-
Ezara Ankaphunzitsa Chilamulo cha MulunguZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 66
Ezara Ankaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu
Panali patatha zaka 70 kuchokera pamene Aisiraeli anabwerera ku Yerusalemu. Komabe panali Aisiraeli ena amene ankakhalabe madera ena a mu ufumu wa Perisiya. Mmodzi mwa anthu amenewa anali Ezara ndipo ankaphunzitsa anthu Chilamulo cha Yehova. Ezara anamva kuti Aisiraeli ena amene ankakhala ku Yerusalemu sankatsatira Chilamulo ndiye anaganiza zoti apite kuti akawathandize. Mfumu Aritasasita anamuuza kuti: ‘Mulungu anakupatsa nzeru kuti uziphunzitsa Chilamulo chake. Pita ku Yerusalemu ndipo ungathe kutenga aliyense amene akufuna kupita nawe.’ Ezara anakumana ndi onse amene ankafuna kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapemphera kwa Yehova kuti awathandize kuti ayende bwino pa ulendowu ndipo kenako ananyamuka.
Patatha miyezi 4 anafika ku Yerusalemu. Akalonga anauza Ezara kuti: ‘Aisiraeli asiya kumvera Yehova ndipo akwatira akazi amene amalambira milungu yabodza.’ Ndiye kodi Ezara anatani? Iye anagwada pamaso pa anthu onse n’kupemphera kuti: ‘Yehova, mwatichitira zambiri, koma ifeyo takuchimwirani.’ Anthuwo analapa koma panali zinthu zina zolakwika zomwe ankafunika kukonza. Choncho Ezara anasankha akulu ndi oweruza kuti athandize anthuwo. Mmene pankatha miyezi itatu n’kuti anthu onse amene sankalambira Yehova atathamangitsidwa.
Panali patadutsa zaka 12 ndipo pa nthawiyi Aisiraeli anamanganso mpanda wa Yerusalemu. Choncho anasonkhanitsa anthu n’kuyamba kuwawerengera Chilamulo cha Mulungu. Ezara atangotsegula buku la Chilamulo, anthu onse anaimirira. Iye anatamanda Yehova ndipo nawonso anthuwo anakweza manja potamanda Yehova. Kenako Ezara anayamba kuwerenga Chilamulocho ndipo anthuwo ankamvetsera mwatcheru. Iwo anavomereza kuti anali atasiya kulambira Yehova ndipo analira. Tsiku lotsatira Ezara anapitiriza kuwawerengera Chilamulocho. Anthuwa anazindikira kuti ankafunika kuchita Chikondwerero cha Misasa ndipo nthawi yomweyo anayamba kukonzekera.
Aisiraeli anachita chikondwererochi kwa masiku 7 ndipo anasangalala komanso anathokoza Yehova powapatsa zokolola zambiri. Panali pasanachitike Chikondwerero cha Misasa ngati chimenechi kuyambira m’nthawi ya Yoswa. Chikondwererochi chitatha, anthuwo anasonkhana n’kupemphera kuti: ‘Yehova, munatipulumutsa ku ukapolo, munatidyetsa m’chipululu komanso munatipatsa dziko lokongola. Koma ifeyo takhala tikukuchimwirani mobwerezabwereza. Munatitumizira aneneri koma sitinanawamvere. Komabe munatilezera mtima ndipo munasunga lonjezo lanu kwa Abulahamu. Tsopano tikukulonjezani kuti tizikumverani.’ Atatero analemba lonjezo lawolo ndipo akalonga, Alevi komanso ansembe anatsimikiza lonjezolo ndi chidindo chawo.
“Osangalala ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu nʼkuwasunga!”—Luka 11:28
-
-
Mpanda wa Yerusalemu UnamangidwansoZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 67
Mpanda wa Yerusalemu Unamangidwanso
Zimene tafotokoza m’mutu wapitawu zisanachitike, panachitikanso zinthu zina. Nehemiya anali Mwisiraeli ndipo ankagwira ntchito kwa Mfumu Aritasasita ku Susani. Ndiyeno mchimwene wake anafika kuchokera ku Yuda n’kumuuza kuti: ‘Anthu amene anabwerera ku Yerusalemu ali pa mavuto. Mpanda wa mzinda umene Ababulo anauwononga sunakonzedwe.’ Nehemiya anakhumudwa kwambiri. Iye anaganiza zopita ku Yerusalemu kuti akathandize anthuwo ndiye anapemphera kuti mfumu imulole kupita.
Kenako mfumu inazindikira kuti Nehemiya sakusangalala. Ndiyeno inamufunsa kuti: ‘Ukuoneka wachisoni. Watani?’ Nehemiya anayankha kuti: ‘Ndilekerenji kuoneka wachisoni pamene mzinda wathu wa Yerusalemu suli bwino.’ Mfumuyo inafunsa kuti: ‘Ndiye ukufuna ndikuchitire chiyani?’ Nthawi yomweyo Nehemiya anapemphera chamumtima. Kenako anati: ‘Mungandilole kuti ndipite ku Yerusalemu kukamanga mpanda?’ Mfumuyo inamulola ndipo inaonetsetsa kuti akhale wotetezeka pa ulendo wake wonsewo. Inalamulanso kuti iye akhale bwanamkubwa wa Yuda ndipo anamupatsa matabwa oti akakonzere zitseko zapageti.
Nehemiya atafika ku Yerusalemu anayendera mpanda wonse. Kenako anasonkhanitsa ansembe ndi atsogoleri n’kuwauza kuti: ‘Akuluakulu, zinthu sizili bwino. Tiyenera kumanganso mpandawu.’ Anthuwo anavomera ndipo ntchito inayambika.
Koma adani a Aisiraeli ankawaseka n’kumati: ‘Nkhandwetu ikhoza kugwetsa kampanda kanuko.’ Koma Aisiraeliwo sanasamale zimenezi ndipo anapitiriza kugwira ntchitoyo. Ankamanga bwinobwino mpandawo ndipo unkaoneka wolimba.
Adaniwo anaganiza zoukira Yerusalemu kuchokera m’mbali zosiyanasiyana. Ayuda atamva zimenezo anachita mantha. Koma Nehemiya anawauza kuti: ‘Musaope. Yehova atithandiza.’ Ndiyeno anaika alonda oti aziteteza anthu amene ankagwira ntchitowo, moti adaniwo sanawaukire.
Patangotha masiku 52 ntchito yonse yomanga mpanda komanso kukonza mageti inatha. Ndiyeno Nehemiya anaitanitsa Alevi onse ku Yerusalemu kuti adzautsegulire. Anakonza zoti pakhale magulu awiri oimba. Maguluwa anadutsa pamalo okwera a mpandawo pamasitepe a Geti la Kukasupe ndipo kenaka analowera mbali zosiyana kuzungulira mzindawo. Ankaimba nyimbo zotamanda Yehova pogwiritsa ntchito zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze. Ezara ndi gulu lina anapita mbali ina ya mzindawo ndipo Nehemiya ndi gulu lina anapita mbali ina. Magulu awiriwa anakumana pamalo amene panali kachisi. Kenako anthu onse, amuna, akazi ndi ana omwe, anapereka nsembe kwa Yehova ndipo anachita chikondwerero. Panali phokoso lachisangalalo.
“Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.”—Yesaya 54:17
-