-
Ufumu Umene Udzalamulire Mpaka KalekaleZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 60
Ufumu Umene Udzalamulire Mpaka Kalekale
Tsiku lina usiku, Nebukadinezara analota maloto odabwitsa. Malotowo anamuvutitsa kwambiri moti sanagonenso. Kenako anaitana amatsenga ake n’kuwauza kuti: ‘Ndiuzeni zimene ndalota.’ Amatsengawo anati: ‘Inuyo mutiuze zimene mwalota ndipo ifeyo tikumasulirani malotowo.’ Koma Nebukadinezara anawauza kuti: ‘Ayi. Inuyo mundiuze zimene ndalota, apo ayi ndikuphani.’ Iwo anamuuzanso kachiwiri kuti: ‘Tiuzeni malotowo ndipo ife tikumasulirani.’ Iye anati: ‘Nonsenu mukungofuna kundipusitsa. Tanenani. Ndalota chiyani?’ Iwo anamuyankha kuti: ‘Palibe munthu amene angathe kuchita zimenezi. Zimene mukufunazi n’zosatheka.’
Nebukadinezara anakwiya kwambiri moti analamula kuti amuna onse anzeru m’dzikolo aphedwe. Apa ndiye kuti nayenso Danieli, Shadireki, Misheki ndi Abedinego akanaphedwa. Danieli atamva zimenezi anapempha mfumu kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake. Kenako iye ndi anzakewo anapemphera kwa Yehova kuti awathandize. Ndiye kodi Yehova anatani?
Kudzera m’masomphenya, Yehova anauza Danieli maloto a Nebukadinezara komanso tanthauzo lake. Tsiku lotsatira Danieli anapita kwa atumiki a mfumu n’kuwauza kuti: ‘Musaphe munthu aliyense. Ine ndikauza mfumu zimene analota.’ Atumikiwo anamutenga n’kupita naye kwa mfumu. Danieli anauza mfumuyo kuti: ‘Mulungu wakudziwitsani zimene zidzachitike m’tsogolo. Zimene munalota ndi izi: Munaona chifaniziro chachikulu. Mutu wake unali wagolide, chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva, mimba ndi ntchafu zake zinali zakopa, miyendo yake inali yachitsulo ndipo mapazi ake anali achitsulo chosakanikirana ndi dongo. Kenako mwala unadulidwa kuphiri ndipo unamenya mapazi a chifanizirocho. Chifanizirocho chinaphwanyika n’kusanduka fumbi lomwe linauluzika ndi mphepo. Ndiyeno mwala uja unakula n’kukhala phiri lalikulu ndipo linadzaza padziko lonse lapansi.’
Kenako Danieli anati: ‘Tanthauzo la maloto anuwa ndi ili: Ufumu wanu ndi mutu wagolidewo. Siliva akuimira ufumu womwe udzabwere pambuyo panu. Kenako padzabwera ufumu wina wangati kopa umenenso udzalamulire padziko lonse. Pambuyo pa umenewo padzabwera ufumu wolimba ngati chitsulo. Pomaliza padzabwera ufumu wogawanika, mbali zake zina zidzakhala zolimba ngati chitsulo koma zina zidzakhala zosalimba ngati dongo. Mwala umene unakula n’kukhala phiri, ukuimira Ufumu wa Mulungu. Ufumuwu udzaphwanya maufumu onse ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.’
Nebukadinezara atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. Kenako anati: ‘Mulungu wako ndi amene wakuululira malotowa. Palibenso Mulungu wina wofanana naye.’ Nebukadinezara anapatsa Danieli udindo woti aziyang’anira anthu onse anzeru. Anamuikanso kukhala wolamulira chigawo chonse cha Babulo. Kodi waona mmene Yehova anayankhira pemphero la Danieli?
“Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene mʼChiheberi amatchulidwa kuti Aramagedo.”—Chivumbulutso 16:16
-
-
Anakana Kulambira FanoZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 61
Anakana Kulambira Fano
Patadutsa nthawi kuchokera pamene Mfumu Nebukadinezara analota, anapanga fano lalikulu la golide. Fanoli analiimika m’chigwa cha Dura ndipo anaitana anthu onse a maudindo akuluakulu m’boma kuphatikizapo Shadireki, Misheki ndi Abedinego. Anthuwo atasonkhana, mfumu inalamula kuti: ‘Mukangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira, mugwade n’kulambira fanoli. Aliyense amene sagwadira fanoli aponyedwa mung’anjo ya moto.’ Kodi anyamata atatu a Chiheberiwo anatani? Kodi analola kugwadira fanolo kapena anatsimikiza kulambira Yehova yekha?
Kenako mfumu inalamula kuti nyimbo iyambe. Aliyense anagwada ndi kulambira fano lija. Koma Shadireki, Misheki ndi Abedinego sanagwade. Anthu ena ataona, anauza mfumu kuti: ‘Anyamata atatu a Chiheberi aja akukanatu kulambira fanoli.’ Nebukadinezara anaitanitsa anyamatawo n’kuwauza kuti: ‘Ndikupatsani mwayi wina woti mulambire fanoli. Ngati simulambira ndikuponyani mung’anjo ya moto ndipo palibe mulungu amene angakupulumutseni m’manja mwanga.’ Iwo anayankha kuti: ‘Musavutike n’kutipatsa mwayi wina. Mulungu wathu akhoza kutipulumutsa. Koma ngati satipulumutsa, dziwani mfumu kuti ife sitingalambire fano lanuli.’
Nebukadinezara atamva zimenezi, anapsa mtima kwambiri. Iye anauza anthu kuti: ‘Sonkhezerani ng’anjo kuwirikiza ka 7 kuti ikhale yotentha kuposa mmene imakhalira!’ Ndiyeno analamula asilikali ake kuti: ‘Amangeni ndipo muwaponye mung’anjomo!’ Ng’anjoyo inali itatentha kwambiri moti asilikaliwo atangoyandikira, anafa nthawi yomweyo. Aheberi atatu aja anaponyedwadi mung’anjomo. Koma Nebukadinezara atasunzumira, anaona kuti mung’anjo muja munali anthu 4 osati atatu. Ataona izi, anachita mantha kwambiri ndipo anafunsa nduna zake kuti: ‘Kodi si paja tinaponya anthu atatu m’motowu? Inetu ndikuonamo anthu 4, ndipo winayo akuoneka ngati mngelo!’
Kenako Nebukadinezara anafika pafupi ndi ng’anjo ija n’kufuula kuti: ‘Tulukani inu atumiki a Mulungu wam’mwambamwamba!’ Anthu onse anadabwa kuona Shadireki, Misheki ndi Abedinego akutuluka koma sanapse paliponse. Khungu, tsitsi komanso zovala zawo sizinapse ndiponso sankamveka fungo lamoto.
Ndiyeno Nebukadinezara anati: ‘Mulungu wa Shadireki, Misheki ndi Abedinego ndi Mulungu wamkulu. Anatumiza mngelo wake kudzawapulumutsa. Palibe mulungu wina wofanana naye.’
Kodi iweyo ungakhale wokhulupirika kwa Yehova ngakhale utakumana ndi mavuto, ngati mmene anachitira anyamata a Chiheberi atatuwa?
“Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.”—Mateyu 4:10
-