NYIMBO 62
Nyimbo Yatsopano
Losindikizidwa
1. Imbira M’lungu, imba nyimbo yatsopano.
Unene kwa onse ntchito zake zonse.
Umutamande, Mulungu ndi wopambana.
Ndi wachilungamo
Poweruza anthu.
(KOLASI)
Imbani
Nyimbo yatsopano.
Imbani,
Yehova ndi Mfumu.
2. Mosangalala fuula kwa Mfumu yathu.
Muzimutamanda ndi nyimbo yokoma.
Tiyeni tonse timuimbire mokweza.
Zeze ndi lipenga
Ziimbe pamodzi.
(KOLASI)
Imbani
Nyimbo yatsopano.
Imbani,
Yehova ndi Mfumu.
3. Nyanja ndi zonse mmenemo zimutamande.
Zolengedwa zake zizimutamanda.
Dziko lapansi nalonso limutamande.
Mapiri ndi zigwa
Zimutamandenso.
(KOLASI)
Imbani
Nyimbo yatsopano.
Imbani,
Yehova ndi Mfumu.
(Onaninso Sal. 96:1; 149:1; Yes. 42:10.)