-
M’manda a Yesu Munalibe Kanthu Chifukwa Anali AtaukitsidwaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 134
M’manda a Yesu Munalibe Kanthu Chifukwa Anali Ataukitsidwa
MATEYU 28:3-15 MALIKO 16:5-8 LUKA 24:4-12 YOHANE 20:2-18
YESU ANAUKITSIDWA
ZIMENE ZINACHITIKA KU MANDA A YESU
ANAONEKERA KWA AZIMAYI ANGAPO
Azimayi omwe anapita kumanda a Yesu anadabwa kwambiri atapeza kuti m’mandamo mulibe thupi la Yesu. Mariya Mmagadala anathamanga kupita kwa “Simoni Petulo ndi kwa wophunzira wina, amene Yesu anali kumukonda.” Wophunzira ameneyo anali mtumwi Yohane. (Yohane 20:2) Koma azimayi ena omwe anatsalira kumanda kuja anaona mngelo. Mkati mwa mandawo munalinso mngelo wina yemwe ‘anavala mkanjo woyera.’—Maliko 16:5.
Mmodzi wa angelowo anawauza kuti: “Musachite mantha, chifukwa ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anapachikidwa. Iye sali pano chifukwa wauka kwa akufa monga ananenera. Bwerani muone pamene anagona. Ndipo pitani mwamsanga mukauze ophunzira ake kuti wauka kwa akufa, moti padakali pano, watsogola kupita ku Galileya.” (Mateyu 28:5-7) Kenako azimayiwo ‘akunjenjemera ndi kunthunthumira kwambiri’ anapita kukauza ophunzira a Yesu zimene zinachitikazo.—Maliko 16:8.
Pa nthawiyi n’kuti Mariya atakumana ndi Petulo komanso Yohane. Mtima ukadali m’mwamba anauza atumwiwo kuti: “Ambuye awachotsa m’manda achikumbutso aja, ndipo sitikudziwa kumene awaika.” (Yohane 20:2) Petulo ndi Yohane atangomva zimenezi analiyatsa liwiro. Yohane anathamanga kwambiri moti ndi amene anayambirira kukafika kumandako. Atafika anasuzumira m’mandamo ndipo anaonamo nsalu zomwe anakulungira Yesu koma iye anakhalabe kunja kwa mandawo.
Koma Petulo anangofikira kulowa ndipo anapeza nsalu zomwe anakulungira Yesu komanso imene anamukulungira kumutu. Kenako Yohane analowa ndipo anaona kuti zimene Mariya anawauza zija zinali zoona. Ngakhale kuti Yesu anali atawauza kale kuti adzaukitsidwa, pa nthawiyi ophunzira akewo sanazindikire kuti waukitsidwa. (Mateyu 16:21) Ophunzirawo anabwerera kwawo atasokonezeka kwambiri. Koma Mariya atabwereranso kumanda kuja sanafune kuchokako.
Mmene zimenezi zinkachitika n’kuti azimayi ena aja akupita kukauza ophunzira ena kuti Yesu waukitsidwa. Ali m’njira anakumana ndi Yesu ndipo anawapatsa moni kuti: “Moni amayi!” Azimayiwo anagwada ‘n’kuweramitsa nkhope zawo pansi.’ Kenako Yesu anawauza kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga, kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.”—Mateyu 28:9, 10.
Asilikali omwe anali kumanda kuja “ananjenjemera ndipo anangouma gwaa ngati akufa” chifukwa cha chivomezi chomwe chinachitika komanso chifukwa chakuti anaona angelo. Koma atadzuka anapita mumzinda ndipo “anakauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitika.” Kenako ansembewo anapita kukakambirana ndi akulu ndipo anagwirizana kuti apatse ndalama asilikali omwe ankalondera kumandawo. Anachita zimenezi n’cholinga choti anthu akawafunsa za nkhaniyi azinama kuti: “Ophunzira ake anabwera usiku kudzamuba ife titagona.”—Mateyu 28:4, 11, 13.
Asilikali achiroma ankatha kuphedwa ngati apezeka akugona pa malo awo antchito, choncho ansembewo analonjeza alondawo kuti: “Bwanamkubwa akamva zimenezi [zoti amagona pa nthawi ya ntchito], tikamunyengerera ndipo inu musade naye nkhawa.” (Mateyu 28:14) Asilikaliwo analandiradi ndalamazo ndipo anachita zimene ansembewo anawauza moti nkhani yoti thupi la Yesu labedwa inafala kwa Ayuda ambiri.
Mariya Mmagadala anali adakali kumanda kuja akulira. Atasuzumira m’manda muja anaona angelo awiri atavala zovala zoyera. Mngelo mmodzi anakhala kumene kunali mutu wa Yesu ndipo wina anakhala kumene kunali mapazi ake. Angelowo anamufunsa kuti: “Mayi iwe, n’chifukwa chiyani ukulira?” Mariya anayankha kuti: “Atenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene awaika.” Kenako Mariya atatembenuka anaona kuti kumbuyo kwake kuli munthu. Munthu uja anamufunsanso funso limene angelo aja anamufunsa koma anawonjezeranso funso lina kuti: “Kodi Ukufuna ndani?” Mariya ankaganiza kuti munthuyo ndi wosamalira munda ndipo anamuuza kuti: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika, ndipo ine ndikamutenga.”—Yohane 20:13-15.
Mariya sankadziwa kuti akulankhula ndi Yesu yemwe anali ataukitsidwa. Koma atangonena kuti, “Mariya!” Mariyayo anazindikira kuti munthuyo ndi Yesu chifukwa cha mmene anamuitanira. Nthawi yomweyo Mariya ananena mosangalala kuti: “Rabboni!” (kutanthauza kuti “Mphunzitsi!”) Iye ankaganiza kuti Yesu akwera kumwamba nthawi yomweyo choncho anamugwira mwamphamvu. Koma Yesu anamuuza kuti: “Usandikangamire. Pakuti sindinakwerebe kwa Atate. Koma pita kwa abale anga ukawauze kuti, ‘Ine ndikukwera kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.’”—Yohane 20:16, 17.
Mariya anathamangira kumene atumwi komanso otsatira ena a Yesu anasonkhana. Atafika anawauza kuti: “Ambuye ndawaona ine!” Zimene Mariya anawauzazi zinangowonjezera zomwe anali atamva kale kuchokera kwa azimayi ena. (Yohane 20:18) Komabe iwo ankangoona ngati zimene azimayiwo anawauza ndi “zopanda pake.”—Luka 24:11.
-
-
Yesu Ataukitsidwa Anaonekera kwa Anthu AmbiriYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 135
Yesu Ataukitsidwa Anaonekera kwa Anthu Ambiri
YESU ANAONEKERA PA MSEWU WOPITA KU EMAU
ANAPITIRIZA KUFOTOKOZERA OPHUNZIRA AKE MALEMBA
TOMASI ANASIYA KUKAYIKIRA
Pofika Lamlungu pa Nisani 16, ophunzira a Yesu anali ndi chisoni chachikulu. Iwo sankamvetsabe kuti n’chifukwa chiyani sanapeze thupi la Yesu m’manda muja. (Mateyu 28:9, 10; Luka 24:11) Tsiku lomwelo, ophunzira awiri ankachoka mumzinda wa Yerusalemu kupita kumudzi wa Emau, womwe unali pamtunda wa makilomita pafupifupi 11 kuchokera ku Yerusalemu. Mmodzi wa ophunzirawa dzina lake anali Keleopa.
Ali m’njira ankakambirana zimene zinachitikazo. Kenako anakumana ndi munthu wina ndipo anayamba kuyenda naye limodzi. Munthuyo anawafunsa kuti: “Kodi ndi nkhani zanji zimene mukukambirana mukuyenda pamsewu pano?” Keleopa anamufunsa kuti: “Kodi iwe ukukhala wekhawekha m’Yerusalemu monga mlendo, moti sukudziwa zimene zachitika mmenemo m’masiku amenewa?” Munthuyo anafunsanso kuti: “Zinthu zotani?”—Luka 24:17-19.
Ophunzirawo anamuyankha kuti: “Zinthu zokhudza Yesu Mnazareti, . . . ife tinali kuyembekezera kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli.”—Luka 24:19-21.
Kenako Keleopa ndi wophunzira winayo anayamba kufotokozera munthu uja zimene zinachitika tsiku limenelo. Iwo anamuuza kuti azimayi ena anapita kumanda a Yesu koma thupi lake sanakalipezeko ndiponso kuti azimayiwo anaona angelo omwe anawauza kuti Yesu waukitsidwa. Anauzanso munthuyo kuti anthu ena anapita kumandako ndipo “anapezadi kuti zili momwemo, mmene amayiwo ananenera.”—Luka 24:24.
Ophunzira awiriwo ankaoneka kuti sakumvetsa komanso asokonezeka ndi zimene zachitikazo. Koma munthuyo anawalankhula mwamphamvu ndipo anawathandiza kusintha maganizo awo olakwika, omwe anawachititsanso kuti akhale okhumudwa kwambiri. Munthuyo anawauza kuti: “Opanda nzeru inu ndi okayikakayika pa zonse zimene aneneri ananena! Kodi sikunali kofunikira kuti Khristu amve zowawa zonsezi ndi kulowa mu ulemerero wake?” (Luka 24:25, 26) Anawafotokozeranso Malemba ambiri omwe ankanena za Khristu.
Atatsala pang’ono kufika m’mudzi wa Emau, ophunzira awiri aja ankafuna kumva zambiri, choncho anauza munthu uja kuti: “Tiyeni tikhalebe limodzi, chifukwa kunja kwayamba kuda ndipo tsiku latha kale.” Munthu uja analola ndipo atalowa m’mudzimo anadyera limodzi chakudya. Pamene ankadya chakudyacho, munthu uja anapemphera, kutenga mkate n’kuunyemanyema kenako anawapatsa kuti adye. Atangochita zimenezi, ophunzirawo anazindikira kuti munthuyo ndi Yesu, koma kenako anazimiririka. (Luka 24:29-31) Tsopano anali ndi umboni woti Yesu waukitsidwadi.
Ophunzirawa anasangalala kwambiri moti anayamba kukambirana zimene zinachitikazo kuti: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumira pamene anali kulankhula nafe mumsewu, ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?” (Luka 24:32) Kenako anabwereranso ku Yerusalemu ndipo atafika kumeneko anapeza atumwi alinso ndi anthu ena. Keleopa asanayambe n’komwe kufotokoza zimene zinawachitikira anamva anthu enanso akunena kuti: “N’zoonadi, Ambuye wauka kwa akufa ndipo waonekera kwa Simoni!” (Luka 24:34) Keleopa ndi wophunzira wina uja anafotokozanso zimene zinawachitikira. Nawonso anali ngati mboni chifukwa anaona ndi maso awo kuti Yesu waukadi.
Koma kenako panachitika chinthu chodabwitsa kwambiri. Yesu anaonekera m’chipinda chomwecho. Zimenezi zinali zodabwitsa chifukwa zitseko zonse zinali zokhoma. Anthuwo anadzikhomera m’nyumba chifukwa choopa Ayuda. Anthu onse omwe anali m’chipindamo anaona Yesu. Iye anawauza modekha kuti: “Mtendere ukhale nanu.” Anthuwo anachita mantha chifukwa ‘ankaganiza kuti aona mzimu,’ ngati mmene anachitira pa nthawi imene Yesu anayenda panyanja ija.—Luka 24:36, 37; Mateyu 14:25-27.
Pofuna kuwathandiza ophunzirawo kudziwa kuti sanali mzimu koma munthu, Yesu anawaonetsa manja ndi mapazi ake n’kuwauza kuti: “N’chifukwa chiyani mukuvutika maganizo? Bwanji mukukayikakayika m’mitima yanu? Onani manja ndi mapazi angawa, mutsimikize kuti ndine ndithu. Ndikhudzeni muone, chifukwa mzimu ulibe mnofu ndi mafupa ngati anga amene mukuwaonawa.” (Luka 24:36-39) Anthuwo anasangalala kwambiri komanso kudabwa, komabe ankakayikira pang’ono.
Pofuna kuwathandiza kuti asiye kukayikira, Yesu anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” Anamupatsa kachidutswa ka nsomba yowotcha ndipo anadya. Kenako anawauza kuti: “Pamene ndinali nanu limodzi [ndisanafe] ndinakuuzani mawu akuti, zonse zokhudza ine zolembedwa m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri ndi m’Masalimo ziyenera kukwaniritsidwa.”—Luka 24:41-44.
Yesu ataonekera kwa Keleopa ndi wophunzira wina uja anawathandiza kumvetsa Malemba. Ndipo zimenezi ndi zimene ankachitanso pa nthawiyi. Iye anauza anthu onse omwe anali m’chipindamo kuti: “Mmene zachitikiramu ndi mmene zinalembedwera kuti Khristu adzazunzika ndi kuuka kwa akufa tsiku lachitatu, ndipo pa maziko a dzina lake, m’mitundu yonse mudzalalikidwa za kulapa kuti machimo akhululukidwe. Kuyambira ku Yerusalemu inu mudzakhala mboni za zimenezi.”—Luka 24:46-48.
Pa gulu la anthu amene anasonkhana m’chipindacho panalibe Tomasi. Koma anthu omwe analipowo atakumana naye anamuuza mosangalala kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Tomasi anayankha kuti: “Ndithu ndikapanda kuona mabala a misomali m’manja mwawo ndi kuika chala changa m’mabala a misomaliwo, ndiponso kuika dzanja langa m’mbali mwa mimba yawo, ine sindikhulupirira ayi.”—Yohane 20:25.
Patatha masiku 8, ophunzira anakumana m’chipinda china ndipo anakhomanso zitseko zonse. Koma pa nthawiyi Tomasi analipo. Yesu anaonekeranso ali ndi thupi ngati munthu ndipo anawapatsa moni kuti: “Mtendere ukhale nanu.” Kenako Yesu anauza Tomasi kuti: “Ika chala chako apa, ndiponso ona m’manja mwangamu. Gwiranso ndi dzanja lako m’mbali mwa mimba yangamu, kuti usakhalenso wosakhulupirira.” Koma Tomasi ananena kuti: “Mbuyanga ndi Mulungu wanga!” (Yohane 20:26-28) Tsopano Tomasi anakhulupirira kuti Yesu waukitsidwadi ndi thupi lauzimu ndipo akuimira Yehova Mulungu.
Yesu anamuuza kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona? Odala ndi amene amakhulupirira ngakhale sanaone.”—Yohane 20:29.
-