Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr23 March tsamba 1-13
  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Timitu
  • MARCH 6-12
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwbr23 March tsamba 1-13

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

MARCH 6-12

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 23-26

“Kulambira kwa Pakachisi Kunali kwa Dongosolo”

it-2 241

Alevi

Davide anakonza dongosolo labwino kwambiri la mmene Alevi azigwirira ntchito yawo. Anasankha ena kukhala oyang’anira ntchito, akapitawo, oweruza, alonda a pachipata komanso oyang’anira chuma. Panalinso Alevi ena ambiri amene ankathandiza ansembe pa ntchito zosiyanasiyana m’kachisi, m’mabwalo a kachisiyo ndiponso m’zipinda zodyeramo. Ntchito zawo zinali monga kuthandiza pa ntchito yopereka nsembe zopsereza, nsembe zina, kuyeretsa zinthu, kuyeza zinthu zosiyanasiyana komanso ntchito za ulonda. Alevi omwe anali oimba anawaika m’magulu 24, mofanana ndi mmene magulu a ansembe analili ndipo ankatumikira mosinthanasinthana. Ntchito zinkaperekedwa mwakuchita maere. Nawonso alonda a pageti ankauzidwa geti limene adzachitirepo ulonda wawo mwakuchita maere.—1Mb 23; 25; 26; 2Mb 35:3-5, 10.

it-2 686

Wansembe

Pochita utumiki wa pakachisi, ansembe anaikidwa m’magulu ndipo ankatsogoleredwa ndi oyang’anira osiyanasiyana. Popereka mautumiki enaake ankachita kaye maere. Panali magulu 24 a ansembe ndipo gulu lililonse linkatumikira pakachisi kwa mlungu umodzi, zimene zikutanthauza kuti pachaka ankachita utumikiwu kawiri. Zikuoneka kuti kukakhala chikondwerero ansembe onse ankatumikira chifukwa chakuti anthu ankapereka nsembe zochuluka kwambiri, monga mmene anachitira pa nthawi yopereka kachisi kwa Mulungu. (1Mb 24:1-18, 31; 2Mb 5:11; yerekezerani ndi 2Mb 29:31-35; 30:23-25; 35:10-19.) Wansembe ankatha kutumikira pa nthawi zinanso malinga ngati sakusokoneza utumiki wa ansembe omwe anasankhidwa kuti atumikire mlungu umenewo. Malinga ndi miyambo ya arabi, pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi, ansembe analipo ochuluka kwambiri moti utumiki umene ankapatsidwa kuti achite pa mlungu umodzi ankaugawanso potengera mabanja amene anali mu gulu limenelo ndipo banja lililonse linkatumikira kwa tsiku limodzi kapena masiku angapo, motengera kuchuluka kwa anthu m’banjalo.

it-2 451-452

Nyimbo

Pokonzekera zimene zidzachitike pakachisi wa Yehova, Davide anasankha Alevi okwana 4,000 kuti akhale oimba. (1Mb 23:4, 5) Mwa amenewa 288 anali “ophunzitsidwa kuimbira Yehova, onse akatswiri.” (1Mb 25:7) Amene ankatsogolera dongosolo lonseli anali amuna atatu odziwa bwino kuimba omwe ndi Asafu, Hemani ndi Yedutuni (akuoneka kuti ankadziwikanso kuti Etani). Popeza aliyense wa amunawa anali wochokera mwa ana atatu a Levi, omwe ndi Gerisomu, Kohati ndi Merari, ndiye kuti m’gulu la oimba nyimbo pakachisi munali anthu ochokera m’mabanja onse akuluakulu atatu a Alevi. (1Mb 6:16, 31-33, 39-44; 25:1-6) Ana onse aamuna a anthu atatu amenewa, ankakwana 24 ndipo onsewo anali m’gulu la akatswiri odziwa kuimba 288 aja. Mwana aliyense anasankhidwa pochita maere kuti akhale mtsogoleri wa gulu limodzi la oimba. Iye ankatsogolera “akatswiri” ena 11 omwe ankaphatikizapo ana ake komanso Alevi ena. Mwanjira imeneyi, Alevi 288 ([1 + 11] × 24 = 288) omwe anali akatswiri odziwa kuimba, anawaika m’magulu okwana 24 mofanana ndi ansembe. Ngati Alevi 3,712 ‘ophunzira’ kuimbawo anagawidwa m’magulu 24 aja, ndiye kuti gulu lililonse linali ndi amuna ena okwana 155. Zimenezi zikutanthauza kuti panali Alevi 13 omwe ankaphunzira kuimba kuchokera kwa katswiri mmodzi. (1Mb 25:1-31) Popeza amene ankaimba malipenga anali ansembe, ndiye kuti iwo anali owonjezera pa Alevi oimba aja.—2Mb 5:12; yerekezerani ndi Nu 10:8.

it-1 898

Alonda a Pachipata

Pakachisi. Atatsala pang’ono kumwalira, Mfumu Davide anasankhiratu Alevi komanso anthu oti azigwira ntchito pakachisi kuphatikizapo alonda a pachipata ndipo onse analipo 4,000. Gulu lililonse linkagwira ntchito kwa masiku 7. Iwo ndi amene ankayang’anira nyumba ya Yehova ndiponso kuonetsetsa kuti zitseko zatsegulidwa komanso kutsekedwa pa nthawi yake. (1Mb 9:23-27; 23:1-6) Kuwonjezera pa ntchito yomwe ankagwira, ena ankasamaliranso ndalama zomwe anthu ankapereka kuti zigwire ntchito pakachisipo. (2Mf 12:9; 22:4) Patapita nthawi, pamene mkulu wa ansembe Yehoyada ankadzoza Yehoasi monga mfumu, panasankhidwa alonda apadera kuti akhale pageti n’cholinga choti ateteze Yehoasi yemwe anali wamng’ono kwa Mfumukazi Ataliya yemwe anakhala mfumukazi mochita kulanda. (2Mf 11:4-8) Pomwe Yosiya ankathetsa kulambira mafano, alonda a pachipata anathandiza nawo pochotsa ziwiya zapakachisi zomwe anthuwo ankagwiritsa ntchito polambira Baala ndipo ziwiyazi zinakaotchedwa kunja kwa mzinda.—2Mf 23:4.

Mfundo Zothandiza

w22.03 22 ¶10

Kulambira Koona Kumachititsa Kuti Muzisangalala Kwambiri

10 Timalambira Yehova tikamaimba nawo nyimbo. (Sal. 28:7) Aisiraeli ankaona kuti kuimba nyimbo n’kofunika kwambiri pa kulambira. Mfumu Davide anasankha Alevi 288 kuti aziimba nyimbo pakachisi. (1 Mbiri 25:1, 6-8) Masiku ano tingasonyeze kuti timakonda Mulungu poimba nyimbo zomutamanda. Sikuti chofunika kwambiri ndi kukhala ndi luso loimba. Taganizirani chitsanzo ichi: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri” tikamalankhula koma zimenezi sizichititsa kuti tisamalankhule mumpingo komanso tikamalalikira. (Yak. 3:2) Mofanana ndi zimenezi, tikhozabe kumaimba nyimbo zotamanda Yehova ngakhale pamene tikuona kuti sitimaimba bwino.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w11 6/1 14-15

Kodi Mulungu Ali ndi Gulu Lake Limene Akulitsogolera?

M’nthawi ya atumwi, mipingo yachikhristu inakhazikitsidwa m’madera ambiri ku Asia ndi ku Ulaya chifukwa chakuti atumwi komanso ophunzira a Yesu ankalalikira mwakhama. Ngakhale kuti mipingo imeneyi inali motalikirana, palibe mpingo umene unkachita zinthu zosiyana ndi mipingo ina. Panali dongosolo labwino limene mipingoyi inkayendera ndipo atumwi ndi amene ankaitsogolera mwachikondi. Mwachitsanzo, Tito anatumidwa ndi mtumwi Paulo kuti ‘akakonze zinthu’ ku Kerete. (Tito 1:5) Komanso Paulo ananena m’kalata imene analembera mpingo wa ku Korinto kuti abale ena anali ndi “luso loyendetsa zinthu.” (1 Akorinto 12:28) Koma kodi ndani anachititsa kuti zinthu zonsezi ziziyenda bwino? Paulo ananena kuti “Mulungu analumikiza” kapena kuti kukhazikitsa dongosolo mumpingo.—1 Akorinto 12:24.

Anthu amene anali ndi udindo mu mpingo wachikhristu ntchito yawo sinali kulamulira Akhristu anzawo. M’malomwake anali ‘antchito anzawo’ amene ankatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu komanso anafunika kukhala “zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (2 Akorinto 1:24; 1 Petulo 5:2, 3) Yesu Khristu, ndiye “mutu wampingo” osati munthu aliyense kapena gulu la anthu opanda ungwiro.—Aefeso 5:23.

Pa nthawi ina mpingo wa ku Korinto unayamba kuchita zinthu zosiyana kwambiri ndi zimene mipingo ina inkachita. Choncho Paulo anawalembera kuti: “Kodi mawu a Mulungu anachokera kwa inu, kapena anafika kwa inu nokha?” (1 Akorinto 14:36) Paulo anagwiritsa ntchito funso limeneli losafunika yankho, pofuna kuwathandiza kumvetsa kuti sankayenera kumachita zinthu zosiyana ndi mipingo ina yachikhristu. Chifukwa chotsatira malangizo a atumwi, mipingo inakula ndiponso inkayenda bwino.—Machitidwe 16:4, 5.

Umboni Wosonyeza Kuti Mulungu Amakonda Atumiki Ake

Nanga bwanji masiku ano? Anthu ena angamaganize kuti sakufunikira kukhala m’chipembedzo chilichonse. Koma Baibulo limasonyeza kuti Mulungu wakhala akugwiritsa ntchito gulu lake kuti akwaniritse zofuna zake. Iye ankatsogolera mwadongosolo Aisiraeli akale komanso Akhristu oyambirira.

Ndiye kodi si zoona kuti masiku anonso Yehova Mulungu akutsogolera anthu ake ngati mmene ankachitira kale? N’zoonekeratu kuti Mulungu akutsogolera atumiki ake mwadongosolo komanso akuonetsetsa kuti ndi ogwirizana ndipo umenewu ndi umboni wakuti amawakonda. Masiku ano Yehova akugwiritsa ntchito gulu lake kukwaniritsa chifuno chake chokhudza anthu. Ndiyeno kodi gulu la Yehova tingalidziwe bwanji? Tiyeni tione mfundo zimene zingatithandize kulidziwa.

▪ Akhristu oona akugwira mwadongosolo ntchito yolalikira. (Mateyu 24:14; 1 Timoteyo 2:3, 4) Yesu analamula otsatira ake kuti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu ku mitundu yonse. Ntchito imeneyi siingatheke patakhala kuti palibe gulu la padziko lonse lochita zinthu mwadongosolo. Mwachitsanzo, inuyo mungathe kudyetsa munthu mmodzi koma mutakhala kuti mukufunika kudyetsa anthu mamiliyoni ambiri, mungafunike kugwira ntchito mogwirizana ndi gulu la anthu lotsogoleredwa bwino komanso logwira ntchito mwadongosolo. N’chimodzimodzinso Akhristu oona. Kuti akwaniritse ntchito yawo yolalikira padziko lonse, afunika ‘kutumikira Mulungu mogwirizana’ (Zefaniya 3:9) Ntchito imeneyi, ikuchitika m’mayiko osiyanasiyana, kwa anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana komanso ochokera m’mitundu yosiyanasiyana. Ndiye kodi ntchito imeneyi ingatheke popanda gulu logwirizana? N’zachidziwikire kuti izi sizingatheke.

▪ Akhristu oona amathandizana komanso kulimbikitsana. Katswiri wokwera mapiri, akamakwera phiri yekha angakhale ndi ufulu wosankha kupita kulikonse kumene akufuna ndipo sangavutike ndi kusamalira anthu ena amene sanazolowere kukwera mapiri. Komabe munthu ameneyu atachita ngozi kapena atakumana ndi vuto lililonse, angavutike kwambiri chifukwa angasowe womuthandiza. N’kupanda nzeru kudzipatula n’kumachita zinthu pawekha. (Miyambo 18:1) Kuti Akhristu akwanitse kugwira ntchito imene Yesu anawapatsa, ayenera kumathandizana. (Mateyu 28:19, 20) Mpingo wachikhristu umapereka malangizo a m’Baibulo, kuphunzitsa komanso kulimbikitsa anthu ndipo izi n’zofunika kwambiri kuti Akhristu apitirizebe kutumikira Yehova. Kodi pakanakhala kuti palibe mpingo wachikhristu, anthu akanamapita kuti kukaphunzitsidwa njira za Yehova?—Aheberi 10:24, 25.

▪ Akhristu oona amatumikira Mulungu mogwirizana. Nkhosa za Yesu zimamva mawu ake ndipo zimakhala “gulu limodzi” komanso zimatsogoleredwa ndi iyeyo. (Yohane 10:16) Nkhosa zimenezi sizimapezeka m’matchalitchi kapena m’magulu ogawanika azipembedzo komanso sizogawikana pa nkhani ya ziphunzitso. Koma nkhosa zonsezi ‘zimalankhula mogwirizana.’ (1 Akorinto 1:10) Kuti anthu azikhala mogwirizana pamafunika dongosolo ndipo kuti pakhale dongosolo pamafunika mgwirizano. Mulungu amadalitsa anthu okhawo amene amakondana komanso kugwirizana.—Salimo 133:1, 3.

Kukonda Mulungu ndiponso choonadi cha m’Baibulo kwachititsa anthu mamiliyoni ambiri kukhala m’gulu limene limatsatira mfundo zimenezi komanso zina zopezeka m’Baibulo. A Mboni za Yehova padziko lonse ndi gulu logwirizana ndipo akuyesetsa kuchita chifuno cha Mulungu. Iwo amakhulupirira kuti lonjezo ili ndi loona: “Ndidzakhala pakati pawo ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.” (2 Akorinto 6:16) Inunso mungapeze madalitso amenewa ngati mutalowa m’gulu la Yehova Mulungu n’kuyamba kumulambira.

MARCH 13-19

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 27-29

“Malangizo Achikondi a Bambo Opita kwa Mwana Wake”

w05 2/15 19 ¶9

Kuteteza Dzina Lathu Monga Akhristu

9 Chidziweni bwino choonadi cha m’Baibulo. Pang’ono ndi pang’ono tingaiwale kuti ndife atumiki a Yehova ngati utumiki wathuwo sukuyendera limodzi ndi kudziwa bwino Malemba. (Afilipi 1:9, 10) Mkhristu aliyense, kaya ndi wachinyamata kapena wachikulire, ayenera kukhala ndi umboni woti iyeyo payekha azikhutira nawo wosonyeza kuti zimene amakhulupirira zilidi choonadi cha m’Baibulo. Paulo anapempha okhulupirira anzake kuti: “Yesani zonse; sungani chokomacho.” (1 Atesalonika 5:21) Akhristu achinyamata omwe akuchokera m’mabanja oopa Mulungu ayenera kuzindikira kuti iwowo sangakhale Akhristu oona mwa kungodalira chikhulupiriro cha makolo awo. Davide analimbikitsa Solomo, mwana wake weniweni kuti ‘am’dziwe Mulungu wa atate wake, ndi kum’tumikira ndi mtima wangwiro.’ (1 Mbiri 28:9) Sizinali zokwanira kwa Solomo wachinyamatayo kumangoonerera mmene bambo akewo akulimbitsira chikhulupiriro chawo mwa Yehova. Nayenso anafunika kum’dziwa Yehova, ndipo anachitadi zimenezo. Iye anapempha Mulungu kuti: “Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa.”—2 Mbiri 1:10.

w12 4/15 16 ¶13

Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

13 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Zimakhala zosangalatsa tikamapezeka pa misonkhano ndiponso mu utumiki wakumunda nthawi zonse. Koma kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu sikumangotanthauza zinthu zokhazo. (2 Mbiri 25:1, 2, 27) Ngati Mkhristu mumtima mwake amakondabe “zinthu za m’mbuyo,” kapena kuti zinthu zina za m’dzikoli, ubwenzi wake ndi Mulungu umakhala pa ngozi. (Luka 17:32) Tikhoza kukhala ‘oyenera ufumu wa Mulungu’ pokhapokha ngati ‘timanyansidwa ndi choipa, n’kugwiritsitsa chabwino.’ (Aroma 12:9; Luka 9:62) Ngakhale kuti zinthu zina m’dziko la Satanali zingaoneke zothandiza kapena zosangalatsa, tiyenera kusamala kuti chinthu china chilichonse chisatilepheretse kutumikira Yehova ndi mtima wonse.—2 Akor. 11:14; werengani Afilipi 3:13, 14.

w17.09 32 ¶20-21

‘Limba Mtima Ndipo Ugwire Ntchitoyi’

20 Davide anauza Solomo kuti Yehova akhala naye mpaka ntchito yonse yomanga kachisiyo itatha. (1 Mbiri 28:20) Solomo ayenera kuti ankaganizira kwambiri mawu amenewa ndipo anamuthandiza kuti asamadziderere chifukwa choti anali wamng’ono komanso wosadziwa zambiri. Iye analimba mtima n’kuyamba ntchitoyo ndipo Yehova anamuthandiza kuti amalize kumanga kachisi wokongolayo m’zaka 7 ndi hafu zokha.

21 Yehova angatithandizenso kuti tizichita zinthu molimba mtima n’kukwaniritsa ntchito yathu m’banja komanso mumpingo. (Yes. 41:10, 13) Tisamakayikire kuti tikakhala olimba mtima polambira Yehova, iye adzatidalitsa panopa komanso m’tsogolo. Choncho tiyeni tonsefe ‘tikhale olimba mtima n’kumagwira ntchito’ zabwino.

Mfundo Zothandiza

w17.03 29 ¶6-7

Kodi Mumakhalabe Bwenzi Labwino Zinthu Zikavuta?

Davide ankagwirizananso ndi anthu ena amene anakhalabe okhulupirika kwa iye pa nthawi ya mavuto. Mmodzi mwa anthuwa anali Husai ndipo Baibulo limati iye anali “mnzake wa Davide.” (2 Sam. 16:16; 1 Mbiri 27:33) Husai ayenera kuti ankagwira ntchito kunyumba ya mfumuyi ndipo nthawi zina ankatumidwa kuchita zinthu zachinsinsi.

Pamene mwana wa Davide dzina lake Abisalomu ankafuna kulanda ufumu, Aisiraeli ambiri anakhala kumbali yake. Koma Husai anakhala kumbali ya Davide. Pamene Davide anathawa, Husai anapita naye limodzi. Davide anakhumudwa kwambiri poona kuti anthu amene ankawakhulupirira komanso mwana wake weniweni amuukira. Koma Husai anakhalabe wokhulupirika kwa Davide ndipo anaika moyo wake pachiswe n’kuchita zimene Davide anamuuza kuti chiwembu cha Abisalomu chilephereke. Sikuti Husai anangochita izi chifukwa choti ankagwira ntchito kwa mfumu. Koma n’chifukwa choti anali wokhulupirika kwa mnzakeyu.—2 Sam. 15:13-17, 32-37; 16:15-23;17:16.

MARCH 20-26

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 1-4

“Mfumu Solomo Inasankha Zinthu Mopanda Nzeru”

it-1 174 ¶5

Gulu la Asilikali

Solomo atayamba kulamulira, analemba malamulo atsopano oti asilikali a Isiraeli azitsatira. Ngakhale kuti ulamuliro wake unali wamtendere, iye anawonjezera mahatchi ndi magaleta. Mahatchi ambiri ankagulidwa ku Iguputo. Mizinda yambiri inkafunika kumangidwa kuti magulu a asilikali atsopanowa azikhalamo. (1Mf 4:26; 9:19; 10:26, 29; 2Mb 1:14-17) Komabe Yehova sanadalitse zonsezi ndipo kumwalira kwa Solomo komanso kugawikana kwa ufumu zinachititsa kuti gulu la asilikali a Isiraeli lithe. Yesaya analemberatu kuti: “Tsoka kwa anthu amene akupita ku Iguputo kukapempha thandizo. Iwo akudalira mahatchi wamba ndi kukhulupirira magaleta ankhondo, chifukwa chakuti ndi ambiri. Akudaliranso mahatchi akuluakulu chifukwa chakuti ndi amphamvu kwambiri, koma sanayang’ane kwa Woyera wa Isiraeli ndipo sanafunefune Yehova.”—Yes 31:1.

it-1 427

Galeta

Mu Isiraeli munalibe mzinda umene unali ndi magaleta ambiri mpaka pamene Solomo anayamba kulamulira. Zinali choncho chifukwa Mulungu anali atachenjezeratu kuti mfumu isadzichulukitsire mahatchi chifukwa mtunduwo sunkatetezedwa ndi mahatchiwo. Lamuloli linachititsa kuti asamagwiritse ntchito magaleta ambiri chifukwa mahatchi ndi amene ankagwiritsidwa ntchito pokoka magaleta. (De 17:16) Pofotokoza za mavuto omwe anthuwo adzakumane nawo akamadzalamuliridwa ndi mfumu, Samueli anawauza kuti: “Idzatenga ana anu kuti azikayenda m’magaleta ake.” (1Sa 8:11) Pa nthawi imene Abisalomu komanso Adoniya ankafuna kulanda ufumu, aliyense anadzipangira galeta ndipo amuna 50 ankathamanga patsogolo pawo. (2Sa 15:1; 1Mf 1:5) Davide atagonjetsa mfumu ya ku Zoba, anasunga mahatchi a magaleta 100.—2Sa 8:3, 4; 10:18.

Pamene Mfumu Solomo ankakhazikitsa gulu la asilikali la Aisiraeli, anawonjezera magaletawo kuti afike pa 1,400. (1Mf 10:26, 29; 2Mb 1:14, 17) Kuwonjezera pa mzinda wa Yerusalemu, mizinda ina yomwe inkadziwika kuti mizinda yosungirako magaleta inali ndi zipangizo zapadera zoti azisamalira zida zonse zankhondo.—1Mf 9:19, 22; 2Mb 8:6, 9; 9:25.

Mfundo Zothandiza

w05 12/1 19 ¶6

Mfundo Zazikulu za M’buku Lachiwiri la Mbiri

1:11, 12. Pempho la Solomo linasonyeza Yehova kuti zimene mfumuyo inafuna kwambiri mu mtima mwake ndi kupeza nzeru ndi kudziwa. Inde, mapemphero athu kwa Mulungu amavumbula zimene mtima wathu umakonda. Ndiye ndi bwino kuganizira mofatsa za zimene timanena m’mapemphero athuwo.

MARCH 27–APRIL 2

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 5-7

“Mtima Wanga Udzakhala Pamenepa Nthawi Zonse”

w02 11/15 5 ¶1

Osaleka Kusonkhana Pamodzi

Pambuyo pake, Davide atakhala mfumu mu Yerusalemu, anasonyeza kuti anali wofunitsitsa ndi mtima wonse kumanga nyumba yoti ilemekeze Yehova. Koma popeza Davide anali munthu wankhondo, Yehova anamuuza kuti: “Sudzamangira dzina langa nyumba.” M’malo mwake, Yehova anasankha mwana wake Solomo kuti amange kachisi. (1 Mbiri 22:6-10) Solomo anapatulira kachisi ameneyu mu 1026 B.C.E., atamaliza ntchito yomanga yomwe inatenga zaka zisanu ndi ziwiri ndi theka. Yehova anavomereza nyumba imeneyi mwakunena kuti: “Ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.” (1 Mafumu 9:3) Yehova akanabweretsa madalitso pa nyumba imeneyo ngati Aisiraeli akanakhalabe okhulupirika. Koma ngati akanasiya kuchita zabwino, Yehova sakanayanjanso malo amenewo, ndipo nyumbayo ikanakhala bwinja.—1 Mafumu 9:4-9; 2 Mbiri 7:16, 19, 20.

it-2 1077-1078

Kachisi

Mbiri yake. Kachisiyu analipo mpaka mu 607 B.C.E., kufikira pamene anawonongedwa ndi asilikali a Babulo omwe ankatsogoleredwa ndi Mfumu Nebukadinezara. (2Mf 25:9; 2Mb 36:19; Yer 52:13) Chifukwa chakuti nthawi zina Aisiraeli ankayamba kulambira konyenga, Mulungu analola kuti mitundu ina izivutitsa Yuda ndi Yerusalemu, ndipo nthawi zina mitunduyi inkatenga chuma cha m’kachisi. Panalinso nthawi zina pamene kachisiyu ankangosiyidwa osasamalidwa. Mfumu Sisaki ya Iguputo inatenga chuma cha m’kachisiyu (993 B.C.E.) m’masiku a Rehobowamu mwana wa Solomo. Ndipotu izi zinachitika patangodutsa zaka 33 kuchokera pamene kachisiyu anatsegulidwa. (1Mf 14:25, 26; 2Mb 12:9) Mfumu Asa (977-937 B.C.E.) inkalemekeza nyumba ya Yehova, koma pofuna kuteteza Yerusalemu, iye anachita zinthu mopusa popereka chiphuphu kwa mfumu ya Siriya, Beni-hadadi Woyamba. Anapereka siliva ndi golide kuchokera pa chuma cha m’kachisi n’cholinga choti mfumu ya Siriyayo ithetse mgwirizano wake ndi Basa mfumu ya Isiraeli.—1Mf 15:18, 19; 2Mb 15:17, 18; 16:2, 3.

Mfundo Zothandiza

w10 12/1 11 ¶7

Iye Amadziwa Bwino “Mtima wa Ana a Anthu”

Pemphero la Solomo limeneli ndi lolimbikitsa kwambiri. Nthawi zina anthu anzathu sangamvetse ‘mliri ndi ululu wathu’ kapena kuti mmene tikumvera mumtima mwathu. (Miyambo 14:10) Koma Yehova amadziwa mitima yathu ndipo amatidera nkhawa kwambiri. Kupemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima kungatithandize kupirira mavuto amene tikukumana nawo. Baibulo limati: ‘Mum’tulire nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w93 2/1 31

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Ngati Mkhristu akudwala kapena ali paulendo ndipo sangathe kupezeka pa mwambo wa Chikumbutso, kodi angachite mwambowo mwezi wotsatira?

Kale ku Isiraeli, Pasika ankachitika chaka chilichonse pa tsiku la 14 la mwezi woyamba wotchedwa Nisani (kapena, Abibu). Koma pa Numeri 9:10, 11, panalembedwa njira ina yapadera yochitira mwambowu. Lembali limati: “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu wina aliyense mwa inu kapena mwa mbadwa zanu, amene wadetsedwa pokhudza mtembo wa munthu, kapena amene ali pa ulendo wautali, akonzebe nsembe ya pasika yopereka kwa Yehova. Azikonza nsembeyo m’mwezi wachiwiri [wotchedwa Iyara, kapena Zivi] pa tsiku la 14, madzulo kuli kachisisira. Azidya nyama ya nsembeyo pamodzi ndi mikate yopanda chofufumitsa, ndiponso masamba owawa.’”

Palembali sakupereka tsiku lina lachiwiri lochita Pasika lomwe linkapatsa Mwiisiraeli aliyense kapena banja lililonse ufulu wosankha tsiku limene lawakomera, (Nisani 14 kapena Zivi 14) chifukwa si aliyense amene ankaloledwa kudya chakudya cha Pasika m’mwezi wachiwiri. Makonzedwewa anali apadera poganizira Mwiisiraeli amene pa Nisani 14 anali wodetsedwa mwamwambo kapena anali kutali ndi kumene mwambowo unkachitikira nthawi zonse.

Nthawi yokhayo yomwe inalembedwa kuti anthu ambiri anachita mwambowu mwanjira imeneyi, ndi pamene mfumu yokhulupirika Hezekiya inayambitsanso kuti anthu azichita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa. Panalibe nthawi yokonzekera chikondwererochi m’mwezi woyamba (popeza ansembe anali asanakonzekere ndiponso anthu sanasonkhane), choncho chinachitika pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri.—2 Mbiri 29:17; 30:1-5.

Kupatulapo pa zochitika zapadera ngati zimenezo, Ayuda ankachita Pasika tsiku limene Mulungu anasankha. (Ekisodo 12:17-20, 41, 42; Levitiko 23:5) Yesu ndi ophunzira ake anachita phwandolo monga momwe Chilamulo chinanenera, sanadzisankhire okha tsiku lochita mwambowu. Luka analemba kuti: “Tsiku la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa linafika, tsiku loyenera kupha nyama yoperekera nsembe ya pasika. Yesu anatumiza Petulo ndi Yohane kuti: ‘Pitani mukatikonzere pasika kuti tidye.’”—Luka 22:7, 8.

Panthawi imeneyo, Yesu anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Kupezeka kwa Akhristu pamwambowo ndi chinthu chofunika kwambiri. Mwambowu ndi wapadera kwambiri kwa a Mboni za Yehova. Mawu a Yesu amasonyeza chifukwa chake. Iye anati: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) Choncho wa Mboni za Yehova aliyense ayenera kukonzekera mwambowu kuti patsikuli pasadzakhale zosokoneza. Mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye udzachitika Lachiwiri, pa 6 April, 1993.

Nthawi zina, zinthu zina zosayembekezereka monga matenda kapena maulendo, zingalepheretse Mkhristu kupezeka pamwambo wa Chikumbutso monga mmene anakonzera. Kodi zikatere ayenera kuchita chiyani?

Pamwambowu, mkate wopanda chofufumitsa ndi vinyo zimayendetsedwa ndipo amene anadzozedwa ndi mzimu wa Mulungu ndipo anasankhidwa kudzapita kumwamba ndi amene amadya. (Mateyu 26:26-29; Luka 22:28-30) Ngati munthu amene amadya zizindikiro chaka chilichonse wadwala kapena ali m’chipatala, akulu a mpingo wake adzakonza zoti mmodzi wa iwo amupititsire mkate ndi vinyo komanso kumufotokozera malemba oyenera a nkhani ya Chikumbutso kenako n’kumupatsa zizindikiro. Ngati Mkhristu wodzozedwa ali kutali ndi mpingo wakwawo, ayenera kukonza zoti adzapite ku mpingo wa m’dera limene adzakhale ali panthawi ya Chikumbutsoyo.

Choncho, ndi pazifukwa zapadera kwambiri zokha zomwe zingachititse Mkhristu wodzozedwa kuchita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye patatha masiku 30 (mwezi umodzi wathunthu) mogwirizana ndi lamulo la pa Numeri 9:10, 11 ndi chitsanzo cha pa 2 Mbiri 30:1-3, 15.

Amene ali m’gulu la “nkhosa zina” za Yesu, okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso, sakulamulidwa kudya mkate ndi kumwa vinyo. (Yohane 10:16) N’zofunika kwambiri kuti iwo azifika pa mwambo wapachakawu, koma samadya zizindikirozo. Choncho ngati mmodzi mwa iwo wadwala kapena ali paulendo ndipo sapezeka pa mpingo ulionse madzulowo, iye akhoza kuwerenga yekha malemba oyenerera (kuphatikizapo malemba ofotokoza nthawi yomwe Yesu anayambitsa mwambowu) ndi kupemphera kwa Yehova. Pankhani imeneyi, sipakufunika makonzedwe alionse owonjezera kapena nkhani yapadera mwezi wotsatira.

APRIL 10-16

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 8-9

“Mfumukazi Inaona Kuti Nzeru Ndi Zamtengo Wapatali”

w99 11/1 20 ¶4

Anthu Ambiri Akhala Opatsa

Mfumukazi ya ku Sheba inatheranso nthawi yaitali ndipo inayesetsa kwambiri kuti ikachezere Solomo. Zimaoneka kuti mzinda wa Sheba unali m’dera limene masiku ano ndi dziko la Republic of Yemen, choncho mfumukaziyo ndi ngamila zake zambiri anayenda ulendo wa makilomita 1,600 kupita ku Yerusalemu. Monga momwe Yesu ananenera, “inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.” Kodi mfumukazi ya ku Sheba inavutikiranji choncho? Inabwera “kudzamva nzeru za Solomo.”—Luka 11:31.

w99 7/1 30 ¶4-5

Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambiri

Mulimonse mmene zinaliri, mfumukazi inafika ku Yerusalemu “ndi anthu ambiri oiperekeza. Inabwera ndi ngamila zitanyamula mafuta a basamu, golide wambiri, ndi miyala yamtengo wapatali.” (1 Mafumu 10:2a) Ena amati “anthu ambiri oiperekeza” amenewo anaphatikizapo anthu okhala ndi zida. Izi zingakhale zomveka, popeza kuti mfumukaziyi inali munthu wolemekezeka kwambiri ndipo inkayenda ndi katundu wamtengo wapatali wa ndalama mamiliyoni ambiri.

Komabe, onani kuti, mfumukazi inamva mbiri ya Solomo kuti “anatchuka chifukwa cha dzina la Yehova.” Choncho uwu sunali ulendo wokachita malonda chabe. Zimaoneka kuti mfumukaziyi kwenikweni inapita kuti ikamve nzeru za Solomo mwinanso kukaphunzira zina za Mulungu wake, Yehova. Popeza iyenera kuti inabadwa kwa Semu kapena Hamu, amene ankalambira Yehova, iyenera kuti inkachita chidwi ndi chipembedzo cha makolo ake.

w99 7/1 30-31

Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambiri

Mfumukazi ya ku Sheba inagoma kwambiri ndi nzeru za Solomo komanso ulemerero wa ufumu wake kotero kuti “inazizira nkhongono.” (1 Mafumu 10:4, 5) Ena amati mfumukaziyo “inabanika.” Katswiri wina wamaphunziro mpaka ananena kuti mwina inakomoka. Kaya panachitika zotani, mfumukaziyi inadabwa ndi zimene inaona ndi kumva. Inati anyamata a Solomo anali odala chifukwa ankamva nzeru za mfumuyi, ndipo inadalitsa Yehova chifukwa chopatsa Solomo ufumu. Kenako mfumukaziyi inapereka kwa mfumuyo mphatso zamtengo wapatali, moti golide yekha anali wokwana ndalama pafupifupi $40,000,000 mogwirizana ndi mitengo ya masiku ano. Nayenso Solomo anapereka kwa mfumukazi ya ku Sheba “zofuna zake zonse zimene inapempha.”—1 Mafumu 10:6-13.

it-2 990-991

Solomo

Mfumukazi ya ku Sheba itaona ulemerero wa kachisi amene Solomo anamanga komanso nyumba yake, chakudya cha patebulo pake, zakumwa zake, mmene atumiki ake operekera zakudya anali kuvalira ndi nsembe zake zopsereza zimene ankapereka panyumba ya Yehova nthawi zonse, “inazizira nkhongono,” ndipo inanena kuti, “ndinangouzidwa hafu chabe. Nzeru zanu ndi ulemerero wanu zaposa zinthu zimene ndinamva.” Ndipo inanenanso kuti atumiki ake amene amaitumikira ndi odala. Itaona zimenezi, mfumukaziyo inatamanda komanso kudalitsa Yehova chifukwa anasonyeza kuti amakonda Aisiraeli powapatsa Solomo kuti azipereka zigamulo ndi kuchita chilungamo.—1Mf 10:4-9; 2Mb 9:3-8.

Mfundo Zothandiza

it-2 1097

Mpando Wachifumu

Mpando wachifumu wa wolamulira wa Isiraeli umene unafotokozedwa mwatsatanetsatane, ndi wokhawo umene Solomo anapanga. (1Mf 10:18-20; 2Mb 9:17-19) Zimaoneka kuti mpandowu unaikidwa mu “Bwalo la Mpando Wachifumu,” mu imodzi mwa nyumba zimene zinali ku Phiri la Moriya ku Yerusalemu. (1Mf 7:7) Mpando wachifumuwo unapangidwa ndi ‘minyanga ya njovu ndipo unakutidwa ndi golide komanso kuseri kwake kunali chotchingira chozungulira. Unalinso ndi moika manja mbali zonse.’ Ngakhale kuti minyanga ya njovu inali zipangizo zomwe anazigwiritsa ntchito popanga mpandowu, njira yomangira yomwe ankaigwiritsa ntchito pakachisi imaonetsa kuti mpandowu unapangidwa ndi matabwa, unakutidwa ndi golide woyenga bwino ndipo anaukongoletsa ndi minyanga ya njovu. Munthu akauona, mpandowu unkaoneka kuti unapangidwa ndi minyanga ya njovu ndi golide. Pambuyo potchula za masitepe 6 okafika kumpando wachifumu Baibulo limapitiriza kuti: “M’mphepete mwake munali zifaniziro ziwiri za mikango itaimirira. Pamasitepe 6 amenewo, panali zifaniziro 12 za mikango itaimirira, mbali iyi ndi iyi.” (2Mb 9:17-19) Zizindikiro za mkango zomwe zimaimira ulamuliro ndi zoyenera. (Ge 49:9, 10; Chv 5:5) Mikango 12 imeneyi imaoneka kuti inkaimira mafuko 12 a Isiraeli, ndipo n’kutheka kuti zinkatanthauza kuti mafukowo azigonjera komanso azithandiza wolamulira amene ali pa mpandowu. Unalinso ndi chopondapo mapazi chagolide. Zimene Baibulo limafotokoza zokhudza mpando wachifumu wa nyanga za njovu ndi wa golidewu kuti unali waulemerero, unali ndi chotchingira komanso unali ndi mikango kutsogolo, zimasonyeza kuti mpandowu umaposa mipando yonse yachifumu imene inalipo panthawiyo, yomwe inapezedwa kaya ndi ofukula za m’mabwinja, yosonyezedwa mu zipilala kapena yomwe olemba mbiri anafotokoza. Yemwe analemba buku la 2 Mbiri anafotokoza zoona pomwe anati: “Panalibenso ufumu wina umene unali ndi mpando wachifumu ngati umenewo.”—2Mb 9:19.

APRIL 17-23

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 10-12

“Muzitsatira Malangizo Anzeru”

w18.06 13 ¶3

Akanatha Kusangalatsa Mulungu

Rehobowamu ayenera kuti anavutika kusankha zochita pa nkhaniyi. Zinali choncho chifukwa chakuti ngati akanachita zimene anthuwo anapempha, iye, banja lake ndiponso anthu ena okhala m’nyumba ya mfumu sakanatha kupeza zinthu zapamwamba zimene anazolowera. Koma ngati akanakana kuchita zimene anthuwo ankafuna, mwina iwo akanamuukira. Kodi Rehobowamu anasankha kuchita chiyani? Poyamba anafunsira malangizo kwa amuna achikulire omwe anali alangizi a Solomo. Koma kenako anapemphanso malangizo kwa achinyamata anzake. Iye anasankha kutsatira malangizo a achinyamatawo ndipo anasankha kuchitira nkhanza anthuwo. Iye anayankha kuti: “Ine ndidzakusenzetsani goli lolemera kwambiri, ndipo ndidzawonjezera goli lanulo. Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu, koma ine ndidzakukwapulani ndi zikoti zaminga.”—2 Mbiri 10:6-14.

w01 9/1 28-29

Mmene Mungasankhire Mwanzeru

Yehova waperekanso anthu okhwima maganizo mumpingo amene tingakambirane nawo zosankha zathu. (Aefeso 4:11, 12) Komabe, pofunsira kwa anthu ena tisatsatire zomwe ena amachita zofunsa anthu ambiri mpaka atapeza yemwe akunena zofuna zawo, ndiyeno n’kutsatira uphungu wake. Tikumbukirenso chitsanzo chotichenjeza cha Rehabiamu. Pamene ankafuna kupanga chosankha chachikulu kwambiri, analandira uphungu wabwino kwabasi kuchokera kwa anthu achikulire amene ankagwira ntchito ndi abambo ake. Koma m’malo motsatira uphungu wawo, iye anakafunsira kwa anyamata anzake. Atatsatira uphungu wa anyamatawo, sanasankhe mwanzeru ndipo zotsatira zake zinali zakuti anthu m’chigawo chachikulu cha ufumu wake anam’pandukira.—1 Mafumu 12:1-17

Tikafuna kufunsira uphungu, tifunsire kwa anthu amene aona zambiri m’moyo ndiponso omwe amadziwa bwino Malemba komanso amene amaona mfundo zabwino zachikhalidwe kukhala zofunika. (Miyambo 1:5; 11:14; 13:20) Ngati n’kotheka, sinkhasinkhani pa mfundo zachikhalidwe zomwe zikugwirizana ndi nkhaniyo ndiponso zomwe mwapeza pakufufuza kwanu. Mukayamba kuona zinthu m’kuunika kwa Mawu a Mulungu, chosankha cholondola chidzaonekeratu.—Afilipi 4:6, 7.

it-2 768 ¶1

Rehobowamu

Kunyada komanso kudzimva kwa Rehobowamu kunachititsa kuti anthuwo agawikane. Mafuko a Yuda ndi Benjamini komanso ansembe ndi Alevi a maufumu onse awiri kuphatikizapo anthu ena a m’mafuko 10 ndi okhawo amene anapitiriza kuthandiza nyumba ya Davide.—1Mf 12:16, 17; 2Mb 10:16, 17; 11:13, 14, 16.

Mfundo Zothandiza

it-1 966-967

Ziwanda Zooneka Ngati Mbuzi

Mawu a Yoswa opezeka pa Yoswa 24:14 amasonyeza kuti Aisiraeli anakhudzidwa kwambiri ndi kulambira konyenga kumene kunkachitika ku Iguputo panthawi imene ankakhala kumeneko, pamene buku la Ezekieli limasonyeza kuti kulambira konyengaku kunapitirira. (Eze 23:8, 21) Pachifukwa chimenechi, akatswiri ena amanena kuti zomwe Mulungu ananena m’chipululu zoletsa Aisiraeli kuti “asamaperekenso nsembe zawo ku ziwanda zooneka ngati mbuzi,” (Le 17:1-7) komanso zomwe Yerobowamu anachita pokhazikitsa ansembe “m’malo okwezeka kuti azitumikira ziwanda zooneka ngati mbuzi ndi mafano a ana a ng’ombe amene iye anapanga,” (2Mb 11:15) zimasonyeza kuti Aisiraeli ankalambira mbuzi mwanjira inayake mofanana ndi zimene zinkachitika kwambiri ku Iguputo makamaka kumunsi kwa Iguputo. Herodito analemba (II, 46) kuti kuchokera pa kulambira kwa ku Iguputoku, Agiriki anayamba kukhulupirira milungu yotchedwa Pan komanso satyrs yomwe inkakhala ndi chilakolako champhamvu cha chiwerewere ndipo n’kupita kwa nthawi inkasonyezedwa kuti inali ndi nyanga, mchira wa mbuzi komanso miyendo ya mbuzi. Anthu ena amanena kuti maonekedwe angati a nyama a milungu yachikunjayi ndi omwe anachititsa anthu kumajambula Satana ali ndi mchira, nyanga komanso mapazi ogawanika zomwe zinafala kwambiri pakati pa Akhristu m’zaka zapakati pa 500 ndi 1000 C.E.

Mmene “nyama za ubweyazi” (seʽi·rimʹ) zinkaonekera sizifotokozedwa. Ngakhale ena amanena kuti zinali mbuzi zenizeni kapena mafano ooneka ngati mbuzi, palibe pamene pamasonyeza zimenezi, komanso malemba sapereka umboni uliwonse. N’kutheka kuti mawu amene anagwiritsidwa ntchitowa amasonyeza kuti m’maganizo mwa anthu omwe ankalambira milungu yonyengayo ankaona kuti inkaoneka ngati mbuzi kapena inali ndi ubweya. Kapenanso n’kutheka kuti mawu akuti “mbuzi” amene anagwiritsidwa ntchito m’malembawa amangosonyeza kuti mafano onse ndi onyansa, ndipo mawu akuti fano nthawi zambiri amachokera ku mawu omwe amatanthauza kuti “ndowe,” koma sikuti amatanthauza kuti mafanowo amapangidwa kuchokera ku ndowe.—Le 26:30; De 29:17.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

be 69 ¶4-5

Zosankha za Munthu Mwini Ndiponso Nkhani za Chikumbumtima

Pamene wophunzira Baibulo kapena wokhulupirira mnzathu akufunsani zimene ayenera kuchita pankhani inayake, kodi muyenera kuyankha motani? Inuyo mungadziwe zimene mukanachita. Koma munthu aliyense ayenera kuyankha pa zimene angasankhe pamoyo wake. (Agal. 6:5) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti analimbikitsa anthu amene anawalalikira ‘kumvera mwa chikhulupiriro.’ (Aroma 16:26) Tiyenera kutengera chitsanzo chabwino chimenechi. Munthu amene amasankha zochita makamaka pofuna kukondweretsa amene amam’phunzitsa Baibulo kapena munthu aliyense, amatumikira anthu, ndipo sakukhala mwa chikhulupiriro. (Agal. 1:10) Choncho, yankho lapafupi ndi lolunjika lingakhale losam’thandiza kwenikweni wofunsayo.

Nangano mungayankhe motani m’njira yogwirizana ndi malangizo a m’Baibulo? Mungam’fotokozere mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo ndi zitsanzo. Nthawi zina, mungam’sonyeze mmene angafufuzire kuti adzipezere yekha mfundo za makhalidwe abwino ndi zitsanzo zimenezo. Mukhozanso kukambirana mfundo za makhalidwe abwinozo ndi mapindu a zitsanzozo, koma musazigwiritse ntchito pa nkhani imene wafunsayo. Tam’funsani munthuyo ngati akuonapo mbali imene ingam’thandize kusankha chinthu mwanzeru. M’limbikitseni kuti aganize mmene mfundo za makhalidwe abwino ndi zitsanzozo zingam’thandizire kusankha njira imene ingakondweretse Yehova. Mukatero, mudzam’thandiza ‘kuzoloweretsa malingaliro ake kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’—Aheb. 5:14

APRIL 24-30

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 13-16

“Kodi Ndi pa Nthawi Iti Pamene Tiyenera Kudalira Yehova?”

w21.03 5 ¶12

Kodi Achinyamata Mungatani Kuti Anthu Ena Azikudalirani?

12 Mfumu Asa ali wachinyamata anali wodzichepetsa komanso wolimba mtima. Mwachitsanzo, bambo ake Abiya atamwalira, Asa anayamba kulamulira ndipo anayamba kuchotsa mafano onse m’dzikolo. Komanso “anauza Ayuda kuti afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatira Chilamulo.” (2 Mbiri 14:1-7) Ndiponso Zera Mwitiyopiya atabwera kudzamenyana nawo ndi asilikali ake 1 miliyoni, Asa anachita zinthu mwanzeru popempha Yehova kuti awathandize. Iye anati: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu. Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu.” Mawu amenewa akusonyeza kuti Asa ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova awapulumutsa. Choncho Asa ankadalira kwambiri Atate wake wakumwamba ndipo “Yehova anagonjetsa Aitiyopiyawo.”—2 Mbiri 14:8-12.

w21.03 5 ¶13

Kodi Achinyamata Mungatani Kuti Anthu Ena Azikudalirani?

13 Mungavomereze kuti zinali zoopsa kwambiri kwa Asa kuti amenyane ndi gulu la asilikali 1 miliyoni. Koma chifukwa chakuti iye anadalira Yehova anapambana. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti iye atakumana ndi vuto lina lomwe linali laling’ono, sanadalire Yehova. Ataopsezedwa ndi mfumu yoipa ya Isiraeli dzina lake Basa, iye anapempha thandizo kwa mfumu ya Siriya. Zimenezi zinam’bweretsera mavuto aakulu. Kudzera mwa mneneri wake Haneni, Yehova anauza Asa kuti: “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Siriya, osadalira Yehova Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya Siriya lathawa m’manja mwanu.” Ndipotu kuchokera nthawi imeneyo, Asa ankangokhalira kumenya nkhondo. (2 Mbiri 16:7, 9; 1 Maf. 15:32) Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani?

w21.03 6 ¶14

Kodi Achinyamata Mungatani Kuti Anthu Ena Azikudalirani?

14 Pitirizani kukhala odzichepetsa ndipo muzidalira Yehova nthawi zonse. Pamene munabatizidwa, munasonyeza kuti mumadalira komanso kumukhulupirira kwambiri. Ndipo Yehova anasangalala n’kukupatsani mwayi wokhala m’banja lake. Panopa chimene muyenera kuchita ndi kupitirizabe kumudalira. Zingakhale zosavuta kudalira Yehova mukamafuna kusankha zochita pa nkhani zofunika kwambiri pa moyo wanu, koma nanga bwanji pa nkhani zing’onozing’ono? N’zofunika kwambiri kuti muzidalira Yehova mukamasankha zochita pa nkhani zosiyanasiyana kuphatikizapo zosangalatsa, ntchito komanso zolinga zimene muli nazo pa moyo wanu. Musamadalire nzeru zanu. M’malomwake muzifufuza mfundo za m’Baibulo zokhudza zimene mukufuna kusankha ndipo muzichita zinthu mogwirizana ndi malangizowo. (Miy. 3:5, 6) Mukamachita zimenezi mudzasangalatsa mtima wa Yehova ndipo anthu ena mumpingo adzayamba kukulemekezani.—Werengani 1 Timoteyo 4:12.

Mfundo Zothandiza

w17.03 19 ¶7

Tizitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

7 Tonsefe tiyenera kufufuza mtima wathu kuti tione ngati timatumikira Mulungu modzipereka kwambiri. Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndimafunitsitsa kusangalatsa Yehova, kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera komanso kuteteza anthu a Mulungu ku zinthu zoipa?’ Asa anafunikatu kukhala wolimba mtima kuti achotse a Maaka pa udindo wokhala “mayi wa mfumu.” Nthawi zina inunso mungafunike kukhala olimba mtima ngati Asa. Mwachitsanzo, kodi mumatani ngati wachibale kapena mnzanu wapamtima wachita tchimo koma sanalape ndipo wachotsedwa mumpingo? Kodi mungalimbe mtima n’kusiya kuchita naye zinthu? Kodi mtima wanu umakulimbikitsani kutsatira malangizo a Mulungu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena