Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
NOVEMBER 4-10
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 105
“Amakumbukira Pangano Lake Mpaka Kalekale”
Kodi Tingatani Kuti Tizikhulupirira Kwambiri Lonjezo la Yehova la Dziko Latsopano?
11 Taganizirani zina mwa zinthu zooneka ngati zosatheka zomwe Yehova analonjeza anthu ake m’mbuyomu. Iye anatsimikizira Abulahamu ndi Sara kuti adzakhala ndi mwana ngakhale kuti anali atakalamba. (Gen. 17:15-17) Anauzanso Abulahamu kuti ana ake adzapatsidwa dziko la Kanani. M’zaka zambiri zimene ana a Abulahamu, Aisiraeli, anali akapolo ku Iguputo, ziyenera kuti zinkaoneka ngati lonjezoli silidzakwaniritsidwa. Koma linakwaniritsidwa. Patapita zaka zambiri, Yehova analengeza kuti Elizabeti yemwe anali wokalamba adzakhala ndi mwana. Iye anauzanso Mariya yemwe anali namwali kuti adzabereka Mwana wake wamwamuna. Yehova anali atalonjeza za kubwera kwa Mwanayu zaka masauzande m’mbuyomo m’munda wa Edeni ndipo anakwaniritsa lonjezoli.—Gen. 3:15.
12 Tikamaganizira zimene Yehova anachitapo m’mbuyomu polonjeza komanso kukwaniritsa malonjezowo, timakhulupirira kwambiri kuti ali ndi mphamvu zobweretsa dziko latsopano. (Werengani Yoswa 23:14; Yesaya 55:10, 11.) Zimenezi zimatithandiza kukhala okonzeka kuthandiza ena kuti adziwe kuti lonjezo la dziko latsopano si maloto chabe. Ponena za kumwamba kwatsopano ndi dziko latsopano, Yehova mwiniyo ananena kuti: “Mawu awa ndi odalirika ndi oona.”—Chiv. 21:1, 5.
it-2 1201 ¶2
Mawu
Zolengedwa zonse, zamoyo ndi zopanda moyo zomwe, zimamvera mawu a Mulungu ndipo iye akhoza kuzigwiritsa ntchito pokwaniritsa zolinga zake. (Sl 103:20; 148:8) Mawu ake ndi odalirika; zimene Mulungu walonjeza saziiwala ndipo amazichitadi. (De 9:5; Sl 105:42-45) Monga iye ananenera, mawu ake “adzakhalapo mpaka kalekale” ndipo sadzabwerera popanda kukwaniritsa cholinga chake.—Yes 40:8; 55:10, 11; 1Pe 1:25.
Mfundo Zothandiza
w86 11/1 18 ¶15
Achinyamata, Mungathandize Kwambiri Kuti Banja Likhale Losangalala Komanso Logwirizana
15 “Kumeneko anamanga mapazi ake [a Yosefe] m’matangadza, khosi lake analiika m’zitsulo mpaka nthawi imene zimene Mulungu ananena zinakwaniritsidwa, mawu a Yehova ndi amene anamuyenga.” (Salimo 105:17-19) Kwa zaka 13, Yosefe anavutika monga kapolo komanso anakhala m’ndende kufikira pamene lonjezo la Yehova linakwaniritsidwa. Zimene zinamuchitikirazi zinamuyenga. Ngakhale kuti Yehova si amene anachititsa mavutowo, iye anawalola ndi cholinga. Kodi Yosefe akanayembekezerabe “mawu a Yehova” ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto aakulu? Kodi iye akanakulitsabe makhalidwe ake abwino, n’kukhalabe woleza mtima, wodzichepetsa, wolimba mwauzimu komanso kukhala wofunitsitsa kuchita utumiki wovuta? Yosefe anapirira mavuto onsewa ndipo anakhala ngati golidi yemwe wayengedwa bwino pamoto. Pamapeto pake anakhala wamtengo wapatali kwambiri kwa Mulungu yemwe anamugwiritsa ntchito m’njira yapadera.—Genesis 41:14, 38-41, 46; 42:6, 9.
NOVEMBER 11-17
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 106
“Iwo Anaiwala Mulungu, Mpulumutsi Wawo”
“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”
13 Aisiraeli ataona mtambo wakuda, mphenzi komanso zizindikiro zina zochokera kwa Mulungu anachita mantha kwambiri. Iwo anapempha Mose kuti iye yekha azilankhulana ndi Yehova paphiri la Sinai kenako aziwafotokozera, ndipo Mose anavomera. (Eks. 20:18-21) Ndiyeno Mose anapita pamwamba pa phirilo ndipo anakhala kwa nthawi yaitali. Kodi pamenepa tingati Aisiraeliwo anasowa mtengo wogwira chifukwa choti mtsogoleri wawo wodalirika anali atachoka? Zikuoneka kuti chikhulupiriro cha Aisiraeliwo chinkaoneka cholimba pakakhala Mose. Tikutero chifukwa izi zitachitika iwo anauza Aroni kuti: “Tipangire mulungu woti atitsogolere, chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.”—Eks. 32:1, 2.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachitatu ndi Chachinayi cha Masalmo
106:36, 37. Mavesiwa akusonyeza kuti kulambira mafano kumagwirizana ndi nsembe zoperekedwa ku ziwanda. Zimenezi zikutanthauza kuti, munthu amene amapembedza mafano angayambe kugwiritsidwa ntchito ndi ziwanda. Baibulo limatilangiza kuti: “Dzisungireni nokha kupewa mafano.”—1 Yohane 5:21.
NOVEMBER 18-24
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 107-108
“Yamikani Yehova, Chifukwa Iye ndi Wabwino”
Mpingo Uyenera Kutamanda Yehova
2 Mpingo si gulu wamba, komanso si bungwe kapena gulu la anthu okonda masewera ndiponso zosangalatsa zinazake. Koma mpingo wapangidwa n’cholinga chotamanda Yehova Mulungu. Zimenezi zakhala choncho kuyambira kalekale, malinga ndi kufotokoza kwa buku la Masalmo. Ndipotu lemba la Salmo 35:18 limati: “Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu, m’chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.” Mofananamo, Salmo 107:31, 32 limatilimbikitsa kuti: “Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwiza zake za kwa ana a anthu! Am’kwezenso mu msonkhano wa anthu.”
Yamikani Yehova Ndipo Adzakudalitsani
4 Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtima woyamikira? Tiyenera kuganizira madalitso amene Yehova watipatsa komanso mmene amatisonyezera chikondi. Wamasalimo anachita zimenezi ndipo anakhudzidwa kwambiri mumtima ndi zinthu zonse zabwino zimene Yehova anachita.—Werengani Salimo 40:5; 107:43.
Mfundo Zothandiza
it-2 420 ¶4
Mowabu
Kenako Davide atayamba kulamulira monga mfumu, panalinso nkhondo pakati pa Isiraeli ndi Mowabu. Amowabu anagonja ndipo anayamba kupereka msonkho kwa Davide. Pambuyo pa nkhondoyo, magulu awiri mwa magulu atatu a asilikali a ku Mowabu anaphedwa. Zimaoneka kuti Davide ankawagoneka pansi n’kuwayeza ndi chingwe. Ndiye ankati akayeza zingwe ziwiri, anthu amenewo ankawapha ndipo akayeza chingwe chimodzi, amenewo ankawasiya ndi moyo. (2Sa 8:2, 11, 12; 1Mb 18:2, 11) N’kuthekanso kuti panali pankhondo yomweyi pamene Benaya mwana wa Yehoyada “anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu.” (2Sa 23:20; 1Mb 11:22) Kupambana kwa Davide pankhondo yolimbana ndi Mowabu kunali kukwaniritsidwa kwa mawu a Balamu amene anawalosera zaka zoposa 400 m’mbuyo mwake kuti: “Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo, ndodo yachifumu idzatuluka mu Isiraeli. Ndipo iye adzaphwanyadi chipumi cha Mowabu ndi mitu ya asilikali onse ankhanza.” (Nu 24:17) Zimaonekanso kuti wolemba masalimo ankatanthauza za kupambana kumeneku pamene ananena kuti Mulungu ankaona kuti Mowabu ndi ‘beseni lake losambiramo.’—Sl 60:8; 108:9.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
ijwyp 90
Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zinthu Zolakwika?
● Musamakokomeze kapena kunyalanyaza zomwe mumalakwitsa.
Baibulo limanena kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.” (Mlaliki 7:20) Munthu aliyense amalakwitsa kapena kulephera zinazake, ndipo zimenezi sizitanthauza kuti ndinu wolephera.
Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: Yesetsani kulimbana ndi mavuto anuwo koma musayembekezere kuti mukhoza kumachita bwino pa chilichonse. Mnyamata wina dzina lake Caleb ananena kuti: “M’malo moganizira kwambiri za zinthu zomwe ndimalakwitsa, ndimayesetsa kuphunzirapo kanthu n’kuona zimene ndingachite kuti ndizichita bwino.”
● Musamadziyerekezere ndi anthu ena
Baibulo limanena kuti: “Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.” (Agalatiya 5:26) Nthawi zina mukhoza kukhumudwa kuona zinthuzi zimene anzanu akutumizirana zosonyeza kuti anali kuphwando kapena kwinakwake kokasangalala koma inuyo sanakuitaneni. Zimenezi zingachititse kuti muyambe kuwaona anzanuwo ngati adani anu.
Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: Muzidziwa kuti anzanu sangakuitanireni ku zochitika zilizonse. Komanso zithunzi zimene anthu amaika pa intaneti kapena kutumizira m’mafoni sizimasonyeza zonse zokhudza mmene zinthu zinalilidi. Mtsikana wina dzina lake Alexis ananena kuti: “Pa intaneti anthu amaikapo zithunzi zobeba zokhazokha kuti ena asirire. Nthawi zambiri zithunzi zosonyeza zinthu zina zosasangalatsa zomwe zinachitika samaziikapo.”
● Muziyesetsa kukhala mwamtendere, makamaka ndi anthu a m’banja lanu.
Baibulo limanena kuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” (Aroma 12:18) N’zoona kuti simungathe kusintha zimene anthu ena amachita, koma inuyo mukhoza kusintha mmene mumachitira zinthu ena akakuchitirani zinazake. Mukhoza kusankha kuti muzikhala mwamtendere ndi anthu.
Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: M’malo mowonjezera mavuto m’banja lanu, muziyesetsa kukhala mwamtendere ngati mmene mungachitire ndi mnzanu wina aliyense. Mtsikana wina dzina lake Melinda ananena kuti: “Palibe amene salakwitsa zinthu, ndipo tonsefe nthawi zina tikhoza kukhumudwitsa anzathu. Timangofunika kusankha kuti tipangapo chiyani, tichita zinthu mwamtendere kapena ayi.”
● Muzikhala ndi mtima woyamikira.
Baibulo limanena kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” (Akolose 3:15) Mtima woyamikira ungakuthandizeni kuti muziona zinthu zomwe zikuyenda bwino pa moyo wanu m’malo momangoganizira zinthu zomwe sizikuyenda bwino.
Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: Muzidziwa mavuto anu, koma zimenezi zisakuchititseni kuiwala zabwino zomwe mumachita. Mtsikana wina dzina lake Rebecca ananena kuti: “Tsiku lililonse ndimalemba m’kabuku kanga chinthu chabwino chimodzi chomwe chachitika. Zimenezi zimandithandiza kudziwa kuti ngakhale ndili ndi mavuto, palinso zabwino zambiri zoti n’kuziganizira.”
● Muzisamala ndi anthu ocheza nawo.
Baibulo limanena kuti: “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Ngati anthu omwe mumakonda kucheza nawo amakonda kulankhula zolakwika, zokayikitsa kapena zokhumudwitsa, nanunso mukhoza kutengera zomwezo.
Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: Ngati anzanu akumana ndi mavuto omwe akuwachititsa kukhala osasangalala, muziwathandiza. Koma mavuto a anzanuwo asamakusokonezeni. Mtsikana wina dzina lake Michelle ananena kuti: “Tisamacheze kwambiri ndi anthu amene amakonda kuona zinthu molakwika. Kucheza kwambiri ndi anthu otere kungangowonjezera mavuto athu.”
NOVEMBER 25–DECEMBER 1
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 109-112
Muzithandiza Yesu, Mfumu Yathu
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachisanu cha Masalmo
110:1, 2—Kodi “Ambuye [wa Davide],” Yesu Kristu, anachita chiyani atakhala kudzanja lamanja la Mulungu? Yesu atauka kwa akufa, anakwera kumwamba ndipo anadikira kudzanja lamanja la Mulungu mpaka mu 1914 pamene anayamba kulamulira monga Mfumu. Nthawi imene Yesu anali kudikirayo, analamulira otsatira ake odzozedwa, powatsogolera pa ntchito yawo yolalikira ndi kupanga ophunzira ndiponso powakonzekeretsa kuti akalamulire limodzi naye mu Ufumu wake.—Mateyu 24:14; 28:18-20; Luka 22:28-30.
Omenyana Ndi Mulungu Sadzapambana!
3 Anthu a Yehova akhala akuukiridwa kuyambira kuchiyambi cha zaka za zana la 20. M’mayiko ambiri, anthu oipa mtima akhala akuyesa kusokoneza, inde, kuthetsa kulalikidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Asonkhezeredwa ndi Mdani wathu wamkulu, Mdyerekezi, amene “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akam’likwire.” (1 Petro 5:8) “Nthawi zawo za anthu akunja” zitatha mu 1914, Mulungu analonga Mwana wake kukhala Mfumu yatsopano ya dziko lapansi, ndi kum’lamula kuti: “Chitani ufumu pakati pa adani anu.” (Luka 21:24; Salmo 110:2) Posonyeza mphamvu zake, Kristu anachotsa Satana kumwamba ndi kum’tsekera kudziko lapansi. Podziwa kuti nthawi yam’thera, Mdyerekezi akulusira Akristu odzozedwa ndi mabwenzi awo. (Chivumbulutso 12:9, 17) Kodi kuukira kobwerezabwereza kwa olimbana ndi Mulungu amenewa kwakhala ndi zotsatira zotani?
Khalani Womapitabe Patsogolo
Langizo lakuti gwiritsani ntchito mphatso yanu limatanthauza kugwiritsa ntchito nzeru. Kodi mumanyamuka nokha kuti mukagwire ntchito yakumunda pamodzi ndi ena? Kodi mumafunafuna mipata yoti muthandize atsopano mumpingo wanu, ang’onoang’ono, kapena olemala? Kodi mumadzipereka pantchito yokayeretsa ku Nyumba ya Ufumu kapena kuthandiza m’njira zosiyanasiyana pamisonkhano ikuluikulu? Kodi mukhoza kumalembetsa nthawi ndi nthawi upainiya wothandiza? Kodi mungatumikire ngati mpainiya wokhazikika kapena kukathandiza kumpingo wosowa? Ngati muli mbale, kodi mukukalamira kuti mukafikire ziyeneretso za m’Malemba za atumiki otumikira ndi akulu? Kudzipereka kwanu kuti muthandize ndi kulandira udindo kuli umboni wa kupita patsogolo.—Sal. 110:3.
Mfundo Zothandiza
it-1 524 ¶2
Pangano
Pangano Lokhala Wansembe Wofanana ndi Melekizedeki. Panganoli linafotokozedwa pa Salimo 110:4, ndipo amene analemba buku la m’Baibulo la Aheberi analigwiritsa ntchito ponena za Khristu pa Aheberi 7:1-3, 15-17. Panganoli ndi la pakati pa Yehova ndi Yesu Khristu basi. Zimaoneka kuti Yesu ankatanthauza pangano limeneli pamene ankachita pangano la ufumu ndi otsatira ake. (Lu 22:29) Yehova analumbira kuti Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu wa kumwamba, adzakhala wansembe mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki. Melekizedeki anali mfumu komanso wansembe wa Mulungu padziko lapansi. Yesu Khristu anali woti adzakhala Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe, osati padziko lapansi koma kumwamba. Iye anaikidwa pa maudindo amenewa atangokwera kumwamba. (Ahe 6:20; 7:26, 28; 8:1) Panganoli lidzakhalapo mpaka kalekale chifukwa Yesu azidzachita zinthu motsogoleredwa ndi Yehova monga Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe mpaka kalekale.—Heb 7:3.
DECEMBER 2-8
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 113-118
Kodi Yehova Tidzamubwezera Chiyani?
Kulani M’chikondi
13 Kuchokera m’mawu a Yesuwo, n’zoonekeratu kuti choyambirira tiyenera kukonda Yehova. Komabe, sitibadwa okhoza kumukonda kwambiri Yehova. N’chinthu chomwe tiyenera kuchikulitsa. Titamva za iye kwa nthawi yoyamba, tinakopeka naye chifukwa cha zomwe tinamvazo. Pang’ono ndi pang’ono, tinaphunzira momwe analengera dziko kuti anthu akhalemo. (Genesis 2:5-23) Tinaphunzira momwe wakhala akuchitira ndi anthu, sanatinyalanyaze pamene tchimo linalowa m’banja la anthu, koma anachitapo kanthu kuti atiwombole. (Genesis 3:1-5, 15) Omwe anali okhulupirika anawachitira chifundo, ndipo pambuyo pake anapereka Mwana wake wobadwa yekha kuti machimo athu athe kukhululukidwa. (Yohane 3:16, 36) Chidziwitso chowonjezeka chimenechi chinakulitsa chiyamiko chathu kwa Yehova. (Yesaya 25:1) Mfumu Davide inati inakonda Yehova chifukwa cha chisamaliro Chake chachikondi. (Salmo 116:1-9) Lerolino, Yehova amatisamalira, kutitsogolera, kutilimbitsa, ndi kutilimbikitsa. Tikamaphunzira zambiri za iye, m’pamene chikondi chathu chimazama.—Salmo 31:23; Zefaniya 3:17; Aroma 8:28.
Landirani Moyamikira Ndipo Perekani ndi Mtima Wonse
Wamasalmo anafunsa kuti: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?” (Sal. 116:12) Kodi ndi zinthu zokoma ziti zimene iye analandira? Yehova anamuthandiza kwambiri pa nthawi imene anali mu “nsautso ndi chisoni.” Yehova ‘analanditsanso moyo wake ku imfa.’ Ndipo nayenso anafuna kuchita zinazake kuti ‘abwezere’ Yehova. Ndiyeno kodi n’chiyani chimene wamasalmoyo akanachita? Iye anati: “Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova.” (Sal. 116:3, 4, 8, 10-14) Iye anatsimikiza kukwaniritsa zonse zimene anawinda kuti adzachitira Yehova ndipo anatsimikiza kupereka mangawa ake onse amene anali nawo kwa Yehova.
Nanunsotu mungathe kuchita zimenezi. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mungatero mwa kutsatira malamulo ndi mfundo za Mulungu pa moyo wanu wonse. Choncho, onetsetsani kuti pa moyo wanu mukuika kulambira Yehova patsogolo ndipo mukulola mzimu wa Mulungu kukutsogolerani pa zilizonse zimene mumachita. (Mla. 12:13; Agal. 5:16-18) Kunena zoona, simungakwanitse kubwezera Yehova zinthu zonse zimene wakuchitirani. Koma ngakhale zili choncho, mukamayesetsa kudzipereka ndi mtima wonse pomutumikira, ‘mumakondweretsa mtima wa Yehova.’ (Miy. 27:11) Ndi mwayitu waukulu kukondweretsa mtima wa Yehova mwa njira imeneyi.
Zimene Tingaphunzire M’buku la Levitiko
9 Phunziro lachiwiri: Timatumikira Yehova chifukwa chomuyamikira. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tikambirane za nsembe zachiyanjano zomwe zinali zofunikanso kwa Aisiraeli pa nkhani yolambira. M’buku la Levitiko timaphunzira kuti Aisiraeli ankatha kupereka nsembe zachiyanjano “posonyeza kuyamikira.” (Lev. 7:11-13, 16-18) Iwo ankapereka nsembezi mwa kufuna kwawo osati chifukwa chotsatira lamulo linalake. Choncho munthu ankasankha yekha kupereka nsembeyi chifukwa chokonda Yehova Mulungu. Munthuyo ankadya nyama imene wapereka nsembeyo limodzi ndi banja lake komanso ansembe. Koma mbali zina za nyamayo ankazipereka kwa Yehova basi. Kodi mbali zake zinali ziti?
10 Phunziro lachitatu: Timachita zonse zimene tingathe potumikira Yehova chifukwa chomukonda. Yehova ankaona kuti mafuta ndi mbali yabwino kwambiri ya nyama. Ananenanso kuti ziwalo zina monga impso zinali zamtengo wapatali. (Werengani Levitiko 3:6, 12, 14-16.) Choncho Yehova ankasangalala kwambiri Aisiraeli akapereka mwa kufuna kwawo mafuta kapena ziwalo ngati zimenezi. Ndipo munthu amene wapereka zimenezi ankasonyeza kuti akufunitsitsa kupatsa Mulungu zinthu zake zamtengo wapatali. Nayenso Yesu anapereka zinthu zake zabwino kwambiri kwa Yehova. Anachita zimenezi pomutumikira ndi mtima wake wonse chifukwa chomukonda. (Yoh. 14:31) Yesu ankasangalala kuchita zimene Mulungu ankafuna ndipo ankakonda kwambiri malamulo ake. (Sal. 40:8) Yehova ayenera kuti ankasangalala kwambiri kuona Yesu akumutumikira ndi mtima wonse.
11 Nafenso timatumikira Yehova mwa kufuna kwathu pofuna kusonyeza kuti timamukonda. Timapatsa Yehova zinthu zathu zabwino kwambiri chifukwa chomukonda ndi mtima wathu wonse. Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri kuona atumiki ake mamiliyoni akumutumikira chifukwa choti amamukonda komanso amakonda njira zake. Timalimbikitsidwa tikakumbukira kuti Yehova amaona zimene timachita komanso chifukwa chimene timachitira zinthuzo ndipo amayamikira. Mwachitsanzo, ngati ndinu achikulire ndipo simungakwanitse kuchita zonse zimene mumafuna, dziwani kuti Yehova amakumvetsani. Mwina mumaona kuti mumachita zochepa, koma Yehova amadziwa kuti mumachita zimene mungathe chifukwa chomukonda kwambiri. Iye amasangalala kulandira zimene mungakwanitse kumupatsa.
Mfundo Zothandiza
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Wamasalimo anaimba mouziridwa kuti: “M’maso mwa Yehova imfa ya anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu.” (Sal. 116:15) Yehova amaona kuti moyo wa munthu aliyense amene amamulambira ndi wamtengo wapatali kwambiri. Koma mawu a pa Salimo 116 sakungonena za imfa ya munthu mmodzi.
Pokamba nkhani ya maliro a Mkhristu, si bwino kugwiritsa ntchito lemba la Salimo 116:15 pofotokoza za munthu womwalirayo ngakhale kuti iye wamwalira ali wokhulupirika kwa Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti mawu a wamasalimoyu sakunena za munthu mmodzi womwalira. Mawuwa akutanthauza kuti Mulungu amaona kuti imfa ya gulu lonse la anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu kwambiri moti sangalole kuti zichitike.—Onani Salimo 72:14; 116:8.
Lemba la Salimo 116:15 limatitsimikizira kuti Yehova sadzalola kuti gulu lonse la atumiki ake liwonongedwe padziko lapansi. Mbiri yathu imasonyeza kuti tapirira mobwerezabwereza kuyesedwa komanso kuzunzidwa koopsa. Izi zikusonyezeratu kuti Mulungu sadzaloladi kuti anthu ake onse awonongeke.
DECEMBER 9-15
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 119:1-56
“Kodi Wachinyamata Angakhale Bwanji Woyera pa Moyo Wake?”
Kodi Mudzakhalabe Oyera M’njira Iliyonse?
10 Pa Aefeso 5:5 Paulo anachenjeza kuti: “Chifukwa mfundo iyi mukuidziwa ndipo mukuimvetsa bwino, kuti munthu wachiwerewere kapena wodetsedwa kapena waumbombo, umene ndi kulambira mafano, sadzalowa mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.” Komabe, anthu masauzande ambiri amadzudzulidwa kapena kuchotsedwa chaka chilichonse chifukwa cha chiwerewere, komwe ndi kuchimwira thupi. (1 Akorinto 6:18) Nthawi zambiri zimenezi zimachitika chifukwa choti anthuwo ‘sakudzifufuza nthawi zonse kuti aone ngati zochita zawo zikugwirizana ndi mawu a Mulungu.’ (Salimo 119:9) Mwachitsanzo, abale ambiri amatayirira pa nthawi ya holide. Iwo amasiya kuchita zinthu ndi Akhristu anzawo n’kuyamba kuchita zinthu ndi anthu amene satumikira Yehova. Poganiza kuti amenewa ndi anthu abwino, Akhristu ena amachita nawo zinthu zokayikitsa. Mofananamo, ena amamasuka kwambiri ndi anzawo ogwira nawo ntchito. Mkulu wina wa Chikhristu ankacheza kwambiri ndi mayi wina amene ankagwira ntchito mpaka anasiya banja lake n’kuyamba kukhala ndi mayiyo. Zimenezi zinachititsa kuti achotsedwe. Izitu zikutsimikiziradi kuti mawu a m’Baibulo akuti, “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino,” ndi oona.—1 Akorinto 15:33.
‘Zikumbutso Zanu Ndizo Zondikondweretsa’
YEHOVA amapatsa anthu ake zikumbutso kuti awathandize kulimbana ndi zovuta za masiku athu ano. Zina mwa zikumbutso zimenezi zimabwera munthu akamawerenga yekha Baibulo, ndipo zina zimachokera mu nkhani kapena ndemanga zoperekedwa pa misonkhano yachikristu. Zambiri zimene timawerenga kapena kumva pa nthawi zimenezi si zachilendo kwa ife. Mosakayikira, tinamvapo zinthu ngati zimenezi m’mbuyomu. Koma popeza sitichedwa kuiwala, tifunika kupitirizabe kudzikumbutsa za zolinga, malamulo, ndi malangizo a Yehova. Tiyenera kuyamikira zikumbutso za Mulungu. Zimatilimbikitsa potikumbutsa zifukwa zomwe zinatichititsa kuyamba kukhala moyo wogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Choncho wamasalmo anaimba kwa Yehova kuti: “Mboni [“zikumbutso,” NW] zanu zomwe ndizo zondikondwetsa.”—Salmo 119:24.
Musamaone Zinthu Zachabe
2 Komabe, zimene timaona zikhozanso kutiwononga. Pali kugwirizana kwambiri pakati pa zimene timaona ndi zimene timaganiza, moti zimene timaona zingatipangitse kuti tizilakalaka zinazake. Ndipo popeza tikukhala m’dziko loipa ndiponso la anthu odzikonda, lomwe wolamulira wake ndi Satana Mdyerekezi, timaona ndi kumva zinthu zimene zingatisocheretse mosavuta ngakhale titangoziyang’ana kanthawi kochepa. (1 Yoh. 5:19) Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti wamasalmo anapempha Mulungu kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.”—Sal. 119:37.
Mfundo Zothandiza
Khulupirirani Mawu a Yehova
2 Nkhani yaikulu mu Salmo 119 yagona pa phindu la mawu, kapena kuti uthenga wa Mulungu. Mwinamwake pofuna kuti azikumbukira mosavuta, mlembi ameneyu analemba nyimboyi motsatira ndondomeko ya zilembo za alifabeti. Mavesi ake onse okwana 176 anawalemba motsatira ndondomeko ya zilembo za alifabeti yachihebri. M’chihebri choyambirira, salmo limeneli lili ndi zigawo 22 ndipo chilichonse mwa zigawo zimenezi chili ndi mizera 8 yomwe ikuyamba ndi chilembo chofanana. Salmo limeneli likutchula mawu, chilamulo, zikumbutso, njira, malangizo, malemba, malamulo ndi maweruzo a Mulungu. M’nkhani ino komanso mu nkhani yotsatira tikambirana Salmo 119 malinga ndi mmene analimasulira m’Baibulo kuchokera ku Chihebri. Kusinkhasinkha zochitika pa moyo wa atumiki a Yehova akale ndi amakono omwe, kutithandiza kumvetsa bwino nyimbo youziridwa ndi Mulungu imeneyi, ndiponso kukulitsa mtima wathu woyamikira Baibulo, Mawu olembedwa a Mulungu.
DECEMBER 16-22
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 119:57-120
Zimene Tingachite Kuti Tizipirira Mavuto
“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”
2 Mwina mungafunse kuti, “Kodi chilamulo cha Mulungu chinalimbikitsa ndi kutonthoza bwanji wamasalmoyo?” Chomwe chinamulimbikitsa ndi chikhulupiriro chake choti Yehova ankamufunira zabwino. Kudziwa bwino ubwino wotsatira chilamulo chimenecho kunachititsa wamasalmoyo kukhala wosangalala, ngakhale anali ndi mavuto amene adani ake anam’bweretsera. Iye anadziwa kuti Yehova wamuchitira zabwino. Ndiponso, kugwiritsa ntchito malangizo a m’chilamulo cha Mulungu kunachititsa wamasalmoyo kukhala wanzeru kuposa adani ake ndipo kunateteza moyo wake. Kumvera chilamulo kunam’patsa mtendere wa mumtima ndi chikumbumtima chabwino.—Salmo 119:1, 9, 65, 93, 98, 165.
Kodi Zikumbutso za Yehova Mumazikonda Kwambiri?
3 Zikumbutso za Yehova zinali zamtengo wapatali kwa wamasalmo yemwe anaimba kuti: “Ndinafulumira, osachedwa, kusamalira malamulo anu. Anandikulunga nazo zingwe za oipa; koma sindinaiwala chilamulo chanu.” (Salmo 119:60, 61) Zikumbutso za Yehova zimatithandiza kupirira chizunzo chifukwa chakuti tili n’chidaliro chonse kuti Atate wathu wakumwamba angadule zingwe za zitsenderezo zomwe adani angatikulunge nazo. M’nthawi yake, amatilanditsa ku zipsinjo zoterozo kotero kuti tithe kugwira ntchito yolalikira Ufumu.—Marko 13:10.
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachisanu cha Masalmo
119:71—Kodi kuzunzidwa kungakhale kokoma m’njira yanji? Mavuto angatiphunzitse kudalira Yehova kwambiri, kupemphera kwa iye ndi mtima wonse, ndi kuchita khama pophunzira Baibulo ndi kutsatira zimene limanena. Ndiponso, zimene timachita tikamazunzidwa zingavumbule zolakwika zina pa umunthu wathu zimene tiyenera tikonze. Tikalola mavuto kutiyenga, pamapeto pake sitingakhumudwe nawo.
“Lirani ndi Anthu Amene Akulira”
3 Atate wathu wakumwamba Yehova ndi amene angatitonthoze kuposa munthu aliyense. (Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yomvera ena chisoni ndipo anauza anthu ake kuti: “Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.”—Yes. 51:12; Sal. 119:50, 52, 76.
5 Sitiyenera kukayikira kuti Yehova angatithandize ngati taferedwa. Choncho tiyenera kupemphera kwa iye n’kumuuza mmene tikumvera mumtima mwathu. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amamvetsa chisoni chathu ndipo angatilimbikitse m’njira yoyenerera. Koma kodi amatilimbikitsa bwanji?
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachisanu cha Masalimo
119:96—Kodi mawu akuti “zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire” akutanthauza chiyani? Apa wolemba masalimo akunena za zinthu zimene munthu amaziona kuti ndi zabwino. N’kutheka amaganizira kuti zimene munthu amaziona kuti ndi zabwino zili ndi malire. Koma mosiyana ndi zimenezi, malamulo a Mulungu alibe malire. Malamulo a Mulungu amakhudza mbali zonse za moyo wa munthu.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
ijwbq 157
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Ngozi Zadzidzidzi?
Mulungu si amene amachititsa ngozi zadzidzidzi zimene timaonazi ndipo amamva chisoni akaona anthu omwe akhudzidwa nazo. Ngozizi ndi chimodzi mwa zinthu zomwe zimachititsa anthu kuvutika ndipo posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzazithetsa. Koma panopa, Mulungu amatonthoza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi.—2 Akorinto 1:3.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti ngozi zadzidzidzi si chilango chochokera kwa Mulungu?
Mmene ngozi zadzidzidzi zimachitikira, n’zosiyana kwambiri ndi mmene Yehova ankagwiritsira ntchito mphamvu zake popereka chiweruzo. Tikutero chifukwa:
● Ngozi zadzidzidzi zimapha komanso kuvulaza aliyense, kaya akhale wabwino kapena woipa. Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu akafuna kupereka chilango, ankawononga anthu oipa okha. Mwachitsanzo, Mulungu atawononga mzinda wa Sodomu ndi Gomora anapulumutsa Loti ndi ana ake aakazi awiri. (Genesis 19:29, 30) Nthawi imeneyo Mulungu ankadziwa zimene zinali mumtima mwa munthu aliyense ndipo anawononga anthu omwe anawaona kuti ndi woipa.—Genesis 18:23-32; 1 Samueli 16:7.
● Ngozi zadzidzidzi zimachitika mosayembekezereka. Komabe Mulungu akafuna kuwononga anthu oipa, ankawachenjeza kaye. Anthuwo akamvera, ankatha kupulumuka.—Genesis 7:1-5; Mateyu 24:38, 39.
● Zochita za anthu zikhozanso kuyambitsa ngozi zadzidzidzi. Zili choncho chifukwa anthu ena amawononga chilengedwe ndipo ena amamanga nyumba zawo m’madera omwe nthawi zambiri kumachitika zivomezi, madzi amasefukira komanso kumene nyengo yake ndi yoipa kwambiri. (Chivumbulutso 11:18) Choncho si bwino kuimba Mulungu mlandu ngati anthu akukumana ndi mavuto chifukwa cha zosankha zawo.—Miyambo 19:3.
Kodi ngozi zadzidzidzi ndi chizindikiro choti tikukhala m’masiku otsiriza?
Inde. Baibulo linaneneratu kuti “mapeto a nthawi ino” kapena kuti “masiku otsiriza” ano, kudzakhala mavuto ambiri. (Mateyu 24:3; 2 Timoteyo 3:1) Mwachitsanzo, ponena za nthawi yathu ino Yesu ananena kuti: “Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.” (Mateyu 24:7) Koma posachedwapa Mulungu adzachotsa zonse zomwe zimachititsa kuti anthu azivutika, kuphatikizapo ngozi zadzidzidzi.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kodi Mulungu amawathandiza bwanji anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi?
● Amagwiritsa ntchito Mawu ake potonthoza anthu okhudzidwawo. Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amatikonda komanso amamva chisoni akationa tikuvutika. (Yesaya 63:9; 1 Petulo 5:6, 7) Baibulo limanenanso za nthawi imene Yehova adzakwaniritse lonjezo lake pochotsa ngozi zadzidzidzi.—Onani kabokosi kakuti, “Mavesi a m’Baibulo omwe tingagwiritse ntchito pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi.”
● Amagwiritsa ntchito atumiki ake pothandiza okhudzidwawo. Mulungu amagwiritsa ntchito atumiki ake kuti azitengera chitsanzo cha Yesu. Baibulo linaneneratu kuti Yesu akadzabwera adzalimbikitsa “anthu osweka mtima” komanso adzatonthoza “anthu onse olira.” (Yesaya 61:1, 2) Atumiki a Mulungu amayesetsa kuchitanso chimodzimodzi.—Yohane 13:15.
Mulungu amagwiritsanso ntchito atumiki ake popereka thandizo la chakudya, zovala, malo ogona ndi zinthu zina zofunikira kwa anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi.—Machitidwe 11:28-30; Agalatiya 6:10.
Kodi m’Baibulo muli mfundo zomwe zingatithandize kukonzekera ngozi zadzidzidzi?
Inde. Ngakhale kuti Baibulo silinalembedwe n’cholinga chotithandiza kudziwa mmene tingakonzekerere ngozi zadzidzidzi, lili ndi mfundo zothandiza pa nkhaniyi. Mwachitsanzo limatithandiza:
● Kudziwiratu zoyenera kuchita ngozi zadzidzidzi zisanachitike. Baibulo limanena kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Choncho ndi bwino kukonzekereratu madzi asanafike m’khosi. Zimenezi zingaphatikizepo kusonkhanitsa zinthu zofunika kwambiri zomwe mungadzazigwiritse ntchito ngati patachitika ngozi yadzidzidzi komanso kukambirana ndi achibale anu za malo omwe mungadzakumane.
● Kuona moyo kukhala ofunika kuposa katundu. Baibulo limanena kuti: “Sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndipo sitingatulukemo ndi kanthu.” (1 Timoteyo 6:7, 8) Tizikhala okonzeka kusiya nyumba yathu komanso katundu wathu n’cholinga choti tidzakwanitse kuthawa ngati patachitika ngozi. Nthawi zonse tizikumbukira kuti moyo wathu ndi wofunika kwambiri kuposa chilichonse chomwe tili nacho.—Mateyu 6:25.
Mavesi a m’Baibulo omwe tingagwiritse ntchito pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi
Genesis 18:25: ‘[Mulungu] Sangachite zimenezo, kupha munthu wolungama limodzi ndi woipa. . . . Kodi Woweruza wa dziko lonse lapansi sadzachita cholungama?’
Mfundo yake: Nthawi zonse Mulungu amachita zinthu zoyenera ndipo tisamamuimbe mlandu tikaona anthu abwino akumwalira chifukwa cha ngozi zadzidzidzi.
Salimo 46:1, 2: “Mulungu ndiye pothawira pathu ndi mphamvu yathu, Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso. N’chifukwa chake sitidzaopa, ngakhale dziko lapansi litasintha.”
Mfundo yake: Kaya tikukumana ndi mavuto otani, timadziwa kuti Mulungu ndi amene angatipatse mphamvu.
Yesaya 63:9: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.”
Mfundo yake: Mulungu ndi wachifundo, tikamavutika nayenso zimamukhudza.
Yohane 5:28, 29: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka.”
Mfundo yake: Mulungu adzapereka mphamvu kwa Yesu zoti aukitse akufa, choncho tikuyembekezera kudzaonanso achibale athu omwe anamwalira.
1 Petulo 5:6, 7: “Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu . . . pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.”
Mfundo yake: Mulungu amakhudzidwa ndi zimene zikutichitikira ndipo amafuna kuti tizimufotokozera nkhawa zathu.
Chivumbulutso 21:4: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”
Mfundo yake: Mulungu adzachotsa zonse zimene zimayambitsa mavuto kuphatikizapo ngozi zadzidzidzi.
DECEMBER 23-29
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU SALIMO 119:121-176
Kodi Tingatani Kuti Tizipewa Mavuto?
Muziphunzitsa Chikumbumtima Chanu ndi Malamulo Komanso Mfundo za Mulungu
5 Kuti malamulo a Mulungu azitithandiza, tiyenera kuchita zambiri osati kungowawerenga n’kuwadziwa. Tiziwakonda kwambiri komanso kuwalemekeza. Paja Mawu a Mulungu amati: “Danani ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.” (Amosi 5:15) Koma kodi tingachite bwanji zimenezi? Chofunika ndi kuona zinthu mmene Yehova amazionera. Tiyerekeze kuti muli ndi vuto losowa tulo. Kenako dokotala akukuuzani kuti muzichita masewera olimbitsa thupi, muzidya zakudya zabwino komanso musinthe zinthu zina pa moyo wanu. Ndiyeno mutatsatira malangizowo mukuona kuti mwayamba kupeza tulo bwinobwino. Mukhoza kuthokoza kwambiri dokotalayo chifukwa chokuthandizani.
6 Nayenso Mlengi wathu watipatsa malamulo otithandiza kuti tikhale ndi moyo wabwino komanso tisamakumane ndi mavuto chifukwa cha uchimo. Tangoganizirani mmene timapindulira tikamatsatira malamulo a m’Baibulo pa nkhani ya kunama, chiwembu, kuba, chiwerewere, chiwawa ndiponso kuchita zamizimu. (Werengani Miyambo 6:16-19; Chiv. 21:8) Tikazindikira ubwino woyenda m’njira za Yehova, timayamba kumukonda kwambiri komanso kukonda malamulo ake.
Achinyamata, Kodi Mukuchita Chiyani?
12 Koposa zonse, muyenera kuphunzira kudana, kunyansidwa komanso kuipidwa ndi choipa. (Salimo 97:10) Kodi mungadane bwanji ndi zinthu zimene poyamba zikuoneka ngati zabwino kapena zosangalatsa? Mwa kuganizira zotsatirapo zake. “Musadzinamize, Mulungu sapusitsika. Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho. Chifukwa amene akufesa n’cholinga chopindulitsa thupi lake, adzakolola chiwonongeko kuchokera m’thupi lakelo.” (Agalatiya 6:7, 8) Pamene mwayesedwa kuti muchite zoipa, muziganizira za zotsatirapo zake komanso mmene zingakhudzire Yehova. (Yerekezerani ndi Salimo 78:41.) Muziganiziranso kuti mukhoza kutenga mimba yosayembekezera kapena kutenga matenda opatsirana monga edzi. Taganizirani za mmene mudzamvere mumtima komanso manyazi amene mudzakhale nawo chifukwa choti mwadzichotsera ulemu. Pangakhalenso zotsatirapo zimene mudzavutike nazo kwa nthawi yaitali. Mayi wina wa Chikhristu ananena kuti: “Ine ndi mwamuna wanga tisanakwatirane, aliyese ankachita chiwerewere. Ngakhale kuti panopa tonsefe ndi Akhristu, khalidwe la chiwerewere lomwe tinkachita poyamba limachititsa kuti tizikangana pafupipafupi komanso tizichitirana nsanje.” Kuwonjezera pamenepo munthu sangakhale ndi mwayi wotumikira mumpingo kapenanso akhoza kuchotsedwa. (1 Akorinto 5:9-13) Kodi mungalolere kutaya zinthu zonsezi chifukwa chongofuna kusangalala kwa kanthawi kochepa?
Mfundo Zothandiza
Musamakayikire Kuti ‘Mawu a Mulungu ndi Choonadi’
2 Monga atumiki a Yehova, sitikayikira kuti iye ndi “Mulungu wachoonadi” komanso kuti nthawi zonse amatifunira zabwino. (Sal. 31:5; Yes. 48:17) Timadziwa kuti tingakhulupirire zomwe timawerenga m’Baibulo, chifukwa “mawu onse [a Mulungu] ndi choonadi chokhachokha.” (Werengani Salimo 119:160.) Timavomereza zimene katswiri wina wa Baibulo analemba kuti: “Pa zimene Mulungu ananena palibe chilichonse chabodza kapena zimene sizingachitike mpang’ono pomwe. Anthu a Mulungu amakhulupirira chilichonse chomwe iye wanena chifukwa samukayikira ngakhale pang’ono.”
DECEMBER 30–JANUARY 5
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 120-126
Anafesa Mbewu Akukhetsa Misozi, N’kukolola Akusangalala
Odala Ndi Amene Amapatsa Mulungu Ulemerero
10 Tikasenza goli lokhala ophunzira a Yesu, ndiye kuti tikulimbana ndi Satana. Yakobo 4:7 amalonjeza kuti: “Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani inu.” Apa sitikunena kuti n’zapafupi kuchita zimenezi. Kutumikira Mulungu kumafuna khama. (Luka 13:24) Komano Baibulo, pa Salmo 126:5, limatilonjeza kuti: “Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.” Eya, Mulungu amene ife timam’lambira amayamikira. Iye ali “wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye,” ndipo amadalitsa anthu amene amam’patsa ulemerero.—Ahebri 11:6.
Kodi Chikhulupiriro Chanu Chidzakhala Cholimba?
17 Kodi muli ndi chisoni chifukwa cha imfa ya munthu amene mumamukonda? Yesetsani kulimbitsa chikhulupiriro chanu choti akufa adzaukitsidwa powerenga nkhani za m’Baibulo za anthu omwe anaukitsidwa. Kodi zikukupwetekani chifukwa choti wachibale wanu anachotsedwa mumpingo? Muziphunzira Mawu a Mulungu n’cholinga choti mutsimikizire kuti chilango cha Yehova chimakhala chabwino nthawi zonse. Kaya mwakumana ndi vuto lotani, muziona kuti umenewo ndi mwayi woti mulimbitse chikhulupiriro chanu. Muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. Musamadzipatule, m’malomwake muzichita zinthu limodzi ndi abale ndi alongo anu. (Miy. 18:1) Muzichita zinthu zomwe zingakuthandizeni kupirira ngakhale pamene mukumva kupweteka mukakumbukira zomwe zinakuchitikirani. (Sal. 126:5, 6) Musamasiye kupezeka pamisonkhano, kugwira nawo ntchito yolalikira komanso kuwerenga Baibulo. Ndiponso muziganizira kwambiri zinthu zabwino zomwe Yehova adzakupatseni m’tsogolomu. Mukamaona mmene Yehova akukuthandizirani, mudzayamba kumukhulupirira kwambiri.
Limbikirani Ntchito Yotuta!
13 Mawu opezeka pa Salmo 126:5, 6 ali olimbikitsa kwambiri kwa otuta makamaka amene amazunzidwa. Mawuwo amati: “Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbewu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.” Mawu a wamasalmo onena za kufesa ndi kututa akusonyeza chisamaliro ndi madalitso a Yehova kwa otsala amene anabwerako ku ukapolo ku Babulo wakale. Anakondwa kwambiri atamasulidwa, koma ayenera kuti analira pofesa mbewu m’dziko labwinja lomwe sanalimemo kwa zaka 70 zomwe anali ku ukapolo. Komabe, amene anapitiriza ntchito yawo yofesa ndi kumanga anapeza zokolola zambiri komanso kukhutira ndi ntchito yawo.
14 Tingakhetse misozi poyesedwa kapena pamene ifeyo ndi okhulupirira anzathu tikuzunzidwa chifukwa cha chilungamo. (1 Petro 3:14) Pa ntchito yathu yotutayi, mwina zinthu zingativute poyamba chifukwa chakuti tikuona ngati palibe umboni wosonyeza phindu la khama lathu mu utumiki. Koma ngati tilimbikira kufesa ndi kuthirira, Mulungu adzakulitsa, mwinanso kuposa mmene tingaganizire. (1 Akorinto 3:6) Zimenezi zikusonyezedwa bwino lomwe ndi mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Malemba omwe tagawira.
Mfundo Zothandiza
Mphamvu Zoteteza—“Mulungu Ndi Pothawira Pathu”
15 Choyamba, tiyeni tiganizire mmene Yehova amatetezera moyo wathu. Atumiki a Yehovafe tingayembekezere kuti iye azititeteza ngati gulu. Akanakhala kuti sachita zimenezi, bwenzi Satana akungotipha. Taganizirani izi: Satana, yemwe ndi “wolamulira wa dzikoli,” amafunitsitsa kuthetseratu kulambira koona. (Yohane 12:31; Chivumbulutso 12:17) Maboma ena amphamvu kwambiri akhala akuletsa ntchito yathu yolalikira ndiponso kuyesetsa kuti athetseretu gulu lathu. Koma anthu a Yehova amakhalabe olimba komanso amapitiriza kulalikira. N’chifukwa chiyani maboma amphamvu alephera kuletsa ntchito ya Akhristu omwe amaoneka kuti ndi ochepa komanso opanda chitetezo? N’chifukwa chakuti Yehova amatiteteza ndi mapiko ake amphamvu.—Salimo 17:7, 8.