Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesu Anayeretsa Kachisi
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Yesu akugwiritsa ntchito chikwapu potulutsa nyama m’kachisi ndiponso anagubuduza matebulo a osintha ndalama

      MUTU 76

      Yesu Anayeretsa Kachisi

      M’chaka cha 30 C.E., Yesu anapita ku Yerusalemu pa nthawi ya chikondwerero cha Pasika. Anthu enanso ambiri anapita ku Yerusalemuko kukachita chikondwererochi. Pa nthawiyi, anthu ankapereka nsembe za nyama pakachisi. Ena ankabweretsa nyamazi, koma ena ankagula ku Yerusalemu komweko.

      Yesu atalowa m’kachisi anapeza kuti anthu akugulitsa nyama mmenemo. Tangoganiza! Ankachita malonda m’nyumba mwa Yehova mwenimwenimo! Ndiye kodi Yesu anatani? Nthawi yomweyo anatenga zingwe n’kupanga chokwapulira. Ndiyeno anayamba kuthamangitsa nkhosa ndi ng’ombe zimene zinali m’kachisimo. Anagubuduzanso matebulo a anthu amene ankachita malondawo komanso anakhuthulira pansi ndalama zawo. Iye anauza anthu amene ankagulitsa nkhunda kuti: ‘Chotsani izi muno! Nyumba ya Bambo anga musaisandutse malo ochitira bizinezi!’

      Anthu anadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anachitazi. Ophunzira ake anakumbukira ulosi wonena za Mesiya wakuti: ‘Ndidzakhala wodzipereka kwambiri panyumba ya Yehova.’

      M’chaka cha 33 C.E., Yesu anayeretsanso kachisi kachiwiri pothamangitsa anthu amene ankachita malonda panyumba ya Yehova. Iye sanalole kuti munthu aliyense azinyoza nyumba ya Yehova.

      “Simungakhale akapolo a Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”​—Luka 16:13

      Mafunso: Kodi Yesu anatani ataona anthu akuchita malonda m’kachisi? N’chifukwa chiyani anachita zimenezi?

      Mateyu 21:12, 13; Maliko 11:15-17; Luka 19:45, 46; Yohane 2:13-17; Salimo 69:9

  • Yesu Anakumana ndi Mayi Pachitsime
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Yesu akulankhula ndi mayi wa Chisamariya pachitsime cha Yakobo

      MUTU 77

      Yesu Anakumana ndi Mayi Pachitsime

      Pasika atatha, Yesu ndi ophunzira ake anayamba ulendo wobwerera ku Galileya ndipo anadutsa ku Samariya. Atafika mumzinda wa Sukari, Yesu anaima pachitsime cha Yakobo. Ophunzira ake anamusiya akupuma, n’kupita kukagula chakudya mumzindawo.

      Ndiyeno panafika mayi wina kudzatunga madzi. Yesu anamuuza kuti: “Mundigawireko madzi akumwa mayi.” Mayiyo anati: ‘Bwanji mukupempha madzi kwa ine? Inetu ndine Msamariya. Paja Ayuda salankhula ndi Asamariya.’ Koma Yesu anamuuza kuti: ‘Mukanadziwa kuti ndine ndani, bwenzi mutandipempha kuti ndikupatseni madzi amoyo.’ Mayiyo anafunsa Yesu kuti: ‘Mukutanthauza chiyani? Inu mulibe chotungira ndiye madzi muwatenga kuti?’ Yesu anayankha kuti: ‘Aliyense wakumwa madzi amene ine ndingam’patse sadzamvanso ludzu ngakhale pang’ono.’ Ndiyeno mayiyo anati: “Bambo, ndipatseni madzi amenewo.”

      Kenako Yesu anauza mayiyo kuti: ‘Pitani mukaitane mwamuna wanu.’ Koma mayiyo anati: “Ndilibe Mwamuna.” Yesu anati: ‘Mwanena zoona. Chifukwa mwakwatiwapo ndi amuna 5, ndipo mwamuna amene mukukhala naye panopa si mwamuna wanu.’ Mayiyo atamva zimenezi anati: ‘Ndazindikira kuti ndinu mneneri. Ife timakhulupirira kuti tiyenera kulambira Mulungu m’phiri ili, pamene Ayudanu mumati tiyenera kulambira Mulungu ku Yerusalemu kokha. Koma ndikukhulupirira kuti Mesiya akadzabwera adzatiphunzitsa kuti tizilambira bwanji.’ Ndiyeno Yesu anamuuza zimene anali asanauzepo aliyense. Anati: ‘Ineyo ndine Mesiya.’

      Yesu akulankhula ndi Asamariya

      Mayiyo anathamanga n’kukauza Asamariya kuti: ‘Ndakumana ndi Mesiya. Akudziwa zonse zokhudza ineyo. Tiyeni mukamuone.’ Anthuwo anapita naye limodzi ndipo Yesu anawaphunzitsa zinthu zambiri.

      Asamariyawo anapempha Yesu kuti akhalebe mumzinda wawo. Choncho anakhala nawo kwa masiku awiri n’kumawaphunzitsa ndipo ambiri anamukhulupirira. Iwo anauza mayi uja kuti: ‘Zimene tamva kwa munthuyo zatithandiza kudziwa kuti iyedi ndi mpulumutsi wa dziko.’

      “‘Bwera!’ Komanso aliyense amene akumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi opatsa moyo kwaulere.”​—Chivumbulutso 22:17

      Mafunso: N’chifukwa chiyani mayi wa Chisamariya anadabwa ataona kuti Yesu akulankhula naye? Kodi Yesu anamuuza zinthu ziti?

      Yohane 4:1-42

Mabuku a Chichewa (1974-2026)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena