Anagoma Nawo Chifukwa Amatchula Mfundo Zenizeni
PULOFESA WA PAYUNIVESITE ya ku Spain analembera kalata ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ya m’dziko lakelo poyamikira Galamukani! Iye anati:
“Posachedwapa ndinalandira magazini anu aŵiri a Galamukani! Ndinaona kuti anali ndi nkhani zochititsa chidwi kwambiri zosimba zinthu zosiyanasiyana. Sindili m’chipembedzo chilichonse, koma ndinaona kuti magazini anu amatchula mfundo zenizeni. N’ngooneka mwapamwamba zedi ndipo nkhani zake n’zosakondera mbali imodzi komanso n’zolondoladi. Ndikukuthokozani kwambiri chifukwa cha ntchito imene mumachitayi.”
M’nkhani zake zambiri, Galamukani! imapereka maumboni osiyanasiyana a sayansi amene amathandiza anthu oŵerenga kupeza mayankho okhutiritsa. Umu ndi mmenenso zilili nkhani za m’bulosha la masamba 32 la mutu wakuti Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani? Mwachitsanzo, patimitu takuti “Kodi Moyo Unakhalako Mwamwayi?” ndiponso “Kulinganiza Kumafunikira Wolinganiza,” odziŵa za sayansi ya zakuthambo, ya zamoyo zimene maso satha kuona, ndiponso sayansi ya zachilengedwe amapereka umboni wogwirizana ndi nkhaniyi.
Mungathe kuitanitsa bulosha limeneli lakuti, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani?, polemba zofunika pamizera ili pansipa ndi kutumiza ku adiresi yosonyezedwapoyo kapena ku adiresi yoyenera yosonyezedwa pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Nditumizireni bulosha lakuti Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani?
□ Chonde nditumizireni munthu kuti azichita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Mlalang’amba: Mwa chilolezo cha Anglo-Australian Observatory, anajambula ndi David Malin