-
Zimene Yesu Anachita Ali Wamng’onoZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 72
Zimene Yesu Anachita Ali Wamng’ono
Yosefe ndi Mariya ankakhala ku Nazareti. Ankakhala limodzi ndi Yesu komanso ana awo ena aamuna ndi aakazi. Yosefe ankagwira ntchito ya ukalipentala kuti azipeza ndalama zothandizira banja lake. Iye ankaphunzitsanso banja lakelo za Yehova komanso Chilamulo chake. Yosefe ndi banja lake ankapita kusunagoge kukalambira Yehova nthawi zonse. Komanso chaka chilichonse banjali linkayenda ulendo wautali wopita ku Yerusalemu kukachita nawo chikondwerero cha Pasika.
Yesu ali ndi zaka 12, banja lawo linapitanso ku Yerusalemu ngati mmene linkachitira zaka zonse. Ku Yerusalemuko kunali anthu ambirimbiri amene anabwera kudzachitanso chikondwerero cha Pasika. Chikondwererochi chitatha Yosefe ndi Mariya komanso anthu ena anayamba ulendo wobwerera kunyumba. Iwo ankaganiza kuti Yesu ali nawo limodzi. Koma kenako anazindikira kuti Yesu palibe. Anamuyang’ana pakati pa achibale onse koma sanamupeze.
Yosefe ndi Mariya anabwereranso ku Yerusalemu ndipo anamufufuza kwa masiku atatu koma sanamupeze. Kenako anapita kukamuyang’ana m’kachisi. Anamupeza atakhala pakati pa aphunzitsi angapo ndipo ankamvetsera zimene iwo ankanena komanso ankawafunsa mafunso. Aphunzitsiwo anachita chidwi kwambiri ndi Yesu moti anayamba kumufunsa mafunso. Koma anadabwa kwambiri ndi mmene iye ankawayankhira. Anazindikira kuti Yesu ankadziwa bwino Chilamulo cha Yehova.
Yosefe ndi Mariya anali ndi nkhawa kwambiri. Atakumana naye, Mariya ananena kuti: ‘Takhala tikukufufuza kwa nthawi yaitali. Unali kuti?’ Koma Yesu anayankha kuti: ‘Kodi simumadziwa kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?’
Yesu ananyamuka ndi makolo akewo n’kumapita ku Nazareti. Yosefe anaphunzitsa Yesu ntchito ya ukalipentala. Kodi ukuganiza kuti Yesu ali wamng’ono anali munthu wotani? Pamene iye ankakula nzeru zakenso zinkawonjezeka ndipo ankakondedwa ndi Mulungu komanso anthu.
“Ndimasangalala kuchita zimene mumafuna, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.”—Salimo 40:8
-
-
Yohane Anakonza NjiraZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 73
Yohane Anakonza Njira
Yohane anali mwana wa Zekariya ndi Elizabeti. Iye atakula anakhala mneneri. Yehova anagwiritsa ntchito Yohane pophunzitsa anthu kuti Mesiya akubwera. Yohane sankaphunzitsa m’masunagoge kapena m’tauni koma ankalalikira m’chipululu. Anthu ochokera ku Yerusalemu komanso ku Yudeya konse ankapita kwa Yohane kuti akawaphunzitse. Iye ankawaphunzitsa kuti akuyenera kusiya kuchita zoipa kuti azisangalatsa Mulungu. Anthu ambiri akamva uthenga wakewu, ankalapa ndipo iye ankawabatiza mumtsinje wa Yorodano.
Yohane sankakonda chuma. Ankavala chovala chaubweya wa ngamila ndipo ankadya dzombe ndi uchi. Anthu ambiri ankachita chidwi ndi Yohane. Nawonso Afarisi ndi Asaduki ankapita kukamuona ngakhale kuti iwo anali onyada. Koma Yohane ankawauza kuti: ‘Muyenera kusiya zoipa n’kulapa. Musaganize kuti ndinu apadera chifukwa chakuti mumati ndinu ana a Abulahamu. Umenewo si umboni woti ndinu ana a Mulungu.’
Anthu ambiri ankapita kwa Yohane kukamufunsa kuti: ‘Titani kuti tisangalatse Mulungu?’ Yohane ankauza Ayuda kuti: ‘Ngati muli ndi malaya awiri, enawo mupatseko munthu amene alibiretu.’ Kodi ukudziwa chifukwa chake ananena zimenezi? Ankafuna kuti ophunzira ake adziwe zoti, kuti asangalatse Mulungu ayenera kukhala achikondi.
Okhometsa misonkho ankawauza kuti: ‘Muzichita zinthu mwachilungamo ndipo musamabere aliyense.’ Asilikali ankawauza kuti: ‘Musamalandire ziphuphu komanso musamaname.’
Ansembe ndi Alevi nawonso anapita kwa Yohane ndipo anamufunsa kuti: ‘Kodi ndinu ndani? Anthutu akufuna kukudziwani.’ Koma Yohane ankawayankha kuti: ‘Ndine mawu a winawake wofuula m’chipululu. Ndimathandiza anthu kudziwa Yehova mogwirizana ndi zimene Yesaya analosera.’
Anthu ankasangalala ndi zimene Yohane ankawaphunzitsa. Ambiri ankaganiza kuti mwina ndi Mesiya. Koma Yohane ankawauza kuti: ‘Wina wamkulu kuposa ine akubwera. Ine si woyenera kumasula zingwe za nsapato zake. Paja ine ndimabatiza m’madzi, koma iye adzakubatizani ndi mzimu woyera.’
“Munthu ameneyu anabwera ngati mboni, kuti adzachitire umboni za kuwala nʼcholinga chakuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye.”—Yohane 1:7
-