‘Adzasula Malupanga Awo Kukhala Zolimira’—Liti?
CHIFANIZO chodziŵika kwambiri ku United Nations ku New York City chimasonyeza munthu akusula lupanga kukhala cholimira. Chachokera pa ulosi wa m’Baibulo wa Yesaya chaputala 2, vesi 4, ndi Mika chaputala 4, vesi 3. Kodi mawuŵa adzakwaniritsidwa motani ndipo liti?
Nkhani ya posachedwapa m’nyuzipepala ya The New York Times inali ndi mutu wakuti, “Malonda Ogulitsa Zida Zankhondo Padziko Lonse Afika Madola 30 Biliyoni”! Mu 1999 kodi ndani anagulitsa zida zankhondo zambiri? Linatsogola ndi dziko la United States chifukwa linapeza madola 11.8 biliyoni. Lachiŵiri linali dziko la Russia, linapeza madola ochepera theka la madola amenewo. Komabe, dziko la Russia linapeza madola pafupifupi kuŵirikiza kaŵiri amene linapeza mu 1998. Kenako Germany, China, France, Britain ndi Italy. Nkhani yomweyi inati: “Monga kale, pafupifupi magawo aŵiri mwa atatu a zida zankhondo zonse amazigulitsa kumayiko osauka.”
Pambuyo pa nkhondo ziŵiri za padziko lonse ndi nkhondo zina zikuluzikulu za m’zaka za zana la 20, zimene zinapha ndi kuvulaza anthu ambirimbiri, munthu angafunse kuti, “Kodi anthu adzaphunzira liti kukhala mwamtendere ndi kusiya nkhondo?” Baibulo limasonyeza kuti mtendere umenewu udzakhalapo “masiku otsiriza.” (Yesaya 2:2) Ndipotu, ulosiwu unayamba kale kukwaniritsidwa, popeza anthu pafupifupi sikisi miliyoni a Mboni za Yehova alola ‘kuphunzitsidwa ndi Yehova.’ Choncho, ‘mtendere wawo wakhala waukulu.’—Yesaya 54:13.
Posachedwapa Yehova adzathetsa zida zankhondo zonse ndi nkhondo ndiponso amene amachirikiza zimenezi, popeza ‘adzawononga owononga dziko.’ Ngati mukufuna kudziŵa zambiri pankhani ya kusintha kodabwitsa kumeneku, khalani omasuka kufikira Mboni za Yehova m’dera lanu kapena lemberani kalata ku adiresi yoyenera mwa amene ali patsamba 5.—Chivumbulutso 11:18.