-
Elizabeti Anakhala ndi MwanaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 68
Elizabeti Anakhala ndi Mwana
Patatha zaka zoposa 400 kuchokera pamene mpanda wa Yerusalemu unakonzedwa, wansembe wina ankakhala pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Dzina lake anali Zekariya ndipo mkazi wake anali Elizabeti. Iwo anakhala m’banja zaka zambiri koma analibe mwana. Tsiku lina Zekariya akupereka nsembe m’nyumba yopatulika, anaona mngelo Gabirieli. Zekariya anachita mantha kwambiri, koma Gabirieli anamuuza kuti: ‘Usaope. Ndakubweretsera uthenga wabwino wochokera kwa Yehova. Mkazi wako adzakhala ndi mwana ndipo dzina lake lidzakhala Yohane. Yehova akufuna kuti Yohaneyo adzagwire ntchito yapadera.’ Zekariya anafunsa kuti: ‘Ndingakhulupirire bwanji zimene mukunenazi? Ine ndi mkazi wanga ndife okalamba ndipo n’zosatheka kukhala ndi mwana.’ Gabirieli anati: ‘Mulungu ndi amene wandituma kuti ndidzakuuze zimenezi. Koma poti sukukhulupirira, ukhala wosalankhula mpaka mwanayo adzabadwe.’
Zekariya anakhala m’nyumba yopatulikayo kwa nthawi yaitali mosiyana ndi masiku onse. Ndiyeno atatuluka, anthu ankafuna kudziwa chimene chinamuchedwetsa. Koma Zekariya sankatha kulankhula. Ndiyeno anangoyamba kulankhula pogwiritsa ntchito manja. Anthuwo anazindikira kuti iye walandira uthenga wochokera kwa Mulungu.
Patapita nthawi, zimene mngelo uja ananena zinachitikadi. Elizabeti anakhala woyembekezera ndipo kenako anabereka mwana wamwamuna. Anzake a Elizabeti komanso achibale ake anabwera kudzaona mwanayo ndipo anasangalala kwambiri. Ndiyeno Elizabeti anawauza kuti: ‘Dzina la mwanayu ndi Yohane.’ Anthuwo anati: ‘Koma m’banja lanu mulibe aliyense amene ali ndi dzina limeneli. Bwanji atenge dzina la bambo ake lakuti Zekariya?’ Zitatero, Zekariya analemba kuti: ‘Dzina lake ndi Yohane.’ Atangolemba zimenezi, anayamba kulankhula. Nkhani ya mwanayu inafalikira mu Yudeya monse ndipo anthu ankadabwa kuti: ‘Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani akadzakula?’
Zekariya anadzazidwa ndi mzimu woyera. Ndiyeno ananena kuti: ‘Yehova atamandike. Analonjeza Abulahamu kuti adzatumiza Mesiya kuti atipulumutse. Yohane adzakhala mneneri ndipo adzakonza njira ya Mesiya.’
Pa nthawi yomweyi, zinthu zina zochititsa chidwi zinachitikiranso m’bale wake wa Elisabeti, dzina lake Mariya. M’mutu wotsatira tikambirana nkhani yake.
“Kwa anthu zimenezi nʼzosatheka, koma zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”—Mateyu 19:26
-
-
Gabirieli Anaonekera kwa MariyaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 69
Gabirieli Analankhula ndi Mariya
Elizabeti anali ndi m’bale wake wachitsikana dzina lake Mariya. Iye ankakhala mumzinda wa Nazarete ku Galileya. Mtsikanayu anali pa chibwenzi ndi kalipentala wina dzina lake Yosefe. Ndiyeno patatha miyezi 6 Elizabeti ali woyembekezera, mngelo Gabirieli anapita kwa Mariya n’kumuuza kuti: ‘Moni Mariya. Yehova wakukomera mtima kwambiri.’ Mariya sanamvetse zimene mngeloyu ankatanthauza. Ndiyeno Gabirieli anamuuza kuti: ‘Udzakhala woyembekezera n’kubereka mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu. Iye adzakhala Mfumu ndipo Ufumu wake sudzatha.’
Mariya anafunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zidzatheka bwanji, chifukwa sindinagonepo ndi mwamuna.’ Gabirieli anamuuza kuti: ‘Mulungu sangalephere kuchita chilichonse. Mzimu woyera udzafika pa iwe ndipo udzakhala ndi mwana. Kodi ukudziwa kuti panopa m’bale wako Elizabeti ndi woyembekezera?’ Zitatero, Mariya anayankha kuti: ‘Ndine kapolo wa Yehova. Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.’
Mariya anauyamba ulendo wopita kukaona Elizabeti. Pa nthawiyi, Elizabeti ankakhala mumzinda winawake wakumapiri. Atafika, n’kupereka moni, mwana amene anali m’mimba mwa Elizabeti anayamba kudumpha. Ndiyeno Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera n’kuyamba kunena kuti: ‘Mariya, Yehova wakudalitsa. Ndi mwayi waukulu kuti mayi wa Ambuye wanga wafika m’nyumba mwanga.’ Mariya anati: ‘Moyo wanga ukulemekeza Yehova.’ Mariya anakhala ndi Elizabeti kwa miyezi itatu ndipo kenako anabwerera kwawo ku Nazareti.
Yosefe atamva zoti Mariya ndi woyembekezera ankafuna kuthetsa chibwenzi. Koma ali m’tulo mngelo anamuuza kuti: ‘Usaope kutenga Mariya kuti akhale mkazi wako chifukwa sanachite choipa chilichonse.’ Choncho Yosefe anatengadi Mariya n’kumakakhala naye kwawo.
“Yehova amachita chilichonse chimene wafuna kumwamba ndi padziko lapansi.”—Salimo 135:6
-