Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwhf nkhani 21
  • Muziona Moyenera Zinthu Zimene Zimakukwiyitsani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muziona Moyenera Zinthu Zimene Zimakukwiyitsani
  • Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuona moyenera zinthu zimene zimakukwiyitsani
  • Mafunso othandiza pokambirana
  • Kodi Mungasonyeze Bwanji kuti Mumayamikira Zimene Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Amachita?
    Galamukani!—2017
  • M’banja Mukabuka Mikangano
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Zimene Mungachite Kuti Musamagwire Ntchito Pamene Simuli Kuntchito
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Zimene Mungachite Ngati Mumacheza Kwambiri ndi Munthu Amene si Mwamuna Kapena Mkazi Wanu
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Mfundo Zothandiza Mabanja
ijwhf nkhani 21
Mwamuna wakwiya ndipo wakhala yekha patebulo pamene mkazi wake akusangalala kucheza ndi banja lina.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA

Muziona Moyenera Zinthu Zimene Zimakukwiyitsani

  • Mumakonda kungochita zimene mwaganiza osakonzekera koma mnzanu amakonda kukonzekera chilichonse.

  • Mumakonda kukhala phee ndipo ndinu wamanyazi koma mnzanu ndi womasuka ndipo amakonda kucheza pagulu.

Kodi mwamuna kapena mkazi wanu amachita zinthu zimene zimakukwiyitsani? Kuganizira kwambiri zinthuzi kungasokoneze banja lanu. Paja Baibulo limanena kuti: “Amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.”​—Miyambo 17:9.

Musalole kuti zinthu zimene zimakukwiyitsani zichititse kuti inu ndi mwamuna kapena mkazi wanu musamagwirizane. M’malomwake, muziyesetsa kuona zinthuzo moyenera.

Zimene zili m’nkhaniyi

  • Kuona moyenera zinthu zimene zimakukwiyitsani

  • Zimene mabanja ena amanena

  • Mafunso othandiza pokambirana

Kuona moyenera zinthu zimene zimakukwiyitsani

Mwina zinthu zimene mnzanu amachita zomwe zimakukwiyitsani ndi mbali ina chabe ya khalidwe limene mumalikonda. Taganizirani zitsanzo zitatu izi:

“Nthawi zambiri mwamuna wanga amachedwa kumaliza zinthu komanso kukonzekera akafuna kupita kwinakwake. Koma khalidwe lomweli limamuthandiza kuti azindilezera mtima. Nthawi zina, ndimakwiya iye akachedwa koma pa nthawi imodzimodziyo khalidweli ndi limodzi mwa makhalidwe ake omwe ndimawakonda.”​—Chelsea.

“Mkazi wanga akamakonzekera zinthu amaganizira chinthu china chilichonse. Iye amafuna kuti zinthu zonse zikhale pamalo ake ndipo nthawi zina zimenezi zimandikwiyitsa. Koma khalidwe limeneli limamuthandizanso kuti nthawi zonse akhale wokonzeka.”​—Christopher.

Nthawi zina, ndimaona kuti mwamuna wanga amachita mphwayi ndipo zimandikwiyitsa. Komabe ndimaona kuti sapanikizika ndipo zimenezi n’zomwe zinandichititsa kuyamba kumukonda. Ndimasangalala kwambiri kuti zinthu zikavuta mtima wake umakhalabe m’malo.”​—Danielle.

Mogwirizana ndi zimene Chelsea, Christopher ndi Danielle ananena, nthawi zambiri zinthu zimene mnzanu amachita zomwe zimakukwiyitsani zimangokhala mbali ina ya khalidwe labwino limene ali nalo. Choncho ngati atasiya zimene zimakuvutitsanizo, ndiye kuti anasiyenso zinthu zabwino zimene amachitazo. Zimenezi n’zofanana ndi mmene zilili ndi ndalama yachitsulo. Simungathe kungotaya mbali imodzi chabe popanda kutayanso mbali inayo.

Koma n’zoona kuti makhalidwe ena sakhala ndi mbali ina yabwino. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti anthu ena ‘amakonda kukwiya.’ (Miyambo 29:22) Ngati munthu ali ndi vutoli, ayenera kuchita zonse zimene angathe kuti asiye “kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe.”a​—Aefeso 4:31.

Koma ngati mnzanu ali ndi khalidwe lina lomwe si loipa kwambiri kungoti simusangalala nalo, muzitsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Pitirizani kulolerana . . . ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.”​—Akolose 3:13.

Kuwonjezera pamenepa, muziyesetsa kuona mbali ina yabwino ya khalidwe lomwelo. Mwina mbali imeneyo ndi yomwe inachititsa kuti mukopeke ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Mwamuna wina dzina lake Joseph anati, “Kuganizira kwambiri zinthu zimene zimakukwiyitsani kuli ngati kungoona mbali yakuthwa ya dayamondi osaona kuwala kwake kokongola.”

Zimene mabanja ena amanena

Derrick ndi Haley.

“Ine ndi mkazi wanga tikakwiya chifukwa cha khalidwe la mnzathu, timayesetsa kuganiza nthawi imene khalidwe lomwelo lingakhale lothandiza.”​—Derrick, limodzi ndi mkazi wake, Haley.

Mikiah ndi Curtis.

“Timasiya kudandaula za zinthu zinazake zokhudza mnzathu tikazindikira kuti zinthuzo ndi mbali ina chabe ya makhalidwe amene anatichititsa kuyamba kukonda munthuyo.”​—Mikiah, limodzi ndi mwamuna wake, Curtis.

Mafunso othandiza pokambirana

Aliyense aganizire kaye payekha mmene angayankhire mafunso otsatirawa. Kenako mungakambirane limodzi mayankho anu.

  • Kodi mnzanu ali ndi khalidwe limene mukuona kuti likusokoneza banja lanu? Ngati zili choncho, kodi ndi khalidwe liti?

  • Kodi khalidweli ndi loipadi kapena limangokutopetsani?

  • Nanga kodi khalidweli lili ndi mbali ina yabwino? Ngati zili choncho, kodi mbaliyo ndi yotani, nanga n’chifukwa chiyani mumaikonda?

a Onani nkhani yakuti “Mungatani Kuti Musamakwiye Mopitirira Malire?,” “Kodi Mungapewe Bwanji Kulankhula Mawu Achipongwe? komanso yakuti “Zimene Mungachite Kuti Musamakangane.”

Mfundo zobwereza: Kodi mungatani mnzanu akachita zinthu zimene zimakukwiyitsani?

Muziganizira mfundo zotsatirazi:

  • Kuganizira kwambiri zinthu zimene mnzanu amachita zomwe zimakukwiyitsani kungasokoneze banja lanu.

  • Chinthu chimene chimakukwiyitsani chingakhale mbali ina ya khalidwe limene mumalikonda lomwe linachititsa kuti mukopeke ndi mwamuna kapena mkazi wanuyo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena