Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Angelo akulengeza kwa abusa za kubadwa kwa Yesu

      MUTU 70

      Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

      Pa nthawi ina mu ulamuliro wa Kaisara Augusito, panaperekedwa lamulo loti Ayuda onse abwerere m’mizinda ya kwawo kuti akalembetse m’kaundula. Yosefe ndi Mariya anapita ku Betelehemu komwe kunali kwawo kwa Yosefe. Apa n’kuti Mariya atatsala pang’ono kubereka.

      Atafika ku Betelehemu, anapeza kuti nyumba zonse zogona alendo ndi zodzaza moti anagona m’khola. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu abadwire m’kholamo. Mariya anakulunga mwanayo ndi nsalu zabwino n’kumugoneka modyetsera ziweto.

      Pa nthawiyo, abusa ena ankagona kutchire pafupi ndi ku Betelehemu n’kumayang’anira nkhosa zawo. Mwadzidzidzi, mngelo anafika ndipo pamalo onsewo panawala kusonyeza ulemerero wa Yehova. Abusawo anachita mantha koma mngeloyo anati: ‘Musaope. Ndabwera ndi uthenga wosangalatsa. Lero Mesiya wabadwa ku Betelehemu.’ Nthawi yomweyo, angelo ambirimbiri anaoneka mumlengalenga ndipo ankanena kuti: ‘Alemekezeke Mulungu kumwamba ndipo mtendere ukhale padziko lapansi.’ Kenako angelowo sanaonekenso. Kodi ukudziwa zimene abusawo anachita?

      Abusawo anauzana kuti: ‘Tiyeni ku Betelehemu pompanopompano.’ Nthawi yomweyo ananyamuka ndipo atafika anaona Yosefe ndi Mariya ali ndi kamwana kawo m’khola.

      Aliyense amene anamva zimene angelowo anauza abusawo anadabwa kwambiri. Mariya anaganizira kwambiri mawu a angelowo ndipo sanawaiwale. Abusawo anabwerera kutchire kuja uku akuthokoza Yehova chifukwa cha zonse zimene anaona.

      “Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwere mwakufuna kwanga koma Iyeyo ndi amene anandituma.”​—Yohane 8:42

      Mafunso: Kodi angelo analengeza bwanji za kubadwa kwa Yesu? Kodi abusa aja atafika ku Betelehemu anaona zotani?

      Luka 2:1-20; Yesaya 9:6

  • Yehova Anateteza Yesu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Mariya ndi Yesu akwera pabulu ndipo Yosefe akuyenda nawo limodzi

      MUTU 71

      Yehova Anateteza Yesu

      M’dziko lina lakum’mawa kwa Isiraeli, kunali anthu amene ankakhulupirira kuti nyenyezi zingawathandize kudziwa zinthu. Tsiku lina, anthu ena ochokera kudzikoli anaona chinthu chokhala ngati nyenyezi chikuyenda m’mwamba ndipo anayamba kuchitsatira. Iwo anatsatira “nyenyezi” imeneyo mpaka kukafika ku Yerusalemu. Atafika anayamba kufunsa anthu kuti: ‘Kodi mwana amene adzakhale mfumu ya Ayuda ali kuti? Tabwera kuti tidzamugwadire.’

      Herode atamva zimenezi anada nkhawa kwambiri. Iye anafunsa ansembe aakulu kuti: ‘Paja mfumu imeneyi ikuyenera kubadwira kuti?’ Ansembewo anamuyankha kuti: ‘Aneneri ananena kuti adzabadwira ku Betelehemu.’ Ndiyeno Herode anauza anthu ochokera kum’mawawo kuti: ‘Pitani ku Betelehemu mukafufuze mwanayo. Mukakamupeza mubwere mudzandiuze. Nanenso ndikufuna ndikamugwadire.’ Koma sikuti Herode ankafunadi kuti akamugwadire mwanayo.

      “Nyenyezi” ija inayambanso kuyenda ndipo anthu aja anapitiriza kuitsatira. Ndiyeno inakaima panyumba inayake. Atalowa m’nyumbayo anapeza Yesu ndi amayi ake. Iwo anagwada n’kuweramira mwanayo ndipo anapereka mphatso za golide, lubani ndi mule. Kodi ndi zoona kuti Yehova ndi amene anatuma anthuwa kuti akaone Yesu? Ayi.

      Usiku womwewo, Yehova analankhula ndi Yosefe m’maloto. Anamuuza kuti: ‘Herode akufuna kupha Yesu. Tenga mkazi wako ndi mwanayo ndipo muthawire ku Iguputo. Mukakhale komweko mpaka nthawi imene ndidzakuuzeni kuti mubwerere.’ Nthawi yomweyo, Yosefe ananyamuka ndi banja lake kupita ku Iguputo.

      Ndiyeno Yehova anauza anthu ochokera kum’mawa aja kuti asadzere kwa Herode. Herodeyo atazindikira zoti anthuwo adutsa njira ina, anakwiya kwambiri. Popeza zinali zovuta kuti apeze Yesu, analamula kuti ana aamuna amsinkhu wa Yesu ku Betelehemu aphedwe. Pamene izi zinkachitika, n’kuti Yesu ali ku Iguputo ndipo anali wotetezeka.

      Patapita nthawi, Herode anamwalira. Ndiyeno Yehova anauza Yosefe kuti: ‘Tsopano ukhoza kubwerera.’ Yosefe, Mariya ndi Yesu anabwerera ku Isiraeli ndipo anakafikira ku Nazareti.

      “Ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga . . . . zimene ndinawatumizira kuti achite zidzachitikadi.”​—Yesaya 55:11

      Mafunso: Kodi ndi ndani ankafuna kupha Yesu? Nanga Yehova anateteza bwanji Yesu?

      Mateyu 2:1-23; Mika 5:2

Mabuku a Chichewa (1974-2026)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena