Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mungakhulupirire Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—1993 | June 15
    • Kodi Mungakhulupirire Baibulo?

      NGATI mutanyamula Baibulo, kodi mungayembekeze kupeza kobiri? Bwanji ponena za kobiri lasiliva lamakedzanali?

      Ambiri amawona Baibulo kukhala buku lachikale lokhala ndi nkhani zachilendo ndi makhalidwe osiririka. Komabe, samakhulupirira kuti Baibulo lili ndi mbiri yolondola, chotero amakana kuti siliri Mawu a Mulungu. Komabe, pali umboni wokwanira wosonyeza kulondola kwa Baibulo. Kobiri ili (m’chithunzi chachikulu) lili chitsanzo chabwino. Kodi malembowo akuti bwanji?

      Kobirilo linasulidwa ku Tariso, mzinda wa kum’mwera koma chakum’maŵa kwa mbali yomwe tsopano ili Turkey. Kobirili linasulidwa muulamuliro wa kazembe Mazaeus wa ku Perisiya m’zaka za zana lachinayi B.C.E. Ilo limatchula iye kukhala kazembe wa dera la “Tsidya la Mtsinje,” kutanthauza mtsinje wa Firate.

      Koma kodi nchifukwa ninji mawuwo ali okondweretsa? Chifukwa chakuti mudzapeza mawu ofananawo m’Baibulo lanu. Lemba la Ezara 5:6–6:13 limanena za kulemberana makalata kwa pakati pa Mfumu Dariyo ya Perisiya ndi kazembe wotchedwa Tatinai. Nkhani yake inali yonena za kumanganso kachisi wa ku Yerusalemu kwa Ayuda. Ezara anali mlembi waluntha m’Chilamulo cha Mulungu, ndipo mungamuyembekezere kukhala wachindunji, ndi wolondola m’zimene analemba. Mudzawona pa lemba la Ezara 5:6 ndi 6:13 kuti anatcha Tatinai kukhala “kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo.”

      Ezara analemba zimenezo pafupifupi mu 460 B.C.E., zaka 100 kobirilo lisanasulidwe. Inde, pali anthu ena amene angaganize kuti kutchulidwa kwa nduna yaboma yamakedzanako kulibe ntchito. Koma ngati mungakhulupirire olemba Baibulo pankhani zazing’ono choncho, kodi zimenezi siziyenera kuwonjezera chikhulupiriro chanu m’zinthu zinanso zimene analemba?

      M’nkhani ziŵiri zoyambirira za m’kope lino, mudzapeza zifukwa zowonjezereka zokhalira ndi chikhulupiriro chimenecho.

  • Kodi Mungakonde Kuchezeredwa?
    Nsanja ya Olonda—1993 | June 15
    • Kodi Mungakonde Kuchezeredwa?

      Ngakhale m’dziko lino lodzala ndi mavuto, mungakhoze kupeza chimwemwe kuchokera m’chidziwitso cholongosoka cha Baibulo chonena za Mulungu, Ufumu wake, ndi chifuno chake chabwino kwambiri kwa anthu. Ngati mungafune chidziŵitso chowonjezereka kapena ngati mungakonde kuti wina adze kudzachita nanu phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera pandandanda ya patsamba 2.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena