Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 108
  • Kodi Kukhala Munthu Wotchuka pa Intaneti Kuli Ndi Phindu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kukhala Munthu Wotchuka pa Intaneti Kuli Ndi Phindu?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi kukhala wotchuka kuli ndi mavuto otani?
  • Kunamizira kukhala wotchuka
  • Kodi kukhala ndi anthu ambiri okutsatira komanso okonda zinthu zomwe umaposita pa intaneti kuli ndi phindu?
  • Kodi Ndi Bwino Kucheza pa Intaneti?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Pali Vuto Lililonse Kukhala Wotchuka?
    Galamukani!—2012
  • Phunzitsani Ana Anu Kuti Azigwiritsa Ntchito Intaneti Moyenera
    Galamukani!—2014
  • Kodi ndiyenera kudziwa zotani zokhudza malo ochezera a pa Intaneti?—Gawo 2
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 108
Mtsikana akuyang’ana pafoni yake akumwetulira. Walandira mauthenga 85 okonda zomwe waposita pamalo ochezera a pa intaneti.

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Kukhala Munthu Wotchuka pa Intaneti Kuli Ndi Phindu?

Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Elaine anati: “Nditaona kuti anzanga akusukulu ali ndi anzawo ambirimbiri owatsatira pa intaneti ndinaganiza kuti, ‘Ee, koma ndiye ndi otchukatu.’ Kunena zoona, ndinkawachitira nsanje.”

Kodi inunso munayamba mwamvapo choncho? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani kuti musamakhumudwe chifukwa chakuti sindinu wotchuka pa intaneti.

  • Kodi kukhala wotchuka kuli ndi mavuto otani?

  • Kunamizira kukhala wotchuka

  • Kodi kukhala ndi anthu ambiri okutsatira komanso okonda zinthu zomwe umaposita pa intaneti kuli ndi phindu?

  • Musamanamizire kuti ndinu wodzichepetsa

Kodi kukhala wotchuka kuli ndi mavuto otani?

Pa Miyambo 22:1, Baibulo limati: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.” Choncho sikulakwa kufuna kukhala ndi mbiri yabwino ngakhalenso kufuna kuti anthu ena azikukonda.

Komabe, nthawi zina kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuti anthu azikukonda kungachititse munthu kuyamba kuganiza kuti angakhale wosangalala pokhapokha ngati ali wotchuka. Kodi zimenezi zingakhale ndi vuto lililonse? Onya wazaka 16 angayankhe kuti inde. Taonani zimene ananena:

“Ndaonapo anthu ena akuchita zinthu zachibwana kusukulu kwathu monga kudumpha pamalo ena ake aatali kwambiri n’cholinga choti atchuke.”

Pofuna kuti anthu ena azichita nawo chidwi, ena amadzijambula akuchita zinthu zachibwana kenako n’kuziika pa intaneti. Mwachitsanzo, achinyamata ambiri amaposita pa intaneti mavidiyo osonyeza iwowo akudya mankhwala omwe amagwiritsidwa ntchito m’mashini ochapira, koma zinthu zimenezo n’zoti munthu sayenera kuchita.

Baibulo limati: “Musachite chilichonse ndi mtima . . . wodzikuza.”​—Afilipi 2:3.

Zoti muganizire:

  • Kodi inuyo mumaona kuti kukhala wotchuka pa intaneti n’kofunika?

  • Kodi mungaike moyo kapena thanzi lanu pangozi n’cholinga choti anzanu akuoneni kapenanso kukutamani?

    Zimene achinyamata anzanu amanena

    Leianna.

    “Kutchuka kumakhala koopsa kwambiri munthu akakhala ndi maganizo akuti ayenera kulolera kuchita chilichonse n’cholinga choti atchuke. Munthu wotereyu, amaganiza kuti akamalankhula, kuvala kapenanso kuchita zinthu mwanjira inayake ngakhale pa intaneti, zingamuthandize kuti akhale wotchuka. Munthu ukamachita dala zinthu zosemphana ndi zimene umakhulupirira, kapenanso mfundo zimene umayendera pa moyo wako poganiza kuti ukhala wotchuka, mapeto ake umadzanong’oneza bondo.”​​—Leianna.

Kunamizira kukhala wotchuka

Si nthawi zonse pamene anthu amachita zinthu zoika moyo wawo pangozi n’cholinga choti akhale otchuka. Mtsikana wina wazaka 22 dzina lake Erica anafotokoza njira inanso imene anthu ena amagwiritsa ntchito pofuna kuti atchuke. Iye anati:

“Anthu ena amakonda kuposita zithunzi zambirimbiri zosonyeza mmene moyo wawo ukuyendera kuti azioneka ngati amacheza ndi anthu ambirimbiri. Zimenezi zimachititsa kuti azioneka ngati ndi otchuka.”

Cara wazaka 15 ananena kuti anthu ena amakonda kuchita zinthu mwachinyengo n’cholinga choti aoneke ngati otchuka. Iye anati:

“Ndaonapo anthu akujambulitsa zithunzi zooneka ngati ali kuphwando linalake koma chonsecho ali kunyumba kwawo.”

Matthew wazaka 22 akuvomereza kuti nayenso anachitapo zimenezi. Iye anati:

“Ndinapositapo chithunzi n’kusonyeza ngati ndili ku Mount Everest, koma chonsecho sindinayambe ndapitapo ku Asia.”

Baibulo limati: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

Zoti muganizire:

  • Ngati mumagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, kodi mumachita zinthu mwachinyengo n’cholinga choti mutchuke?

  • Kodi mumaposita zithunzi zosonyezadi mmene inuyo mulili kapenanso kulemba ndemanga zogwirizana ndi mfundo zimene mumayendera pa moyo wanu?

    Zimene achinyamata anzanu amanena

    Hannah.

    “Anthu ena amalolera kuchita china chilichonse n’cholinga chakuti anthu ambiri akonde zimene aposita pa intaneti. Koma kodi inuyo mungakonde kuti anthu azikudziwani kuti ndinu munthu wokonda kulankhula ndi kuvala mosayenera, kapenanso wodzionetsera ndi zimene ali nazo? Kapena mungakonde kuti anthu azikudziwani monga munthu wamakhalidwe abwino komanso woganizira ena? Munthu umasangalala anthu ena akamakukonda, koma muzionetsetsa kuti akukukondani pa zinthu zabwino.”​​—Hannah.

Kodi kukhala ndi anthu ambiri okutsatira komanso okonda zinthu zomwe umaposita pa intaneti kuli ndi phindu?

Anthu ambiri amaganiza kuti angakhale otchuka pa intaneti ngati ali ndi anthu ambiri owatsatira komanso okonda zimene amaposita. Matthew, yemwe tamutchula kale uja, akuvomereza kuti nayenso ankaganiza chonchi. Iye anati:

“Ndinkafunsa anthu kuti, ‘Muli ndi anthu angati amene amakutsatirani pa intaneti?’ kapenanso kuti, ‘Ndi anthu ochuluka bwanji amene amakonda zimene mumaposita pa intaneti?’ Kuti ndiwonjezere chiwerengero cha anthu onditsatira, ndinayamba kutsatira anthu osiyanasiyana poganiza kuti nawonso ayamba kunditsatira. Ndinayamba kamtima kofuna kukhala wotchuka ndipo ndikamagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, maganizo amenewa ankangokulirakulirabe.”

Zithunzi: 1. Mtsikana akuona kuchuluka kwa mauthenga okonda zomwe waposita pamalo ochezera a pa intaneti ndipo akumwetulira. 2. Mtsikana yemweyo akudya chokoleti ndi masiwiti zodzaza mbale. 3. Mtsikanayu wagwira pamimba ndipo akuoneka wokhumudwa.

Kukhala otchuka pa intaneti kuli ngati kudya chakudya chosapatsa thanzi. Chimakoma kwa nthawi yochepa koma sichimakhutitsa.

Mariya wazaka 25, ananena kuti anthu ena amadziona kuti ndi osafunika kapenanso kuti ndi ofunika potengera kuchuluka kwa anthu omwe amawatsatira pa intaneti komanso amene amakonda zimene amaposita. Iye anati:

“Mtsikana akaika chithunzi chake pa intaneti, koma anthu ochepa okha ndi amene amulembera kuti achikonda, iye amayamba kudziona ngati wosaoneka bwino. N’zoona kuti maganizo amenewa ndi olakwika, koma ndi mmene anthu ambiri amamvera. Kuchita zimenezi kuli ngati kudzivutitsa wekha pa intaneti.”

Baibulo limati: “Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.”​—Agalatiya 5:26.

Zoti muganizire:

  • Ngati mumagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, kodi mumaona kuti amakuchititsani kuti muzikonda kudziyerekezera ndi anthu ena?

  • Kodi mumadera nkhawa kwambiri kuchuluka kwa anthu amene akukutsatirani m’malo moganizira za anthu amene angakhale anzanu enieni?

    Zimene achinyamata anzanu amanena

    Joshua.

    “Kuti munthu ukhale wotchuka pa intaneti, umafunika kukhala munthu amene anthu angamamusirire. Ndipo nthawi zambiri zimenezi zimatanthauza kutengera anthu amene ukuwasirirawo. Zimenezi zingakuchititseni kuti muzingoganizira kwambiri mmene anthu amakuonerani komanso zomwe mungamachite kuti azikukondani kwambiri. Si kulakwa kufuna kuti anthu ena azikukonda, koma kufunitsitsa kukhala wotchuka kungachititse kuti munthu ukhale ndi vuto lomangoganizira zomwezo.”​​—Joshua.

Musamanamizire kuti ndinu wodzichepetsa

Kodi munayamba mwamvapo anthu ena akudzitama pa zinthu zomwe akwanitsa kuchita, koma amafotokoza ngati akudandaula?

  • “Kungochokera pamene ndinagula galimoto yatsopano, anthu akhala akumangondipempha kuti akwere nawo.”

  • “Zimandibowa anthu akamangondiyamikira kuti panopa bola ndaondako.”

Munthu wotereyu amalankhula zinthu ngati akudandaula n’cholinga choti aoneke ngati akudzichepetsa, koma m’chenicheni amakhala akudzitama.

Chenjezo: Kudzionetsera kapena kudzitama mwanjira imeneyi nthawi zambiri sikumakhala ndi zotsatirapo zabwino chifukwa anthu amakutulukira. Komanso anthu amadana kwambiri ndi anthu omwe amanamizira kukhala odzichepetsa chifukwa amachita zinthu mwachinyengo kusiyananso ndi anthu omwe amasonyezeratu matama awo.

Ulendo wina mukamadzalemba ndemanga kapena kuika chithunzi chanu pamalo ochezera a pa intaneti, mudzayesetse kuchita zinthu mosamala kuti musadzanamizire kukhala ngati wodzichepetsa. Muzitsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Mlendo akutamande, osati pakamwa pako.”​—Miyambo 27:2.

Kubwereza: Kodi mungatani kuti mupewe msampha wofuna kukhala munthu wotchuka pa intaneti?

  • Muzionetsetsa kuti zimene mumaposita pa intaneti zimasonyezadi mmene inuyo mulili komanso n’zogwirizana ndi mfundo zimene mumayendera pa moyo wanu.

  • Muzikhala oona mtima mukamaposita zinthu pa intaneti.

  • Muzikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya anthu okutsatirani komanso amene amakonda zimene mumaika pa intaneti.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena