-
Kupeza Chuma Chenicheni mu Hong KongNsanja ya Olonda—1993 | May 15
-
-
chipambano m’kuchitira umboni wa m’khwalala. Amakambitsirananso ndi anthu kumalo awo antchito mwa kufikira anthu ogwira ntchito muofesi, ogulitsa m’sitolo, alimi, ndi anthu ochokera kuulendo wokasodza ku South China Sea.
Kunganenedwedi kuti “zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka” mu Hong Kong. (Mateyu 9:37) Pakali pano, chiŵerengero cha Mboni za Yehova kwa anthu m’dzikolo chili pa 1 kwa 2,300. Pozindikira kufulumira kwa ntchito yotuta, pafupifupi 600 mwa ofalitsa Ufumu 2,600 ndiwo apainiya kumeneko, kapena ofalitsa anthaŵi yonse a mbiri yabwino. Mboni za Yehova mu Hong Kong, mofanana ndi ena kwina kulikonse, zimazindikira kuti “madalitso a Yehova alemeretsa.” (Miyambo 10:22) Chifukwa chake, izo zimagwira ntchito zolimba kuti zithandize anthu ena ambiri m’chitaganya chotukukacho kupeza chuma checheni.
-
-
Kodi Mumatsatira Yehova ndi Mtima Wonse?Nsanja ya Olonda—1993 | May 15
-
-
Kodi Mumatsatira Yehova ndi Mtima Wonse?
“OLUNGAMA alimba mtima ngati mkango.” (Miyambo 28:1) Amasonyeza chikhulupiriro, amadalira Mawu a Mulungu, ndipo amapita patsogolo muutumiki wa Yehova molimba mtima pokumana ndi upandu uliwonse.
Pamene Aisrayeli anali mu Sinai Mulungu atawalanditsa muundende wa ku Igupto m’zaka za zana la 16 B.C.E., makamaka amuna aŵiri anasonyeza kuti anali olimba mtima monga mikango. Iwo anasonyezanso kukhulupirika kwa Yehova poyang’anizana ndi
-