Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • scl tsamba 91-92
  • Nkhawa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhawa
  • Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
scl tsamba 91-92

Nkhawa

Kodi muli ndi nkhawa chifukwa choopa mavuto monga umphawi, njala ndi kusowa pokhala?

Miy 10:15; 19:7; 30:8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mlr 3:19​—Mneneri Yeremiya limodzi ndi anthu ena ambiri anasowa pokhala mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa

    • 2Ak 8:1, 2; 11:27​—Akhristu a ku Makedoniya anali pa umphawi wadzaoneni, mtumwi Paulo nayenso ankasowa zinthu monga chakudya, zovala ndi pokhala

  • Malemba otonthoza:

    • Sl 37:25; 145:15; Miy 10:3; Mt 6:25-34

    • Onaninso De 24:19

Kodi muli ndi nkhawa chifukwa choopa kuti simungapeze anzanu, muzingokhala nokhanokha kapenanso simungakondedwe?

Yob 19:19; Mla 4:10, 12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mf 18:22; 19:9, 10​—Mneneri Eliya ankaona kuti watsala yekhayekha monga mtumiki wokhulupirika wa Yehova

    • Yer 15:16-21​—Mneneri Yeremiya ankadziona kuti ali yekhayekha pakati pa anthu omwe ankakonda kumangosangalala m’malo momvetsera uthenga wake

  • Malemba otonthoza:

    • Sl 25:15, 16; 1Pe 5:7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:

    • 1Mf 19:1-19​—Yehova anathandiza mneneri Eliya pomupatsa madzi ndi chakudya, kumumvetsera pamene ankafotokoza nkhawa zake, komanso kumulimbikitsa pomukumbutsa kuti Iye ndi wamphamvu

    • Yoh 16:32, 33​—Yesu ankadziwa kuti otsatira ake adzamusiya yekhayekha koma ankadziwanso kuti Yehova ali naye nthawi zonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena