-
Khoti la Sanihedirini Linaweruza Mlandu wa Yesu Kenako Anapita Naye kwa PilatoYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 127
Khoti la Sanihedirini Linaweruza Mlandu wa Yesu Kenako Anapita Naye kwa Pilato
MATEYU 27:1-11 MALIKO 15:1 LUKA 22:66–23:3 YOHANE 18:28-35
YESU ANAIMBIDWANSO MLANDU NDI KHOTI LA SANIHEDIRINI M’MAWA
YUDASI ISIKARIYOTI ANADZIMANGIRIRA
YESU ANATUMIZIDWA KWA PILATO KUTI AKAIMBIDWE MLANDU
Pamene Petulo ankakana Yesu kachitatu n’kuti kutatsala pang’ono kucha. Oweruza a khoti la Sanihedirini omwe ankaimba Yesu mlandu mosatsatira malamulo anali atamaliza kuweruza mlanduwu komanso anali atabwerera kwawo. Pofika m’mawa, lomwe linali tsiku Lachisanu, oweruza aja anakumananso. Iwo anakumana pofuna kuchititsa anthu kuganiza kuti mlandu wa Yesu waweruzidwa m’mawa wa Lachisanulo potsatira malamulo. Anthuwa anabweranso ndi Yesu pa nthawi imeneyi.
Apanso anthuwa anafunsa Yesu kuti: “Tiuze ngati ndiwe Khristu.” Koma Yesu anawayankha kuti: “Ngakhale ndikuuzeni, simukhulupirira. Komanso nditakufunsani, simungathe n’komwe kuyankha.” Komabe Yesu anawafotokozera molimba mtima kuti iyeyo ndi ndani mogwirizana ndi zimene zinanenedwa kale m’buku la Danieli pa Danieli 7:13. Yesu ananena kuti: “Kuyambira tsopano Mwana wa munthu adzakhala kudzanja lamanja lamphamvu la Mulungu.”—Luka 22:67-69; Mateyu 26:63.
Anthuwo anapitirizabe kumufunsa kuti: “Kodi ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Yesu anawayankha kuti: “Inunso mukunena nokha kuti ndine amene.” Zikuoneka kuti Yesu atanena mawu amenewa, anthuwo anapeza chifukwa chomveka chomuimba mlandu wonyoza Mulungu n’cholinga choti amuphe. Anthuwa anafunsa kuti: “Tifuniranjinso umboni wina?” (Luka 22:70, 71; Maliko 14:64) Pamenepo anamanga Yesu n’kupita naye kwa wolamulira wachiroma dzina lake Pontiyo Pilato.
Mosakayikira Yudasi Isikariyoti anaona anthu amene anabwera kudzagwira Yesu akumutenga n’kupita naye kwa Pilato. Atazindikira kuti Yesu waweruzidwa kuti ayenera kuphedwa, anamva chisoni komanso kudziimba mlandu. Koma m’malo molapa kwa Mulungu, Yudasi anapita kukabweza ndalama 30 zasiliva zija. Iye anauza ansembe aakulu kuti: “Ndachimwa popereka munthu wolungama.” Koma anthuwa sanamumvere chisoni moti anamuyankha kuti: “Ife sizikutikhudza zimenezo. Udziwa wekha chochita!”—Mateyu 27:4.
Kenako Yudasi anaponya ndalama 30 zasiliva zija m’kachisimo ndipo anakonza zongodzipha. Pamene ankadzimangirira, nthambi ya mtengo umene anamangapo chingwe inathyoka ndipo anagwera pamiyala moti anaphulika.—Machitidwe 1:17, 18.
Pamene anthuwo ankapita ndi Yesu kunyumba kwa Pontiyo Pilato n’kuti kudakali m’mawa. Koma Ayuda amene anamutengawo anakana kulowa m’nyumba chifukwa ankaona kuti kulowa m’nyumba ya munthu yemwe sanali Myuda kukanawachititsa kuti akhale odetsedwa. Ndipo ngati akanakhala odetsedwa, sakanayenera kudya nawo chakudya cha pa Nisani 15, lomwe linali tsiku loyamba la Chikondwerero cha Mkate Wopanda Chofufumitsa. Chikondwererochi chinkachitikanso pa nthawi imene ankachita mwambo wa Pasika.
Ndiyeno Pilato anatuluka m’nyumba yake n’kufunsa anthuwo kuti: “Kodi mukumuimba mlandu wanji munthu ameneyu?” Anthuwo anayankha kuti: “Munthu uyu akanakhala wosachita zoipa, sitikanabwera naye kwa inu.” N’kutheka kuti Pilato anaona kuti anthuwo akumukakamiza kuchita zimene iyeyo sakufuna, choncho ananena kuti: “M’tengeni eniakenu mukamuweruze mogwirizana ndi chilamulo chanu.” Zimene Ayudawo anayankha zinasonyeza kuti ankafunadi kupha Yesu chifukwa ananena kuti: “N’zosaloleka kwa ife kupha munthu aliyense.”—Yohane 18:29-31.
Ngati Ayuda akanapha Yesu pa nthawi ya chikondwerero cha Pasika anthu akanachita zachipolowe. Koma ngati Ayudawo akanachititsa Aroma kuti aphe Yesu pa mlandu woukira boma, ndiye kuti anthu sakanawaimba mlandu. Pa nthawiyi Aroma ankaloledwa kupha munthu ngati waukira boma.
Atsogoleri achipembedzo sanauze Pilato kuti anali atapeza Yesu ndi mlandu wonyoza Mulungu. Choncho anayamba kupeka zifukwa zina. Iwo ananena kuti: ‘Ife tapeza munthu uyu [1] akupandutsa mtundu wathu, [2] akuletsa anthu kuti asamakhome msonkho kwa Kaisara, komanso [3] akunena kuti ndi Khristu mfumu.’—Luka 23:2.
Pilato, yemwe ankaimira ulamuliro wa Aroma, anada nkhawa kwambiri atamva kuti Yesu ankanena kuti ndi mfumu. Pilato analowanso m’nyumba mwake kenako anaitana Yesu n’kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?” Pofunsa funso limeneli, zinali ngati Pilato akufunsa kuti, ‘Kodi ukuphwanya dala lamulo la mu ufumu wa Aroma ponena kuti ndiwe mfumu pomwe mfumu ina ilipo kale, yomwe ndi Kaisara?’ Yesu ankafuna kudziwa kuti Pilato anamva zotani zokhudza iyeyo, choncho anamufunsa kuti: “Kodi zimenezi mukunena nokha, kapena ena akuuzani za ine?”—Yohane 18:33, 34.
Pilato anayankha ngati kuti sankadziwa kena kalikonse kokhudza Yesu koma anasonyeza ngati ali ndi chidwi choti amudziwe. Iye anayankha Yesu kuti: “Kodi ine ndine Myuda ngati?” Ananenanso kuti: “Anthu a mtundu wako omwe ndi ansembe aakulu ndi amene akupereka kwa ine. Kodi unachita chiyani?”—Yohane 18:35.
Yesu sanayese kuthawa nkhani yonena za Ufumu ndipo zimene anayankha zinadabwitsa kwambiri Pilato.
-
-
Pilato Komanso Herode Sanamupeze Yesu ndi MlanduYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 128
Pilato Komanso Herode Sanamupeze Yesu ndi Mlandu
MATEYU 27:12-14, 18, 19 MALIKO 15:2-5 LUKA 23:4-16 YOHANE 18:36-38
PILATO KOMANSO HERODE ANAFUNSA YESU MAFUNSO
Yesu sanabise kwa Pilato kuti iye ndi mfumu. Ngakhale kuti anayankha zimenezi, ufumu wake sunali woti ulowe m’malo mwa ulamuliro wa Aroma. Yesu ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” (Yohane 18:36) Ndi zoona kuti Yesu ndi Mfumu koma Ufumu wake si wochokera padzikoli.
Koma Pilato sanasiyire nkhaniyo pomwepo. Iye anafunsanso kuti: “Chabwino, koma kodi ndiwe mfumu?” Yesu anathandiza Pilato kudziwa kuti akuganiza molondola chifukwa anamuyankha kuti: “Mukunena nokha kuti ndine mfumu. Chimene ndinabadwira, ndiponso chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvera mawu anga.”—Yohane 18:37.
Nthawi ina Yesu anauza Tomasi kuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo.” Ndiyeno pa nthawiyi Pilato anamva Yesu akunena kuti anatumizidwa padziko lapansi kuti adzachitire umboni “choonadi” ndipo choonadi chimenechi ndi chonena za Ufumu wake. Yesu anali wokonzeka kukhala wokhulupirika poikira kumbuyo choonadichi ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti aphedwe. Pilato anamufunsa kuti: “Choonadi n’chiyani?” koma sanadikire kuti Yesu amufotokozere. Iye ankaona kuti wamva mfundo zokwanira moti atha kumuweruza Yesu.—Yohane 14:6; 18:38.
Pilato anabwereranso panja pomwe panali gulu la anthu. Iye anauza ansembe aakulu komanso anthu ena omwe anali nawo kuti: “Sindikupeza mlandu uliwonse mwa munthu uyu.” Pamene ankanena mawu amenewa Yesu anali ataima pambali pake. Gulu la anthulo linakwiya kwambiri ndi zimene Pilato ananenazi ndipo linkakuwa kuti: “Iyeyu akusokoneza anthu mwa kuphunzitsa mu Yudeya monse, ngakhalenso kuyambira ku Galileya mpaka kudzafika kuno.”—Luka 23:4, 5.
Pilato ayenera kuti anadabwa kwambiri ataona kuti Ayudawo ankakakamira kuti Yesu ali ndi mlandu. Pamene ansembe aakulu komanso akulu ankakuwa, Pilato anafunsa Yesu kuti: “Kodi sukumva zonse zimene akukunenezazi?” (Mateyu 27:13) Yesu sanayankhe kalikonse. Ngakhale kuti anthu ankamunamizira zinthu zambiri zoipa, Pilato anadabwa kuti pa nthawi yonseyi Yesu anali wodekha.
Ayuda ananena kuti Yesu anasokoneza anthu ‘kuyambira ku Galileya.’ Atamva zimenezi Pilato anadziwa kuti Yesu anali wa ku Galileya. Choncho Pilato anapezerapo mwayi wofuna kuthawa udindo woweruza Yesu. Herode Antipa (yemwe anali mwana wa Herode Wamkulu) ndi amene ankalamulira ku Galileya ndipo pa nthawiyi n’kuti ali ku Yerusalemu ku mwambo wa Pasika. Ndiyeno Pilato anatumiza Yesu kwa Herode. Herode Antipa ndi amene analamula kuti Yohane M’batizi adulidwe mutu. Yohane M’batizi ataphedwa, Herode anamva kuti Yesu akuchita zinthu zodabwitsa moti iye anayamba kuganiza kuti Yesu ndi Yohane ndipo wauka kwa akufa.—Luka 9:7-9.
Herode anasangalala atadziwa kuti akumana ndi Yesu. Sikuti ankasangalala chifukwa chakuti ankafuna kuthandiza Yesu kapenanso kuti ankafuna kumva ngati panalidi zifukwa zomveka zoimbira Yesu mlandu. Iye ankangofuna kuona Yesu ndipo ‘ankayembekezera kuona chizindikiro chimene iye angachite.’ (Luka 23:8) Koma Yesu sanachite zimene Herode ankayembekezera ndipo pamene ankamufunsa mafunso, Yesu sanayankhe chilichonse. Chifukwa chokhumudwa, Herode ndi asilikali ake ‘anapeputsa’ Yesu kapena kuti kumuchititsa manyazi. (Luka 23:11) Anamuveka chovala chonyezimira ndipo anamuchitira zachipongwe. Kenako Herode analamula kuti Yesu abwererenso kwa Pilato. M’mbuyomu, Herode ndi Pilato sankagwirizana koma kungoyambira nthawi imeneyi anayamba kugwirizana.
Yesu atafikanso kwa Pilato, Pilato anasonkhanitsa ansembe aakulu, olamulira a Ayuda komanso gulu la anthu n’kuwauza kuti: “Inetu ndamufunsa pamaso panu, ndipo sindinamupeze ndi chifukwa chomuimbira milandu imene mukumunenezayi. Ndipotu ngakhale Herode sanam’peze ndi mlandu, n’chifukwa chake wam’bweza kwa ife. Ndithudi ameneyu sanachite chilichonse choyenera chilango cha imfa. Choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”—Luka 23:14-16.
Pilato ankafunitsitsa kumasula Yesu atadziwa kuti ansembe anapereka Yesu chifukwa chakuti ankadana naye. Koma panalinso chifukwa china chimene Pilato ankafunira kumasula Yesu. Atakhala pampando wake woweruzira, mkazi wake anamutumizira uthenga wonena kuti: “Nkhani ya munthu wolungamayu isakukhudzeni. Inetu ndavutika kwambiri lero m’maloto [amene Mulungu anamulotetsa] chifukwa cha iyeyu.”—Mateyu 27:19.
Popeza Pilato anali ndi mphamvu zomasula Yesu, kodi anakwanitsadi kuchita zimenezi?
-
-
Pilato Ananena Kuti: “Taonani! Mwamuna Uja ndi Uyu!”Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 129
Pilato Ananena Kuti: “Taonani! Mwamuna Uja Ndi Uyu!”
MATEYU 27:15-17, 20-30 MALIKO 15:6-19 LUKA 23:18-25 YOHANE 18:39–19:5
PILATO ANAYESA KUMASULA YESU
AYUDA ANAPEMPHA KUTI AWAMASULIRE BARABA
YESU ANAZUNZIDWA KOMANSO ANAMUCHITIRA ZACHIPONGWE
Pilato anauza anthu amene ankafuna kuti Yesu aphedwe kuti: “Inetu . . . sindinamupeze ndi chifukwa chomuimbira milandu imene mukumunenezayi. Ndipotu ngakhale Herode sanam’peze ndi mlandu.” (Luka 23:14, 15) Chifukwa chakuti Pilato ankafuna kumasula Yesu, anagwiritsa ntchito njira ina. Iye anauza anthuwo kuti: “Muli ndi mwambo wakuti ndizikumasulirani munthu mmodzi pa pasika. Kodi mukufuna ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?”—Yohane 18:39.
Pilato ankadziwa munthu wina dzina lake Baraba yemwe anali m’ndende chifukwa chakuti anali wakuba, woukira boma komanso chigawenga. Ndiyeno anafunsa anthuwo kuti: “Kodi mukufuna ndikumasulireni ndani, Baraba kapena Yesu, uja amamuti Khristu?” Anthuwo ananena kuti awamasulire Baraba osati Yesu. Iwo ananena zimenezi chifukwa anachita kuuzidwa ndi ansembe aakulu. Pamenepo Pilato anafunsanso kuti: “Ndani mwa awiriwa amene mukufuna kuti ndikumasulireni?” Gulu la anthulo linafuula kuti: “Baraba.”—Mateyu 27:17, 21.
Pilato atakhumudwa ndi zimene anthuwo anayankha, anawafunsa kuti: “Nanga Yesu, uja amamuti Khristu, ndichite naye chiyani?” Anthuwo anafuula kuti: “Apachikidwe ameneyo!” (Mateyu 27:22) N’zomvetsa chisoni kuti anthuwa ankafuna kuti munthu yemwe anali wosalakwa aphedwe. Ndiyeno Pilato anafunsa kuti: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani? Ine sindikumupeza ndi chifukwa chilichonse chomuphera, choncho ndimukwapula ndi kumumasula.”—Luka 23:22.
Pilato anayesetsa kuti amasule Yesu koma anthu okwiyawo anafuula kuti: “Apachikidwe basi!” (Mateyu 27:23) Atsogoleri achipembedzo ndi amene anasokoneza maganizo a anthuwa n’cholinga choti aphetse Yesu yemwe anali munthu wosalakwa. Ndipotu masiku 5 m’mbuyomo Yesu yemweyu ndi amene analowa mu Yerusalemu ngati Mfumu ndipo anthu anamulandira ndi manja awiri. Ngati ophunzira a Yesu analipo pa nthawi imene anthu ankafuula kuti Yesu apachikidwe, ndiye kuti sanalankhule kalikonse komanso sankafuna kuti anthu awazindikire.
Ndiyeno Pilato anazindikira kuti zimene ankafuna kuchita kuti amasule Yesu sizitheka. Gulu la anthulo litayamba kuchita zachipolowe, Pilato anatenga madzi n’kusamba m’manja anthuwo akuona. Kenako anawauza kuti: “Ndilibe mlandu wa magazi a munthu uyu. Zonse zili kwa inu.” Ngakhale kuti Pilato analankhula zimenezi anthuwo sanasinthe maganizo awo. M’malomwake anamuyankha kuti: “Magazi ake akhala pa ife ndi pa ana athu.”—Mateyu 27:24, 25.
Pofuna kusangalatsa anthuwo, Pilato anachita zinthu zomwe ankadziwa kuti sizoyenera. Anamasula Baraba mogwirizana ndi zomwe anthuwo ankafuna koma anamuvula Yesu malaya kenako n’kumukwapula.
Asilikali atamaliza kumenya Yesu analowa naye m’nyumba. Gulu la asilikalilo linasonkhananso ndipo linapitiriza kumuchitira zinthu zachipongwe. Asilikaliwo analuka chisoti chachifumu chaminga chomwe anachikanikiza m’mutu mwake. Anapatsanso Yesu bango kuti atenge kudzanja lake lamanja ndipo anamuveka chinsalu chofiira chomwe nthawi zambiri ankavala ndi anthu olemekezeka. Kenako anayamba kumunena monyoza kuti: “Mtendere ukhale nanu, inu Mfumu ya Ayuda!” (Mateyu 27:28, 29) Kuwonjezera pamenepo ankamulavulira komanso kumumenya mbama. Anamulandanso bango lija n’kuyamba kumumenya nalo m’mutu, ndipo zimenezi zinkachititsa kuti minga za “chisoti chachifumu” chija zimubaye kwambiri m’mutu.
Pilato anachita chidwi kwambiri ataona kuti Yesu anali wodekha komanso wolimba mtima pa nthawi yonse imene anthu ankamuchitira zinthu zachipongwe. Choncho pofuna kuti asapezeke wolakwa pa mlanduwu, Pilato anafunanso kumasula Yesu ndipo ananena kuti: “Onani! Ndikumutulutsa panja pano kwa inu, kuti mudziwe kuti sindikupeza mlandu mwa iye.” Mwina Pilato anatulutsa Yesu ali ndi mabala komanso akutuluka magazi n’cholinga choti anthuwo asinthe maganizo awo. Ndiyeno Yesu ataimirira pamaso pa anthu ouma mtimawo, Pilato ananena kuti: “Taonani! Mwamuna uja ndi uyu!”—Yohane 19:4, 5.
Ngakhale kuti Yesu anali atamenyedwa komanso kuvulazidwa anakhalabe wodekha moti ngakhale Pilato analankhula mwaulemu komanso mosonyeza kuti ankamumvera chisoni.
-
-
Pilato Anapereka Yesu Ndipo Anthu Anamutenga Kuti AkamupheYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 130
Pilato Anapereka Yesu Ndipo Anthu Anamutenga Kuti Akamuphe
MATEYU 27:31, 32 MALIKO 15:20, 21 LUKA 23:24-31 YOHANE 19:6-17
PILATO ANAYESANSO KUMASULA YESU
YESU ANAWERUZIDWA NDIPO ANAMUTENGA KUTI AKAMUPHE
Yesu anazunzidwa kwambiri komanso kunyozedwa moti Pilato anayesa kangapo kuti amumasule. Ngakhale kuti Pilato anachita zimenezi, ansembe aakulu komanso otsatira awo sanasinthe maganizo. Iwo ankangofuna kuti Yesu aphedwe basi. Ankangofuula kuti: “M’pachikeni! M’pachikeni!” Koma Pilato anawauza kuti: “M’tengeni mukamupachike nokha, chifukwa ine sindikupeza mlandu uliwonse mwa iye.”—Yohane 19:6.
Ayuda analephera kupereka zifukwa zomveka zomwe zikanachititsa Pilato kuweruza kuti Yesu aphedwe pa mlandu woukira boma, m’malomwake anayambanso kumuimba mlandu wokhudza chipembedzo. Anthuwa anabwerezanso mlandu womwe anamunamizira ku khoti la Sanihedirini uja, woti Yesu ankanyoza Mulungu. Iwo ananena kuti: “Tili ndi chilamulo ife, ndipo malinga ndi chilamulocho iyeyu ayenera kufa, chifukwa akudziyesa mwana wa Mulungu.” (Yohane 19:7) Umenewu unali ngati mlandu winanso watsopano womwe Pilato ankafunika kuweruza.
Pilato anabwerera m’nyumba mwake kuti akaganizirenso zomwe angachite kuti amasule Yesu. Pa nthawiyi Yesu anali atazunzika kwambiri komanso mkazi wa Pilato analota zokhudza Yesu. (Mateyu 27:19) Koma kodi Pilato anaweruza bwanji mlandu winawu womwe Ayuda ankaimba Yesu woti ndi “mwana wa Mulungu”? Pilato ankadziwa kuti Yesu ndi wa ku Galileya. (Luka 23:5-7) Komabe anamufunsa kuti: “Kodi umachokera kuti?” (Yohane 19:9) Mwina Pilato anafunsa Yesu funso limeneli poganiza kuti Yesu anakhalapo ndi moyo kalekale ndiponso kuti mwina anachokera kumwamba.
Pilato anamva Yesu akunena yekha kuti ndi mfumu koma Ufumu wake suli mbali ya dzikoli. Yesu anaona kuti sakufunika kufotokozera Pilato zinthu zambiri zokhudza ufumu zomwe anali atamuuzapo m’mbuyomo, choncho anangokhala chete. Chifukwa chakuti Yesu sanamuyankhe, Pilato anapsa mtima ndipo ananena mokwiya kuti: “Kodi sukundilankhula? Kodi sukudziwa kuti ine ndili ndi mphamvu yokumasula, komanso yokupachika?”—Yohane 19:10.
Koma Yesu anangoyankha kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba. Ndiye chifukwa chake munthu amene wandipereka ine kwa inu ali ndi tchimo lalikulu kwambiri.” (Yohane 19:11) Ponena mawu amenewa, Yesu sankatanthauza kuti ndi munthu mmodzi yekha amene anali ndi mlandu womupereka. Iye ankatanthauza kuti Kayafa, anthu ena omwe ankamuthandiza kuweruza mlanduwu komanso Yudasi Isikariyoti anali ndi mlandu waukulu wopereka Yesu poyerekeza ndi Pilato.
Pilato anayesanso kumasula Yesu chifukwa chakuti anagoma kwambiri ndi zimene Yesuyo analankhula komanso mmene ankaonekera. Iye ankaopanso kuti mwina Yesu akhoza kukhala kuti anachokera kumwamba. Koma Ayuda ananenanso zinthu zina zomwe zinachititsa mantha Pilato. Iwo anamuopseza kuti: “Mukamumasula ameneyu, ndiye kuti si inu bwenzi la Kaisara. Munthu aliyense wodziyesa yekha mfumu, ameneyo ndi wotsutsana ndi Kaisara.”—Yohane 19:12.
Pilato anatulutsanso Yesu panja ndipo iye anakhala pa mpando woweruzira kenako anauza Ayudawo kuti: “Taonani! Mfumu yanu imeneyi!” Koma Ayudawo sanavomereze zimenezo moti anafuula kuti: “Muthane naye! Muthane naye! M’pachikeni!” Pilato anawafunsa kuti: “Kodi ndipachike mfumu yanu?” Ngakhale kuti Ayuda ankadana ndi ulamuliro wa Aroma koma n’zodabwitsa kuti pa nthawiyi, ansembe aakulu ananena molimba mtima kuti: “Tilibe mfumu ina koma Kaisara.”—Yohane 19:14, 15.
Chifukwa cha mantha, Pilato anachita zimene Ayudawo ankafuna. Anapereka Yesu kuti akaphedwe. Asilikali anamuvula chovala chofiira chija n’kumuveka malaya ake akunja. Pamene Yesu ankapita kumene ankati akamuphereko, ananyamula yekha mtengo wake wozunzikirapo.
Pamene asilikali ankamutenga Yesu kuti akamuphe n’kuti kuli chakum’mawa Lachisanu, pa Nisani 14. Yesu ayenera kuti anali atatopa kwambiri chifukwa sanagone kuchokera Lachinayi m’mawa ndipo kungoyambira nthawi imeneyo anakumana ndi mavuto ambiri. Chifukwa chakuti mtengowo unali wolemera kwambiri, Yesu anatopa kwambiri moti sanakwanitsenso kuyenda. Choncho asilikali omwe ankayenda naye anakakamiza munthu wina yemwe ankangodziyendera kuti anyamule mtengowo mpaka kumene ankapita. Munthuyo anali Simoni wochokera ku Kurene, ku Africa. Anthu ambiri ankatsatira Yesu ndipo ena ankadziguguda chifukwa cha chisoni, pomwe ena ankangolira chifukwa cha zimene zinkachitikazo.
Yesu anauza azimayi ena omwe ankalira kuti: “Ana aakazi a Yerusalemu inu, lekani kundilirira. Koma mudzilirire nokha ndi ana anu. Chifukwa masiku akubwera pamene anthu adzanena kuti, ‘Odala ndi akazi osabereka, amene sanaberekepo, komanso amene mabere awo sanayamwitsepo!’ M’masiku amenewo iwo adzayamba kuuza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza zitunda kuti, ‘Tikwirireni!’ Pakuti ngati akuchita izi pamene mtengo uli wauwisi, kuli bwanji mtengowo ukadzauma?”—Luka 23:28-31.
Ponena mawu amenewa Yesu ankanena za mtundu wa Ayuda. Anayerekezera mtunduwu ndi mtengo womwe ukuuma koma udakali wauwisi pang’ono. Mtengowo unali udakali wauwisi chifukwa iye anali adakalipo komanso kuti panali Ayuda ena ochepa omwe ankamukhulupirira. Koma nthawi inafika pamene Ayuda okhulupirika anachoka pakati pa mtunduwo ndipo zinali ngati mtengowo wafa chifukwa unangokhala mtundu wakufa mwauzimu. Zinali zomvetsa chisoni pamene asilikali achiroma anabwera n’kudzawononga mtunduwu. Pa nthawiyi zinali ngati kuti Mulungu akugwiritsira ntchito Aromawo kuti alange mtundu wa Ayuda.
-
-
Mfumu Yosalakwa Inavutika Itapachikidwa PamtengoYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 131
Mfumu Yosalakwa Inavutika Itapachikidwa Pamtengo
MATEYU 27:33-44 MALIKO 15:22-32 LUKA 23:32-43 YOHANE 19:17-24
ANTHU ANAKHOMERERA YESU PAMTENGO WOZUNZIKIRAPO
CHIKWANGWANI CHIMENE ANAKHOMA PAMTENGO WA YESU CHINACHITITSA KUTI ANTHU AMUNYOZE
YESU ANALONJEZA MUNTHU WINA KUTI ADZAKHALA NDI MOYO M’PARADAISO PADZIKO LAPANSI
Asilikali achiroma anatenga Yesu komanso anthu awiri omwe anali akuba kuti akawaphe. Anthuwa anapita nawo kumalo otchedwa Gologota kapena kuti Malo a Chibade omwe anali pafupi ndi mzinda. Munthu ankatha kuona zimene zinkachitika pamalowa ngakhale ataima “chapatali.”—Maliko 15:40.
Atafika pamalowa anawavula zovala n’kuwapatsa vinyo wosakaniza ndi mule komanso ndulu. Azimayi omwe ankakhala ku Yerusalemu ndi amene ankakonza vinyoyu ndipo vinyoyu ankathandiza kuti anthu amene akupita kukaphedwawo asamve kupweteka kwambiri. Aroma sankaletsa kuti anthu omwe akukaphedwa amwe vinyoyo. Koma Yesu atalawa vinyoyo anakana kuti amwe. N’chifukwa chiyani anakana? Iye ankafuna kuti pa nthawi yovutayi asasokonezeke maganizo, zomwe zikanamuthandiza kudziwa chilichonse chimene chinkachitika komanso ankafuna kuti akhale wokhulupirika mpaka pamapeto a moyo wake.
Yesu anamugoneka pamtengo womwe ankafuna kum’pachikawo. (Maliko 15:25) Asilikali aja anakhomerera manja ndi mapazi a Yesu ndi misomali zomwe zinachititsa kuti amve kupweteka kwambiri. Pamene ankadzutsa mtengowo, Yesu anamva kupweteka kwambiri chifukwa kulemera kwa thupi lake kunkachititsa kuti mmene anamukhomerera ndi misomali muja muzing’ambika. Koma Yesu sanakalipire asilikaliwo m’malomwake anapemphera kuti: “Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa chimene akuchita.”—Luka 23:34.
Aroma ankati akapachika munthu, ankaika chikwangwani chomwe ankalembapo mlandu umene munthuyo wapalamula. Pa nthawi imene ankapachika Yesu, Pilato analemba chikwangwani chonena kuti: “Yesu Mnazareti, Mfumu ya Ayuda.” Analemba mawu amenewa mu Chiheberi, Chilatini ndi Chigiriki moti aliyense ankatha kuwerenga. Zimene Pilato analembazi zinasonyeza kuti anadana kwambiri ndi Ayuda omwe anakakamira kuti Yesu aphedwe. Ansembe aakulu anakwiya ndi zimenezi ndipo anamuuza Pilato kuti “Musalembe kuti ‘Mfumu ya Ayuda,’ koma kuti iye ananena kuti, ‘Ndine Mfumu ya Ayuda.’” Koma Pilato sanafunenso kuti achite zimene Ayudawo ankafuna ndipo anawayankha kuti: “Zimene ndalemba, ndalemba.”—Yohane 19:19-22.
Chifukwa chokwiya, ansembewo anabwerezanso umboni wabodza umene ananena poimba Yesu mlandu ku khoti la Sanihedirini. N’chifukwa chake anthu amene ankadutsa pamalopo ankangopukusa mitu yawo n’kumanena monyoza kuti: “Iwe wogwetsa kachisi ndi kum’manga m’masiku atatu, dzipulumutse. Tsika pamtengo wozunzikirapowo.” Nawonso ansembe aakulu ndi alembi ankanena monyoza kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikum’kanika! Tsopanotu Khristu, Mfumu ya Isiraeli, itsike pamtengo wozunzikirapowo, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” (Maliko 15:29-32) Nazonso zigawenga zija zinayamba kunyoza Yesu ngakhale kuti anali wosalakwa. Chigawenga china chinali kudzanja lamanzere ndipo china chinali kumanja kwake.
Asilikali 4 achiroma omwe anali pamalopo anayambanso kumuseka Yesu. Asilikaliwa ayenera kuti ankamwa vinyo wowawasa ndiye pofuna kunyoza Yesu anatenga vinyo wina n’kumuyandikitsa kukamwa kwake, ngakhale kuti sakanatha kulandira kuti amwe. Aroma ataona zimene zinalembedwa pa chikwangwani chomwe anachikhomerera pamwamba pamtengo wa Yesu, anayamba kumunyoza kuti: “Ngati ulidi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” (Luka 23:36, 37) Zimenezitu zinali zomvetsa chisoni kwambiri. Munthu yemwe anasonyeza kuti anali njira, choonadi ndi moyo ananyozedwa komanso anamuchitira zachipongwe. Koma anapirira zonsezi molimba mtima popanda kunyoza asilikali achiroma omwe ankamuchitira zachipongwe, Ayuda omwe ankaonerera zomwe zinkachitikazo komanso zigawenga ziwiri zomwe zinapachikidwa naye limodzi.
Asilikali 4 omwe ankalondera Yesu, anatenga malaya ake akunja n’kuwagawa m’zigawo 4 ndipo anachita mayere kuti agawane. Koma malaya am’kati a Yesu anali apamwamba kwambiri chifukwa “analibe msoko, anali owombedwa kuchokera pamwamba mpaka pansi.” Asilikaliwo anakambirana kuti: “Malaya awa tisawang’ambe, koma tiyeni tichite maere kuti tidziwe amene angatenge malaya amenewa.” Pochita zimenezi anakwaniritsa zimene Malemba amanena kuti: “Iwo anagawana malaya anga akunja pakati pawo, ndipo anachita maere pa malaya anga amkati.”—Yohane 19:23, 24; Salimo 22:18.
Patapita nthawi, mmodzi wa zigawenga zija anazindikira kuti Yesu analidi mfumu. Munthu ameneyu anadzudzula mnzakeyo ndipo ananena kuti: “Kodi iwe suopa Mulungu eti, poona kuti nawenso ukulandira chilango chofanana ndi cha munthu ameneyu? Ifetu m’pake kulangidwa chonchi, pakuti tikulandiriratu zonse zotiyenera malinga ndi zimene tinachita. Koma munthu uyu sanalakwe chilichonse.” Kenako anapempha Yesu kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.”—Luka 23:40-42.
Yesu anamuyankha kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine” osati mu Ufumu koma “m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Zimene Yesu analonjeza munthuyu zinali zosiyana ndi zimene analonjeza atumwi ake. Iye anauza atumwi ake kuti adzakhala pamipando yachifumu pamodzi ndi iyeyo mu Ufumu. (Mateyu 19:28; Luka 22:29, 30) Koma zikuoneka kuti munthuyu, yemwe anali Myuda, anamvapo za Paradaiso wa padziko lapansi yemwe Yehova anapatsa Adamu ndi Hava kuti akhalemo ndi ana awo. Tsopano munthuyu anafa ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi.
-
-
“Ndithudi munthu uyu Analidi Mwana wa Mulungu”Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 132
“Ndithudi Munthu Uyu Analidi Mwana wa Mulungu”
MATEYU 27:45-56 MALIKO 15:33-41 LUKA 23:44-49 YOHANE 19:25-30
YESU ANAFERA PAMTENGO
PAMENE YESU ANKAFA PANACHITIKA ZINTHU ZODABWITSA
Tsopano nthawi inali “cha m’ma 12 koloko” masana, ndipo kunagwa mdima womwe unali wodabwitsa “m’dziko lonselo mpaka 3 koloko masana.” (Maliko 15:33) Mdimawu sunachitike chifukwa cha kadamsana. Kadamsana amachitika mwezi ukangoyamba kumene kuoneka koma zimenezi zinachitika pa nthawi imene anthu ankachita mwambo wa Pasika ndipo pa nthawi imeneyi mwezi umaoneka wathunthu. Mdima umenewu unatenga nthawi yaitali poyerekeza ndi nthawi ya mdima wa kadamsana womwe umangotenga maminitsi ochepa. Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu ndi amene anachititsa mdima umenewu.
Kodi anthu omwe ankanyoza Yesu anatani ataona zimenezi? Nthawi imene kunachita mdimawu azimayi 4 anafika pafupi ndi mtengo umene anapachikapo Yesu. Azimayiwa anali Mariya mayi ake a Yesu, Salome, Mariya Mmagadala ndi Mariya yemwe anali mayi a mtumwi Yakobo Wamng’ono.
Mtumwi Yohane anali ndi mayi ake a Yesu omwe ankalira “chapafupi ndi mtengo wozunzikirapo.” Mariya ankangoyang’anitsitsa mwana wake yemwe anamubereka ndi kumulera, atapachikidwa pamtengo komanso akuvutika ndi ululu. Mariya ankangoona ngati kuti “lupanga lalitali” lalasa moyo wake. (Yohane 19:25; Luka 2:35) Ngakhale kuti Yesu ankamva kupweteka kwambiri, ankaganizira za moyo wa mayi ake. Movutikira kwambiri anayang’ana Yohane ndikuuza mayi akewo kuti: “Mayi, kuyambira lero, uyu akhala mwana wanu.” Kenako anayang’ananso Mariya n’kuuza Yohane kuti: “Kuyambira lero awa akhala mayi ako.”—Yohane 19:26, 27.
Yesu anapatsa mtumwi yemwe ankamukonda udindo wosamalira mayi ake, omwe pa nthawiyi anali mkazi wamasiye. Pa nthawiyi Yesu ankadziwa kuti ana ena a Mariya, omwe anali abale ake, anali asanayambe kumukhulupirira. Choncho pamene Yesu ankapereka udindowu kwa Yohane ankatanthauza kuti Yohane ayenera kusamalira Mariya pa zinthu zauzimu komanso pa zinthu zofunika pa moyo wake wa tsiku ndi tsiku. Pamenepatu Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri.
Mdima uja utangotsala pang’ono kutha, Yesu ananena kuti: “Ndikumva ludzu.” Zimenezi zinakwaniritsa ulosi wina womwe unalembedwa kalekale. (Yohane 19:28; Salimo 22:15) Yesu anazindikira kuti Atate ake sankamutetezanso n’cholinga choti asonyeze kuti ndi wokhulupirika mpaka pa mapeto a moyo wake. Kenako Yesu anafuula mwina mu chilankhulo cha Chiaramu chomwe anthu a ku Galileya ankalankhula kuti: “Eli, Eli, lama sabachthani?” Mawuwa amatanthauza kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” Anthu ena omwe anaima pafupi naye sanamvetse zomwe ananena moti ananena kuti: “Tamverani! Akuitana Eliya.” Ndiyeno munthu wina anathamanga n’kutenga bango lomwe anaikako chinkhupule chomwe kenako anachiviika m’vinyo wowawasa ndipo anapatsa Yesu kuti amwe. Koma anthu ena ananena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”—Maliko 15:34-36.
Kenako Yesu anafuula kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” (Yohane 19:30) Yesu anali atakwaniritsadi zimene Atate wake anamutuma kuti adzachite padziko lapansi. Pamapeto pake Yesu ananena kuti: “Atate, ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.” (Luka 23:46) Ponena mawu amenewa Yesu anasonyeza kuti ankapereka moyo wake m’manja mwa Yehova ndipo ankakhulupirira kuti amuukitsa. Kenako Yesu anaweramitsa mutu wake n’kutsirizika.
Yesu atangomwalira kunachitika chivomezi champhamvu chomwe chinaswa miyala. Chivomezichi chinali champhamvu moti manda omwe anali kunja kwa mzinda wa Yerusalemu anatseguka ndipo mitembo ya anthu inaponyedwa kunja. Anthu omwe ankadutsa m’mbali mwa mandawo ataona mitemboyo analowa “mumzinda woyera” ndipo anauza anthu zomwe anaona.—Mateyu 12:11; 27:51-53.
Yesu atangomwalira, chinsalu chachikulu chomwe chinkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa chinang’ambika pakati, kuchokera pamwamba mpaka pansi. Zimene zinachitikazi zinasonyeza kuti Mulungu anakwiyira anthu amene anapha Mwana wake komanso zinatanthauza kuti tsopano anthu anali ndi mwayi wopita kumwamba, komwe ndi Malo Oyera Koposa.—Aheberi 9:2, 3; 10:19, 20.
Anthu amene anaona zimene zinachitika Yesu atamwalira anachita mantha ndipo mpake kuti anachitadi mantha. Kapitawo wa asilikali amene analipo pamene Yesu ankaphedwa ananena kuti: “Ndithudi munthu uyu analidi Mwana wa Mulungu.” (Maliko 15:39) N’kutheka kuti msilikaliyu analipo pa nthawi imene Pilato ankaweruza Yesu pa mlandu woti ndi Mwana wa Mulungu. Koma tsopano anali ndi umboni woti Yesu sanalakwe chilichonse komanso kuti ndi Mwana wa Mulungu.
Anthu ena amene anaona zomwe zinachitikazo anabwerera ku nyumba zawo “akudziguguda pachifuwa” posonyeza kuti ali ndi chisoni komanso manyazi. (Luka 23:48) Ena anthu amene ankaona zochitikazo chapatali anali azimayi amene nthawi zina ankayenda ndi Yesu. Zinthu zodabwitsa zimene zinachitikazo zinawalimbikitsa kwambiri.
-
-
Anakonza Thupi la Yesu ndi Kukaliika M’mandaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 133
Anakonza Thupi la Yesu ndi Kukaliika M’manda
MATEYU 27:57–28:2 MALIKO 15:42–16:4 LUKA 23:50–24:3 YOHANE 19:31–20:1
ANATSITSA THUPI LA YESU PAMTENGO
ANAKONZA THUPI LA YESU POKONZEKERA KUKALIIKA M’MANDA
AZIMAYI ANAPEZA KUTI M’MANDA MULIBE KANTHU
Lachisanu masana pa Nisani 14 panachitika zinthu zambiri zodabwitsa. Pamene dzuwa linkalowa, tsiku la Nisani 15 linayamba ndipo tsikuli linali la Sabata. Pa nthawiyi Yesu anali atamwalira kale koma anthu awiri amene anakhomeredwa naye limodzi aja anali asanamwalire. Chilamulo chinkanena kuti munthu akapachikidwa pamtengo, mtembo wake ‘usamakhale pamtengopo usiku wonse’ koma azimuika m’manda “tsiku lomwelo.”—Deuteronomo 21:22, 23.
Komanso Lachisanu masana anthu ankakonzeratu chakudya ndiponso kugwiriratu ntchito zina zofunika, tsiku la Sabata lisanafike. Chifukwa cha zimenezi tsikuli ankalitchula kuti Tsiku Lokonzekera. Dzuwa litalowa, Sabata “lalikulu” linayamba. (Yohane 19:31) Linali Sabata lalikulu chifukwa Nisani 15 linali tsiku loyamba la Chikondwerero cha Mkate Wopanda Chofufumitsa ndipo nthawi zonse tsikuli linkakhala Sabata. Chikondwererochi chinkachitika kwa masiku 7. Levitiko 23:5, 6) Koma pa nthawiyi, tsikuli linali pa Loweruka, lomwe mlungu uliwonse linkakhala la Sabata.
Chifukwa cha zimenezi, Ayuda anapempha Pilato kuti afulumizitse imfa ya Yesu komanso ya zigawenga zija. Kodi akanachita bwanji zimenezi? Polamula kuti awathyole miyendo. Kuti munthu amene wapachikidwa athe kupuma, ankakhala ngati akudzikankhira m’mwamba pogwiritsa ntchito miyendo yake. Koma akakhala kuti amuthyola miyendo, ankalephera kuchita zimenezi choncho sankachedwa kufa.Ndiyeno asilikali anapita n’kukathyola miyendo ya zigawenga ziwiri zija. Koma poti anapeza Yesu atafa kale sanamuthyole miyendo. Zimenezi zinakwaniritsa ulosi wa pa Salimo 34:20 womwe umati: “Amateteza mafupa onse a wolungamayo. Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.”
Pofuna kutsimikizira kuti Yesu wafadi, msilikali wina anamubaya ndi mkondo chapambali ndipo mkondowo unalasa pafupi ndi mtima. “Nthawi yomweyo panatuluka magazi ndi madzi.” (Yohane 19:34) Zimenezi zinakwaniritsanso ulosi wina womwe unanena kuti: “Iwo adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa.”—Zekariya 12:10.
Ndiyeno panali “munthu wina wachuma” dzina lake Yosefe wa ku Arimateya. Munthuyu anali mmodzi wa anthu olemekezeka m’khoti la Sanihedirini ndipo analipo pa nthawi imene Yesu ankaphedwa. (Mateyu 27:57) Ankadziwika kuti anali “munthu wabwino ndi wolungama” yemwenso “anali kuyembekezera ufumu wa Mulungu.” Yosefe sanagwirizane ndi zimene khoti la Sanihedirini linaweruza pa mlandu wa Yesu chifukwa iye anali “wophunzira wa Yesu koma wamseri chifukwa anali kuopa Ayuda.” (Luka 23:50; Maliko 15:43; Yohane 19:38) Iye analimba mtima n’kukapempha Pilato kuti amupatse thupi la Yesu. Pilato anafunsa kapitawo wa asilikali ngati Yesu analidi atafa ndipo msilikaliyo anamutsimikizira kuti wafadi. Kenako Pilato analoleza Yosefe kuti akhoza kukatenga thupilo.
Yosefe anagula nsalu yoyera komanso yapamwamba kenako anakatsitsa thupi la Yesu pamtengo paja. Anakulunga thupi la Yesu ndi nsaluyo pokonzekera kuti amuike m’manda. Nikodemo, yemwe “anabwera kwa [Yesu] usiku poyamba paja” anamuthandiza kukonza mtembowo. (Yohane 19:39) Nikodemo anatenga mule wosakaniza ndi aloye wopitirira makilogalamu 33. Anakulunga thupi la Yesu ndi nsalu zomwe anazipaka zonunkhiritsa potsatira zimene Ayuda ankachita poika maliro.
Yosefe anali ndi manda, omwe anali asanaikemo munthu, chapafupi ndi pamene anapachika Yesu. Mandawo anali ogobedwa pa chimwala chachikulu ndipo thupi la Yesu analiika mmenemo. Kenako anagubuduza chimwala chachikulu n’kutseka pakhomo la mandawo. Iwo anachita zimenezi mofulumira tsiku la Sabata lisanayambe. N’kutheka kuti Mariya Mmagadala komanso Mariya, yemwe anali mayi ake a Yakobo Wamng’ono ankathandiza nawo pokonza thupi la Yesu. Koma anabwerera kunyumba mofulumira kuti ‘akakonze zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira’ oti adzapake thupi la Yesu pambuyo pa Sabata.—Luka 23:56.
Tsiku lotsatira, lomwe linali Sabata, ansembe aakulu ndi Afarisi anapita kwa Pilato n’kumuuza kuti: “Ife takumbukira kuti wonyenga uja adakali moyo ananena kuti, ‘Patapita masiku atatu ndidzauka.’ Choncho lamulani kuti akhwimitse chitetezo pamandapo kufikira tsiku lachitatu, kuti ophunzira ake asabwere kudzamuba ndi kuuza anthu kuti, ‘Anauka kwa akufa!’ pakuti chinyengo chotsirizachi chidzakhala choipa kwambiri kuposa choyamba chija.” Pilato anawayankha kuti: “Inu muli nawo asilikali olondera. Pitani kakhwimitseni chitetezo monga mmene mukudziwira.”—Mateyu 27:63-65.
Lamlungu m’mawa kwambiri, Mariya Mmagadala, Mariya mayi ake a Yakobo pamodzi ndi azimayi ena anatenga zonunkhiritsa n’kupita kumanda kuja kuti akakonze thupi la Yesu. Ali m’njira ankafunsana kuti: “Nanga ndani amene akatigubuduzire chimwala chija pakhomo la manda achikumbutso?” (Maliko 16:3) Koma pa nthawiyi kunali kutachitika chivomezi ndipo anapezanso kuti mngelo wa Mulungu wakankha chimwala chija, asilikali olondera palibe komanso m’manda muja mulibe kanthu.
-