PHUNZIRO 58
Pitirizani Kukhala Wokhulupirika kwa Yehova
Akhristu enieni salola kuti munthu kapena chinthu chilichonse chiwalepheretse kulambira Yehova. Sitikukayikira kuti nanunso mumaona choncho. Yehova amasangalala kwambiri akamaona kuti mukupitiriza kukhala wokhulupirika kwa iye. (Werengani 1 Mbiri 28:9.) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingakulepheretseni kukhala wokhulupirika kwa Yehova? Nanga n’chiyani chingakuthandizeni kuti musasiye kukhala wokhulupirika kwa Yehova?
1. Kodi anthu ena angachititse bwanji kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova?
Anthu ena amafuna titasiya kutumikira Yehova. Kodi anthu amenewa angakhale ndani? Anthu ena amene anasiya kutumikira Yehova amanena mabodza okhudza gulu la Mulungu n’cholinga choti ifenso tisiye kutumikira Yehova. Anthu amenewa amatchedwa ampatuko. Komanso atsogoleri ena azipembedzo amafalitsa mabodza n’cholinga chofuna kusokoneza anthu omwe amangotengeka ndi zilizonse kuti asiye kutumikira Yehova. Tiyenera kupeweratu kutsutsana ndi anthu ampatuko, kuwerenga mabuku awo kapena zimene amalemba pa intaneti, kutsegula mawebusaiti awo kapenanso kuonera mavidiyo awo. Ponena za anthu amene amachititsa ena kuti asiye kutumikira Yehova mokhulupirika, Yesu anati: “Asiyeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Choncho ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.”—Mateyu 15:14.
2. Kodi zimene timasankha pa moyo wathu zingachititse bwanji kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova?
Ngati timakonda Yehova tidzapewa kuchita chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo chabodza. Tidzapewa kukhala kapena kugwira ntchito m’gulu linalake lachipembedzo kapenanso kuchita chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo chabodza. Yehova amatichenjeza kuti: “Tulukani [mu Babulo Wamkulu] anthu anga.”—Chivumbulutso 18:2, 4.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene mungachite kuti aliyense asakulepheretseni kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Muonanso mmene mungasonyezere kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova potuluka mu Babulo Wamkulu.
3. Samalani ndi aphunzitsi abodza
Kodi tiyenera kutani tikamva ena akunena zinthu zoipa zokhudza gulu la Yehova? Werengani Miyambo 14:15, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kuti tisamangokhulupirira zilizonse zimene tamva?
Werengani 2 Yohane 9-11, kenako mukambirane mafunso awa:
Malinga ndi lembali, kodi tizitani ndi anthu ampatuko?
Ngakhale kuti sitingacheze mwachindunji ndi anthu ampatuko, kodi tingasokonezedwe bwanji ndi zimene amaphunzitsa?
Kodi mukuganiza kuti Yehova angamve bwanji tikamamvetsera zinthu zabodza zokhudza iyeyo kapenanso gulu lake?
4. Muzikhalabe wokhulupirika kwa Yehova munthu wina akachita tchimo
Kodi tiyenera kuchita chiyani tikadziwa kuti munthu wina mumpingo wachita tchimo lalikulu? Onani mfundo yomwe ikupezeka m’Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli. Werengani Levitiko 5:1.
Mogwirizana ndi vesili, tikadziwa kuti munthu wina wachita tchimo lalikulu, tiyenera kuuza akulu zimene tikudziwa pa nkhaniyo. Komabe tisanachite zimenezi, tiyenera kuuza munthu wochimwayo kuti akaulule yekha kwa akulu za tchimo lakelo. Ndiyeno akalephera kuchita zimenezi, ifeyo tiyenera kusonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova pokanena kwa akulu. Kodi tikachita zimenezi timasonyeza bwanji kuti tili ndi chikondi chokhulupirika kwa . . .
Yehova Mulungu?
munthu yemwe wachimwayo?
anthu ena onse mumpingo?
Ngati Mkhristu mnzanu wachita zoipa, muyenera kumuthandiza
5. Tulukani mu Babulo Wamkulu
Werengani Luka 4:8 ndi Chivumbulutso 18:4, 5, kenako muyankhe mafunso awa:
Kodi sindinafufutitse dzina langa kuchipembedzo chabodza?
Kodi ndili m’bungwe limene limachita zinthu zogwirizana ndi chipembedzo chinachake?
Kodi ntchito imene ndimagwira imathandizira zochita za chipembedzo chabodza?
Kodi pali zinthu zinanso zimene ndingachite kuti ndisiyiretu kuchita zinthu zogwirizana ndi chipembedzo chabodza?
Ngati funso linalake ndaliyankha kuti inde, kodi ndiyenera kusintha zinthu ziti?
Pa zinthu zonse zomwe takambiranazi muzionetsetsa kuti zomwe mungasankhe zizikuthandizani kukhala ndi chikumbumtima choyera komanso zizisonyeza kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova.
Kodi mungatani mutapemphedwa kuti mupereke ndalama zothandizira pa ntchito zachifundo za chipembedzo chinachake?
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Ndikufunika kudziwa zimene ampatuko amanena zokhudza Mboni za Yehova kuti nditeteze choonadi.”
Kodi mukuona kuti ndi nzeru kuchita zimenezi? N’chifukwa chiyani mukutero?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Kuti tipitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova tiyenera kupewa kugwirizana ndi anthu amene amafuna kutisocheretsa.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani sitiyenera kumvetsera zimene ampatuko amaphunzitsa?
Ngati tadziwa kuti m’bale kapena mlongo wachita tchimo lalikulu, kodi tiyenera kuchita chiyani?
Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikumvera chenjezo lakuti tituluke m’chipembedzo chabodza?
ONANI ZINANSO
Onani zimene mukuyenera kuchita anthu ena akamanena zinthu zabodza zokhudza Mboni za Yehova.
“Kodi Mukudziwa Nkhani Yonse?” (Nsanja ya Olonda, August 2018)
Kodi mungadziwe bwanji kuti mabungwe kapena zinthu zinazake zikugwirizana ndi Babulo Wamkulu?
Kodi ndi zinthu ziti zimene anthu ena otsutsa achita pofuna kufooketsa chikhulupiriro chathu?
Munkhani yakuti, “Kuyambira Ndili Mwana Ndinkafunitsitsa Kudziwa Mulungu,” werengani nkhani ya wansembe wachipembedzo cha Chishinto yemwe anatuluka m’chipembedzo chabodza.