13 Miyezi ya Kalendala ya M’Baibulo
Mwezi wa Ayuda unali kuyambira pamene mwezi weniweni wakhala, kukafika pamene mwezi wotsatira wakhala.—Yes. 66:23.
MIYEZI |
NYENGO |
MBEWU |
|
---|---|---|---|
Yopatulika |
Yanthawi zonse |
||
1 |
7 |
Yorodano asefukira chifukwa cha mvula ndi chipale chofewa |
Kukolola fulakesi. Kuyamba kukolola balere |
2 |
8 |
Chilimwe chiyamba. Kawirikawiri kuthambo kumakhala kopanda mitambo |
Kukolola balere. Kukolola tirigu m’madera otsika |
3 |
9 |
Kunja kumatentha. Mpweya wabwino |
Kukolola tirigu. Nkhuyu zoyambirira. Maapulo ena |
4 |
10 |
Kutentha kumawonjezeka. Kumagwa mame ambiri |
Mphesa zoyambirira. Zomera ndi akasupe zimauma |
5 |
11 |
Kutentha kumafika pachimake |
Kuyamba kukolola mphesa |
6 |
12 |
Kutentha kumapitirizabe |
Kukolola mphesa ndi nkhuyu za m’chilimwe |
7 |
1 |
Chilimwe chikutha. Mvula yoyambirira imagwa |
Kumaliza kukolola. Kuyamba kulima |
8 |
2 |
Mvula yowaza |
Kubzala tirigu ndi balere. Kukolola maolivi |
9 |
3 |
Mvula imawonjezeka. Madzi amaundana. Chipale chofewa chimagwa m’mapiri |
Udzu umakula |
10 |
4 |
Kumazizira kwambiri. Kumagwa mvula. Chipale chofewa chimagwa m’mapiri |
Zigwa zimakhala zobiriwira. Mbewu zimachita maluwa |
11 |
5 |
Kuzizira kumachepa. Mvula imapitiriza kugwa |
Amondi amachita maluwa. Mitengo ya mkuyu imaphukira |
12 |
6 |
Kumachita mabingu ndi mvula yamatalala |
Karobu amachita maluwa. Kukolola zipatso za m’gulu la malalanje |
13 |
M’zaka 19 zilizonse anali kuwonjezera mwezi wina wapadera maulendo 7. Kawirikawiri umenewu unali mwezi wachiwiri wa Adara (Veadara) |
(Onani m’Baibulo lenileni kuti mumvetse izi)
1 NISANI (ABIBU) March—April
14 Pasika
15-21 Mkate Wopanda Chofufumitsa
16 Nsembe ya zipatso zoyamba kucha
Balere
2 IYARA (ZIVI) April—May
Pa 14 Pasika Wochitika Nthawi Yake Itadutsa (Nu 9:10-13)
Tirigu
3 SIVANI May—June
Pa 6 Chikondwerero cha Masabata (Pentekosite)
Nkhuyu Zoyambirira
4 TAMUZI June—July
Mphesa Zoyambirira
5 ABA July—August
Zipatso za M’chilimwe
6 ELULI August—September
Mphesa, Nkhuyu
7 TISHIRI (ETANIMU) September—October
Pa 1 Tsiku loliza lipenga
Pa 10 Mwambo Wophimba Machimo
Pa 15-21 Chikondwerero cha Misasa kapena kuti Chikondwerero cha Zokolola
Pa 22 Msonkhano wapadera
Kulima
8 HESHIVANI (BULU) October—November
Maolivi
9 KISILEVI November—December
Pa 25 Chikondwerero cha Kupereka Kachisi kwa Mulungu
Ziweto zili m’khola nyengo yachisanu
10 TEBETI December—January
Zomera Zikukula
11 SEBATI January—February
Amondi Wachita Maluwa
12 ADARA February—March
Pa 14, 15 Purimu
Malalanje
13 VEADARA March