Zimene mungachite kuti muzipindula kwambiri pophunzira Baibulo
Choyamba kambiranani zimene zili patsamba 2 ndi 3, kenako onerani VIDIYO.
MBALI YOYAMBA
Kuti mukonzekere phunziro lililonse, muziwerenga mbali yoyamba. Cholinga cha mafunso (A) komanso malemba (B) ndi kutsindika mfundo zikuluzikulu. Malemba amene alembedwa kuti “werengani” muziwawerenga mokweza mukamaphunzira ndi mphunzitsi wanu.
MBALI YAPAKATI
Mawu oyamba (C) omwe ali pansi pa kamutu kakuti Fufuzani Mozama akufotokoza mfundo zomwe mukambirane. Mitu ing’onoing’ono (D) ikufotokozera mfundo zazikulu zomwe zili m’phunziro lililonse. Limodzi ndi mphunzitsi wanu, werengani malemba, yankhani mafunso ndi kuonera mavidiyo.
MAVIDIYO ndi ZINTHU ZONGOMVETSERA zikuthandizani kumvetsa bwino mfundo zimene mukuphunzira. Mavidiyo ena akusonyeza zochitika zenizeni. Pamene mavidiyo ena akusonyeza zinthu zongoyerekezera zimene zimachitikadi pa moyo wathu.
Onetsetsani zithunzi ndi mawu ake (E), ndipo ganizirani mmene mungayankhire funso limene lili pambali yakuti Anthu Ena Amanena kuti (F).
MBALI YOMALIZA
Malizani phunziro lililonse pokambirana mbali ya Zomwe Taphunzira komanso Kubwereza (G). Lembani deti limene mwamaliza phunziro. Mbali yakuti Zoti Muchite (H) ikufotokoza zimene mukufunika kuchita kuti mupitirizebe kuphunzira kapena kugwiritsa ntchito zomwe mwaphunzira. Pansi pa mutu wakuti Onani Zinanso (I) pali zinthu zina zomwe mungakonde kuwerenga kapenanso kuonera.
Zimene Zili M’bukuli
|
|
|
|
Mmene mungapezere malemba m’Baibulo
M’Baibulo muli mabuku ang’onoang’ono okwana 66. Linagawidwa mbali ziwiri: Malemba a chiheberi ndi Chiaramu (“Chipangano Chakale”) ndiponso Malemba a Chigiriki (“Chipangano Chatsopano”).
Malemba omwe ali m’bukuli akuyamba ndi dzina la buku la m’Baibulo (A), chaputala (B), kenako vesi kapena mavesi (C).
Mwachitsanzo, Yohane 17:3 akutanthauza buku la Yohane, chaputala 17 vesi 3.