6 “Gehena,” Mawu Ophiphiritsira Kuwonongeratu
Chiheberi, הנם גי (geh hin·nomʹ, “chigwa cha Hinomu”); Chigiriki, γέεννα (geʹen·na); Chilatini, ge·henʹna
Mawu akuti “Gehena” amatanthauza “chigwa cha Hinomu” chifukwa “Gehena” ndi kalembedwe kachigiriki ka mawu achiheberi akuti geh hin·nomʹ. Pa Yos 18:16, pamene pali mawu akuti “chigwa cha Hinomu,” Baibulo lachigiriki la Septuagint lili ndi mawu akuti “Gehena.” Mawuwa amapezeka m’malo 12 m’Malemba Achigiriki, kuyambira pa Mt 5:22. Baibulo la Dziko Latsopano lili ndi mawu akuti “Gehena” pamalo onse amene mawu achigirikiwo anali kupezeka m’Malemba oyambirira. Malowo ndi awa: Mt 5:22, 29, 30; 10:28; 18:9; 23:15, 33; Mko 9:43, 45, 47; Lu 12:5 ndi Yak 3:6.
Chigwa cha Hinomu chinakhala malo otayako ndi otenthako zonyansa zonse zochokera mu Yerusalemu. Mitembo ya nyama anali kuitaya kumeneko kuti ipserere ndi moto, umene anali kuusonkhezera poponyako miyala ya sulufule. Ndiponso anali kutayako mitembo ya zigawenga zimene zanyongedwa, zimene anali kuziona kuti n’zosayenera kuikidwa m’manda achikumbutso motsatira bwinobwino mwambo wake. Mitembo imeneyo ikagwera m’motowo inali kupserera, koma ikatsakamira penapake kumbali kwa chigwa chakuyacho, inkayamba kuvunda n’kudyedwa ndi mphutsi. Mphutsizi sizinali kufa mpaka zitamaliza minofu yonse, n’kusiya mafupa okhaokha.
Ku Gehena sanali kuponyako nyama zamoyo kapena anthu amoyo kuti apse kapena kuzunzidwa ayi. N’chifukwa chake mawuwa sangatanthauze malo enaake osaoneka kumene mizimu ya anthu imazunzidwa kwamuyaya m’moto weniweni, kapena kumene imangodyedwa kwamuyaya ndi mphutsi zosafa. Mitembo yoponyedwa kumeneko sinali kuikidwa motsatira bwinobwino mwambo woika munthu m’manda achikumbutso, amene anali chizindikiro cha chiyembekezo cha kuukitsidwa. Choncho, mawu akuti Gehena anagwiritsidwa ntchito ndi Yesu ndiponso ophunzira ake pophiphiritsira kuwonongedweratu, kufafanizidwa m’chilengedwe chonse cha Mulungu, kapena “imfa yachiwiri,” yosabwererako.