Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Angelo
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 5
    • Kodi Angelo Ali Ndi Maudindo Otani?

      Yesu Khristu ndi mkulu wa angelo ndipo ali ndi udindo waukulu komanso mphamvu zochuluka. Malemba amasonyeza kuti dzina lake lina ndi Mikayeli.​—1 Atesalonika 4:16; Yuda 9.

      Aserafi amagwira ntchito zapamwamba komanso amalandira ulemu wambiri poyerekeza ndi angelo ena. Aserafi ndi amene amakhala pafupi ndi mpando wachifumu wa Mulungu.​—Yesaya 6:1-3.

      Akerubi nawonso amagwira ntchito zapamwamba komanso zapadera zogwirizana kwambiri ndi ulemerero wa Mulungu Wamphamvuyonse. Nthawi zambiri Baibulo limawafotokoza kuti amapezeka pamalo amene pali ulemerero wa Mulungu.—Genesis 3:24; Ezekieli 9:3; 11:22.

      Angelo ena ambirimbiri amagwira ntchito zopereka mauthenga komanso amaimira Mulungu pokwaniritsa cholinga chake.b​—Aheberi 1:7, 14.

  • Kodi Aliyense Ali Ndi Mngelo Amene Amamuyang’anira?
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 5
    • NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA ZAMBIRI ZOKHUDZA ANGELO?

      Kodi Aliyense Ali Ndi Mngelo Amene Amamuyang’anira?

      Baibulo silinena kuti munthu aliyense ali ndi mngelo wake amene amamuyang’anira. N’zoona kuti Yesu anati: “Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, [ophunzira a Yesu] chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.” (Mateyu 18:10) Koma sikuti apa Yesu ankatanthauza kuti aliyense ali ndi mngelo amene amamuyang’anira. M’malomwake ankatanthauza kuti angelo amachita chidwi ndi wophunzira wa Yesu aliyense ndipo amafuna kuti zinthu zizimuyendera bwino. Choncho atumiki a Mulungu sachita dala zinthu zoika moyo pangozi poganiza kuti angelo a Mulungu awateteza.

      Kodi zimenezi zikutanthauza kuti angelo sathandiza anthu? Ayi. (Salimo 91:11) Anthu ena amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu amawateteza komanso amawatsogolera pogwiritsa ntchito angelo. Mmodzi wa anthu amenewa ndi a Kenneth amene tawatchula m’nkhani yoyamba ija. N’kuthekadi kuti Mulungu ndi amene anathandiza a Kenneth. Nthawi zambiri a Mboni za Yehova amaona umboni wosonyeza kuti angelo amawathandiza pa ntchito yawo yolalikira. Komabe popeza angelo saoneka, sitingafotokoze mwatsatanetsatane zonse zimene amachita pothandiza anthu m’njira zosiyanasiyana. Koma sikulakwa ngati munthu akuthokoza Yehova chifukwa choti akuona kuti wamuthandiza pogwiritsa ntchito angelo.​—Akolose 3:15; Yakobo 1:17, 18.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena