-
Yesu Anagwiritsa Ntchito Mtengo wa Mkuyu Pophunzitsa Anthu za ChikhulupiriroYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 105
Yesu Anagwiritsa Ntchito Mtengo wa Mkuyu Pophunzitsa Anthu za Chikhulupiriro
MATEYU 21:19-27 MALIKO 11:19-33 LUKA 20:1-8
ANAPHUNZIRA KUFUNIKA KOKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO CHIFUKWA CHA MTENGO WA MKUYU UMENE UNAFOTA
ANTHU ANAFUNSA YESU KUMENE ANKATENGA ULAMULIRO WOCHITIRA ZINTHU
Lolemba masana Yesu anachoka ku Yerusalemu n’kubwerera ku Betaniya, mzinda womwe unali m’mphepete mwa phiri la Maolivi chakum’mawa. Mosakayikira anakagona kunyumba kwa Lazaro, Mariya ndi Marita omwe anali anzake.
Tsiku lotsatira pa Nisani 11 m’mawa, Yesu ndi ophunzira ake anayambanso ulendo wopita ku Yerusalemu kukachisi. Kameneka kanali komaliza kuti Yesu akapezeke pakachisi komanso linali tsiku lake lomaliza kuti alalikire poyera. Kenako patapita masiku ochepa anachita mwambo wa Pasika, anakhazikitsa mwambo wokumbukira imfa yake, anaimbidwa mlandu ndipo pamapeto pake anaphedwa.
Ali m’njira popita ku Yerusalemu, Petulo anaona mtengo womwe Yesu anautemberera chadzulo lake ndipo ananena kuti: “Rabi, onani! mkuyu umene munautemberera uja wafota.”—Maliko 11:21.
Koma n’chifukwa chiyani Yesu anachititsa kuti mtengowu ufote? Zimene Yesu ananena zimatithandiza kudziwa yankho la funso limeneli. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro, osakayika, mudzatha kuchita zimene ndachitira mkuyu umenewu. Komanso kuposa pamenepa, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano ukadziponye m’nyanja,’ ndipo zidzachitikadi. Chinthu chilichonse chimene mudzapempha m’mapemphero anu, mudzalandira ngati muli ndi chikhulupiriro.” (Mateyu 21:21, 22) Pamenepa Yesu ankabwereza mfundo imene anali atanenapo kale m’mbuyomu kuti ngati munthu atakhala ndi chikhulupiriro akhoza kusuntha phiri.—Mateyu 17:20.
Choncho pamene Yesu anachititsa kuti mtengowo ufote, anaphunzitsa anthu za kufunika kokhulupirira Mulungu. Iye ananenanso kuti: “Pa zinthu zonse zimene mukupempherera ndi kupempha, khalani ndi chikhulupiriro ngati kuti mwazilandira kale, ndipo mudzazilandiradi.” (Maliko 11:24) Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri kwa anthu onse amene amatsatira Yesu. Inalinso yothandiza kwambiri kwa atumwi amene anali atatsala pang’ono kukumana ndi mavuto aakulu. Zimene Yesu anachita pochititsa kuti mtengowo ufote zinasonyezanso kufunika kokhala ndi chikhulupiriro champhamvu.
Mofanana ndi mmene mtengo wamkuyu uja unkaonekera, ndi mmenenso mtundu wa Isiraeli unalili. Aisiraeli anachita pangano ndi Mulungu ndipo zinkaoneka ngati ankatsatira Chilamulo. Koma mtundu umenewu unalibe chikhulupiriro ndiponso sunkabala zipatso zabwino. Iwo anafika mpaka pokana Mwana wa Mulungu. Choncho pamene Yesu anachititsa kuti mtengo wa mkuyu umene sunkabala zipatso uja ufote, anasonyeza zimene zidzachitikire mtunduwu womwe unalibe chikhulupiriro komanso umene sunkabala zipatso.
Pasanapite nthawi yaitali, Yesu ndi ophunzira ake anafika ku Yerusalemu. Monga mwa chizolowezi chake Yesu anakalowa m’kachisi n’kuyamba kuphunzitsa. Ansembe aakulu komanso akulu atakumbukira zimene Yesu anachitira anthu osintha ndalama chadzulo lake, anamufunsa kuti: “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndani anakupatsani ulamuliro umenewu?”—Maliko 11:28.
Yesu anayankha kuti: “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo inenso ndikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zinthu zimenezi. Kodi ubatizo wa Yohane unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu? Ndiyankheni.” Yesu atawafunsa zimenezi nkhani inawatembenukira. Ansembe komanso akulu anayamba kukambirana zoti amuyankhe. Iwo ankafunsana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye anena kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ Koma nanga tinganene kuti ‘Unachokera kwa anthu’ ngati?” . . . Anali kuopa khamu la anthu, chifukwa anthu onsewo anali kukhulupirira kuti Yohane analidi mneneri.”—Maliko 11:29-32.
Anthu amene ankatsutsa Yesu analephera kupeza yankho lolondola moti anangomuyankha kuti: “Sitikudziwa.” Nayenso Yesu powayankha ananena kuti: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”—Maliko 11:33.
-
-
Mafanizo Awiri Onena za Munda wa MpesaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 106
Mafanizo Awiri Onena za Munda wa Mpesa
MATEYU 21:28-46 MALIKO 12:1-12 LUKA 20:9-19
FANIZO LONENA ZA ANA AWIRI
FANIZO LA ALIMI OSAMALIRA MUNDA WA MPESA
Ali kukachisi Yesu anasokoneza ansembe aakulu ndi akulu amene anamufunsa kuti awauze kumene ankatenga ulamuliro umene ankachitira zinthu. Zimene anawayankha zinawasowetsa chonena. Kenako Yesu ananena fanizo limene linasonyeza kuti ansembe aakulu ndi akuluwo anali anthu otani.
Iye anati: “Munthu wina anali ndi ana awiri. Ndipo anapita kwa mwana woyamba n’kumuuza kuti: ‘Mwana wanga, lero upite kukagwira ntchito m’munda wa mpesa.’ Iye poyankha anati, ‘Ndipita bambo,’ koma sanapite. Kenako anapita kwa mwana wachiwiri uja n’kumuuzanso chimodzimodzi. Iye poyankha anati, ‘Ayi sindipita.’ Koma pambuyo pake anamva chisoni ndipo anapita. Ndani mwa ana awiriwa amene anachita chifuniro cha bambo ake?” (Mateyu 21:28-31) Anthuwa sanavutike kupeza yankho la funsoli. Mwana wachiwiri ndi amene pomaliza anachita zimene bambo ake ankafuna.
Ndiyeno Yesu anauza anthu amene ankamutsutsawo kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti okhometsa msonkho ndi mahule akukusiyani m’mbuyo n’kukalowa mu ufumu wa Mulungu.” Poyamba okhometsa msonkho komanso mahule sankatumikira Mulungu. Koma kenako anthu amenewa analapa ndipo anayamba kutumikira Mulungu. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene mwana wachiwiri uja anachita. Koma atsogoleri achipembedzo anali ngati mwana woyamba uja. Iwo ankaoneka ngati ankatumikira Mulungu koma zoona zake n’zoti sankamutumikira. Yesu ananena kuti: “Pakuti Yohane [M’batizi] anabwera kwa inu m’njira yachilungamo, koma inu simunam’khulupirire. Koma okhometsa msonkho ndi mahule anam’khulupirira, Ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunamve chisoni n’kusintha maganizo anu kuti mum’khulupirire.”—Mateyu 21:31, 32.
Yesu atamaliza kunena fanizo limeneli ananenanso fanizo lina. Ananena fanizo lachiwirili pofuna kusonyeza kuti atsogoleri achipembedzo sankafuna kutumikira Mulungu komanso kuti anali anthu oipa. Iye ananena kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa ndi kumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa, ndi kumanga nsanja. Atatero anausiya m’manja mwa alimi n’kupita kudziko lina. Tsopano nyengo ya zipatso itakwana, iye anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akam’patseko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo. Koma iwo anam’gwira, n’kumumenya ndi kum’bweza chimanjamanja. Iye anatumizanso kapolo wina kwa iwo koma ameneyu anamutema m’mutu ndi kumuchitira zachipongwe. Anatumizanso wina, koma ameneyo anamupha. Ndiyeno anatumizanso akapolo ena ambiri. Ena mwa iwo anawamenya ndipo ena anawapha.”—Maliko 12:1-5.
Kodi anthu amene ankamva Yesu akunena fanizo limeneli anamvetsa tanthauzo lake? N’kutheka kuti anthuwo anakumbukira mawu amene Yesaya analemba akuti: “Ine ndine Yehova wa makamu ndipo Isiraeli ndi munda wanga wa mpesa. Amuna a ku Yuda ndiwo mitengo ya mpesa imene ndinali kuikonda. Ine ndinali kuyembekezera chilungamo koma ndinaona anthu akuphwanya malamulo.” (Yesaya 5:7) Anthu komanso zinthu zimene Yesu anatchula m’fanizoli ndi zofanana ndi zimene Yesaya ananena. Tikutero chifukwa mwiniwake wa mundawo ndi Yehova ndipo munda wa mpesa ndi mtundu wa Aisiraeli, womwe unkatetezedwa ndi Chilamulo cha Mulungu. Yehova ankatumiza aneneri kuti azilangiza anthu ake komanso kuwathandiza kuti azibala zipatso zabwino.
Koma ‘alimiwo’ anazunza komanso kupha “akapolo” amene mwinimunda uja anawatuma. Yesu anapitiriza kufotokoza kuti: “Tsopano [mwiniwake wa mundawo] anatsala ndi mmodzi yekha, mwana wake wokondedwa. Anatumizanso mwanayo kwa iwo ngati wotsirizira, n’kunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ Koma alimiwo anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa. Bwerani, tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ Choncho anamugwira n’kumupha.”—Maliko 12:6-8.
Kenako Yesu anawafunsa anthuwo kuti: “Kodi mwinimunda wa mpesawo adzachita chiyani?” (Maliko 12:9) Atsogoleri achipembedzowo anayankha kuti: “Chifukwa chakuti ndi oipa, adzawawononga koopsa ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa alimi ena, amene angam’patse zipatso m’nyengo yake.”—Mateyu 21:41.
Ponena mawu amenewa, atsogoleri achipembedzowa anadziweruza okha mosadziwa chifukwa iwo anali m’gulu la “alimi” ogwira ntchito ‘m’munda wa mpesa’ wa Yehova, womwe unkaimira mtundu wa Isiraeli. Chimodzi mwa zipatso zimene Yehova ankayembekezera kwa alimiwo chinali choti azikhulupirira Mwana wake, yemwenso ndi Mesiya. Yesu anayang’ana atsogoleri achipembedzowo n’kunena kuti: “Kodi simunawerengepo lemba limene limati, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana, umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri’? Kodi simunawerenge kuti ‘Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’?” (Maliko 12:10, 11) Kenako Yesu ananena mfundo imene ankafuna kuti anthuwo amvetse. Iye anati: “Ichi n’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu n’kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.”—Mateyu 21:43.
Alembi komanso ansembe aakulu anazindikira kuti Yesu “anali kunena za iwo mufanizolo.” (Luka 20:19) Pa nthawi imeneyi anthuwo anafunitsitsa kupha Yesu, yemwe anali “wolandira cholowa.” Koma sanamuphe chifukwa ankaopa gulu la anthu, lomwe linkaona kuti Yesu ndi mneneri.
-
-
Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la UkwatiYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 107
Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la Ukwati
FANIZO LA PHWANDO LA UKWATI
Yesu atatsala pang’ono kumaliza utumiki wake anapitirizabe kugwiritsa ntchito mafanizo pofuna kuti anthu onse adziwe zimene alembi komanso ansembe aakulu ankachita. Chifukwa cha zimenezi, alembi komanso ansembe aakuluwo ankafuna kumupha. (Luka 20:19) Koma Yesu anafotokozanso fanizo lina. Iye anati:
“Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati wa mwana wake. Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa ku phwando laukwati, koma anthuwo sanafune kubwera.” (Mateyu 22:2, 3) Yesu anayamba kufotokoza fanizoli ndi mawu akuti “Ufumu wakumwamba.” Ndiye kuti “mfumu” ya m’fanizoli ndi Yehova Mulungu. Nanga mwana wa mfumuyo komanso anthu amene anaitanidwa ku phwando laukwati ndi ndani? Pamenepanso n’zosavuta kuzindikira kuti mwana wa mfumuyo ndi Mwana wa Yehova, amene ankanena fanizoli ndipo amene anaitanidwawo ndi anthu amene adzalamulire ndi Mwanayo mu Ufumu wakumwamba.
Kodi ndani amene anali oyamba kuitanidwa? Ayenera kuti anali Ayuda chifukwa ndi amene Yesu ndi atumwi ankawalalikira za Ufumu. (Mateyu 10:6, 7; 15:24) Mu 1513 B.C.E., Ayudawo anapanga pangano ndi Mulungu ndipo anavomereza kuti adzatsatira Chilamulo chimene anawapatsa. Choncho Ayuda anali anthu oyambirira kupanga “ufumu wa ansembe.” (Ekisodo 19:5-8) Koma kodi anaitanidwa liti ku “phwando la ukwati?” Anayamba kuitanidwa mu 29 C.E. pamene Yesu anayamba kulalikira za Ufumu wakumwamba.
Kodi Aisiraeli ambiri anatani ataitanidwa? Yesu ananena kuti “anthuwo sanafune kubwera.” Atsogoleri achipembedzo komanso anthu ambiri sanavomereze kuti Yesu anali Mesiya komanso Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu.
Koma Yesu anasonyeza kuti Ayudawo adzapatsidwanso mwayi wina. Iye anati: “Kenako inatumanso akapolo ena kuti, ‘Kauzeni oitanidwawo kuti: “Ine ndakonza chakudya chamasana, ng’ombe zanga komanso nyama zanga zonenepa zaphedwa, ndipo zinthu zonse zakonzedwa kale. Bwerani ku phwando laukwati.”’ Koma anthuwo ananyalanyaza ndi kuchoka. Wina anapita kumunda wake, wina kumalonda ake. Koma enawo anagwira akapolo akewo, ndi kuwachitira zachipongwe n’kuwapha.” (Mateyu 22:4-6) Ndipo zimenezi ndi zimene zinachitika mpingo wachikhristu utangokhazikitsidwa kumene. Nthawi imeneyi, Ayuda anali ndi mwayi wolowa nawo mu Ufumu koma ambiri anakana mwayi umenewu mpaka kufika pozunza ‘akapolo a mfumu.’—Machitidwe 4:13-18; 7:54, 58.
Kodi mtunduwu unakumana ndi zotani chifukwa chochita zimenezi? Yesu ananena kuti: “Pamenepo mfumu ija inakwiya kwambiri, ndipo inatumiza asilikali ake kukawononga opha anthu amenewo ndi kutentha mzinda wawo.” (Mateyu 22:7) Zimenezi zinachitika mu 70 C.E. pamene Aroma anawononga “mzinda [wa Ayuda]” wa Yerusalemu.
Chifukwa chakuti Ayuda anakana mfumu itawaitana, ndiye kuti palibe aliyense amene akanaitanidwa? Ayi. Tikutero chifukwa fanizo la Yesu limapitiriza kuti: “Kenako [mfumu] anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzedwa ndithu, koma oitanidwa aja anali osayenera. Chotero pitani m’misewu yotuluka mumzinda, ndipo aliyense amene mukam’peze, mukamuitanire phwando laukwatili.’ Choncho akapolowo anapita m’misewu ndi kusonkhanitsa onse amene anawapeza, oipa ndi abwino omwe. Ndipo chipinda chodyeramo phwando laukwati chinadzaza ndi anthu oyembekezera kulandira chakudya.”—Mateyu 22:8-10.
Izi zinayamba kuchitika pamene mtumwi Petulo anayamba kuthandiza anthu a mitundu ina, omwe sanali Ayuda komanso amene sanatembenukire ku Chiyuda, kuti nawonso akhale Akhristu. Mwachitsanzo mu 36 C.E., Koneliyo, yemwe anali kapitawo wa gulu la asilikali achiroma, ndi anthu a m’banja lake analandira mzimu wa Mulungu. Zimenezi zinawapatsa mwayi wolowa mu Ufumu wakumwamba umene Yesu ananena.—Machitidwe 10:1, 34-48.
Fanizo la Yesu linasonyezanso kuti si onse amene anabwera ku phwandolo omwe “mfumu” inawavomereza. Yesu anati: “Pamene mfumu ija inalowa kukayendera alendowo, inaona munthu wina mmenemo amene sanavale chovala chaukwati. Chotero inamufunsa kuti, ‘Bwanawe! Walowa bwanji muno usanavale chovala cha ukwati?’ Iye anasowa chonena. Kenako mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘M’mangeni manja ndi miyendo ndipo mum’ponye kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’ “Pakuti oitanidwa ndi ambiri, koma osankhidwa ndi owerengeka.”—Mateyu 22:11-14.
N’kutheka kuti atsogoleri achipembedzo amene anamva Yesu akunena zimenezi sanamvetse zimene ankatanthauza. Komabe anthuwa anakwiya kwambiri ndipo anatsimikiza kuti athane ndi Yesu chifukwa ankawachititsa manyazi.
-
-
Yesu Analepheretsa Afarisi Kuti AmugwireYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 108
Yesu Analepheretsa Afarisi Kuti Amugwire
MATEYU 22:15-40 MALIKO 12:13-34 LUKA 20:20-40
PEREKANI ZA KAISARA KWA KAISARA
KODI ANTHU AMENE ADZAUKITSIDWE ADZAKWATIRA KAPENA KUKWATIWANSO?
MALAMULO AKULUAKULU
Atsogoleri achipembedzo anakwiya kwambiri ndi Yesu chifukwa ananena mafanizo omwe anasonyeza kuti atsogoleriwo anali anthu oipa kwambiri. Afarisi anagwirizana zoti amugwire. Iwo anapangana zoti Yesu akalankhula zinazake amugwire n’kukamupereka kwa wolamulira wachiroma moti anapatsa ndalama ena mwa ophunzira awo kuti akamugwire.—Luka 6:7.
Ophunzira a Afarisiwo anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti mumanena ndi kuphunzitsa molondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. Kodi n’kololeka kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” (Luka 20:21, 22) Yesu sanapusitsike ndi funso lawo lachinyengolo. Ngati Yesu akanayankha kuti, ‘Ayi, sikololeka kupereka msonkho,’ akanaimbidwa mlandu woukira boma la Aroma. Komanso ngati akanayankha kuti, ‘Inde, muzikhoma msonkho,’ anthu omwe ankadana ndi ulamuliro wa Aroma akanaganiza kuti Yesu ali ku mbali ya Aroma ndipo akanamuukira. Ndiye kodi Yesu anawayankha bwanji?
Iye ananena kuti: “Onyenga inu! Bwanji mukundiyesa? Ndionetseni khobidi la msonkho.” Pamenepo anam’bweretsera khobidi limodzi la dinari. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi ndi mawu akewa n’zandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” Pamenepo iye anawauza kuti: “Ndiye perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”—Mateyu 22:18-21.
Anthuwo anagoma kwambiri ndi zimene Yesu anawayankha moti anasowa chonena n’kungochokapo. Ichi chinali chiyambi chabe chifukwa anthu aja atalephera kumukola, panabweranso gulu la atsogoleri achipembedzo kudzamuyesa.
Asaduki omwe sankakhulupirira kuti anthu omwe anamwalira adzauka, anafunsa Yesu funso lokhudza za kuuka kwa akufa komanso za ukwati wa pachilamu. Iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, Mose anati, ‘Ngati munthu wamwalira wopanda ana, m’bale wake ayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana.’ Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira kenako n’kumwalira. Koma popeza kuti analibe ana, mkazi uja anakwatiwa ndi m’bale wa mwamuna wake. Zinachitika chimodzimodzi kwa wachiwiri ndi wachitatu, mpaka kwa onse 7 aja.Pamapeto pake mkaziyo nayenso anamwalira. Kodi pamenepa, pouka kwa akufa, mkazi ameneyu adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatira?”—Mateyu 22:24-28.
Poyankha Asadukiwo, Yesu anagwiritsa ntchito mawu amene Mose analemba omwenso Asadukiwo ankawakhulupirira. Iye ananena kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu? Akadzauka kwa akufa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba. Koma zakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge m’buku la Mose, m’nkhani ya chitsamba chaminga, mmene Mulungu anamuuzira kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’? Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.” (Maliko 12:24-27; Ekisodo 3:1-6) Gulu la anthulo linadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anawayankha.
Yesu anasowetsa chonena Afarisi ndi Asaduki, kenako magulu awiriwa anapanga gulu limodzi ndipo anapitanso kwa Yesu kuti akamuyese. Mlembi wina pa gululo anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?”—Mateyu 22:36.
Yesu anayankha kuti: “Loyamba n’lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi. Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.’ Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ Kulibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.”—Maliko 12:29-31.
Mlembiyo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi, ndipo palibenso wina, koma Iye yekha.’ Kunena za kukonda Mulungu ndi mtima wonse, maganizo onse, mphamvu zonse, komanso kukonda mnzako mmene umadzikondera wekha, n’zofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.” Pamenepo Yesu, pozindikira kuti mlembiyo wayankha mwanzeru anamuuza kuti: “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.”—Maliko 12:32-34.
Kwa masiku atatu, kuyambira pa Nisani 9, 10 ndi 11, Yesu anakhala akuphunzitsa m’kachisi. Anthu ena anasangalala kumva zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo m’modzi mwa anthuwo anali mlembiyu. Koma atsogoleri achipembedzo sanasangalale naye moti palibe amene “analimba mtima kumufunsanso.”
-
-
Anadzudzula Atsogoleri Achipembedzo Omwe AnkamutsutsaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 109
Anadzudzula Atsogoleri Achipembedzo Omwe Ankamutsutsa
MATEYU 22:41–23:24 MALIKO 12:35-40 LUKA 20:41-47
KODI KHRISTU NDI MWANA WA NDANI?
YESU ANANENA POYERA KUTI ANTHU AMENE ANKAMUTSUTSA ANALI ACHINYENGO
Atsogoleri achipembedzo analephera kuchititsa Yesu manyazi komanso analephera kumugwira kuti akamupereke kwa Aroma. (Luka 20:20) Ndiyeno pa Nisani 11, Yesu ali kukachisi anthu omwe ankamutsutsa anabwera kuti adzamukole mawu koma zinthu zinatembenuka. Yesu ndi amene anayamba kuwapanikiza ndipo ananena poyera kuti iyeyo ndi Mesiya. Iye anawafunsa kuti: “Mukuganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” (Mateyu 22:42) Anthu ankadziwa kuti Khristu kapena kuti Mesiya adzachokera mumzera wa Davide ndipo ndi zimene anthuwo anayankha Yesu.—Mateyu 9:27; 12:23; Yohane 7:42.
Yesu anawafunsanso kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani mouziridwa ndi mzimu, Davide anamutcha ‘Ambuye,’ muja anati, ‘Yehova wauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako”’? Chotero ngati Davide anamutcha kuti ‘Ambuye,’ akukhala bwanji mwana wake?”—Mateyu 22:43-45.
Afarisiwo sanayankhe chifukwa ankayembekezera kuti munthu wochokera mumzera wa Davide ndi amene adzawalanditse ku ulamuliro wa Aroma. Ndiyeno Yesu anagwiritsa ntchito mawu amene Davide ananena pa Salimo 110:1, 2 pofuna kusonyeza kuti Mesiya sadzakhala wolamulira wamba. Yesu anafotokoza kuti Mesiya ndi Mbuye wa Davide ndipo adzayamba kugwiritsa ntchito mphamvu zake akadzakhala kudzanja lamanja la Mulungu. Zimene Yesu anawayankha zinawasowetsa chonena.
Pa nthawi imene Yesu ankalankhula zimenezi, ophunzira ake komanso anthu ena ankangomvetsera. Ndiyeno Yesu anayamba kulankhula nawo ndipo anawachenjeza za alembi ndi Afarisi. Yesu anawauza kuti anthu amenewa “adzikhazika pampando wa Mose” kuti aziphunzitsa anthu Chilamulo cha Mulungu. Yesu anauza anthuwo kuti: “Muzichita ndi kutsatira zilizonse zimene angakuuzeni, koma musamachite zimene iwo amachita, chifukwa iwo amangonena koma osachita.”—Mateyu 23:2, 3.
Kenako Yesu anafotokoza zinthu zomwe zinasonyeza kuti alembi ndi Afarisi anali achinyengo. Iye anati: “Iwo amakulitsa timapukusi tokhala ndi malemba timene amavala monga zodzitetezera.” Ayuda ena ankavala timapukusi tomwe tinkaoneka ngati kabokosi kakang’ono pachipumi kapena padzanja ndipo tinkakhala ndi mawu a m’Chilamulo. Koma Afarisi ankavala timapukusi tatikulu kuposa timeneti pofuna kusonyeza anthu kuti iwo anali odzipereka kwambiri potsatira Chilamulo. Afarisiwa ‘ankakulitsanso ulusi wopota wa m’mphepete mwa zovala zawo.’ Aisiraeli ankafunika kuika ulusi wopota m’mphepete mwa zovala zawo, koma Afarisi ankawonetsetsa kuti ulusi wa zovala zawo uzikhala wautali kwambiri. (Numeri 15:38-40) Ankachita zimenezi “kuti anthu awaone.”—Mateyu 23:5.
Yesu ankadziwanso kuti ophunzira ake akhoza kutengera mtima wofuna kukhala otchuka, choncho anawalangiza kuti: “Koma inu musamatchulidwe kuti Rabi, chifukwa mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha, ndipo nonsenu ndinu abale. Komanso musamatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, pakuti Atate wanu ndi mmodzi, wakumwamba Yekhayo. Musamatchedwe ‘atsogoleri,’ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.” Ndiye ophunzirawo ankayenera kudziona bwanji, nanga ankafunika kuchita bwanji zinthu ndi anthu ena? Yesu anawauza kuti: “Koma wamkulu kwambiri pakati panu akhale mtumiki wanu. Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.”—Mateyu 23:8-12.
Kenako Yesu ananena zimene zidzachitikire alembi ndi Afarisi achinyengowo. Iye anati: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mukutseka ufumu wakumwamba kuti anthu asalowemo. Pakuti inuyo simukulowamo, mukuletsa amene akufuna kulowamo kuti asalowe.”—Mateyu 23:13.
Yesu anadzudzula Afarisi chifukwa chakuti sankaona zinthu zofunika ngati mmene Yehova amazionera ndipo zimenezi zinkaonekera pa malamulo osamveka amene iwo ankaika. Mwachitsanzo, iwo ankanena kuti: “Ngati munthu walumbirira kachisi palibe kanthu, koma ngati munthu walumbirira golide wa m’kachisi, asunge lumbiro lake.” Iwo ankasonyeza kuti anali okonda chuma chifukwa ankaganizira kwambiri za golide wa m’kachisi m’malo moganizira kuti kachisiyo ndi malo amene ankalambirirako Yehova. Komanso ‘ankanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.”—Mateyu 23:16, 23; Luka 11:42.
Yesu ananena kuti Afarisiwa anali ‘atsogoleri akhungu, amene ankasefa zakumwa zawo kuti achotsemo kanyerere koma ankameza ngamila.’ (Mateyu 23:24) Afarisi ankasefa vinyo wawo kuti achotsemo nyerere chifukwa nyerereyo inali m’gulu la tizilombo todetsedwa. Koma chifukwa chakuti ankanyalanyaza zinthu zofunika kwambiri za m’Chilamulo, zinali ngati kuti akumeza ngamila yomwenso inali nyama yodetsedwa.—Levitiko 11:4, 21-24.
-
-
Tsiku Lomaliza Limene Yesu Anapezeka pa KachisiYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 110
Tsiku Lomaliza Limene Yesu Anapezeka pa Kachisi
MATEYU 23:25–24:2 MALIKO 12:41–13:2 LUKA 21:1-6
YESU ANAPITIRIZA KUDZUDZULA ATSOGOLERI ACHIPEMBEDZO
ANANENERATU KUTI KACHISI ADZAWONONGEDWA
MKAZI WAMASIYE ANAPONYA TIMAKOBIDI TIWIRI TATING’ONO
Pa nthawi imene Yesu anapezeka pa kachisi komaliza, anapitiriza kuulula zinthu zachinyengo zimene alembi ndi Afarisi ankachita moti anawatchula mosapita m’mbali kuti ndi onyenga. Ponena zimenezi Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo. Iye anati: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumayeretsa kunja kwa kapu ndi mbale, koma mkati mwake mutadzaza zolanda ndi kusadziletsa. Mfarisi wakhungu iwe, yeretsa mkati mwa kapu ndi mbale choyamba, kuti kunja kwakenso kukhale koyera.” (Mateyu 23:25, 26) Ngakhale kuti Afarisi ankayesetsa kwambiri kuti azioneka bwino komanso kutsatira mwambo wodziyeretsa, iwo sankafuna kusintha makhalidwe awo komanso kukonza mitima yawo.
Afarisi anasonyezanso kuti anali achinyengo chifukwa ankayesetsa kumanga ndi kukongoletsa manda a aneneri chonsecho Yesu ananena kuti anali “ana a anthu amene anapha aneneri.” (Mateyu 23:31) Ndipo zimene Yesu ananenazi zinalidi zoona chifukwa anthuwo ankafunanso kumupha.—Yohane 5:18; 7:1, 25.
Kenako Yesu anafotokoza zimene atsogoleri achipembedzowa ankayembekezera kukumana nazo ngati sakanalapa. Iye anati: “Njoka inu, ana a mphiri, mudzathawa bwanji chiweruzo cha Gehena?” (Mateyu 23:33) Anthu ankawotcha zinyalala m’chigwa cha Hinomu chomwe chinali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu ndipo zimene Yesu ananenazi zinathandiza anthuwo kumvetsa kuti alembi ndi Afarisi adzawonongedwa ndipo sadzakhalakonso ngati mmene zinkakhalira ndi zinthu zimene zinkaponyedwa m’chigwachi.
Ophunzira a Yesu ndi amene anadzakhala omuimira monga “aneneri, anthu anzeru ndi aphunzitsi” iye atapita kumwamba. Koma kodi anthu anawachitira zotani ophunzirawa? Pamene Yesu ankalankhula ndi atsogoleri achipembedzowo ananena kuti: “Ena [mwa ophunzira anga] mudzawapha ndi kuwapachika, ndipo ena mudzawakwapula m’masunagoge mwanu ndi kuwazunza mumzinda ndi mzinda, kuti magazi onse olungama okhetsedwa padziko lapansi abwere pa inu, kuyambira magazi a Abele wolungama mpaka magazi a Zekariya . . . amene inu munamupha.” Anawachenjezanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti, Zinthu zonsezi zidzaubwerera m’badwo uwu.” (Mateyu 23:34-36) Izi ndi zimene zinachitika mu 70 C.E. pamene asilikali a Aroma anawononga Yerusalemu ndipo Ayuda ambiri anaphedwa.
Yesu anavutika maganizo kwambiri ataganizira zinthu zochititsa mantha zimenezi. Chifukwa cha chisoni iye ananena kuti: “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneri iwe ndi woponya miyala anthu otumizidwa kwa iwe. Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, muja nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko. Koma anthu inu simunafune zimenezo. Tsopano tamverani! Mulungu wachoka n’kukusiyirani nyumba yanuyi.” (Mateyu 23:37, 38) Anthu amene anamva Yesu akunena zimenezi ayenera kuti anadabwa kuti ankanena za “nyumba” iti. Kodi mwina Yesu ankanena za kachisi wokongola kwambiri wa ku Yerusalemu amene ankaoneka ngati ankatetezedwa ndi Mulungu?
Kenako Yesu ananenanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Kuyambira tsopano simudzandionanso kufikira pamene mudzanene kuti, ‘Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!’” (Mateyu 23:39) Ponena mawu amenewa, Yesu ankanena ulosi wopezeka pa Salimo 118:26 womwe umati: “Wodala ndi Iye wobwera m’dzina la Yehova.Takudalitsani anthu inu potuluka m’nyumba ya Yehova.” Zimenezi zinasonyeza kuti kachisiyo akadzawonongedwa, palibe aliyense amene azidzapitako kuti akapemphere m’dzina la Mulungu.
Tsopano Yesu anapita kumbali ina ya kachisiyo komwe kunali mabokosi oponyamo ndalama. Mabokosi amenewa anali ndi kabowo pamwamba ndipo anthu ankaponya zopereka zawo mmenemo. Yesu ankayang’anitsitsa Ayuda ambiri amene ankapereka ndalama zawo. Anthu olemera ‘ankaponyamo makobidi ambiri.’ Koma kenako Yesu anaona mayi wina wosauka amenenso anali wamasiye akuponya “timakobidi tiwiri tating’ono.” (Maliko 12:41, 42) Yesu anadziwa kuti Mulungu anasangalala kwambiri ndi mphatso ya mayiyo.
Ndiyeno, Yesu anaitana ophunzira ake n’kuwauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa onse amene aponya ndalama moponya zoperekamo.” Yesu anafotokoza chifukwa chake ananena zimenezi. Iye anati: “Zili choncho chifukwa onsewo aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zochirikizira moyo wake.” (Maliko 12:43, 44) Mayiyu ankaganiza komanso kuchita zinthu mosiyana kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo.
Tsopano Yesu anachoka pa kachisi ndipo limeneli linali tsiku lomaliza kupezeka pakachisi. Tsikuli linali Nisani 11. Pamene ankachoka, wophunzira wake wina ananena kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikuonekera!” (Maliko 13:1) Miyala ina imene anamangira kachisiyo inali yaikulu kwambiri ndipo inkachititsa kuti kachisiyo azioneka wokongola komanso wolimba kwambiri. Choncho ophunzirawo anadabwa kwambiri Yesu atanena kuti: “Kodi waziona nyumba zapamwamba zimenezi? Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”—Maliko 13:2.
Yesu atanena zimenezi, iye ndi ophunzira ake anawoloka khwawa la Kidironi n’kupita pamalo enaake m’phiri la Maolivi. Pa nthawi imeneyi Yesu anali ndi ophunzira ake 4. Ophunzirawo anali Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane. Ali pamalo amenewa Yesu ndi ophunzira akewo ankatha kuona kachisi wokongola uja yemwe anali m’munsi mwa phirilo.
-
-
Atumwi Anapempha ChizindikiroYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 111
Atumwi Anapempha Chizindikiro
MATEYU 24:3-51 MALIKO 13:3-37 LUKA 21:7-38
OPHUNZIRA 4 ANAPEMPHA CHIZINDIKIRO
MAULOSI ANAYAMBA KUKWANIRITSIDWA M’NTHAWI YA ATUMWI
TIYENERA KUKHALA TCHERU
Lachiwiri masana pa Nisani 11, Yesu ndi ophunzira ake 4 anali atakhala pansi m’phiri la Maolivi. Mayina a ophunzirawa anali Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane. Yesu anali atatsala pang’ono kumaliza utumiki wake wa padziko lapansi womwe anaugwira mwakhama kwambiri. Iye ankaphunzitsa anthu kukachisi masana ndipo usiku ankakagona kunja kwa mzinda. Anthu ankamvetsera mwachidwi zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo ‘ankalawirira m’mawa kwambiri kupita kwa iye kukachisi kuti akamumvetsere.’—Luka 21:37, 38.
Ophunzira 4 aja anapita kwa Yesu ali payekha. Iwo ankada nkhawa chifukwa Yesu anali atangowauza kumene zimene zidzachitikire kachisi kuti sipadzakhala mwala pa mwala unzake. Ophunzirawa ankaganizira zinthu zambiri. Nthawi ina m’mbuyomu Yesu anawauza kuti: “Khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzafika.” (Luka 12:40) Anawauzanso za “tsikulo, pamene Mwana wa munthu adzaonekera.” (Luka 17:30) Kodi zimene anawauzazi zinali zogwirizana ndi nkhani yomwe anali atangowauza yokhudza zimene zidzachitikire kachisi? Ophunzirawo ankafunitsitsa kudziwa zambiri moti anafunsa Yesu kuti: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?”—Mateyu 24:3.
Zikuoneka kuti ophunzirawa ankaganizira za kuonongedwa kwa kachisi amene ankamuona pamene anali paphiripo. Anafunsanso za kuonekera kwa Mwana wa munthu. Ayenera kuti anakumbukiranso fanizo la Yesu lonena za “munthu wina wa m’banja lachifumu” amene “anapita kudziko lakutali kuti akalandire ufumu ndi kubwerako.” (Luka 19:11, 12) Ophunzirawa ankafunanso kudziwa zinthu zina zimene zidzachitike ku “mapeto a nthawi ino.”
Poyankha ophunzirawa, Yesu anawauza chizindikiro chimene chidzawathandize kudziwa mapeto a nthawi imene ulamuliro wa Ayuda komanso kachisi zidzawonongedwe. Koma Yesu ananenanso kuti chizindikirochi chidzathandizanso Akhristu ena m’tsogolo kudziwa kuti ayamba kukhala m’nthawi ya “kukhalapo” kwake komanso kudziwa kuti mapeto a nthawi ya pansi pano atsala pang’ono kufika.
Pamene zaka zinkadutsa, atumwi anaona kuti zimene Yesu ananena zikuchitikadi. Ndipotu zinthu zambiri zimene Yesu ananena zinayamba kuchitika m’nthawi yawo. Choncho Ayuda amene anakhala tcheru sanadabwe ndi zimene zinachitika mu 70 C.E. M’chakachi ulamuliro wa Ayuda komanso kachisi zinawonongedwa mogwirizana ndi zimene Yesu ananena zaka 37 m’mbuyomo. Komabe si zinthu zonse zimene Yesu ananena zomwe zinachitika pofika mu 70 C.E. Ndiye kodi n’chiyani chomwe chidzakhale chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu monga wolamulira mu Ufumu? Yesu anafotokozera atumwiwo zimene zidzachitike.
Iye ananeneratu kuti mudzamva za “nkhondo ndi mbiri za nkhondo” komanso kuti “mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:6, 7) Anawauzanso kuti: “Kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala m’malo osiyanasiyana.” (Luka 21:11) Komanso Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Anthu adzakugwirani ndi kukuzunzani.” (Luka 21:12) Padzakhala aneneri onyenga ndipo adzasocheretsa anthu ambiri. Anthu ambiri adzakhala osamvera malamulo ndipo chikondi cha anthu ambiri chidzazirala. Yesu ananenanso kuti “uthenga wabwino . . . wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.
Zimene Yesu ananena zinayamba kukwaniritsidwa mzinda wa Yerusalemu utatsala pang’ono kuwonongedwa komanso pa nthawi imene unkawonongedwa ndi Aroma. Koma kodi zimenezi zinadzakwaniritsidwanso m’tsogolo kuposa mmene zinakwaniritsidwira m’mbuyomo? Kodi inuyo mumaona umboni wotsimikizira kuti zimene Yesu ananena zikukwaniritsidwa kwambiri masiku ano?
Chinthu china chimene Yesu ananena kuti chidzakhala chizindikiro cha kukhalapo kwake, ndi kuonekera kwa ‘chinthu chonyansa komanso chowononga.’ (Mateyu 24:15) Mu 66 C.E., chinthu chonyansachi chinaonekera pamene “magulu ankhondo” a Aroma, omwe ananyamula zizindikiro za mafano komanso mbendera zawo, anazungulira mzinda wa Yerusalemu ndipo anawononga mbali zina za mpanda wa mzindawo. (Luka 21:20) Choncho “chinthu chonyansa” chinaima pa malo amene sichinkayenera kuima chifukwa Ayuda ankaona kuti ‘malowa anali oyera.’
Yesu ananenanso kuti: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.” Mu 70 C.E., Aroma anawononga mzinda wa Yerusalemu. Kuwonongedwa kwa ‘mzinda woyera’ wa Ayuda komanso kachisi chinalidi chisautso chachikulu ndipo anthu ambiri anaphedwa. (Mateyu 4:5; 24:21) Zimene zinachitika pa nthawiyi zinali zoopsa kwambiri kuposa zinthu zonse zomwe zinachitikirapo mzindawu komanso anthu ake ndipo kupembedza kwa Ayuda kunathanso m’nthawi imeneyi. Zimenezi zikusonyeza kuti ulosi umenewu ukamadzakwaniritsidwanso m’tsogolo padzachitika zinthu zoopsa kwambiri.
TIYENERA KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO M’MASIKU OTSIRIZA ANO
Pamene Yesu ankakambirana ndi atumwi ake za chizindikiro cha kukhalapo kwake monga Mfumu komanso za mapeto a dziko loipali ananenanso zinthu zina. Anawachenjeza za “onamizira kukhala Khristu ndi aneneri onyenga.” Iye ananena kuti anthu amenewa adzachita zimenezi “kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse ngakhale osankhidwawo.” (Mateyu 24:24) Koma anthu osankhidwawo sadzasocheretsedwa. Kukhalapo kwa Khristu sikudzakhala koonekera koma anthu amene adzanamizire kuti ndi Khristu adzaonekera.
Pofotokoza zimene zidzachitike pa chisautso chachikulu chimene chidzayambe dziko la Satanali likadzatsala pang’ono kutha, Yesu ananena kuti: “Dzuwa lidzachita mdima ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka.” (Mateyu 24:29) Atumwi amene anamva zinthu zochititsa mantha zimene Yesu ananenazi, sanamvetse zimene zidzachitike koma anadziwa kuti zidzakhala zoopsa kwambiri.
Koma kodi anthu adzatani akadzaona zoopsazi? Yesu ananena kuti: “Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha ndi kuyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi kumene kuli anthu, pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.” (Luka 21:26) Pamenepatu Yesu ankafotokoza za nthawi imene kudzachitike zinthu zoopsa kwambiri zimene anthu sanazionepo n’kale lonse.
N’zolimbikitsa kwambiri kuti Yesu anathandiza ophunzira ake kudziwa kuti si anthu onse amene adzalire akadzaona “Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:30) Tikutero chifukwa Yesu anali atafotokoza kale kuti Mulungu adzalowererapo “chifukwa cha osankhidwawo.” (Mateyu 24:22) Ndiye kodi ophunzira okhulupirika adzatani akadzaona zinthu zimene Yesu anafotokozazi? Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti: “Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire chilili ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.”—Luka 21:28.
Koma kodi ophunzira a Yesu amene adzakhale ndi moyo pa nthawi imeneyi adzadziwa bwanji kuti mapeto ayandikira? Yesu ananena fanizo la mtengo wa mkuyu. Iye anati: “Nthambi yake yanthete ikaphuka ndi kuchita masamba, mumadziwa kuti dzinja lili pafupi. Inunso chimodzimodzi, mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni. Ndithu ndikukuuzani kuti m’badwo uwu sudzatha wonse kuchoka kufikira zinthu zonsezi zitachitika.”—Mateyu 24:32-34.
Choncho ophunzirawo akadzayamba kuona mbali zosiyanasiyana za chizindikirocho zikukwaniritsidwa, adzazindikire kuti mapeto ayandikira. Pofuna kuchenjeza ophunzira ake amene adzakhale ndi moyo pa nthawi imeneyo, Yesu ananena kuti:
“Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha. Pakuti monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire. M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo. Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:36-39) Yesu anayerekezera zimene zidzachitike pa nthawiyo ndi zimene zinachitika pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chimene chinachitika padziko lonse lapansi.
Ophunzira amene anamva Yesu akunena zimenezi pamene anali pa phiri la Maolivi, mosakayikira anadziwa kufunika kokhala tcheru. Tikutero chifukwa Yesu ananenanso kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzafikira onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi. Chotero khalani maso ndipo muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.”—Luka 21:34-36.
Zimene Yesu ananenazi zinasonyezanso kuti zimene analosera zidzachitika kwa nthawi yaitali. Ulosiwu sunkanena za zinthu zomwe zidzachitike pa zaka zochepa kapena zimene zidzachitikire mzinda wa Yerusalemu kapena mtundu wa Ayuda okha. Iye ankanena zinthu zimene zidzachitikire anthu “onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi.”
Ananena kuti ophunzira ake ayenera kukhala maso, kukhala tcheru komanso kukhala okonzeka. Iye ananenanso fanizo lina pofuna kuthandiza ophunzirawo kumvetsa mfundo imeneyi. Ananena kuti: “Dziwani ichi: Ngati mwininyumba angadziwe nthawi yobwera mbala, angakhale maso ndipo sangalole kuti mbala zithyole ndi kulowa m’nyumba mwake. Pa chifukwa chimenechi, nanunso khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.”—Mateyu 24:43, 44.
Yesu ananenanso zinthu zina zomwe zinathandiza ophunzira ake kuti aziyembekezera zinthu zabwino. Iye anawauza kuti zimene ananena zikamadzakwaniritsidwa, padzakhala “kapolo” amene adzakhala tcheru komanso adzakhala akugwira ntchito. Ndiyeno Yesu anafotokoza zinthu zimene ophunzirawo akanatha kuzimvetsa. Anawauza kuti: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera? Kapolo ameneyu adzakhala wodala ngati mbuye wake pobwera adzam’peza akuchita zimenezo! Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse.” Koma ngati ‘kapoloyo’ atayamba khalidwe loipa n’kuyamba kuchitira nkhanza antchito anzake, Mbuye wake “adzam’patsa chilango choopsa.”—Mateyu 24:45-51; yerekezerani ndi Luka 12:45, 46.
Komabe sikuti Yesu ankatanthauza kuti ophunzira ake ena adzayamba khalidwe loipa. Ndiye kodi pamenepa Yesu ankafuna kuti ophunzira ake amvetse mfundo iti? Iye ankafuna kuti ophunzira ake azikhala tcheru komanso kuti azigwira ntchito ndipo anathandiza ophunzira ake kumvetsa zimenezi m’fanizo lina limene ananena.
-
-
Fanizo la Anamwali Limatiphunzitsa Kufunika Kokhala TcheruYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 112
Fanizo la Anamwali Limatiphunzitsa Kufunika Kokhala Tcheru
YESU ANANENA FANIZO LA ANAMWALI 10
Yesu anayankha funso limene atumwi ake anamufunsa pamene ankafuna kudziwa chizindikiro cha kukhalapo kwake komanso chizindikiro chakuti dziko la Satanali latsala pang’ono kutha. Chifukwa chodziwa zimene zinkadetsa nkhawa atumwi ake, Yesu ananena fanizo lina pofuna kuwapatsa malangizo othandiza. Anthu amene adzakhale ndi moyo m’nthawi ya kukhalapo kwake ndi amene adzaone kukwaniritsidwa kwa zimene Yesu ananena m’fanizoli.
Iye anayamba kunena fanizoli kuti: “Ufumu wakumwamba udzakhala ngati anamwali 10 amene anatenga nyale zawo n’kupita kukachingamira mkwati. Anamwali asanu anali opusa, ndipo asanu anali ochenjera.”—Mateyu 25:1, 2.
Yesu sankatanthauza kuti hafu ya ophunzira ake amene adzalandire nawo Ufumu wakumwamba ndi opusa ndipo enawo ndi ochenjera. Koma iye ankatanthauza kuti pa nkhani yokhudza Ufumu, wophunzira wake aliyense ayenera kusankha kukhala tcheru kapena kulola kuti asokonezedwe. Ndipotu Yesu sankakayikira kuti mtumiki wake aliyense adzakhala wokhulupirika komanso kuti adzalandira madalitso ochokera kwa Atate ake.
M’fanizoli, anamwali onse 10 anapita kukalandira mkwati komanso anakhala nawo m’gulu loperekeza mkwati. Pamene mkwatiyo akufika ndi mkwatibwi wake kunyumba imene amukonzera, anamwaliwa ankayenera kuyatsa nyale zawo kuti amuunikire njira posonyeza kuti akupereka ulemu. Koma kodi chinachitika n’chiyani?
Yesu ananena kuti: “Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta owonjezera. Koma ochenjerawo anatenga mafuta owonjezera m’mabotolo awo limodzi ndi nyale zawo. Popeza kuti mkwati anali kuchedwa, onse anayamba kuwodzera kenako anagona.” (Mateyu 25:3-5) Mkwatiyo sanafike pa nthawi imene ankamuyembekezera moti anamwaliwo anayamba kugona poona kuti wachedwa kwambiri. Atumwiwo ayenera kuti anakumbukira fanizo limene Yesu ananena la munthu wina wa m’banja lachifumu amene anapita kudziko lakutali ndipo patapita nthawi ‘anabwerera kwawo pambuyo polandira ufumu.’—Luka 19:11-15.
M’fanizoli, Yesu ananenanso zimene zinachitika mkwati atafika. Ananena kuti: “Pakati pa usiku kunamveka mawu ofuula akuti, ‘Mkwati uja wafika! Tulukani mukam’chingamire.’” (Mateyu 25:6) Kodi anapezadi anamwaliwo ali okonzeka komanso ali tcheru?
Yesu anapitiriza kuti: “Nthawi yomweyo anamwali onsewo anadzuka ndi kukonza nyale zawo. Opusa aja anauza ochenjera kuti, ‘Tigawireniko mafuta anu, chifukwa nyale zathu zatsala pang’ono kuzima.’ Ochenjerawo anayankha kuti, ‘Mwina satikwanira tikagawana ndi inu. Pitani kwa ogulitsa kuti mukagule anu.’”—Mateyu 25:7-9.
Choncho anamwali 5 opusa aja sanakhale tcheru ndipo sanakonzekere kufika kwa mkwati. Analibe mafuta okwanira m’nyale zawo ndipo anafunika kupeza mafuta ena. Yesu ananena kuti: “Atanyamuka kupita kukagula, mkwati anafika, ndipo anamwali okonzekerawo analowa naye limodzi m’nyumba imene munali phwando laukwati, ndipo chitseko chinatsekedwa. Pambuyo pake anamwali ena aja nawonso anafika n’kunena kuti, ‘Ambuye, ambuye, titsegulireni!’ Poyankha iye anati, ‘Kunena zoona, sindikukudziwani inu.’” (Mateyu 25:10-12) Anamwaliwo anakumana ndi zinthu zomvetsa chisoni chifukwa sanali okonzeka komanso chifukwa chakuti sanali tcheru.
Atumwiwo anadziwa kuti Yesu ndiye anali mkwati wa m’fanizoli chifukwa nthawi inanso m’mbuyomo anadziyerekezerapo ndi mkwati. (Luka 5:34, 35) Nanga anamwali ochenjerawo ankaimira ndani? Pamene Yesu ankanena za “kagulu ka nkhosa,” kamene kadzapatsidwa Ufumu ananena kuti: “Mangani m’chiuno mwanu ndipo nyale zanu zikhale chiyakire.” (Luka 12:32, 35) Choncho atumwiwo anazindikira kuti pamene Yesu ankanena fanizo la anamwali ankanena za iwowo. Ndiye kodi mfundo ya Yesu inali yoti chiyani ponena fanizoli?
Mfundo ya Yesu inali yodziwikiratu chifukwa anamaliza n’kunena kuti: “Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—Mateyu 25:13.
Pamenepatu n’zoonekeratu kuti Yesu analangiza otsatira ake okhulupirika kuti ayenera ‘kukhalabe maso’ pa nthawi ya kukhalapo kwake. Iye adzabwera ndithu ndipo otsatira akewa ayenera kukhala okonzeka komanso kuchita zinthu mwakhama mofanana ndi anamwali 5 ochenjera aja. Zimenezi zikanawathandiza kuti apitirize kukhala ndi chiyembekezo komanso kudzalandira mphoto yawo.
-
-
Fanizo la Matalente Limatiphunzitsa Kufunika Kochita Zinthu MwakhamaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 113
Fanizo la Matalente Limatiphunzitsa Kufunika Kochita Zinthu Mwakhama
YESU ANANENA FANIZO LA MATALENTE
Yesu ananenanso fanizo lina pa nthawi imene anali ndi ophunzira ake 4 pa phiri la Maolivi paja. Masiku angapo m’mbuyomo pamene Yesu anali ku Yeriko, ananena fanizo la ndalama za mina pofuna kusonyeza kuti padzadutsa nthawi yaitali Ufumu usanabwere. Fanizo limene ananena pa nthawi imeneyi limanena zinthu zina zofanana ndi zimene ananena m’fanizo la ndalama za mina. Fanizoli limafotokozanso zinthu zina pa nkhani ya kukhalapo kwake komanso zimene zidzachitike dziko la Satanali likadzatsala pang’ono kutha. Limasonyezanso kuti ophunzira ake ayenera kuchita khama pamene akugwiritsa ntchito zinthu zimene apatsidwa.
Yesu ananena kuti: “Zili ngati munthu amene anali kupita kudziko lina, ndipo anaitanitsa akapolo ake ndi kuwasungitsa chuma chake.” (Mateyu 25:14) Atumwi anazindikira mwamsanga kuti “munthu” amene Yesu ankanena m’fanizoli anali iyeyo. Tikutero chifukwa m’mbuyomo Yesu anali atadziyerekezerapo ndi munthu amene anapita ku dziko lakutali “kuti akalandire ufumu.”—Luka 19:12.
Munthu wa m’fanizoli asanapite kudziko lakutali, anapereka chuma chake chamtengo wapatali kwa akapolo kapena kuti antchito ake. Pa zaka zitatu ndi hafu zimene Yesu anachita utumiki wake ankalalikira kwambiri za uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu ndipo anaphunzitsanso ophunzira ake kuti azigwira ntchitoyi. Tsopano anali atatsala pang’ono kuchoka ndipo ankadziwa kuti ophunzira ake adzapitiriza kugwira ntchito imene anawaphunzitsa.—Mateyu 10:7; Luka 10:1, 8, 9; yerekezerani ndi Yohane 4:38; 14:12.
Kodi munthu wa m’fanizoli anagawa bwanji “chuma chake”? Yesu ananena kuti: “Woyamba anam’patsa ndalama zokwana matalente asanu, wachiwiri anam’patsa matalente awiri, ndipo wachitatu anam’patsa talente imodzi. Aliyense anam’patsa malinga ndi luso lake, ndipo iye anapita kudziko lina.” (Mateyu 25:15) Kodi antchitowa anachita chiyani ndi chuma chimene anapatsidwachi? Kodi anachita zinthu mwakhama pofuna kuthandiza Mbuye wawoyo? Yesu anauza atumwiwo kuti:
“Nthawi yomweyo amene analandira matalente asanu uja ananyamuka kukachita nawo malonda ndipo anapindula matalente enanso asanu. Chimodzimodzinso amene analandira matalente awiri uja, anapindula enanso awiri. Koma amene analandira imodzi yokha uja anapita kukakumba pansi n’kubisa ndalama yasiliva ya mbuye wakeyo.” (Mateyu 25:16-18) Kodi chinachitika n’chiyani Mbuye wawo atabwera?
Yesu ananena kuti: “Patapita nthawi yaitali, mbuye wa akapolowo anabwera ndi kuwerengerana nawo ndalama.” (Mateyu 25:19) Antchito awiri oyambirira anachita zonse zomwe akanatha aliyense “malinga ndi luso lake.” Wantchito aliyense anachita zinthu mwakhama ndipo anapindula pa ndalama zimene anapatsidwa zija. Amene analandira matalente 5, anapezanso matalente ena 5 ndipo amene anapatsidwa matalente awiri, anapezanso ena awiri. (Nthawi imeneyo munthu ankafunika kugwira ntchito zaka pafupifupi 19 kuti apeze ndalama zokwana talente imodzi.) Mbuye uja anayamikira wantchito aliyense kuti: “Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe! Unakhulupirika pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti uziyang’anira zinthu zambiri. Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.”—Mateyu 25:21.
Koma izi si zimene zinachitikira wantchito amene analandira talente imodzi uja. Wantchito ameneyu ananena kuti: “Ambuye, ndinadziwa kuti inu ndinu munthu wovuta. Mumakolola kumene simunafese, ndipo mumatuta tirigu kumene simunapete. Choncho ndinachita mantha ndipo ndinapita kukabisa talente yanu ija pansi. Nayi ndalama yanu, landirani.” (Mateyu 25:24, 25) Iye sanaganize n’komwe zosungitsa ndalamayo kwa osunga ndalama kuti Mbuye wake adzapeze phindu. Choncho zimene wantchitoyu anachita zinali zosathandiza kwa mbuye wake.
Moti zinali zomveka kuti Mbuyeyo anatchula munthu ameneyu kuti: “Kapolo woipa ndi waulesi iwe.” Iye analandidwanso zinthu zimene anali nazo ndipo anazipereka kwa wantchito wina amene akanagwira ntchito mwakhama. Kenako Mbuyeyo ananena mfundo imene amayendera. Iye anati: “Pakuti amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri ndipo adzakhala nazo zambiri, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.”—Mateyu 25:26, 29.
Ophunzira a Yesu anali ndi zinthu zambiri zoti aziganizire ndipo fanizoli linawachititsanso kuti aganizire zinthu zina. Iwo anadziwa kuti Yesu anawapatsa mwayi waukulu kwambiri wothandiza anthu ena kuti akhale ophunzira ake. Yesu ankayembekezera kuti ophunzirawo adzagwira ntchitoyi mwakhama. Koma sankayembekezera kuti ophunzira ake onse adzachita zofanana pogwira ntchito yolalikira imene anawapatsa. Mogwirizana ndi zimene ananena m’fanizo lija aliyense ayenera kuchita zinthu “malinga ndi luso lake.” Choncho zimene zinachitikira wantchito womalizayu zikusonyezeratu kuti Yesu sangasangalale ndi munthu “waulesi” komanso amene akulephera kuchita zonse zomwe angathe pofuna kupindulitsa Mbuye wake.
Atumwiwo ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi zimene Yesu anawalonjeza. Iye anati: “Amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri.”
-
-
Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi MbuziYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 114
Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi
YESU ANANENA FANIZO LA NKHOSA NDI MBUZI
Yesu ali paphiri la Maolivi ananena fanizo la anamwali 10 komanso la ndalama za matalente. Pomaliza kuyankha funso la atumwi ake lokhudza chizindikiro cha kukhalapo kwake komanso chizindikiro chakuti dziko la Satanali latsala pang’ono kutha, Yesu ananenanso fanizo lina. Fanizoli limanena za nkhosa ndi mbuzi.
Yesu anayamba kufotokoza zimene zinachitika m’fanizoli kuti: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero.” (Mateyu 25:31) Pamene ankanena fanizoli, Yesu anasonyezeratu kuti ankanena za iyeyo chifukwa nthawi zambiri ankadzitchula kuti “Mwana wa munthu.”—Mateyu 8:20; 9:6; 20:18, 28.
Kodi fanizo limeneli lidzakwaniritsidwa liti? Lidzakwaniritsidwa Yesu “akadzafika mu ulemerero wake” limodzi ndi angelo n’kukhala “pampando wake wachifumu waulemerero.” M’mbuyomo Yesu anali atanenapo kale kuti “Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu” pamodzi ndi angelo ake. Kodi zimenezi zidzachitika liti? Zidzachitika “chisautso chikadzangotha.” (Mateyu 24:29-31; Maliko 13:26, 27; Luka 21:27) Choncho fanizoli lidzakwaniritsidwa Yesu akadzabwera mu ulemerero wake m’tsogolo. Kodi adzachita chiyani pa nthawi imeneyo?
Yesu ananena kuti: “Mwana wa munthu akadzafika. . . , mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye ndipo adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzere kwake.”—Mateyu 25:31-33.
Ponena za nkhosa zomwe zidzakhale kudzanja lake lamanja Yesu ananena kuti: “Pamenepo mfumu idzauza a kudzanja lake lamanja kuti, ‘Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Lowani mu ufumu umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.” (Mateyu 25:34) N’chifukwa chiyani Mfumuyi inakonda nkhosa?
Mfumuyo inanena kuti: “Ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya. Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino. Ndinali wamaliseche koma inu munandiveka. Ndinadwala koma inu munandisamalira. Ndinali m’ndende koma inu munabwera kudzandiona.” Ndiyeno anthu ‘olungama’ omwe ndi nkhosazo anafunsa mmene anachitira zinthu zimenezo. Mfumu inayankha kuti: “Pa mlingo umene munachitira zimenezo mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munachitira ine amene.” (Mateyu 25:35, 36, 40, 46) Mosakayikira anthuwa sanachite zinthu zabwino zimenezi ali kumwamba chifukwa kumwamba kulibe anthu odwala kapena anjala. Choncho zimenezi ziyenera kukhala zinthu zimene anachitira abale ake a Khristu padziko lapansi.
Nanga n’chiyani chimene chinachitikira mbuzi zomwe zinaikidwa ku dzanja lake la manzere? Yesu anafotokoza kuti: “Kenako [Mfumu] adzauza a kumanzere kwake kuti, ‘Chokani pamaso panga inu otembereredwa. Pitani kumoto wosatha wokolezedwera Mdyerekezi ndi angelo ake. Pakuti ndinamva njala koma inu simunandipatse chakudya. Ndinamva ludzu koma inu simunandipatse chakumwa. Ndinali mlendo koma inu simunandilandire bwino. Ndinali wamaliseche koma inu simunandiveke. Ndinadwala komanso ndinali m’ndende, koma inu simunandisamalire.’” (Mateyu 25:41-43) Mpake kuti mbuzi zidzalandira chiweruzo chimenechi chifukwa cholephera kusonyeza chifundo kwa abale ake a Khristu pa nthawi imene anali padziko lapansi.
Atumwi anazindikira kuti chiweruzo chimene chidzaperekedwe m’tsogolo sichidzasintha mpaka kalekale. Yesu anawauza kuti: “Pamenepo [Mfumu] adzawayankha kuti, ‘Ndithu ndikukuuzani, Popeza simunachitire zimenezo mmodzi wa aang’ono awa, simunachitirenso ine.’ Ndipo iwowa adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu, koma olungama ku moyo wosatha.”—Mateyu 25:45, 46.
Zimene Yesu ananena poyankha funso la atumwi, zimathandiza kwambiri otsatira ake kuganizira za khalidwe lawo komanso zochita zawo.
-