Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kn37 tsamba 1-4
  • Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!
  • Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chipembedzo Chonyenga . . .
  • Mmene Mungadziwire Chipembedzo Choona
  • Chipembedzo Choona . . .
  • Zipembedzo Zabodza Zimaphunzitsa Zinthu Zonama Zokhudza Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?
    Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
  • Kanani Chipembedzo Chonyenga!
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Pewani Kulambira Konyenga!
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!
kn37 tsamba 1-4

Uthenga kwa Anthu Onse Na.37

Uthenga kwa Anthu Onse

Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!

▪ Kodi chipembedzo chonyenga n’chiyani?

▪ Kodi chidzatha bwanji?

▪ Kodi inuyo zidzakukhudzani motani?

Kodi chipembedzo chonyenga n’chiyani?

Kodi mukuvutika maganizo ndi umbanda umene ukuchitika m’dzina la chipembedzo? Kodi mumasokonezeka maganizo chifukwa cha nkhondo, uchigawenga, ndi katangale yemwe anthu amene amati amatumikira Mulungu akuchita? N’chifukwa chiyani chipembedzo chikuoneka kuti n’chimene chikuyambitsa mavuto ambiri?

Si zipembedzo zonse zimene zimachititsa mavutowa koma n’chipembedzo chonyenga chokha. Munthu amene amapatsidwa ulemu waukulu pankhani zachipembedzo, Yesu Kristu, anasonyeza kuti chipembedzo chonyenga chimapangitsa anthu kuchita zinthu zoipa, mofanana ndi “mtengo wamphuchi [umene umabala] zipatso zoipa.” (Mateyu 7:15-17) Kodi chipembedzo chonyenga chimabala zipatso zotani?

Chipembedzo Chonyenga . . .

◼ CHIMALOWA MU NKHONDO NDIPONSO MU NDALE: “Ku Asia ngakhalenso kwina kulikonse, atsogoleri ofuna maudindo akuluakulu, akupusitsa anthu opembedza mopanda ulemu n’cholinga choti akwaniritse zofuna zawo,” inatero magazini ya Asiaweek. Motero, magaziniyo inachenjeza kuti: “Dziko likuoneka kuti latsala pang’ono kusokonezeka.” Mtsogoleri wina wachipembedzo wotchuka kwambiri ku United States anati: “Choyamba muyenera kupha zigawenga, kuti zisiye kupha anthu.” Ndipo anati n’kuchita motani zimenezi? Ananena kuti: “Iphani zigawenga zonse m’dzina la Mulungu.” Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limati: “Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza.” (1 Yohane 4:20) Ndipo Yesu ananena kuti: “Kondanani nawo adani anu.” (Mateyu 5:44) Kodi n’zipembedzo zingati zimene mukuganiza kuti anthu ake amalowa mu nkhondo?

◼ CHIMAPHUNZITSA ZINTHU ZA BODZA: Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti munthu ali ndi mzimu umene suufa. Pogwiritsa ntchito chiphunzitso chimenechi, zambiri mwa zipembedzo zimenezi zimapezerapo mwayi olipiritsa anthu awo ndalama, kuti apempherere mizimu ya anthu amene amwalira. Komabe, Baibulo limaphunzitsa zinthu zosiyana ndi zimenezi. “Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Yesu anaphunzitsa kuti akufa adzaukitsidwa, ndipo izi zikanakhala zosafunika ngati anthu akanakhala kuti ali ndi mzimu umene suufa. (Yohane 11:11-25) Kodi chipembedzo chanu chimaphunzitsa kuti anthu ali ndi mzimu umene suufa?

◼ CHIMALEKERERA CHIWEREWERE: M’mayiko ena, zipembedzo zina zimaika anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha kukhala atsogoleri awo ndiponso zikulimbikitsa boma kuti livomereze kuti anthu azikwatirana amuna kapena akazi okhaokha. Ngakhale matchalitchi amene amatsutsa khalidwe la chiwerewere, amalekerera atsogoleri awo amene amagona ana. Koma kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani ponena za chiwerewere? Limanena mosapita m’mbali kuti: “Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena [amuna, NW] akudziipsa ndi amuna . . . sadzalowa Ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Kodi mukudziwa zina mwa zipembedzo zimene zimalekerera chiwerewere?

Kodi tsogolo la zipembedzo zimene zimabala zipatso zovunda, n’lotani? Yesu anachenjeza kuti: “Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.” (Mateyu 7:19) Inde, chipembedzo chonyenga chidzadulidwa ndi kuwonongedwa! Koma kodi zimenezi zidzachitika liti ndipo motani? Yankho la funsoli lili m’masomphenya aulosi amene amapezeka m’buku la m’Baibulo la Chivumbulutso, m’machaputala 17 ndi 18.

Kodi Chipembedzo Chonyenga Chidzatha Motani?

Tayerekezani kuti mukuona mkazi wachigololo atakhala pamsana pa chilombo choopsa kwambiri. Chilombocho chili ndi mitu seveni ndiponso nyanga teni. (Chivumbulutso 17:1-4) Kodi mkazi wachigololoyu akuimira ndani? Mkaziyu ali ndi mphamvu “pa mafumu a dziko.” Wavala chibakuwa, amagwiritsa ntchito zonunkhiritsa, ndiponso ndi wachuma kwambiri. Kuphatikiza apo, ‘akusokeretsa mitundu yonse,’ ndi nyanga kapena kuti zochita zake zamizimu. (Chivumbulutso 17:18; 18:12, 13, 23) Baibulo limatithandiza kuzindikira kuti mkazi wachigololo ameneyu ndi chipembedzo cha padziko lonse lapansi. Sikuti akuimira chipembedzo chimodzi chokha ayi, koma zipembedzo zonse zimene zikubala zipatso zoipa.

Chilombo chimene mkazi wachigololoyu wakwerapo chikuimira maulamuliro andale a padzikoli.a (Chivumbulutso 17:10-13) Chipembedzo chonyenga chakwera pamsana pa chilombo chandale chimenechi, poyesa kuchilamulira pa zosankha zake ndi kuchiuza kopita.

Komabe, posachedwapa pachitika zinthu zodabwitsa kwambiri. “Nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzam’khalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzam’psereza ndi moto.” (Chivumbulutso 17:16) Mwadzidzidzi ndiponso moimitsa mutu, maulamuliro andale a padzikoli adzaukira chipembedzo chonyenga n’kuchiwonongeratu! Kodi chimene chidzachititse zimenezi n’chiyani? Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limayankha kuti: ‘Mulungu anapatsa kumtima kwawo kuchita za m’mtima mwake.’ (Chivumbulutso 17:17) Inde, Mulungu adzalanga chipembedzo chonyenga chifukwa cha zinthu zonse zoipa zimene chakhala chikuchita m’dzina lake. Mwachilungamo, adzamuwononga pogwiritsa ntchito andale amene wakhala akuchita nawo chigololowo.

Kodi mungachite chiyani ngati simukufuna kudzawonongedwa limodzi ndi chipembedzo chonyenga? “Tulukani m’menemo, anthu anga,” akutilimbikitsa motero mthenga wa Mulungu. (Chivumbulutso 18:4) Indedi, ino ndiye nthawi yotuluka m’chipembedzo chonyenga! Koma kodi n’kuti kumene mungathawire? Osati kuti musiye kukhulupirira kuti kuli Mulungu ayi, chifukwa anthu okhulupirira zimenezi alibe tsogolo labwino. (2 Atesalonika 1:6-9) Malo abwino omwe mungathawireko ndi ku chipembedzo choona basi. Koma kodi chipembedzo choonacho mungachidziwe bwanji?

Mmene Mungadziwire Chipembedzo Choona

Kodi ndi zipatso zokoma ziti zimene chipembedzo choona chiyenera kubala?—Mateyu 7:17.

Chipembedzo Choona . . .

◼ CHIMADZIWIKA NDI CHIKONDI: Olambira oona “siali a dziko lapansi,” siogawanika chifukwa chosiyana mtundu kapena chikhalidwe, ndipo ‘amakondana wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:35; 17:16; Machitidwe 10:34, 35) Iwo saphana, koma amakhala okonzeka kuferana ngati kuli kofunika kutero.—1 Yohane 3:16.

◼ CHIMAKHULUPIRIRA MAWU A MULUNGU: Chipembedzo choona sichiphunzitsa “miyambo” ndi “kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu,” m’malo mwake ziphunzitso zake zimachokera m’Mawu a Mulungu, omwe ndi Baibulo. (Mateyu 15:6-9) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti,“lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero.”—2 Timoteo 3:16.

◼ CHIMALIMBITSA MABANJA NDIPONSO CHIMALIMBIKITSA MAKHALIDWE ABWINO:

Chipembedzo choona chimaphunzitsa amuna ‘kukonda akazi awo monga ngati matupi a iwo okha,’ chimathandiza akazi kuti ‘aziopa [kapena kuti akhale ndi ulemu waukulu kwa] amuna awo,’ ndipo chimaphunzitsa ana kuti ‘azimvera akuwabala.’ (Aefeso 5:28, 33; 6:1) Kuphatikiza apo, anthu amene ali ndi maudindo, amaphunzitsidwa kukhala ndi makhalidwe opereka chitsanzo chabwino.—1 Timoteo 3:1-10.

Kodi pali chipembedzo china chilichonse chimene chimachita zimenezi? Buku lina lakuti Holocaust Politics, lomwe linasindikizidwa m’chaka cha 2001, linati: “Kukanakhala kuti anthu ambiri amachita zimene Mboni za Yehova zimalalikira ndi kuchita, sibwenzi Anazi atapha anthu ambiri pankhondo yachiwiri yapadziko lonse komanso sibwenzi kuli kupululana mafuko.”

Indedi, m’mayiko 235, Mboni za Yehova sikuti zimangolalikira makhalidwe abwino a m’Baibulo ayi, koma zimachitanso mogwirizana ndi zimene zikulalikirazo. Tikukulimbikitsani kupempha Mboni za Yehova kuti zikuthandizeni kuphunzira zimene Mulungu amafuna kwa inu kuti muthe kumulambira monga mmene iye amafunira. Tsopano ndi nthawi yoti muchitepo kanthu. Musachedwe. Mapeto a chipembedzo chonyenga ali pafupi!—Zefaniya 2:2, 3.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Dikirani!

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mumve nkhaniyi mwatsatanetsatane, onani kabuku kakuti Dikirani! kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, tsamba 12 ndi 13.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Chipembedzo chonyenga chimalamulira “mafumu a dziko”

[Mawu Otsindika patsamba 3]

“Tulukani m’menemo, anthu anga”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena