Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w22 April tsamba 30-tsamba 31 ndime 3
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Tizilemekeza “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yothetsa Banja ndi Kupatukana
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Pambuyo pa Tsiku la Ukwati
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
w22 April tsamba 30-tsamba 31 ndime 3

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Ngati Mkhristu wathetsa banja osati pa zifukwa za m’Malemba n’kukwatirana ndi munthu wina, kodi mpingo umaona bwanji ukwati wakalewo komanso watsopanowo?

Zikatere mpingo uziona kuti ukwati wakalewo unatha pamene mwamunayo anakwatira mkazi wina ndipo uziona ukwati watsopanowo monga wovomerezeka. Kuti timvetse chifukwa chake tikutero, tiyeni tikambirane zimene Yesu ananena pa nkhani ya kuthetsa banja ndi kukwatiranso.

M’bale akuyang’ana banja la m’bale ndi mlongo wina pamisonkhano.

Pa Mateyu 19:9, Yesu anatchula chifukwa chimodzi chokha cha m’Malemba chothetsera banja. Iye anati: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.” Pa mawu a Yesuwa tikuphunzirapo kuti (1) chigololo ndi chifukwa chokhacho cha m’Malemba chimene chingachititse kuti banja lithe komanso (2) mwamuna yemwe wasiya mkazi wake osati pa zifukwa za m’Malemba, wachita chigololo.a

Kodi mawu a Yesuwa akutanthauza kuti mwamuna yemwe wachita chigololo ndipo wathetsa banja lake, amakhala womasuka mwa Malemba kukwatiranso? Osati kwenikweni. Mwamuna akachita chigololo, mkazi wake wosalakwayo ndi amene amakhala ndi ufulu wosankha kumukhululukira kapena ayi. Ngati mkaziyo wasankha kuti asamukhululukire ndipo athetsa banjalo mwalamulo, onse angakhale omasuka kukwatiranso ngati nkhani yothetsa banja lawolo yatha kukhoti.

Nthawi zina mkazi wosalakwayo angafune kupitirizabe kukhala pa banja ndi mwamunayo ndipo angamuuze kuti akufuna kumukhululukira. Koma bwanji ngati mwamuna yemwe wachita chigololoyo wakana kuti mkazi wakeyo amukhululukire ndipo watenga chikalata chothetsera banja? Popeza kuti mkaziyo amafuna kumukhululukira n’kupitirizabe kukhala naye pa banja, mwamunayo sangakhale womasuka mwa Malemba kukwatiranso. Ngati iye wakwatiranso mkazi wina pomwe sali womasuka kutero, ndiye kuti wachitanso chigololo kachiwiri. Zikatero akulu amafunika kupanganso komiti yoweruza kuti isamalire nkhani yakeyo.​—1 Akor. 5:1, 2; 6:9, 10.

Munthu yemwe sali womasuka mwa Malemba akakwatiranso, kodi mpingo umaona bwanji ukwati wake wakale komanso watsopano? Kodi ukwati wakalewo umakhala kuti udakalipobe mogwirizana ndi Malemba? Kodi mkazi wosalakwayo amakhalabe ndi ufulu wosankha kukhululukira kapena kusakhululukira mwamunayo? Kodi mpingo uziona ukwati watsopanowo ngati wachigololo?

M’mbuyomu, mpingo unkaona kuti ukwati watsopanowo ndi wachigololo ngati mkazi wosalakwayo adakali moyo, sanakwatiwe komanso sanachite tchimo ladama. Koma pamene Yesu ankafotokoza zokhudza kuthetsa banja ndi kukwatiranso, sananene chilichonse chokhudza wosalakwayo. M’malomwake iye anafotokoza kuti mwamunayo akathetsa banja lake popanda zifukwa za m’Malemba n’kukwatiranso, wachita chigololo. Choncho kusiya mkazi ndi kukwatiranso, komwe Yesu anati ndi kuchita chigololo, kumathetsa banja loyambalo.

“Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”​—Mat. 19:9.

Ngati ukwati watha chifukwa choti mwamuna wathetsa banjalo ndipo wakwatiranso, sizingathekenso kuti mkazi wosalakwayo asankhe kumukhululukira kapena ayi. Mkaziyo sangavutikenso maganizo pa nkhani yosankha kuti amukhululukire kapena ayi. Kuwonjezera pamenepa, mmene mpingo umaonera ukwati watsopanowo, sizingadalire kuti mkazi wosalakwayo anamwalira, anakwatiwanso kapena anachita dama.b

Muchitsanzo takambiranachi, mwamuna anachita chigololo, zomwe zinachititsa kuti banja lawo lithe. Nanga bwanji ngati mwamuna sanachite chigololo koma anathetsa banja lake n’kukwatiranso mkazi wina? Kapena bwanji ngati mwamuna anachita chigololo atathetsa kale banja lakelo ndipo anakwatiranso ngakhale kuti mkazi wake ankafuna kumukhululukira? Muzitsanzo zonsezi, kusiya mkazi ndi kukwatiranso, komwe ndi kuchita chigololo, kumathetsa banja loyambalo. Choncho ukwati watsopanowo umakhala wovomerezeka mwalamulo. Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya November 15, 1979, tsamba 32, inafotokoza kuti: “Mwamunayo amakhala kuti walowa m’banja latsopano ndipo sangangolithetsa n’kubwererana ndi mkazi wake wakale, chifukwa ukwati woyambawo unatha pamene anathetsa banjalo, kuchita chigololo ndi kukwatiranso.”

Kusintha kamvedwe pa nkhaniyi, sikukutanthauza kuti tiziona mopepuka kupatulika kwa ukwati kapena kuchepetsa kukula kwa tchimo la chigololo. Mwamuna amene amathetsa banja lake popanda zifukwa za m’Malemba n’kuwatiranso mkazi wina pamene mwa Malemba sali womasuka kutero, angakumane ndi komiti yoweruza pa mlandu wachigololo. (Ngati mkazi watsopanoyo ndi Mkhristu, nayenso angakumane ndi komiti yoweruza pa mlandu wachigololo kapena dama.) Ngakhale kuti ukwati watsopanowo sungamaonedwe ngati wachigololo, mwamunayo sangayenerere kupatsidwa maudindo apadera mumpingo kwa zaka zambiri mpaka anthu atasiya kukhumudwa ndi zolakwika zomwe anachitazo ndi kuyamba kumulemekeza. Akulu asanamupatse utumiki uliwonse, angaganizirenso mmene zinthu zilili kwa mkazi yemwe anachitiridwa zachinyengoyo limodzi ndi ana ang’onoang’ono omwe mwamuna wolakwayo anasiya.​—Mal. 2:14-16.

Poganizira mavuto omwe amakhalapo chifukwa chothetsa banja popanda zifukwa za m’Malemba n’kukwatiranso, Akhristu amachita zinthu mwanzeru potsanzira Yehova n’kumaona kuti ukwati ndi wopatulika monga mmene iye amawuonera.​—Mlal. 5:4, 5; Aheb. 13:4.

a Munkhaniyi, tiziyerekekezera kuti amene wachita chigololoyo ndi mwamuna ndipo wosalakwayo ndi mkazi. Komabe pa Maliko 10:11, 12, Yesu anafotokoza momveka bwino kuti malangizo ake pa nkhaniyi, amakhudza onse, amuna ndi akazi omwe.

b Zimenezi zikusintha kamvedwe kathu koyamba komwe kankafotokoza kuti ukwati watsopanowo umaonedwa monga wachigololo mpaka pamene mkazi wosalakwayo wamwalira, wakwatiwanso kapena wachita tchimo ladama.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena