-
Kodi Yehova Adzakukumbukirani Motani?Nsanja ya Olonda—2000 | February 1
-
-
Kodi Yehova Adzakukumbukirani Motani?
“MUNDIKUMBUKIRE, Mulungu wanga.” Kwa maulendo angapo Nehemiya anapempha Mulungu m’mawu amenewo. (Nehemiya 5:19; 13:14, 31) N’kwachibadwa kuti pamene anthu ali m’vuto lalikulu, amatembenukira kwa Mulungu ndi mawu odandaula ngati amenewo.
Koma, kodi anthu amalingalira chiyani pamene akupempha Mulungu kuti awakumbukire? Mwachionekere, iwo amayembekezera Mulungu kuwachitira zoposa kungokumbukira mayina awo. Mosakayikira iwo amayembekezera mofanana ndi momwe anachitira mmodzi wa apandu omwe anaphedwa pamodzi ndi Yesu. Mpandu ameneyu, mosiyana ndi winayo, anachonderera Yesu kuti: “Ndikumbukireni mmene muloŵa Ufumu wanu.” Anafuna kuti Yesu asangomukumbukira chabe kuti iye anali yani koma kum’chitira kanthu kenakake, kumuukitsa.—Luka 23:42.
Nthaŵi zonse, Baibulo limasonyeza kuti kwa Mulungu, “kukumbukira” kumatanthauza kuchitapo kanthu motsimikiza. Mwachitsanzo, dziko lapansi litamizidwa ndi chigumula kwa masiku 150, “Mulungu anakumbukira Nowa . . . , ndipo Mulungu anapititsa mphepo pa dziko lapansi, naphwa madzi.” (Genesis 8:1) Zaka mazana angapo pambuyo pake, Samsoni, atachititsidwa khungu komanso kumangidwa ndi Afilisti, anapemphera kuti: “Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthaŵi ino yokha.” Yehova anam’kumbukira Samsoni mwa kum’patsa mphamvu zoposa zaumunthu kotero kuti athe kubwezera yekha chilango pa adani a Mulungu. (Oweruza 16:28-30) Ponena za Nehemiya, Yehova anadalitsa zoyesayesa zake, ndipo kulambira koona kunabwezeretsedwa m’Yerusalemu.
“Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo,” analemba motero mtumwi Paulo. (Aroma 15:4) Ngati tikumbukira Yehova mwa kufuna kuchita chifuno chake, monga momwe anachitira atumiki ake okhulupirika m’mbuyomo, tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzatikumbukira mwa kutithandiza kupeza zofuna zathu za tsiku ndi tsiku, mwa kutichirikiza m’mayesero athu, ndiponso mwa kutipulumutsa pamene adzadzetsa chiweruzo pa anthu opanda umulungu.—Mateyu 6:33; 2 Petro 2:9.
-
-
Kodi Mungafune Kukuchezerani?Nsanja ya Olonda—2000 | February 1
-
-
Kodi Mungafune Kukuchezerani?
Ngakhale m’dziko lino lodzala ndi mavuto, mungapeze chimwemwe mwa kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chonena za Mulungu, Ufumu wake, ndi chifuniro chake chabwino kwambiri kwa anthu. Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 30.
-