-
Gulu Lamphamvu la Asilikali a YehovaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 52
Gulu Lamphamvu la Asilikali a Yehova
Beni-hadadi anali mfumu ya Siriya ndipo ankakonda kupita kukamenyana ndi Aisiraeli. Koma nthawi zonse mneneri Elisa ankadziwitsa mfumu ya Isiraeli ndipo mfumuyo inkathawa. Ndiyeno Beni-hadadi anaganiza zotuma asilikali ake kuti akagwire Elisa. Iye anamva kuti Elisayo ali ku Dotani.
Asilikali a Siriya anafika ku Dotani usiku n’kuzungulira mzindawo. M’mawa, mtumiki wa Elisa atatuluka panja anaona gulu lalikulu la asilikali. Iye anachita mantha kwambiri ndipo anafuula kuti: ‘Mayo ine mbuyanga! Titani?’ Koma Elisa anamuuza kuti: ‘Usaope, ifetu tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.’ Ndiyeno Yehova anatsegula maso a mtumikiyo ndipo anaona kuti m’mapiri onse ozungulira mzindawo munali mahatchi ndi magaleta ankhondo oyaka moto.
Pamene asilikali a Siriya ankafuna kugwira Elisa, iye anapemphera kuti: ‘Chonde Yehova achititseni khungu.’ Mwadzidzidzi, asilikali aja anapezeka kuti sakuzindikira kumene ali ngakhale kuti ankaona. Zitatero Elisa anawauza kuti: ‘Mwasocheratu. Bwerani kuno ndikuperekezeni kwa munthu amene mukufuna.’ Asilikaliwo anayamba kumutsatira mpaka kukafika ku Samariya kumene mfumu ya Aisiraeli inkakhala.
Apa m’pamene asilikaliwo anazindikira kumene ali. Mfumuyo itawaona inafunsa Elisa kuti: ‘Kodi ndiwaphe?’ Kodi Elisa anaona ngati umenewu unali mwayi woti aphe anthu amene ankafuna kumuphawo? Ayi. M’malomwake anauza mfumuyo kuti: ‘Musawaphe. Apatseni chakudya adye kenako muwalole kuti azipita.’ Choncho mfumuyo inawakonzera phwando lalikulu. Atamaliza kudya ananyamuka n’kumapita kwawo.
“Ndipotu ife sitikayikira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi zimene amafuna, amatimvera.”—1 Yohane 5:14
-
-
Yehoyada Anali Wolimba MtimaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 53
Yehoyada Anali Wolimba Mtima
Yezebeli anali ndi mwana wamkazi dzina lake Ataliya. Mwanayu anali woipa ngati mayi ake. Ataliya anakwatiwa ndi mfumu ya Yuda. Mwamuna wake atamwalira, mwana wake wamwamuna anakhala mfumu. Ndiyeno mwana wakeyo atamwaliranso, Ataliya anayamba kulamulira. Iye anayesetsa kupha anthu onse akubanja lachifumu amene akanalowa ufumu. Anapha ngakhale adzukulu ake ndipo anthu onse ankamuopa kwambiri.
Mkulu wa Ansembe Yehoyada ndi mkazi wake Yehoseba anadziwa kuti zimene Ataliya ankachitazi zinali zoipa. Choncho anatenga Yehoasi, yemwe anali mdzukulu wake wa Ataliya, n’kukamubisa m’kachisi ndipo anakulira kumeneko. Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti Ataliya akazindikira akhoza kuwapha.
Yehoasi atakwanitsa zaka 7, Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a magulu a asilikali ndi Alevi n’kuwauza kuti: ‘Muime pamakomo a kachisi ndipo muonetsetse kuti aliyense asalowe muno.’ Ndiyeno Yehoyada anamuika Yehoasi kukhala mfumu ya Yuda n’kumuveka chipewa chachifumu. Atatero, Ayuda anafuula kuti: ‘Mfumu ikhale ndi moyo wautali!’
Ataliya atamva phokoso la anthu, anathamangira kukachisi. Ataona mfumu yatsopanoyo, anafuula kuti: ‘Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!’ Zitatero atsogoleri a asilikali aja anamugwira n’kumutulutsira kunja ndipo anakamupha. Koma Ataliya anali atasocheretsa kwambiri Ayuda.
Yehoyada anathandiza kuti Ayuda achite pangano ndi Yehova ndipo analonjeza kuti azilambira iye yekha. Anawauzanso kuti akagwetse kachisi wa Baala n’kuphwanya mafano onse. Kuwonjezera apo, anasankha ansembe ndi Alevi oti azitumikira pakachisi kuti anthu ayambirenso kulambira Yehova. Ndiponso anaika alonda oti azikhala pageti n’cholinga choti azionetsetsa kuti aliyense wodetsedwa asalowe. Ndiyeno Yehoyada ndi atsogoleri a magulu a asilikali aja anatenga Yehoasi n’kupita naye kunyumba ndipo anamukhazika pampando wachifumu. Ayuda anasangalala kwambiri. Apa tsopano iwo akanatha kulambira Yehova bwinobwino, popanda kuopsezedwa ndi Ataliya kapena kusokonezedwa ndi anthu olambira Baala. Kodi waona mmene kulimba mtima kwa Yehoyada kunathandiza anthu ambiri?
“Musachite mantha ndi amene amapha thupi koma sangathe kupha moyo. Mʼmalomwake, muziopa amene angathe kuwononga zonse ziwiri, moyo ndi thupi lomwe mʼGehena.”—Mateyu 10:28
-