yake idzakhudzire dzina la Mulungu, Yesu ananena kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Kenako panamveka mawu amphamvu ochokera kumwamba omwe anayankha zimene Yesu ananena kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”—Yohane 12:27, 28.

      Anthu amene anali pafupi anadabwa kwambiri. Ena ankaganiza kuti amva kugunda kwa bingu pomwe ena ananena kuti: “Mngelo walankhula naye.” (Yohane 12:29) Koma anthuwo anali atamva Yehova akulankhula. Kameneka sikanali koyamba kuti anthu amve Mulungu akulankhula zinthu zokhudza Yesu.

      Zaka zitatu ndi hafu m’mbuyomo, pa nthawi ya ubatizo wa Yesu, Yohane M’batizi anamva Mulungu akulankhula za Yesu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” Kenako mwambo wa Pasika wa mu 32 C. E. utachitika, Yesu anasandulika ndipo zimenezi zinachitika Yakobo, Yohane ndi Petulo akuona. Pa nthawiyi anthu atatuwa anamva Mulungu akulankhula kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.” (Mateyu 3:17; 17:5) Koma pa nthawi yachitatuyi m’pamene anthu ambiri anamva Yehova akulankhula.

      Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Sikuti mawu amenewa amveka chifukwa cha ine ayi, koma chifukwa cha inu.” (Yohane 12:30) Choncho mawu a Mulunguwa anatsimikizira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu yemwenso ndi Mesiya amene anthu ankamuyembekezera.

      Yesu anakhala wokhulupirika pa nthawi yonse imene anali ndi moyo padziko lapansi. Chifukwa cha zimenezi anapereka chitsanzo kwa anthu komanso anatsimikizira kuti Satana Mdyerekezi, yemwe ndi wolamulira wa dzikoli, ayenera kuwonongedwa. Yesu ananena kuti: “Tsopano dziko ili likuweruzidwa, wolamulira wa dzikoli aponyedwa kunja tsopano.” Imfa ya Yesu siinasonyeze kuti wagonjetsedwa ndi Satana koma inasonyeza kuti wapambana. Tikutero chifukwa Yesuyo anafotokoza kuti: “Koma ine ndikadzakwezedwa m’mwamba padziko lapansi, ndidzakokera anthu osiyanasiyana kwa ine.” (Yohane 12:31, 32) Imfa ya Yesu inachititsa kuti Yesuyo akoke anthu ambiri ndipo zimenezi zinatsegulira anthuwo mwayi woti adzapeze moyo wosatha.

      Yesu atanena zoti ‘adzakwezedwa m’mwamba,’ anthuwo anati: “Ife tinamva m’Chilamulo kuti Khristu adzakhala kosatha. Nanga inu mukunena bwanji kuti Mwana wa munthu adzakwezedwa m’mwamba? Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndani?” (Yohane 12:34) Anthu ambiri sanavomereze kuti Yesu ndi Mwana weniweni wa munthu kapena kuti Mesiya amene Mulungu analonjeza. Iwo sanavomereze zimenezi ngakhale kuti panali umboni wokwanira komanso kuti anamva Mulungu akulankhula.

      Yesu ananenanso kuti iye ndi “kuwala” ngati mmene ananenera nthawi ina m’mbuyomo. (Yohane 8:12; 9:5) Iye anauza anthuwo kuti: “Kuwala kukhalabe pakati panu kanthawi pang’ono. Yendani pamene kuwalako mudakali nako, kuti mdima usakugwereni, . . . Pamene kuwala mudakali nako, sonyezani chikhulupiriro mwa kuwalako, kuti mukhale ana ake a kuwala.” (Yohane 12:35, 36) Yesu atangolankhula zimenezi anachoka chifukwa nthawi yoti aphedwe inali isanakwane. Tsikuli linali Nisani 10 ndipo Yesu ankayenera ‘kukwezedwa m’mwamba’ kapena kuti kupachikidwa pamtengo pa nthawi ya Pasika pa Nisani 14.—Agalatiya 3:13.

      Pa nthawi yonse imene Yesu ankachita utumiki wake Ayuda ambiri sanafune kumukhulupirira ndipo zimenezi zinkakwaniritsa ulosi umene Yesaya analemba. Yesaya ananeneratu kuti maso a anthu adzachita khungu ndipo mitima yawo idzauma moti anthuwo sadzatembenuka n’kuchira. (Yesaya 6:10; Yohane 12:40) Ayuda ambiri anakana kwa mtuwagalu umboni wotsimikizira kuti Yesu ndiye Mpulumutsi amene analonjezedwa komanso kuti iye ndiye njira yopezera moyo.

      Panali anthu ena ngati Nikodemo, Yosefe wa ku Arimateya komanso olamulira ena ambiri amene ‘anakhulupirira’ Yesu. Koma kodi anthu amenewa anachitadi zinthu zosonyeza kuti ankakhulupiriradi Yesu kapena anabwerera m’mbuyo mwina chifukwa choopa kuchotsedwa m’sunagoge kapena chifukwa ‘chokonda kwambiri ulemerero wa anthu’?—Yohane 12:42, 43.

      Yesu anafotokoza zimene zimachitika ngati munthu wayamba kumukhulupirira. Iye anati: “Wokhulupirira ine sakhulupirira ine ndekha, komanso amakhulupirira iye amene anandituma ine. Amene wandiona ine waonanso amene anandituma.” Mfundo zimene Mulungu anauza Yesu kuti aphunzitse komanso zimene anapitiriza kulalikira zinali zofunika kwambiri moti Yesuyo ananena kuti: “Aliyense wondinyalanyaza ndi kusalandira mawu anga, ali naye mmodzi womuweruza. Mawu amene ine ndalankhula ndi amene adzamuweruze pa tsiku lomaliza.”—Yohane 12:44, 45, 48.

      Kenako Yesu anamaliza ndi kunena kuti: “Sindinalankhulepo zongoganiza pandekha, koma Atate amene ananditumawo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula. Komanso ndikudziwa kuti lamulo lake limatanthauza moyo wosatha.” (Yohane 12:49, 50) Yesu ankadziwa kuti sipapita nthawi yaitali asanapereke moyo wake ngati nsembe yoombola anthu amene amamukhulupirira.—Aroma 5:8, 9.

      • Pa nkhani yokhudza Yesu, kodi mawu a Mulungu anamveka maulendo atatu ati

      • Kodi ndi olamulira ati amene anakhulupirira Yesu, koma n’chifukwa chiyani sananene poyera zimenezi?

      • Fotokozani chimene chidzachititse kuti anthu adzaweruzidwe pa “tsiku lomaliza.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena