Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesu Ankalalikira Uthenga wa Ufumu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Yesu ndi wophunzira wake akulalikira

      MUTU 78

      Yesu Ankalalikira Uthenga wa Ufumu

      Yesu atangobatizidwa, anayamba kulalikira kuti: ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ Iye ankalalikira mu Galileya ndi mu Yudeya monse ndipo ophunzira ake ankapita naye limodzi. Yesu atabwerera kwawo ku Nazareti, anapita kusunagoge n’kuyamba kuwerenga mokweza mpukutu wa Yesaya. Iye anati: ‘Yehova wandipatsa mzimu woyera kuti ndilalikire uthenga wabwino.’ Anthu a ku Nazareti ankafuna kuona Yesu akuchita zozizwitsa. Koma zimene anawerengazi zikusonyeza kuti, chifukwa chachikulu chimene Mulungu anam’patsira mzimu woyera, chinali choti azilalikira uthenga wabwino. Kenako Yesu anauza anthuwo kuti: ‘Lero ulosi uwu wakwaniritsidwa.’

      Yesu atachoka kumeneku anapita kunyanja ya Galileya komwe anakapeza ophunzira ake 4 akuwedza nsomba. Iye anawauza kuti: ‘Nditsatireni, ndikusandutsani asodzi a anthu.’ Ophunzirawa anali Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane. Nthawi yomweyo iwo anasiya bizinezi yawo yopha nsomba n’kuyamba kumutsatira. Anayenda naye ku Galileya konse n’kumalalikira za Ufumu wa Mulungu. Ankalalikira m’masunagoge, m’misika komanso m’misewu. Kulikonse kumene ankapita anthu ambiri ankawatsatira. Nkhani yokhudza Yesu inali m’kamwam’kamwa moti mpaka inafika ku Siriya.

      Yesu anapatsa otsatira ake ena mphamvu zochiritsa komanso kutulutsa ziwanda. Iye ankalalikira m’mizinda komanso m’midzi limodzi ndi ophunzira ake ena. Azimayi angapo okhulupirika ankathandiza Yesu ndi otsatira ake. Ena mwa azimayiwa anali Mariya Mmagadala, Jowana komanso Suzana.

      Kenako Yesu anaphunzitsa otsatira akewa n’kuwatumiza kuti akalalikire. Iwo analalikira ku Galileya konse. Anthu ochuluka anakhala ophunzira a Yesu ndipo anabatizidwa. Ambiri ankafuna kuphunzira moti Yesu anawayerekezera ndi m’munda woti ukufunika kukolola. Anati: ‘Pemphani Yehova kuti atumize antchito okakolola.’ Kenako anasankha ophunzira 70 n’kuwatumiza awiriawiri kuti akalalikire ku Yudeya konse. Iwo ankaphunzitsa anthu onse za Ufumu. Ophunzirawa atabwerako, anafotokozera Yesu zinthu zosangalatsa zimene zinachitika. Mdyerekezi sanathe kulepheretsa ntchito yolalikirayi.

      Yesu anathandiza ophunzira akewo kuti adzathe kupitiriza ntchito yofunikayi iye akadzapita kumwamba. Anawauzanso kuti: ‘Muzilalikira padziko lonse komanso muziphunzitsa anthu Mawu a Mulungu ndipo muziwabatiza.’

      “Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.”​—Luka 4:43

      Mafunso: Kodi Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yotani? Kodi ophunzira ake ankasangalala ndi ntchitoyi?

      Mateyu 4:17-25; 9:35-38; 28:19, 20; Maliko 1:14-20; Luka 4:14-21; 8:1-3; 10:1-22

  • Yesu Anachita Zozizwitsa Zambiri
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Anthu odwala abwera kwa Yesu kuti awachiritse

      MUTU 79

      Yesu Anachita Zozizwitsa Zambiri

      Yesu anabwera padzikoli kudzalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Yehova anamupatsa mzimu woyera kuti azitha kuchita zozizwitsa. Anachita zimenezi pofuna kusonyeza zimene Yesu adzachite akamadzalamulira dziko lapansili. Yesu ankatha kuchiritsa matenda alionse. Akapita kulikonse, anthu ankamupempha kuti awachiritse ndipo ankawachiritsadi. Ankachiritsa anthu amene ali ndi vuto losaona komanso losamva, ofa ziwalo ndiponso ankatulutsa ziwanda. Ngakhale kungogwira zovala zake, munthu ankatha kuchira. Kulikonse kumene Yesu wapita, anthu ankamutsatira. Ngakhale pa nthawi imene akufuna kukhala payekha, anthu akamutsatira sankawathamangitsa.

      Tsiku lina anthu anabwera ndi munthu wofa ziwalo kunyumba imene Yesu anali. Koma sanathe kulowa chifukwa m’nyumbamo munali anthu ambiri. Choncho anthuwo anaboola padenga n’kutsitsira munthuyo m’kati. Yesu ataona munthuyo anamuuza kuti: ‘Imirira uziyenda.’ Munthuyo anayambadi kuyenda ndipo anthu anadabwa kwambiri.

      Yesu akulowa m’mudzi wina anthu akhate 10 anaima chapatali n’kukuwa kuti: ‘Yesu tithandizeni!’ Pa nthawiyo munthu wodwala khate sankaloledwa kukhala pafupi ndi anthu ena. Yesu anauza akhatewo kuti apite kukachisi. Chilamulo cha Yehova chinkati munthu wakhate akachira, azipita kukachisi kukadzionetsa kwa ansembe. Ali m’njira, onse anazindikira kuti achira. Zitatero mmodzi anabwerera n’kupita kukathokoza Yesu ndipo ankatamanda Mulungu. Pa akhate 10 onsewo, ndi mmodzi yekhayu amene anapita kukathokoza.

      Panalinso mayi wina amene anadwala kwa zaka 12 ndipo ankafunitsitsa atachira. Choncho ataona Yesu anayamba kumutsatira ndipo kenako anagwira m’mphepete mwa malaya ake akunja. Nthawi yomweyo anachira. Zimenezi zitachitika Yesu anafunsa kuti: “Ndi ndani wagwira malaya anga akunjawa?” Mayiyo anachita mantha, komabe anabwera pafupi n’kumuuza Yesu chilungamo. Yesu anamulimbikitsa pomuuza kuti: ‘Mwanawe, pita mu mtendere.’

      Komanso mtsogoleri wina wa sunagoge dzina lake Yairo anapempha Yesu kuti: ‘Tiyeni tipite kunyumba kwanga kuti mukachiritse mwana wanga wamkazi yemwe akudwala kwambiri.’ Koma Yesu asanafike kunyumba kwa Yairo, mwanayo anamwalira. Yesu atafikako, anapeza anthu ambiri amene anabwera kudzakhala ndi banjalo pa nthawi yovutayi. Yesu anawauza kuti: ‘Musalire, mwanayu sanamwalire koma akugona.’ Kenako anagwira dzanja la mwanayo n’kunena kuti: “Mtsikana iwe, dzuka!” Nthawi yomweyo anadzuka n’kukhala tsonga ndipo Yesu anauza makolo ake kuti amupatse chakudya. Ukuganiza kuti makolo akewo anamva bwanji ataona kuti mwana wawo ali moyo?

      Yesu waukitsa mwana wamkazi wa Yairo

      “Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera ndi mphamvu. Popeza Mulungu anali naye, anayenda mʼdziko lonse nʼkumachita zabwino ndiponso kuchiritsa anthu onse amene Mdyerekezi ankawazunza.”​—Machitidwe 10:38

      Mafunso: Kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kuti azitha kuchiritsa matenda onse? Kodi n’chiyani chinachitikira mwana wamkazi wa Yairo?

      Mateyu 9:18-26; 14:36; Maliko 2:1-12; 5:21-43; 6:55, 56; Luka 6:19; 8:41-56; 17:11-19

Mabuku a Chichewa (1974-2026)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena