“Chonde Ndithandizeni! Ndinu Nokha Amene Ndikudalira”
DOKOTALA WINA wa payunivesite ya zachipatala yotchedwa Kaunas Medical University m’dziko la Lithuania anamaliza kalata yake imene analembera ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dzikolo ndi mawu amene ali pamwambawo. Dokotalayo anafotokoza kuti:
“Ndinayamba kuŵerenga buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza ndili ku ntchito. Ndinaganiza zoti ndigwiritse ntchito mfundo zimene zili m’bukuli polemba nkhani zanga zina, koma tsoka ilo, bukuli linasoŵa. N’zosakayikitsa kuti munthu wina analitenga. Zimenezi zinandidandaulitsa kwambiri chifukwa chakuti ndinali nditataya chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Chonde ndikomereni mtima ponditumizira buku linanso.
“Bukuli ndikulifuna kwambiri chifukwa chakuti ndimayendera sukulu ndipo kusukuluzo ndimacheza ndi achinyamata, choncho bukuli limandithandiza kuyankha mafunso ambiri amene achinyamatawo amandifunsa. Mukanditumizira lina, ndidzalisunga kunyumba ndipo ndidzalisamala kwambiri. Bukuli lili ndi zinthu zofunika kwambiri, n’chifukwa chake munthu wina analitenga. M’nthaŵi zovuta zino, n’kofunika kupeza zinthu zokulimbitsa kuchokera kwinakwake. Chonde ndithandizeni! Ndinu nokha amene ndikudalira.”
Buku la Achichepere Akufunsa limayankha mafunso ambiri amene achinyamata amadzifunsa, monga akuti: “Kodi Ndingachititse Motani Makolo Anga Kundipatsa Ufulu Wowonjezereka?,” “Kodi Ndiyenera Kuchoka Panyumba?,” “Kodi Ndingapange Motani Mabwenzi Enieni?,” “Kodi Ndiyenera Kusankha Ntchito Yophunziridwa Yotani?,” “Bwanji Ponena za Kugonana Ukwati Usanachitike?,” ndiponso “Kodi Ndingadziŵe Motani Ngati Chili Chikondi Chenicheni?” Imeneyi ndi mitu yochepa chabe m’bukuli. Kuti mulandire buku lanu lotere, chonde lembani zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Nditumizireni buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.