Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Danieli Anaponyedwa M’dzenje la Mikango
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Anthu ansanje apeza Danieli akupemphera pafupi ndi windo lotsegula

      MUTU 64

      Danieli Anaponyedwa M’dzenje la Mikango

      Pa nthawi ina Dariyo Mmedi anayamba kulamulira ku Babulo. Iye anaona kuti Danieli anali ndi luso lapadera choncho anamusankha kuti akhale nduna komanso kuti aziyang’anira nduna zinzake. Nduna zinazo ndi anthu ena anayamba kumuchitira nsanje ndipo ankafuna kumupezera chifukwa. Iwo ankadziwa kuti Danieli ankakonda kupemphera kwa Yehova katatu tsiku lililonse. Choncho anauza Dariyo kuti: ‘Mfumu, mukhazikitse lamulo loti aliyense azipemphera kwa inuyo basi. Munthu akapanda kumvera lamuloli, aziponyedwa m’dzenje la mikango.’ Zimenezi zinamusangalatsa Dariyo ndipo anakhazikitsadi lamuloli.

      Danieli atangomva za lamulo latsopanoli, anapita kunyumba kwake. Ndipo windo lili chitsegulireni, anagwada n’kuyamba kupemphera kwa Yehova. Anthu amene ankamuchitira nsanje aja ataona, analowa n’kumupeza akupemphera. Zitatero anathamangira kwa Dariyo n’kukamuuza kuti: ‘Mfumu, Danieli sakumvera lamulo lanu lija. Akupitirizabe kupemphera kwa Mulungu wake katatu tsiku lililonse.’ Popeza Dariyo ankakonda kwambiri Danieli, sankafuna kuti aphedwe. Choncho kwa tsiku lonse, anayesetsa kuti apeze njira yomupulumutsira. Koma poti sizinkatheka kuti munthu aliyense asinthe lamulo limene mfumu yasainira, Dariyo analamula kuti Danieli aponyedwe m’dzenje la mikango yolusa.

      Tsiku limeneli Dariyo sanagone ndipo ankangoganizira za Danieli. Ndiyeno kutacha, anathamangira kudzenje kuja ndipo anafunsa Danieli mofuula kuti: ‘Kodi Mulungu wako wakupulumutsa?’

      Danieli anayankha kuti: ‘Mngelo wa Yehova anatseka pakamwa pa mikango moti sinandivulaze.’ Dariyo atamva zimenezi anasangalala kwambiri. Ndiye analamula kuti Danieli atulutsidwe m’dzenje muja. Iye anatuluka wosakandika paliponse. Zitatero mfumu inalamula kuti: ‘Ponyani m’dzenjemu anthu amene amafunira zoipa Danieli.’ Atangowaponya m’dzenjemo, mikango ija inawakhadzulakhadzula.

      Ndiyeno Dariyo analamula anthu ake onse kuti: ‘Aliyense azitamanda Mulungu wa Danieli chifukwa wamupulumutsa m’dzenje la mikango.’

      Kodi iweyo umapemphera kwa Yehova tsiku lililonse ngati mmene Danieli ankachitira?

      Daniel in the lions’ pit

      “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.”​—2 Petulo 2:9

      Mafunso: Kodi Danieli ankachita chiyani katatu patsiku? Kodi Yehova anachita chiyani kuti apulumutse Danieli?

      Danieli 6:1-28

  • Esitere Anapulumutsa Anthu a Mtundu Wake
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Mfumukazi Esitere akukaonekera kwa Mfumu Ahasiwero

      MUTU 65

      Esitere Anapulumutsa Anthu a Mtundu Wake

      Mfumukazi Esitere

      Esitere anali mtsikana wa Chiyuda ndipo ankakhala mumzinda wa Susani ku Perisiya. Banja lawo linatengedwa ndi Nebukadinezara kuchokera ku Yerusalemu. Ndiyeno ku Perisiyako ankaleredwa ndi wachibale wake, dzina lake Moredekai, yemwe ankagwira ntchito kwa Mfumu Ahasiwero.

      Pa nthawi ina, Mfumu Ahasiwero ankafuna mfumukazi yatsopano. Ndiye atumiki ake anamubweretsera akazi onse okongola a m’dzikolo. Esitere analinso gulu lomweli. Mfumuyo inasankha Esitere kuti akhale mfumukazi. Koma Moredekai anauza Esitere kuti asaulule zoti iye ndi Myuda.

      M’dzikolo munali munthu wina dzina lake Hamani. Iye ankayang’anira nduna za mfumu koma anali wonyada kwambiri ndipo ankafuna kuti aliyense azimuweramira. Koma Moredekai sankaweramira Hamani. Choncho Hamani anakwiya kwambiri moti ankafuna kupha Moredekai ndipo atamva zoti Moredekai ndi Myuda, anakonza zoti aphe Ayuda onse. Anauza mfumu kuti: ‘Ayudatu ndi anthu oopsa kwambiri moti muyenera kuwapha onse.’ Zitatero mfumuyo inamupatsa mphamvu yokonza lamulo ndipo inamuuza kuti: ‘Chita chilichonse chimene ukuona kuti chithandiza.’ Hamani anakonza lamulo louza anthu kuti aphe Ayuda onse pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara. Koma Yehova ankaona zonsezi.

      Esitere sankadziwa za lamuloli. Choncho Moredekai anamutumizira chikalata chonena za lamuloli komanso uthenga wakuti: ‘Pita ukalankhule ndi mfumu za nkhaniyi.’ Esitere anati: ‘Aliyense wopita kwa mfumu asanaitanidwe, amaphedwa. Patha masiku 30 mfumu isanandiitane. Koma ndipitabe. Akakandiloza ndi ndodo, ndiye kuti sindiphedwa. Koma akakapanda kutero ndiye kuti ndikaphedwa.’

      Esitere anapitadi kwa mfumu ndipo inamuloza ndi ndodo. Kenako inamufunsa kuti: ‘Esitere, ukufuna ndikuchitire chiyani?’ Esitere anayankha kuti: ‘Ndikupempha kuti inuyo ndi Hamani mubwere kuphwando limene ndikonze.’ Atapita kuphwandolo, anawapempha kuti abwerenso tsiku lotsatira. Pa ulendo wachiwiriwu, mfumu inafunsanso Esitere kuti: ‘Ukufuna ndikuchitire chiyani?’ Iye anayankha kuti: ‘Pali munthu wina amene akufuna kupha ineyo komanso anthu a mtundu wanga. Chonde, tipulumutseni.’ Mfumuyo inafunsa kuti: ‘Ndani akufuna kukuphani?’ Iye anati: ‘Ndi Hamani woipa ali apayu.’ Ahasiwero anakwiya kwambiri moti analamula kuti Hamani aphedwe nthawi yomweyo.

      Komano panalibe munthu aliyense, ngakhale mfumuyo, amene akanafafaniza lamulo lija. Choncho mfumuyo inasankha Moredekai kuti akhale mkulu wa nduna zake ndipo anamupatsa mphamvu yokonza lamulo latsopano. Ndiyeno Moredekai anakonza lamulo lopatsa Ayuda mphamvu kuti akadzaukiridwa adzathe kudziteteza. Tsiku la 13 la mwezi wa Adara litafika, Ayuda anadziteteza kwa adani awo ndipo anawagonjetsa. Kuchokera pa nthawiyi Ayuda anayamba kukondwerera tsiku limeneli chaka chilichonse.

      “Adzakupititsani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa ndinu otsatira anga, kuti iwowo komanso anthu a mitundu ina aphunzire za ine.”​—Mateyu 10:18

      Mafunso: Kodi Hamani anakonzera Ayuda chiwembu chotani? Kodi Esitere anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova?

      Esitere 2:5-20; 3:1-15; 4:1-17; 5:1-8; 7:1-10; 8:1-14; 9:1-28

Mabuku a Chichewa (1974-2026)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena