-
Anawaphunzitsa Kudzichepetsa pa Pasika WomalizaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 116
Anawaphunzitsa Kudzichepetsa pa Pasika Womaliza
MATEYU 26:20 MALIKO 14:17 LUKA 22:14-18 YOHANE 13:1-17
YESU ANADYA PASIKA WAKE WOMALIZA NDI ATUMWI
ANASAMBITSA MAPAZI A OPHUNZIRA AKE POFUNA KUWAPHUNZITSA MFUNDO YOFUNIKA
Petulo ndi Yohane anafika mwamsanga ku Yerusalemu kuti akakonzekere mwambo wa Pasika. Kenako Yesu ndi ophunzira ake ena 10 anawatsatira. Madzulo dzuwa likulowa, Yesu ndi ophunzira ake anatsika m’phiri la Maolivi kupita ku Yerusalemu. Limeneli linali tsiku lomaliza kuti Yesu aone dzuwa likulowa ndipo anadzalionanso ataukitsidwa.
Kenako Yesu ndi ophunzira ake aja analowa mumzinda ndipo anapita kunyumba imene anakadyerako Pasika. Atafika ku nyumbayi anakwera masitepe n’kupita m’chipinda chapamwamba. Atalowa m’chipindamo anapeza kuti zonse zofunika pa mwambowu zakonzedwa kale. Yesu ankayembekezera kupezeka pa mwambo umenewu chifukwa ananena kuti: “Ndinali wofunitsitsa kudya pasika uyu limodzi ndi inu ndisanalowe m’masautso.”—Luka 22:15.
Zaka zambiri m’mbuyomo, anthu anali atayambitsa mwambo woyendetsa makapu angapo kwa anthu amene apezeka pa mwambo wa Pasika. Ndiyeno Yesu atalandira imodzi mwa makapuwo, anayamika kenako ananena kuti: “Landirani kapu iyi, nonse imwani mopatsirana. Ndithu ndikukuuzani, Kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utafika.” (Luka 22:17, 18) Pamene ananena mawu amenewa zinaonekeratu kuti imfa yake yayandikira.
Mwambo wa Pasika uli mkati Yesu anachita chinthu china chodabwitsa kwambiri. Anaimirira n’kuvula malaya ake akunja ndi kutenga thaulo. Kenako anathira madzi m’beseni limene linali chapafupi. Nthawi imeneyo munthu akalandira alendo ankaonetsetsa kuti wantchito wake wasambitsa mapazi a alendowo. (Luka 7:44) Koma chifukwa chakuti mwiniwake wa nyumbayo panalibe, Yesu ndi amene anagwira ntchito imeneyi. Aliyense wa atumwiwo akanatha kugwira ntchitoyi koma palibe amene anadzipereka mwina chifukwa chakuti ankakanganabe kuti wamkulu ndani. Ophunzirawo ayenera kuti anachita manyazi Yesu atayamba kuwasambitsa mapazi.
Atafika pamene panali Petulo, Petulo anakana kuti Yesu amusambitse mapazi. Iye ananena kuti: “Ndithu, sizitheka kuti inu musambitse mapazi anga.” Yesu anamuuza kuti: “Ndikapanda kukusambitsa, palibe chako kwa ine.” Ndiyeno Petulo anayankha ndi mtima wonse kuti: “Ambuye, musandisambitse mapazi okha, komanso manja ndi mutu womwe.” Petulo ayenera kuti anadabwa ndi zimene Yesu ananena chifukwa anati: “Amene wasamba m’thupi amangofunika kusamba mapazi okha basi, chifukwa thupi lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, koma osati nonsenu.”—Yohane 13:8-10.
Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake onse 12 kuphatikizapo Yudasi Isikariyoti. Atamaliza kuwasambitsa mapazi, anavala malaya ake akunja aja ndipo anakhalanso pansi. Kenako anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa zimene ndachita kwa inu? Inu mumanditcha kuti ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Ambuye,’ mumalondola, pakuti ndinedi. Choncho ngati ine, wokhala Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi. Pakuti ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi. Ndithudi ndikukuuzani, Kapolo saposa mbuye wake, ndiponso wotumidwa saposa amene wamutuma. Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.”—Yohane 13:12-17.
Pamenepatu Yesu anaphunzitsa otsatira ake khalidwe la kudzichepetsa. Choncho wotsatira aliyense wa Yesu ayenera kupewa mtima wofuna kukhala pa malo apamwamba poganiza kuti iyeyo ndi wofunika kwambiri kuposa anzake ndiponso kuti ena azimutumikira. M’malomwake ayenera kutsatira chitsanzo cha Yesu, osati posambitsa anthu ena mapazi, koma pokhala wofunitsitsa kutumikira ena modzichepetsa ndiponso mosakondera.
-
-
Chakudya Chamadzulo Cha AmbuyeYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 117
Chakudya Chamadzulo cha Ambuye
MATEYU 26:21-29 MALIKO 14:18-25 LUKA 22:19-23 YOHANE 13:18-30
YESU ANANENA KUTI YUDASI NDI AMENE AMUPEREKE
YESU ANAYAMBITSA MWAMBO WOKUMBUKIRA IMFA YAKE
Asanachite mwambo wa Pasika, Yesu anaphunzitsa atumwi ake khalidwe la kudzichepetsa pamene anawasambitsa mapazi. Ndiyeno mwambo wa Pasikawo utatha, Yesu ananena mawu amene Davide analosera akuti: “Munthu amene ndinali kukhala naye mwamtendere, amene ndinali kumukhulupirira, munthu amene anali kudya chakudya changa, wakweza chidendene chake kundiukira.” Kenako ananena kuti: “Mmodzi wa inu andipereka.”—Salimo 41:9; Yohane 13:18, 21.
Atumwi anayang’anana ndipo anayamba kufunsa kuti: “Ambuye, kodi ndine kapena?” Nayenso Yudasi Isikariyoti anafunsa nawo. Popeza kuti Yohane anakhala pafupi ndi Yesu, Petulo anauza Yohane kuti afunse kuti munthuyo ndi ndani. Choncho Yohane anayandikira Yesu n’kumufunsa kuti: “Ambuye, mukunena ndani?”—Mateyu 26:22; Yohane 13:25.
Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse chidutswa cha mkate chimene ndisunse.” Ndiyeno Yesu anatenga mkate n’kusunsa m’mbale ina imene inali patebulopo n’kupatsa Yudasi kenako ananena kuti: “Mwana wa munthu akuchokadi, monga Malemba amanenera za iye, koma tsoka kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu! Zikanakhala bwino munthu ameneyu akanapanda kubadwa.” (Yohane 13:26; Mateyu 26:24) Kenako Satana anayamba kulamulira maganizo a Yudasi. Chifukwa chakuti Yudasi ankachita zinthu zachinyengo analola kuti Satana amugwiritse ntchito ndipo zimenezi zinachititsa kuti akhale “mwana wa chiwonongeko.”—Yohane 6:64, 70; 12:4; 17:12.
Kenako Yesu anauza Yudasi kuti: “Zimene wakonza kuchita, zichite mwamsanga.” Popeza kuti Yudasi ankasunga bokosi la ndalama, atumwi enawo anaganiza kuti Yesu ankamuuza kuti: “‘Ugule zofunikira zonse za chikondwerero,’ kapena kuti apereke kenakake kwa osauka.” (Yohane 13:27-30) M’malomwake Yudasi ananyamuka kuti akapeze njira yoperekera Yesu.
Usiku umene anachita mwambo wa Pasika, Yesu anayambitsa mwambo wina watsopano. Anatenga mkate, anapemphera, anaunyema n’kuupereka kwa atumwi ake kuti adye. Atawapatsa ananena kuti: “Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) Atumwiwo ankapatsirana mkatewo kuti aliyense adye.
Kenako Yesu anatenga kapu ya vinyo, anapemphera n’kuipereka kwa atumwi ake. Aliyense ankati akamwa ankapereka kapuyo kwa mnzake kuti amwe. Pamene atumwiwo ankamwa vinyoyo Yesu ananena kuti: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.”—Luka 22:20.
Pochita zimenezi Yesu anakhazikitsa mwambo wokumbukira imfa yake ndipo otsatira ake ayenera kuchita mwambo umenewu chaka chilichonse pa Nisani 14. Akamachita mwambo umenewu amakumbukira zimene Yesu komanso Atate wake anachita pothandiza anthu okhulupirika kuti adzamasuke ku uchimo ndi imfa. Mwambo wa Pasika unkakumbutsa Ayuda kuti Mulungu anawapulumutsa koma mwambo wa tsopano umene Yesu anayambitsawu umasonyeza kuti Mulungu anakonza njira yopulumutsira anthu onse amene angakhulupirire Yesu.
Yesu ananena kuti magazi ake “adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo akhululukidwe.” Ena mwa anthu amene adzakhululukidwe machimo awo ndi atumwi ake komanso anthu ena okhulupirika. Anthu amenewa ndi amene akalamulire ndi Yesu mu Ufumu wa Atate ake.—Mateyu 26:28, 29.
-
-
Anakangananso Kuti Wamkulu NdaniYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 118
Anakangananso Kuti Wamkulu Ndani
MATEYU 26:31-35 MALIKO 14:27-31 LUKA 22:24-38 YOHANE 13:31-38
YESU ANAPEREKA MALANGIZO PA NKHANI YOFUNA UDINDO WAPAMWAMBA
YESU ANANENERATU KUTI PETULO AMUKANA
OTSATIRA A YESU AMADZIWIKA NDI CHIKONDI
Usiku wake womaliza Yesu anaphunzitsa atumwi ake khalidwe la kudzichepetsa powasambitsa mapazi. N’chifukwa chiyani zinali zoyenera kuti Yesu awaphunzitse khalidwe limeneli? Chifukwa chakuti atumwiwa ankavutika kusonyeza khalidweli. Iwo ankatumikira Mulungu ndi mtima wonse koma ankavutikabe ndi nkhani yakuti wamkulu ndani pakati pawo. (Maliko 9:33, 34; 10:35-37) Zimenezi zinaonekeranso usiku womwewu.
Zimene zinachitika n’zakuti “panabuka mkangano woopsa pakati [pa atumwiwo] za amene anali kuoneka wamkulu kwambiri.” (Luka 22:24) Yesu ayenera kuti anamva chisoni kwambiri ataona kuti atumwiwo akukangananso chifukwa cha nkhani imeneyi. Kodi Yesu anatani?
M’malo mokalipira atumwi akewo chifukwa cha zimene anachitazo komanso chifukwa cha maganizo awo olakwikawo, Yesu analeza mtima n’kuwauza kuti: “Mafumu a mitundu ya anthu amachita ulamuliro pa anthu awo, ndipo amene ali ndi mphamvu pa anthuwo amatchedwa Opereka zabwino. Inu musakhale otero. . . . Kodi wamkulu ndani, amene akudya patebulo kapena amene akutumikira?” Kenako anawakumbutsa chitsanzo chabwino chimene ankawasonyeza nthawi zonse powauza kuti: “Koma ine ndili pakati panu monga wotumikira.”—Luka 22:25-27.
Ngakhale kuti atumwiwa ankalakwitsa zina ndi zina, anasonyeza kuti anali okhulupirika chifukwa anapitirizabe kuyenda ndi Yesu pa nthawi imene ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Chifukwa chakuti atumwiwo anali okhulupirika, Yesu ananena kuti: “Ndikuchita nanu pangano, mmene Atate wanga wachitira pangano la ufumu ndi ine.” (Luka 22:29) Atumwiwa anasonyeza kuti anali otsatira a Yesu okhulupirika moti Yesu anawauza kuti adzalamulira naye mu Ufumu wake chifukwa cha pangano limene anapangana nawo.
Ngakhale kuti atumwi anali ndi mwayi wokalamulira ndi Yesu, pa nthawiyi anali adakali ochimwa ndipo ankalakwitsa zina ndi zina. Yesu anawauza kuti: “Satana akufuna anthu inu, kuti akupeteni ngati tirigu,” amene amauluzika akamapetedwa. (Luka 22:31) Anawachenjezanso kuti: “Nonsenu muthawa ndi kundisiya ndekha usiku uno, pakuti Malemba amati, ‘Ndidzapha m’busa, ndipo nkhosa za m’gululo zidzabalalika.’”—Mateyu 26:31; Zekariya 13:7.
Koma Petulo ananena motsimikiza kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!” (Mateyu 26:33) Yesu anauza Petulo kuti usiku umenewo tambala asanalire kawiri amukana. Ndiyeno Yesu ananenanso kuti: “Ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe. Chotero iwenso, ukabwerera, ukalimbikitse abale ako.” (Luka 22:32) Komabe Petulo ananenetsa kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” (Mateyu 26:35) Atumwi enawo ananenanso chimodzimodzi.
Ndiyeno Yesu anauza ophunzira akewo kuti: “Ndikhala nanu kanthawi kochepa chabe. Mudzandifunafuna, ndipo monga ndinauzira Ayuda aja kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kukafikako,’ tsopano ndikuuzanso inuyo. Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yohane 13:33-35.
Yesu atangonena kuti akhala nawo kanthawi kochepa chabe, Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, mukupita kuti?” Pomuyankha anamuuza kuti: “Kumene ndikupita sunganditsatire padakali pano, koma udzanditsatira m’tsogolo.” Petulo anadabwa kwambiri ndipo ananena kuti: “Ambuye, n’chifukwa chiyani sindingakutsatireni padakali pano? Ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha inu.”—Yohane 13:36, 37.
Kenako Yesu anakumbutsa atumwiwo za nthawi imene anawatuma kuti akalalikire ku Galileya. Pa nthawi imeneyo anawauza kuti asatenge thumba la ndalama kapena chakudya. (Mateyu 10:5, 9, 10) Ndiyeno anawafunsa kuti: “Munasowa kanthu kodi?” Iwo anayankha kuti: “Ayi.” Koma kodi tsopano anayenera kuchita chiyani? Yesu anawauza kuti: “Amene ali ndi chikwama cha ndalama achitenge, chimodzimodzinso thumba la chakudya. Ndipo amene alibe lupanga agulitse malaya ake akunja n’kugula lupanga. Pakuti ndikukuuzani kuti mawu olembedwawa ayenera kukwaniritsidwa mwa ine. Mawuwo ndi akuti, ‘Ndipo anamutenga ngati mmodzi wa anthu osamvera malamulo.’ Pakuti chimene chikukhudza ine chikukwaniritsidwa.”—Luka 22:35-37.
Ponena mawu amenewa Yesu ankatanthauza kuti apachikidwa pamtengo pamodzi ndi anthu ochita zoipa ndiponso kuti kenako ophunzira ake adzazunzidwa kwambiri. Ophunzirawo ankaona kuti anali okonzeka moti ananena kuti: “Ambuye, onani! Tili ndi malupanga awiri awa.” Iye anawauza kuti: “Amenewa ndi okwanira.” (Luka 22:38) Chifukwa chakuti ophunzirawo anayankha kuti anali ndi malupanga awiri, Yesu anapezerapo mwayi wowaphunzitsa mfundo ina yofunika kwambiri.
-
-
Yesu Ndi Njira, Choonadi ndi MoyoYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 119
Yesu Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
YESU ANAPITA KUKAKONZA MALO
ANALONJEZA OTSATIRA AKE KUTI ADZAWATUMIZIRA MTHANDIZI
ATATE NDI WAMKULU KUPOSA YESU
Mwambo wa chakudya chamadzulo utatha, Yesu anakhalabe m’chipinda chapamwamba chija ndi atumwi ake. Iye anawauza kuti: “Mitima yanu isavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupiriraninso ine.”—Yohane 13:36; 14:1.
Yesu analimbikitsa atumwi ake okhulupirika kuti asadzadandaule iye akadzachoka. Anawauza kuti: “M’nyumba ya Atate wanga muli malo ambiri okhalamo. . . . Ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengerani kwathu, kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko.” Koma atumwiwo sanadziwe kuti Yesu ankanena zoti akupita kumwamba. Moti Tomasi anafunsa kuti: “Ambuye, ife sitikudziwa kumene mukupita. Ndiye njira yake tingaidziwe bwanji?”—Yohane 14:2-5.
Yesu anayankha kuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo.” Pamenepa iye ankatanthauza kuti munthu akhoza kulowa m’nyumba yakumwamba ya Atate wake ngati munthuyo atakhulupirira Yesu, kukhulupirira zimene amaphunzitsa komanso kutsatira zimene ankachita pa moyo wake. N’chifukwa chake ananena kuti: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”—Yohane 14:6.
Filipo, yemwe ankamvetsera mwatcheru pamene Yesu ankalankhula, anapempha kuti: “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo tikhutira.” Zikuoneka kuti Filipo ankafuna kuona Mulungu m’masomphenya ngati mmene zinachitikira kwa Mose, Eliya komanso Yesaya. Koma atumwiwo sankafunika kuchita kuona masomphenya chifukwa Yesu ananena kuti: “Anthu inu, ndakhala nanu nthawi yonseyi, koma kodi iwe Filipo sunandidziwebe? Amene waona ine waonanso Atate.” Yesu anali ndi makhalidwe ofanana ndi a Atate wake, choncho anthu amene ankakhala ndi Yesu komanso kuona zimene ankachita anali ngati akuona Atate wake. Komabe Atate ndi wamkulu kwa Mwana chifukwa Yesu ananena kuti: “Zinthu zimene ine ndimanena kwa inu sindilankhula za m’maganizo mwanga.” (Yohane 14:8-10) Pamenepatu atumwiwo ayenera kuti anadziwa kuti zonse zimene Yesu ankaphunzitsa zinkachokera kwa Atate wake.
Atumwi anamuona Yesu akuchita zinthu zodabwitsa komanso anamumva akulalikira uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu. Koma tsopano iye anawauza kuti: “Wokhulupirira ine, nayenso adzachita ntchito zimene ine ndimachita, ndipo adzachita ntchito zazikulu kuposa zimenezi.” (Yohane 14:12) Yesu sankatanthauza kuti atumwi ake adzachita zinthu zazikulu kuposa zimene iye anachita. Koma ankatanthauza kuti adzalalikira kwa nthawi yaitali, m’madera akutali komanso kwa anthu ambiri.
Pamene Yesu ankachoka sikuti atumwi akewo anangowasiya. Iye anawalonjeza kuti: “Ngati mutapempha chilichonse m’dzina langa, ine ndidzachichita.” Anawauzanso kuti: “Ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani mthandizi wina kuti adzakhale nanu kosatha. Mthandizi ameneyo ndi mzimu wa choonadi.” (Yohane 14:14, 16, 17) Anawalonjeza kuti adzawatumizira mzimu woyera womwe udzawathandize ndipo zimenezi zinachitika pa tsiku la mwambo wa Pentekosite.
Kenako Yesu ananena kuti: “Kwatsala kanthawi pang’ono ndipo dziko silidzandionanso. Koma inu mudzandiona, chifukwa ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo.” (Yohane 14:19) Ponena mawu amenewa, Yesu ankatanthauza kuti akadzaukitsidwa, ophunzira ake adzamuona ndi thupi ngati lathuli komanso kuti m’tsogolo adzawaukitsa ndi matupi auzimu kuti akakhale naye kumwamba.
Ndiyeno Yesu ananena mfundo ina yosavuta kumvetsa. Iye anati: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda. Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsera bwinobwino kwa iye.” Yesu atanena mawu amenewa mtumwi Yudasi yemwe ankadziwikanso kuti Tadeyo anafunsa kuti: “Ambuye, bwanji mukufuna kudzionetsera bwinobwino kwa ife koma osati ku dzikoli?” Yesu anamuyankha kuti: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda. . . . Amene sandikonda ine sasunga mawu anga.” (Yohane 14:21-24) Mosiyana ndi otsatira ake, anthu a m’dzikoli saona Yesu ngati njira, choonadi ndi moyo.
Kodi ophunzira akanatha bwanji kukumbukira zinthu zonse zimene Yesu anawaphunzitsa? Yesu anawauza kuti: “Koma mthandizi, amene ndi mzimu woyera, amene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse ndi kukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani.” Mawu amenewa anali olimbikitsa kwambiri kwa atumwiwa chifukwa anali ataonapo Yesu akuchita zinthu zamphamvu mothandizidwa ndi mzimu woyera. Anawauzanso kuti: “Ndikusiyirani mtendere, ndikupatsani mtendere wanga. . . . Mitima yanu isavutike kapena kuchita mantha.” (Yohane 14:26, 27) Choncho ophunzirawo sankafunika kudandaula chifukwa Yesu anawalonjeza kuti Atate wake adzawatsogolera komanso kuwateteza.
Ophunzirawo anali atatsala pang’ono kuona umboni wosonyeza kuti Mulungu adzawateteza. Yesu ananena kuti: “Wolamulira wa dziko akubwera. Iye alibe mphamvu pa ine.” (Yohane 14:30) Mdyerekezi anakwanitsa kulowa mwa Yudasi n’kuyamba kumulamulira. Koma Mdyerekezi sakanasokoneza maganizo a Yesu kuti achite zinthu zotsutsana ndi Mulungu chifukwa Yesu analibe uchimo. Komanso sakanachititsa kuti Yesu akhalebe m’manda mpaka kalekale. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yesu ananena kuti: “Ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atatewo anandipatsa.” Yesu ankakhulupirira kuti Atate wake adzamuukitsa.—Yohane 14:31.
-
-
Anali Ngati Nthambi Zobala Zipatso Komanso Anali Mabwenzi a YesuYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 120
Anali Ngati Nthambi Zobala Zipatso Komanso Anali Mabwenzi a Yesu
MTENGO WA MPESA WENIWENI NDI NTHAMBI ZAKE
ZIMENE MUNTHU ANGACHITE KUTI APITIRIZE KUKONDEDWA NDI YESU
Yesu analimbikitsa atumwi ake okhulupirika ndipo analankhula nawo monga mabwenzi ake a pamtima. Nthawiyi unali usiku kwambiri mwinanso kupitirira 12 koloko ya usiku. Kenako Yesu anauza atumwi akewo fanizo lolimbikitsa kwambiri.
Iye anayamba kufotokoza fanizolo kuti: “Ine ndine mtengo wa mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye mlimi.” (Yohane 15:1) Fanizoli ndi lofanana ndi zimene zinafotokozedwapo zaka zambiri m’mbuyomo zokhudza mtundu wa Isiraeli womwe unkadziwika monga mtengo wa mpesa wa Yehova. (Yeremiya 2:21; Hoseya 10:1, 2) Koma pa nthawiyi Yehova anali atakana mtunduwu. (Mateyu 23:37, 38) Choncho m’fanizoli, Yesu ananena mfundo yatsopano. Ananena kuti iyeyo ndi mtengo wa mpesa umene Atate wake ankaulimira kuchokera pa nthawi imene Yesuyo anadzozedwa ndi mzimu woyera m’chaka cha 29 C.E. Koma zimene Yesu ananena zinasonyeza kuti mtengo wa mpesawo umaimiranso zinthu zina osati iye yekha. Iye ananena kuti:
“Nthambi iliyonse mwa ine yosabala zipatso [Atate wanga] amaidula, ndipo iliyonse yobala zipatso amaiyeretsa mwa kuitengulira kuti ibale zipatso zambiri. . . . Nthambi singabale zipatso payokha, pokhapokha ngati ndi yolumikizikabe kumpesawo. Chimodzimodzi inunso, simungabale zipatso mukapanda kukhala olumikizika kwa ine. Ine ndine mtengo wa mpesa, inu ndinu nthambi zake.”—Yohane 15:2-5.
Yesu anali atangolonjeza ophunzira ake okhulupirika kuti akadzapita kumwamba, adzawatumizira mzimu woyera womwe udzawathandize. Patapita masiku 51, atumwiwo pamodzi ndi anthu ena analandira mzimu woyera ndipo pa nthawiyi anakhala nthambi za mtengo wa mpesa. Ndipotu atumwi pamodzi ndi anthu enawo, omwe anapanga “nthambi” za mtengo wa mpesa, anayenera kukhala ogwirizana ndi Yesu. N’chifukwa chiyani zimenezi zinali zofunika?
Yesu ananena kuti: “Amene ali wolumikizika kwa ine, inenso n’kukhala wolumikizika kwa iye, ameneyo amabala zipatso zochuluka, chifukwa simungathe kuchita kalikonse popanda ine.” Choncho otsatira okhulupirika a Yesu omwe anali ngati “nthambi” za mtengo wa mpesa, akanatha kubala zipatso zambiri potsanzira makhalidwe a Yesu, kulalikira za Ufumu wa Mulungu mwakhama komanso kuthandiza anthu ambiri kuti akhale ophunzira ake. Kodi chikanachitika n’chiyani ngati munthu akanasiya kugwirizana ndi Yesu komanso kubala zipatso? Yesu ananena kuti: “Ngati munthu sakhala wolumikizika kwa ine, amaponyedwa kunja.” Komanso Yesu ananena kuti: “Ngati mukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.”—Yohane 15:5-7.
Kenako Yesu anabwerezanso mfundo yomwe anali atainenapo kawiri m’mbuyomo. Mfundoyi ndi yokhudza kusunga malamulo ake. (Yohane 14:15, 21) Iye anafotokoza zinthu zimene zikanathandiza atumwiwo kudziwa ngati ankatsatiradi malamulo ake. Ananena kuti: “Mukasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’chikondi changa, monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.” Komabe munthu amene amakonda Yehova Mulungu ndi Mwana wake ayenera kuchitanso zinthu zina. Yesu ananena kuti: “Lamulo langa ndi ili, mukondane monga mmene inenso ndakukonderani. Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake. Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.”—Yohane 15:10-14.
Patadutsa maola ochepa Yesu anapereka moyo wake m’malo mwa anthu onse amene amamukhulupirira ndipo zimenezi zinasonyeza kuti amawakonda kwambiri. Zimene Yesu anachitazi zimalimbikitsa otsatira ake kuti azitengera chitsanzo chake posonyezana chikondi chololera kuvutikira ena. Chikondi chimenechi chidzathandiza kuti anthu adzawazindikire ngati mmene Yesu ananenera kuti: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yohane 13:35.
Atumwiwo ayenera kuti anamvetsa zimene zinachititsa Yesu kuti awatchule kuti “mabwenzi.” Yesu ananena kuti: “Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.” Atumwiwa analitu ndi mwayi wapadera kwambiri wokhala pa ubwenzi ndi Yesu komanso wodziwa zimene Atate wake anamuuza. Koma kuti azigwirizanabe ndi Yesu ankafunika ‘kupitiriza kubala zipatso.’ Kenako Yesu anawauza zimene zikanachitika ngati akanatsatiradi mfundo imeneyi. Iye anati: ‘Chilichonse chimene mungapemphe Atate m’dzina langa adzakupatsani.’—Yohane 15:15, 16.
Ngati ophunzirawa, omwe anali ngati nthambi za mtengo wa mpesa, akanapitiriza kukondana akanatha kupirira mavuto amene anali atatsala pang’ono kukumana nawo. Anawachenjeza kuti dziko lidzadana nawo koma anawalimbikitsanso kuti: “Ngati dziko likudana nanu, mukudziwa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu. Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake. Koma popeza simuli mbali ya dzikoli, . . . pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.”—Yohane 15:18, 19.
Yesu anafotokozanso chifukwa china chimene chidzachititse dziko kudana ndi atumiki ake. Iye ananena kuti: “Adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha dzina langa, chifukwa amene anandituma ine sakumudziwa.” Yesu ananena kuti zozizwitsa zimene ankachita zinachititsa kuti anthu amene ankadana naye akhale ndi mlandu pamaso pa Mulungu chifukwa ananena kuti: “Ndikanapanda kuchita pakati pawo ntchito zimene wina aliyense sanachitepo, akanakhala opanda tchimo, koma tsopano aona ndipo adana nane, ndi kudananso ndi Atate wanga.” Zimene anthu amenewa ankachita podana ndi Yesu zinkakwaniritsa ulosi.—Yohane 15:21, 24, 25; Salimo 35:19; 69:4.
Yesu anawalonjezanso kuti adzawatumizira mzimu woyera kuti udzawathandize. Mzimu woyerawu womwe ndi wamphamvu kwambiri umathandiza otsatira onse a Yesu ‘kuchitira umboni,’ komwe ndi kubala zipatso.—Yohane 15:27.
-
-
“Limbani Mtima Ndaligonjetsa Dziko”Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 121
“Limbani Mtima Ndaligonjetsa Dziko”
YESU ANALI ATATSALA PANG’ONO KUCHOKA NDIPO ATUMWI SAKANAMUONANSO
CHISONI CHIMENE ATUMWI ANALI NACHO CHINADZASANDUKA CHISANGALALO
Yesu ndi atumwi ake anakonzeka zotuluka m’chipinda chapamwamba chimene anachitiramo mwambo wa Pasika. Koma asanatuluke Yesu anawapatsanso malangizo ena. Iye anati: “Ndalankhula zimenezi kwa inu kuti musapunthwe.” N’chifukwa chiyani Yesu anawapatsa malangizo amenewa? Iye anawauza kuti: “Anthu adzakuchotsani m’sunagoge. Ndipo nthawi ikubwera pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wachita utumiki wopatulika kwa Mulungu.”—Yohane 16:1, 2.
N’kutheka kuti atumwiwo anavutika maganizo kwambiri atamva zimenezi. Ngakhale kuti Yesu anali atawauza kale kuti dziko lidzadana nawo koma anali asanawauzepo kuti adzaphedwa. N’chifukwa chiyani Yesu sanawauze zimenezi? Iye anati: “Zinthu izi sindinakuuzeni pa chiyambi pomwe, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.” (Yohane 16:4) Choncho Yesu anawauza zimenezi asanachoke n’cholinga chowakonzekeretsa maganizo kuti asadzakhumudwe.
Yesu anawauzanso kuti: “Tsopano ndikupita kwa amene anandituma, ndipo palibe aliyense wa inu amene akundifunsa kuti, ‘Mukupita kuti?’” Chakumadzulo tsiku lomwelo, atumwiwo anafunsa Yesu kumene ankapita. (Yohane 13:36; 14:5; 16:5) Koma tsopano atumwiwa atamva kuti adzazunzidwa anachita mantha ndipo anadzimvera chisoni. Chifukwa cha chisonicho analephera kumufunsa za ulemelero umene Yesu ankayembekezera komanso mmene ulemelerowo ukanathandizira anthu amene amalambira Mulungu. Ataona kuti atumwiwo ali ndi chisoni, Yesu ananena kuti: “Chifukwa ndalankhula zimenezi kwa inu, chisoni chadzaza m’mitima yanu.”—Yohane 16:6.
Kenako Yesu ananena kuti: “Ndikupita kuti inu mupindule. Pakuti ngati sindipita, ndiye kuti mthandizi uja sabwera kwa inu. Koma ndikapita, ndikamutumiza kwa inu.” (Yohane 16:7) Kuti ophunzira a Yesu alandire mzimu woyera, pankafunika kuti Yesuyo afe, aukitsidwe kenako apite kumwamba. Ndiyeno ali kumwambako, Yesu akanatumiza mzimu woyera womwe ukanathandiza anthu ake onse padziko lapansi.
Mzimu woyera ‘udzapereka umboni wotsimikizika ku dzikoli wonena za tchimo, za chilungamo, ndi za chiweruzo.’ (Yohane 16:8) Mzimu woyera unapereka umboni wotsimikizira kuti Yesu analidi Mwana wa Mulungu ndiponso kuti anthu sanamukhulupirire. Yesu atakwera kumwamba zinasonyeza kuti anali munthu wolungama komanso zinasonyeza chifukwa chake Satana, amene ndi “wolamulira wa dziko lino,” ayenera kuweruzidwa.—Yohane 16:11.
Yesu ananenanso kuti: “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma padakali pano simungathe kuzimvetsa zonsezo.” Yesu atatumiza mzimu woyera, mzimuwo unathandiza ophunzirawo kuti amvetse “choonadi chonse” moti kuyambira nthawi imeneyo zimene ankachita komanso kulankhula zinali zogwirizana ndi choonadicho.—Yohane 16:12, 13.
Koma kenako atumwiwo anadabwa ndi zimene Yesu ananena. Iye anati: “Kwa kanthawi simudzandionanso, ndipo kwa kanthawi mudzandiona.” Iwo anayamba kufunsana zimene Yesu ankatanthauza. Yesu atazindikira zimenezi anawafotokozera kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mudzagwetsa misozi ndi kulira mofuula, koma dzikoli lidzasangalala. Mudzamva chisoni, koma chisoni chanu adzachisandutsa chimwemwe.” (Yohane 16:16, 20) Yesu anaphedwa tsiku lotsatira chakumasana. Ataphedwa, atsogoleri achipembedzo anasangalala pomwe ophunzira ake anali ndi chisoni. Koma Yesu ataukitsidwa, ophunzira ake anasiya kumva chisoni n’kuyamba kusangalala ndipo anasangalala kwambiri Yesu atawatumizira mzimu woyera wa Mulungu.
Yesu anayerekezera zimene atumwiwo ankayembekezera kukumana nazo ndi zimene zimachitikira mzimayi amene watsala pang’ono kubereka. Iye ananena kuti: “Pamene mayi akubereka amazunzika kwambiri, chifukwa nthawi yake yafika. Koma mwana akabadwa, sakumbukiranso kupweteka konse kuja chifukwa cha chimwemwe kuti munthu wabadwa padziko.” Koma anawalimbikitsa kuti: “Inunso muli ndi chisoni panopa. Koma ndidzakuonaninso, ndipo mitima yanu idzasangalala. Palibenso amene adzathetse chimwemwe chanu.”—Yohane 16:21, 22.
Pa nthawiyi, atumwi anali asanapempheko chilichonse m’dzina la Yesu. Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Pa tsikulo mudzapempha m’dzina langa.” Sikuti ankayenera kuchita zimenezi chifukwa chakuti Atate sakanawayankha. Tikutero chifukwa Yesu ananena kuti: “Atateyo amakukondani, chifukwa munandikonda ine . . . monga nthumwi ya Atate.”—Yohane 16:26, 27.
Zimene Yesu anauza atumwiwo zinawalimbikitsa kwambiri moti iwo ananena kuti: “Pa chifukwa chimenechi tikukhulupirira kuti munachokeradi kwa Mulungu.” Koma atumwiwa anali atatsala pang’ono kuyesedwa. Yesu anawauza zimene ankayembekezera kukumana nazo kuti: “Taonani! Nthawi ikubwera, ndipo yafika kale. Mubalalika aliyense kupita kunyumba kwake, ndipo mundisiya ndekha.” Koma anawatsimikizira kuti: “Ndanena zimenezi kwa inu kuti mukhale mu mtendere chifukwa cha ine. M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.” (Yohane 16:30-33) Pamenepatu sikuti Yesu ankatanthauza kuti angowasiya osawathandiza. Yesu ankadziwa kuti atumwiwo adzagonjetsanso dziko mofanana ndi iyeyo ngati akanapitirizabe kuchita chifuniro cha Mulungu pamene akuyesedwa ndi Satana komanso dzikoli.
-
-
Pemphero Lomaliza la Yesu Ali M’chipinda ChapamwambaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 122
Pemphero Lomaliza la Yesu Ali M’chipinda Chapamwamba
MADALITSO AMENE ANTHU ADZAPEZE CHIFUKWA CHODZIWA MULUNGU KOMANSO MWANA WAKE
ZIMENE MALEMBA AMATANTHAUZA PONENA KUTI YEHOVA, YESU NDI OPHUNZIRA NDI AMODZI
Yesu atatsala pang’ono kupita kumwamba, anakonzekeretsa maganizo a ophunzira ake. Iye anachita zimenezi chifukwa chakuti ankawakonda kwambiri. Atamaliza kuwapatsa malangizo anayang’ana kumwamba n’kuyamba kupemphera kwa Atate wake kuti: “Lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni. Inu mwamupatsa ulamuliro pa anthu onse, kuti onse amene inu mwamupatsa, awapatse moyo wosatha.”—Yohane 17:1, 2.
Zimene Yesu ananenazi zinasonyeza kuti ankaona kuti kulemekeza Yehova ndi nkhani yofunika kwambiri. Koma ndi zolimbikitsa kwambiri kuti ananenanso za chiyembekezo cha moyo wosatha. Poti Yesu ali ndi “ulamuliro pa anthu onse,” anthuwo akhoza kudzalandira madalitso chifukwa cha nsembe yake. Koma ndi anthu ochepa okha amene adzalandire madalitsowo. N’chifukwa chiyani zili choncho?Chifukwa chakuti Yesu adzapereka madalitso kwa anthu okhawo amene amachita zimene iye ananena. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.
Kuti munthu adzapeze moyo wosatha ayenera kudziwa komanso kukhala pa ubwenzi ndi Atate komanso Mwana wake. Ayenera kumaona zinthu mmene Atate komanso Mwana amazionera. Ayeneranso kuyesetsa kusonyeza makhalidwe abwino amene Atate ndiponso Mwanayo ali nawo pochita zinthu ndi anthu ena. Ndipo ayenera kukumbukira kuti kulemekeza Mulungu ndi kofunika kwambiri poyerekeza ndi kupulumuka. Kenako Yesu anapitiriza kufotokoza mfundo yonena za kulemekeza Mulungu. Iye ananena kuti:
“Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa. Ndipo tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.” (Yohane 17:4, 5) Pamenepatu Yesu ankapempha Atate wake kuti akadzamuukitsa adzamupatsenso ulemelero umene anali nawo kumwamba.
Komabe ponena mawu amenewa, sikuti Yesu sankakumbukira zimene anachita pa nthawi ya utumiki wake. Tikutero chifukwa iye anapemphera kuti: “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu. Anali anu, koma munawapereka kwa ine, ndipo iwo asunga mawu anu.” (Yohane 17:6) Yesu ankatchula dzina la Mulungu, lomwe ndi Yehova, polalikira. Kuwonjezera pamenepo anathandizanso atumwi ake kudziwa makhalidwe a Mulungu ndiponso mmene amachitira zinthu ndi anthu.
Atumwiwo anafika pomudziwa bwino Yehova, anadziwa udindo wa Mwana wake komanso anadziwa zimene Yesu anawaphunzitsa. Yesu ananena modzichepetsa kuti: “Mawu amene munandipatsa ndawapereka kwa iwo. Iwo awalandira ndipo adziwa ndithu kuti ine ndinabwera monga nthumwi yanu, ndipo akhulupirira kuti ndinu amene munandituma.”—Yohane 17:8.
Kenako zimene Yesu ananena zinasonyeza kuti pali kusiyana pakati otsatira ake ndi anthu ena onse. Iye anati: “Choncho ndikupempha m’malo mwa iwo, sindikupemphera dziko, koma awo amene mwandipatsa, chifukwa iwo ndi anu. . . . Atate Woyera, ayang’anireni chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa, kuti akhale amodzi mmene ife tilili. . . . Ine ndawasunga moti palibe aliyense wa iwo amene wawonongeka kupatulapo mwana wa chiwonongeko,” yemwe ndi Yudasi Isikariyoti. Pa nthawiyi Yudasi anali akukonza chiwembu kuti apereke Yesu.—Yohane 17:9-12.
Yesu anapitiriza kupemphera kuti: “Dziko likudana nawo. . . . Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire kuopera woipayo. Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:14-16) Atumwi komanso ophunzira ena anali akadali m’dziko lomwe wolamulira wake ndi Satana koma ankayenera kukhala osiyana ndi anthu a m’dzikoli komanso kupewa makhalidwe oipa. Kodi akanachita bwanji zimenezi?
Iwo ankayenera kukhala oyera kapena kuti opatulika kuti azitumikira Mulungu. Iwo akanachita zimenezi potsatira choonadi chopezeka m’Malemba Achiheberi komanso choonadi chimene Yesu anawaphunzitsa. Yesu anapempheranso kuti: “Ayeretseni ndi choonadi. Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Patapita nthawi, Mulungu anagwiritsa ntchito atumwi ena kulemba mabuku omwe anakhala mbali ya “choonadi” chomwe chimathandiza kuti munthu akhale woyera komanso wopatulika pamaso pa Mulungu.
Koma patapita nthawi panapezeka anthu enanso omwe anavomereza “choonadi.” N’chifukwa chake Yesu sanangopempherera “awa okha, [kutanthauza anthu omwe anali nawo pa nthawiyo] komanso amene amakhulupirira [Yesu] kudzera m’mawu awo.” Kodi Yesu anawapempherera chiyani anthu onsewa? Iye anapempha Atate ake kuti: “Onsewa akhale amodzi, mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana, kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife.” (Yohane 17:20, 21) Zimenezi sizikutanthauza kuti Yesu ndi Atate wake ndi munthu mmodzi. Koma ndi amodzi chifukwa chakuti amachita zinthu zonse mogwirizana. Choncho Yesu ankapemphera kuti otsatira ake akhale ogwirizana ngati mmene iyeyo ndi Atate wake alili.
Yesu anali atangouza kumene Petulo komanso atumwi enawo kuti akupita kukawakonzera malo. Yesu ankatanthauza kuti akawakonzera malo kumwamba. (Yohane 14:2, 3) Kenako Yesu ananenanso mfundo imeneyi m’pemphero. Iye anati: “Atate, ine ndikufuna kuti amene mwandipatsawa adzakhale limodzi ndi ine kumene ine ndidzakhale, kuti adzaone ulemerero wanga umene inu mwandipatsa, chifukwa munandikonda musanayale maziko a dziko.” (Yohane 17:24) Ponena mawu amenewa, Yesu ankatanthauza kuti zaka zambiri m’mbuyomo Adamu ndi Hava asanabereke ana, Mulungu ankakonda kwambiri Mwana wake wobadwa yekha amene kenako anadzakhala Yesu Khristu.
Pomaliza pempheroli, Yesu ananenanso za dzina la Atate wake komanso za chikondi chimene Mulungu anali nacho pa atumwi komanso anthu ena amene adzalandire “choonadi.” Iye anati: “Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”—Yohane 17:26.
-
-
Anapemphera Pamene Anali ndi Chisoni KwambiriYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 123
Anapemphera Pamene Anali ndi Chisoni Kwambiri
MATEYU 26:30, 36-46 MALIKO 14:26, 32-42 LUKA 22:39-46 YOHANE 18:1
ZIMENE ZINACHITIKA YESU ATAPITA KUMUNDA WA GETSEMANE
THUKUTA LAKE LINAONEKA NGATI MADONTHO A MAGAZI
Yesu atamaliza kupemphera ndi atumwi ake ‘anaimba nyimbo zotamanda Mulungu’ kenako “anatuluka n’kupita kuphiri la Maolivi.” (Maliko 14:26) Iwo analowera chakummawa komwe kunali munda wa Getsemane umene Yesu ankakonda kupitako nthawi zambiri.
Atafika kumundako, komwe kunali mitengo yambiri ya maolivi, Yesu anauza atumwi ake 8 kuti amudikire ndipo iye anatengana ndi atumwi atatu. N’kutheka kuti Yesu anawauza kuti adikirire pamalo olowera m’mundawo chifukwa ananena kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.” Yesu anatengana ndi Petulo, Yakobo ndi Yohane ndipo analowa m’mundamo. Iye anavutika kwambiri mumtima ndipo anauza atumwi atatuwo kuti: “Moyo wanga ukumva chisoni chofa nacho. Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”—Mateyu 26:36-38.
Yesu anawasiyanso atumwi atatu aja n’kuyenda kamtunda pang’ono kenako “anadzigwetsa pansi ndipo anayamba kupemphera.” Kodi Yesu ankapempha chiyani kwa Atate wake pa nthawi yovutayi? Iye anapemphera kuti: “Atate, zinthu zonse n’zotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.” (Maliko 14:35, 36) Kodi ankatanthauza chiyani ponena mawu amenewa? Kodi ankafuna kuthawa udindo wopulumutsa anthu? Ayi.
Yesu ali kumwamba ankaona mmene Aroma ankazunzira komanso kuphera anthu. Choncho ankadziwa zimene akumane nazo chifukwa pa nthawiyi anali ndi thupi ngati lathuli ndipo ankamva kupweteka. Koma Yesu ankavutika kwambiri chifukwa ankadziwa kuti aphedwa ngati chigawenga ndipo zimenezi zikanachititsa kuti anthu anyoze dzina la Atate wake. Pa nthawiyi anali atatsala ndi maola ochepa kuti apachikidwe pamtengo ngati mmene zinkakhalira ndi munthu amene wanyoza Mulungu.
Atapemphera kwa kanthawi, Yesu anabwerera kwa atumwi ake atatu aja ndipo anawapeza akugona. Iye anafunsa Petulo kuti: “Zoona anthu inu simungathe kukhalabe maso limodzi ndi ine ola limodzi? Khalani maso ndipo pempherani kosalekeza kuti musalowe m’mayesero.” Yesu ankadziwa kuti atumwi ake atopa kwambiri komanso kunali kutada. N’chifukwa chake ananena kuti: “Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”—Mateyu 26:40, 41.
Kenako Yesu anapitanso kukapemphera kachiwiri ndipo anapempha Mulungu kuti amuchotsere “kapu iyi.” Atabwerako anapezanso atumwi atatuwo akugona ngakhale kuti pa nthawiyi ankafunika kuti akhale akupemphera kuti asalowe m’mayesero. Yesu atawafunsa chifukwa chake ankagonanso “anasowa chomuyankha.” (Maliko 14:40) Yesu anapitanso kachitatu ndipo anagwada n’kuyamba kupemphera.
Yesu ankada nkhawa kwambiri kuti akaphedwa ngati chigawenga zichititsa kuti anthu anyoze dzina la Atate wake. Yehova anamva zimene Mwana wake ankamupempha moti anamutumizira mngelo kuti amulimbikitse. Komabe Yesu sanasiye kuchonderera Atate wake ndipo anapitiriza “kupemphera ndi mtima wonse.” Pa nthawiyi Yesu anavutika maganizo kwambiri chifukwa chodziwa udindo waukulu womwe anali nawo. Ngati akanalephera kupilira akanataya mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale komanso anthu amene ankamukhulupirira sakanakhala ndi chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. Yesu anavutika kwambiri moti “thukuta lake linaoneka ngati madontho amagazi amene akugwera pansi.”—Luka 22:44.
Yesu atabwerera kachitatu anapezanso ophunzira ake akugona. Iye ananena kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula! Taonani! Ola lakuti Mwana wa munthu aperekedwe m’manja mwa ochimwa layandikira. Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”—Mateyu 26:45, 46.
-
-
Khristu Anaperekedwa Kenako AnamangidwaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 124
Khristu Anaperekedwa Kenako Anamangidwa
MATEYU 26:47-56 MALIKO 14:43-52 LUKA 22:47-53 YOHANE 18:2-12
YUDASI ANAPEREKA YESU M’MUNDA WA GETSEMANE
PETULO ANADULA KHUTU LA MUNTHU WINA
YESU ANAMANGIDWA
Yudasi anafika kumene kunali Yesu nthawi itapitirira 12 koloko usiku. Pa nthawiyi ansembe anali atagwirizana zoti alipire Yudasi ndalama 30 zasiliva kuti apereke Yesu. Choncho Yudasi anatsogolera gulu la ansembe aakulu, Afarisi komanso gulu la asilikali achiroma pamodzi ndi mtsogoleri wawo pamene ankafunafuna Yesu. Pamene asilikaliwo ankapita komwe kunali Yesu anatenga zida.
Zikuoneka kuti Yudasi anapita kwa ansembe aakulu Yesu atangomutulutsa m’chipinda chimene anachitira mwambo wa Pasika. (Yohane 13:27) Ansembe aakuluwo anasonkhanitsa alonda komanso gulu la asilikali. N’kutheka kuti poyamba Yudasi anapita ndi anthuwo kunyumba imene Yesu ndi atumwi ake anachitirako mwambo wa Pasika. Koma atachoka kumeneko, Yudasi ndi gululo anawoloka chigwa cha Kidironi n’kulowera kumunda wa Getsemane. Kuwonjezera pa zida zimene ananyamula zija, anthuwo anatenganso miyuni ndi nyale zomwe zikusonyeza kuti anali okonzeka kukafunafuna Yesu.
Pamene Yudasi ndi gulu la anthuli ankakwera phiri la Maolivi, Yudasi ankadziwa kumene akanapeza Yesu. Tikutero chifukwa masiku angapo apitawo, Yesu ndi atumwi ake ankakonda kuima m’munda wa Getsemane akamapita ku Yerusalemu komanso pobwerera ku Betaniya. Koma poti unali usiku, Yesu ayenera kuti anabisika ndi zithunzithunzi za mitengo ya maolivi yomwe inali m’mundamo. Ndiye kodi asilikaliwo, omwe mwina anali asanaonepo Yesu, akanamuzindikira bwanji? Pofuna kuwathandiza, Yudasi anawauza kuti akawapatsa chizindikiro. Iye anawauza kuti: “Amene ndim’psompsone ndi ameneyo. Mum’gwire ndi kupita naye osam’taya.”—Maliko 14:44.
Atafika m’mundamo Yudasi anaona Yesu ali ndi atumwi ake ndipo anapita pamene panali Yesu n’kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu Rabi!” Kenako anapsompsona Yesu mwachikondi. Koma Yesu anamufunsa kuti: “Bwanawe, ukupezeka kuno ndi cholinga chotani?” (Mateyu 26:49, 50) Yesu anadziyankha yekha ponena kuti: “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa munthu mwa kupsompsona?” (Luka 22:48) Kenako Yesu anasiya kuganizira zimene Yudasi anachita ndipo anayamba kulankhula ndi gulu la anthulo.
Yesu anayandikira gulu la anthulo moti miyuni ndi nyale zimene anthuwo anatenga zinkamuunika. Iye anawafunsa kuti: “Mukufuna ndani?” Iwo anayankha kuti: “Yesu Mnazareti.” Yesu ananena molimba mtima kuti: “Ndine amene.” (Yohane 18:4, 5) Pamenepo anthuwo anagwa pansi chifukwa choti sankadziwa zimene zichitike.
Yesu akanatha kuthawa pa nthawi imeneyi koma anangoima n’kuwafunsanso kuti akufuna ndani. Anthuwo atayankhanso kuti, “Yesu Mnazareti,” iye anawayankha mtima uli m’malo kuti: “Ndakuuzani kuti ndine amene. Choncho ngati mukufuna ine, awa alekeni azipita.” N’zochititsa chidwi kuti ngakhale pa nthawi yovuta ngati imeneyi, Yesu anakumbukira zimene ananena kuti sadzatayapo ophunzira ake ngakhale mmodzi. (Yohane 6:39; 17:12) Yesu anasunga atumwi ake okhulupirika ndipo sanataye ngakhale mmodzi kupatulapo Yudasi, yemwe anali “mwana wa chiwonongeko.” (Yohane 18:7-9) Choncho anapempha kuti anthuwo alole ophunzira ake kuti azipita.
Atumwiwo ataona kuti asilikali omwe anagwa aja adzuka n’kupita pamene panali Yesu, anazindikira zimene zinkachitika. Kenako anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?” (Luka 22:49) Koma Yesu asanayankhe, Petulo anasolola limodzi mwa malupanga awiri omwe atumwiwo anali nawo. Nthawi yomweyo anadula khutu la kudzanja lamanja la wantchito wa mkulu wa ansembe yemwe dzina lake linali Makasi.
Koma Yesu anagwira khutu la Makasi n’kumuchiritsa. Kenako anaphunzitsa mfundo yofunika kwambiri ndipo anauza Petulo kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake , pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.”Yesu anali wokonzeka kuti anthu amugwire chifukwa kenako ananena kuti: “Nanga Malemba amene ananeneratu kuti izi ziyenera kuchitika adzakwaniritsidwa bwanji?” (Mateyu 26:52, 54) Ndiyeno ananenanso kuti: “Kodi sindiyenera kumwa za m’kapu imene Atate wandipatsa?” (Yohane 18:11) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yesu ankafunitsitsa kuti zofuna za Mulungu zichitike moti analolera kufa.
Ndiyeno Yesu anafunsa gulu la anthulo kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukukalimbana ndi wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndinali kukhala pansi m’kachisi ndi kuphunzitsa, koma simunandigwire. Koma zonsezi zachitika kuti malemba a aneneri akwaniritsidwe.”—Mateyu 26:55, 56.
Gulu la asilikali, mkulu wa asilikali komanso akuluakulu a Ayuda anagwira Yesu n’kumumanga. Atumwi ataona zimenezi anathawa. Koma “mnyamata wina” sanathawe nawo. N’kutheka kuti mnyamata ameneyu anali Maliko yemwe anali wophunzira wa Yesu ndipo cholinga chake chinali choti azitsatira kumene gululo linkapita ndi Yesu. (Maliko 14:51) Anthu ena pa gululo anazindikira mnyamatayu ndipo ankafuna kumugwira. Chifukwa cha zimenezi mnyamatayu anathawa n’kusiya nsalu yake.
-
-
Atamugwira Anapita Naye kwa Anasi Kenako kwa KayafaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 125
Atamugwira Anapita Naye kwa Anasi Kenako kwa Kayafa
MATEYU 26:57-68 MALIKO 14:53-65 LUKA 22:54, 63-65 YOHANE 18:13, 14, 19-24
ANAPITA NDI YESU KWA ANASI AMENE KALE ANALI MKULU WA ANSEMBE
KHOTI LA SANIHEDIRINI LINAIMBA MLANDU YESU MOPANDA CHILUNGAMO
Anthu amene anagwira Yesu, anamumanga ngati chigawenga ndipo anapita naye kwa Anasi yemwe anakhalapo mkulu wa ansembe m’mbuyomu. Anasi anali pa udindowu pa nthawi imene Yesu anadabwitsa anthu omwe ankaphunzitsa m’kachisi Yesuyo ali wamng’ono. (Luka 2:42, 47) Patapita nthawi ana ena a Anasi anakhala akulu a ansembe koma pa nthawiyi Kayafa yemwe anali mpongozi wake ndi amene anali mkulu wa ansembe.
Pamene Anasi ankafunsa Yesu mafunso, Kayafa anasonkhanitsa oweruza a m’khoti la Sanihedirini. Khoti la Sanihedirini linkapangidwa ndi oweruza 71 ndipo ena mwa oweruzawa anali mkulu wa ansembe komanso anthu ena omwe anakhalapo pa udindowu m’mbuyomu.
Anasi anafunsa Yesu “za ophunzira ake ndi za chiphunzitso chake.” Yesu anayankha kuti: “Ndalankhula poyera ku dzikoli. Nthawi zonse ndinali kuphunzitsa m’masunagoge ndi m’kachisi, kumene Ayuda onse anali kusonkhana, ndipo sindinalankhule kanthu mseri. N’chifukwa chiyani mukufunsa ine? Funsani amene anamva zimene ndinali kunena kwa iwo.”—Yohane 18:19-21.
Ndiyeno mmodzi wa alonda amene anaimirira chapafupi anamenya Yesu mbama n’kunena kuti: “Ungamuyankhe choncho wansembe wamkulu?” Yesu ankadziwa kuti sanalakwe chilichonse ndiye anayankha kuti: “Ngati ndalankhula molakwika, pereka umboni wa cholakwikacho. Koma ngati ndalankhula moyenera, n’chifukwa chiyani ukundimenya?” (Yohane 18:22, 23) Kenako Anasi analamula kuti Yesu apite naye kwa mpongozi wake Kayafa.
Pamene Yesu ankafika ndi gulu la anthulo n’kuti mkulu wa ansembe, akulu komanso alembi omwe ankapanga khoti la Sanihedirini atasonkhana kale. Anthuwa anakumana kunyumba kwa Kayafa. Malamulo sankalola kuti munthu aziimbidwa mlandu usiku wa tsiku limene ankachita mwambo wa Pasika. Ngakhale kuti anthuwa ankadziwa zimenezi, anaimbabe Yesu mlandu kuti akwaniritse zolinga zawo zoipa.
Gululi linaonetseratu kuti linali lokondera. Tikutero chifukwa nthawi ina m’mbuyomo Yesu ataukitsa Lazaro, khoti la Sanihedirini linapangana kuti liphe Yesu. (Yohane 11:47-53) Ndipo pofika tsiku la Pasikali n’kuti patapita masiku angapo kuchokera pamene atsogoleri achipembedzo anapangana kuti agwire Yesu n’kumupha. (Mateyu 26:3, 4) Moti asanayambe kumuzenga mlanduwu, anthuwo anali ataweruza kale m’maganizo mwawo kuti Yesu ndi wolakwa ndipo ayenera kuphedwa.
Kuwonjezera pa kukumana pa tsiku lomwe kunkachitika mwambo wa Pasika, ansembe aakulu komanso anthu ena omwe ankapanga khoti la Sanihedirini sanatsatirenso malamulo chifukwa anapangana zoti apeze anthu oti akapereke umboni wabodza n’cholinga choti aimbe Yesu mlandu. Anapeza anthu ambiri koma anthuwo ankapereka maumboni osiyana. Kenako panabwera anthu awiri omwe ananena kuti: “Ife tinamva iyeyu akunena kuti, ‘Ine ndidzagwetsa kachisi uyu amene anamangidwa ndi manja, ndipo m’masiku atatu okha ndidzamanga wina osati womangidwa ndi manja.’” (Maliko 14:58) Komabe umboni umene anthu awiriwa anapereka sunkagwirizana.
Kenako Kayafa anafunsa Yesu kuti: “Sukuyankha chilichonse? Kodi n’zoona zimene awa akukunenezazi?” (Maliko 14:60) Yesu sanayankhe chilichonse pa zinthu zabodza zimene mboni ziwiri zija zinanena. Ataona kuti sakuyankha, Kayafa yemwe anali mkulu wa ansembe anagwiritsanso ntchito njira ina n’cholinga choti Yesu alankhule.
Kayafa ankadziwa kuti Ayuda ankakwiya kwambiri akamva munthu aliyense akunena kuti ndi Mwana wa Mulungu. Nthawi ina m’mbuyomu Yesu atanena kuti Mulungu ndi Atate wake, Ayuda ankafuna kumupha chifukwa iwo ankaona kuti Yesu ‘akudziyesa wofanana ndi Mulungu.’ (Yohane 5:17, 18; 10:31-39) Chifukwa chodziwa zimenezi, Kayafa anafunsa Yesu mochenjera kuti: “Ndikukulumbiritsa pali Mulungu wamoyo, utiuze ngati ndiwedi Khristu Mwana wa Mulungu!” (Mateyu 26:63) N’zoona kuti Yesu anadzitchula kuti ndi Mwana wa Mulungu. (Yohane 3:18; 5:25; 11:4) Ngati Yesu akanakana zikanaoneka ngati akukana zoti ndi Mwana wa Mulungu komanso kuti ndi Khristu. Choncho anayankha kuti: “Inde ndinedi, ndipo anthu inu mudzaona Mwana wa munthu atakhala kudzanja lamanja lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera ndi mitambo yakumwamba.”—Maliko 14:62.
Yesu atangonena zimenezi, Kayafa anang’amba malaya ake n’kunena mokwiya kuti: “Wanyoza Mulungu! Nanga n’kufunanso mboni zina pamenepa? Pano mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu. Tsopano inu mukuona bwanji pamenepa?” A khoti la Sanihedirini anagwirizana ndi zimene Kayafa ananena moti anayankha kuti: “Ayenera kuphedwa basi.”—Mateyu 26:65, 66.
Kenako anthu anayamba kunyoza Yesu, kumumenya nkhonya ndipo ena anamumenya mbama komanso kumulavulira. Anamuphimba kumaso ndi kumumenya mbama, kenako anayamba kulankhula monyoza kuti: “Losera. Wakumenya ndani?” (Luka 22:64) Usiku umenewu Mwana wa Mulungu anazunzidwa kwambiri komanso anamuweruza mopanda chilungamo pa mlandu womwe anaweruza mosatsatira malamulo.
-
-
Petulo Anakana Yesu Kunyumba kwa KayafaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 126
Petulo Anakana Yesu Kunyumba kwa Kayafa
MATEYU 26:69-75 MALIKO 14:66-72 LUKA 22:54-62 YOHANE 18:15-18, 25-27
PETULO ANAKANA YESU
Yesu atagwidwa m’munda wa Getsemane atumwi anathawa chifukwa ankachita mantha. Koma mtumwi Petulo “ndiponso wophunzira wina” anayamba kutsatira gulu lomwe linagwira Yesu. Zikuoneka kuti wophunzira winayo anali mtumwi Yohane. (Yohane 18:15; 19:35; 21:24) N’kutheka kuti atumwi awiriwa anakumana ndi gulu lomwe linagwira Yesu pamene ankapita kunyumba kwa Anasi. Anasi atalamula kuti gulu la anthulo lipite ndi Yesu kwa Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe, Petulo ndi Yohane ankawatsatira chapatali. Atumwiwo ayenera kuti anali ndi mantha poganizira zimene zikanawachitikira komanso ankadera nkhawa Mbuye wawo.
Yohane ankadziwana ndi Kayafa choncho sanavutike kulowa pageti la kunyumba kwa Kayafa. Koma Petulo anadikirirabe panja pa geti mpaka pamene Yohane anabwera kudzapempha mtsikana yemwe ankagwira ntchito ngati mlonda kuti amulowetse. Kenako mtsikanayo analola kuti Petulo alowe.
Chifukwa choti usiku umenewo kunkazizira kwambiri, anthu amene anasonkhana panja pa nyumba ya Kayafa ankawotha moto. Petulo ankawotha nawo motowo podikirira “kuti aone zotsatira” za mlandu wa Yesu. (Mateyu 26:58) Chifukwa cha kuwala kwa motowo, mtsikana uja anazindikira Petulo ndipo ananena kuti: “Kodi inunso si inu mmodzi wa ophunzira a munthu ameneyu?” (Yohane 18:17) Koma si mtsikana yekhayo amene anazindikira Petulo, panalinso anthu ena amene anamuzindikira n’kunena kuti ankayenda ndi Yesu.—Mateyu 26:69, 71-73; Maliko 14:70.
Petulo atadziwa kuti anthuwo amuzindikira, anakhumudwa kwambiri chifukwa sankafuna kuti anthu amudziwe moti anachoka n’kukakhala pageti. Petulo anakana zoti ankayenda ndi Yesu, moti munthu wina atamufunsa iye ananena kuti: “Ngakhale kumudziwa, sindikumudziwa ameneyo, ndipo sindikumvetsa kuti ukunena chiyani.” (Maliko 14:67, 68) Petulo anayambanso “kutemberera ndi kulumbira,” zomwe zikutanthauza kuti anali wokonzeka kulumbira kuti zimene ankanenazo zinali zoona komanso kuti anali wokonzeka kukumana ndi mavuto aliwonse ngati zomwe ankanenazo zikanadziwika kuti si zoona.—Mateyu 26:74.
Pamene zimenezi zinkachitika, n’kuti mlandu wa Yesu uli mkati m’chipinda cham’mwamba cha nyumba ya Kayafa. Petulo komanso anthu ena amene ankadikirira pa bwalo la nyumbayo ankangoona anthu akutuluka komanso kulowa kukapereka umboni.
Petulo akamalankhula ankamveka kuti ndi wa ku Galileya choncho zinkachita kuonekeratu kuti zimene ankanena zinali zabodza. Komanso munthu wina pa gululo anali wachibale wake wa Makasi, yemwe Petulo anamudula khutu uja. Munthuyo anafunsa Petulo kuti: “Ndinakuona iwe m’munda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?” Petulo atakananso kachitatu tambala analira ngati mmene Yesu ananenera.—Yohane 13:38; 18:26, 27.
Zikuoneka kuti pamene tambala ankalira, Yesu anali ataima pakhonde la chipinda cham’mwamba lomwe linali moyang’anizana ndi pa bwalo pa nyumbayo. Yesu atatembenuka anaphana maso ndi Petulo. Petulo ayenera kuti anadzimvera chisoni kwambiri mumtima mwake chifukwa anakumbukira zimene Yesu ananena ali m’chipinda chomwe anadyeramoPasika chija. Ndiyeno tangoganizani mmene Petulo anamvera atazindikira kuti wakanadi Yesu katatu. Nthawi yomweyo anatuluka mumpandawo ndipo analira mopwetekedwa mtima kwambiri.—Luka 22:61, 62.
Koma chinachitika n’chiyani kuti Petulo, yemwe ankadziona kuti ndi wolimba mwauzimu komanso wokhulupirika, akane Mbuye wake? Pa nthawiyi anthu ankapotoza choonadi komanso ankachita zinthu zoti Yesu aoneke ngati chigawenga choopsa. Choncho m’malo moti Petulo aikire kumbuyo munthu amene anali wosalakwa, iye anakana Munthu ‘amene anali ndi mawu amoyo wosatha.’—Yohane 6:68.
Zimene zinachitikira Petulo zikutithandiza kudziwa kuti ngati munthu sanakonzekere bwinobwino, ngakhale atakhala wodzipereka kwambiri komanso atakhala ndi chikhulupiriro cholimba, akhoza kugwa mwauzimu atakumana ndi mavuto kapena zinthu zomwe zingayese chikhulupiriro chake mwadzidzidzi. Choncho atumiki onse a Mulungu ayenera kuphunzirapo kanthu pa zimene zinachitikira Petulo.
-